Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 6/1 tsamba 26-29
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Atenga Njira ya Moyo Yofupa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Atenga Njira ya Moyo Yofupa
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Alandira Mphatso ya Utumiki Waumishonale
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kumaliza Maphunziro kwa Kalasi ya Gileadi ya 85 Chochitika Chosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Alimbikitsidwa Kukulitsa Maluso Abwino a Kulankhulana
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 6/1 tsamba 26-29

Omaliza Maphunziro a Gileadi Atenga Njira ya Moyo Yofupa

“HA, CHOCHITIKACHI nchosangalatsa motani nanga, kumaliza maphunziro kwa kalasi ya Gileadi ya 90!” Ndi mawu amenewo, tcheyamani, Karl F. Klein wa Bungwe Lolamulira, anatsegula programu yomaliza maphunziro. Pokumbukira pamene Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower inayamba, iye anawonjezera kuti: “Kodi ndani akanalingalira, kalelo mu 1943, pamene kalasi yoyamba ya Gileadi idamaliza maphunziro kuti zaka 48 pambuyo pake tikasonkhanabe pamodzi kaamba ka kumaliza maphunziro kwa kalasi inanso​—ya 90?”

Komabe, pa March 3, 1991, tsiku lofunda kwambiri m’New Jersey, alendo oitanidwa oposa 4,000 ndi ziŵalo za banja la Beteli anasonkhana m’Holo Yosonkhanira m’Mzinda wa Jersey, kudutsa mtsinje kuchoka ku Mzinda wa New York, kaamba ka kumaliza maphunziro kwa amishonale atsopanoŵa. Asanautenge moyo waumishonale, omaliza maphunziroŵa akalandira uphungu womalizira patsiku lawo lomaliza maphunziroli.

Programu inayamba ndi nyimbo. Pambuyo pake, onse opezekapo anakhudzidwa mwakuya pamene Frederick W. Franz, pulezidenti wa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower wa zaka zakubadwa 97, anapereka pemphero lotsegulira. Ndiyeno, pambuyo pa zokambapo zotsegulira za tcheyamani, omaliza maphunzirowo​—ndi onse opezekapo​—anamvetsera mwachidwi ku mpambo wa nkhani zazifupi, ndi zogwira ntchito.

Max H. Larson wa Komiti ya Fakitale anayamba kulankhula, pa mutu wakuti “Antchito Anzake a Yehova.” Pambuyo polunjikitsa chidwi ku chingalawa chopulumukira chimene Nowa ndi banja lake anamanga, iye anati: ‘Lerolino Yehova akusonkhanitsa banja la dziko lonse la mamiliyoni ambiri, ndipo afuna kupulumutsa banja lalikulu limeneli kupyola chisautso chachikulu.’ Motani? Eya, kupyolera mwa chingalawa chamakono​—paradaiso wauzimu! ‘Inu,’ iye anakumbutsa omaliza maphunzirowo, ‘mudzapita ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi, kumene mudzakhala antchito anzake a Yehova m’kumanga chingalawa chamakono.’ Poŵakonzekeretsa kaamba ka zakutsogolo, iye anati: ‘Inu mudzafunikira kugwira ntchito. Mudzafunikira kuleza mtima. Mudzakumana ndi zopinga. Pano mpamene mudzafunikira maluso amene mwapeza m’maphunziro anu.’

Daniel Sydlik, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, posachedwapa anachezetsa amishonale okhala ndi zaka zambiri ku Japan ndi Costa Rica. Akumafutukula mutu wakuti “Njira ya Moyo Wanu Njofupa,” iye anagaŵana nawo malingaliro othandiza omwe anatenga kuchokera kwa amishonale achipambanowo. Iye anafotokoza kuti mlongo wina anapereka uphungu womwe amayi ŵake anampatsa wakuti: ‘Konda utumiki wakumunda. Khala paubwenzi ndi anthu. Gaŵana ndi ena moyo wako, ndipo kudzatanthauza chimwemwe kwa iwe.’ Mlongo winanso anati: ‘Mkati mwa zakazi, tazindikira kuti ngati sitiyembekezera zochuluka kwa ena, sitidzagwiritsidwa mwala mosavuta. Kachitidwe kalikonse ka chifundo ndi kulingalira kamene kamatidzera kamatanthauza zambiri kwa ife.’ Kugwiritsira ntchito uphungu wothandiza wotero mosakaikira kudzathandiza omaliza maphunzirowo kukhala amishonale achipambano.

“Mukhale oleza mtima pa onse,” amatero 1 Atesalonika 5:14. Leon Weaver wa Komiti ya Dipatimenti Yautumiki anathirira ndemanga palembali pamene ankalankhula pa mutu wakuti “Khalani Oleza Mtima m’Zochita Zanu Zonse.” Kodi ndani akuphatikizidwa m’mawuwo “onse” kwa amene tiyenera kusonyeza kuleza mtima? Mlankhuliyo anayankha nati: ‘Awo amene mudzapeza muutumiki wakumunda. Abale ndi alongo m’mpingo wanu watsopano. Amishonale anzanu. Awo okhala panthambi. Mnzanu wamuukwati. Inumwini.’ Kodi nkukhaliranji woleza mtima m’zochita zathu zonse? ‘Abale ndi alongo,’ mlankhuliyo anafotokoza motero, ‘kuleza mtima kumachepetsa kupsinjika ndi nkhaŵa. Kuleza mtima kumadzetsa mtendere. Kuleza mtima kumasunga chiyembekezo kukhala chamoyo. Kuleza mtima kumatithandiza kusunga chimwemwe chathu muutumiki.’

Albert D. Schroeder, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira ndi wolemba anthu woyambirira wa Sukulu ya Gileadi, anatsatirapo kulakhula. Akumalankhula pa mutu wakuti “Pitirizanibe Kutsanzira Chitsanzo Chanu​—Yesu Kristu,” iye anazika ndemanga zake pa Afilipi mutu 2. ‘Mukhale nawo mtima [“Uku kukhale kulingalira kwanu,” mawu amtsinde a NW] mkati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,’ limatero vesi 5. Mlankhuli anafotokoza kuti, ‘Ichi chimasonyeza kuti tifunikira kukhala ndi kulingalira kolinganizika, monga momwedi Yesu iyemwini analiri ndikulingalira kolinganizika.’ Kuyambira ndi vesi 6, iye kenaka anapanga kusanthula kosangalatsa, kusonyeza kuti Paulo choyamba akupereka umboni wakuti Yesu anali ndikulingalira kolinganizika (mavesi 6-8) ndiyeno anandandalitsa njira m’zimene Yehova anamfupira kaamba ka njira yake yachimvero (mavesi 9-11). ‘Imeneyi ndimbali ya mwaŵi wanu,’ iye anamaliza motero, ‘kulalikira Ambuye Yesu Kristu, kuthandiza ena kukhala ndi mtima umene iye anali nawo.’

Kodi ndimawu otsazikira otani amene alangizi asukulu ali nawo kwa ophunzira awo? Jack D. Redford analankhula pa mutu wakuti “Kulingalira Kudzakudikira.” (Miyambo 2:10, 11) ‘Pamene mupita tsopano,’ anafotokoza motero, ‘chimwemwe chanu sichidzadalira pa amene inu muli kapena zimene muli nazo kapena ngakhale chenicheni chakuti muli omaliza maphunziro a Gileadi. Chimwemwe chanu chidzadalira pa mmene mumalingalirira. Ngati musonyeza kulingalira ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso chanu, mudzakhala achimwemwe.’ Akusonyeza kufunika kwa kulingalira, iye anafotokoza kuti: ‘Chosiyanitsa pakati pa kachitidwe kabwino ndi koipa ndicho kulingalira. Chimene muganiza chimadziŵitsa chimene mudzachita.’ J. D. Redford anamaliza ndi mawu achilimbikitso kwa ophunzirawo akuti: ‘M’dziko muli anthu ambiri aluntha zedi amene amalingalira moipa, ndipo muli anthu ambiri aluntha pang’ono amene akhala olingalira aluso. Chotero pezani luso limenelo. Khalani otsimikiza mtima kugwiritsira ntchito maganizo anu. Gwiritsirani ntchito chidziŵitso chanu. Lakani mavuto. Khalani ndi unansi wabwino ndi anthu. Landirani ulamuliro. Khalani obala zipatso m’ntchito yanu. Pirirani m’ntchito yanu yopatsidwa.’

Ulysses V. Glass, wolemba anthu wa sukuluyo, anasankha mutu wakuti “Yehova Agwira Dzanja Lathu,” yozikidwa pa Salmo 37:23, 24. ‘Ndiyenera kuyamikira kalasiyi,’ iye anatero, ‘kaamba ka chikondwerero chawo m’kuphunzira.’ Iye anaŵakumbutsa za zithandizo zina zimene Yehova anapereka kuŵachirikiza​—Mawu a Mulungu, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru pansi pa chitsogozo cha Yesu kuti apereke tanthauzo ndi kumveketsa Malemba, mabuku osiyanasiyana, misonkhano yampingo ndi misonkhano yaikulu. ‘Zithandizo zimene mwagwiritsira ntchito m’maphunziro anu,’ anapitiriza motero, ‘ziri ngati ndodo yauzimu. Timazifunikira kaamba ka chichirikizo chauzimu, ndiponso zimatitheketsa kulankhula ndi ulamuliro popereka Mawu a Mulungu kwa ena.’ Pomaliza iye anali ndi uphungu uwu kwa ophunzirawo: ‘Ngati mtima wanu ngwodzala ndi chikondi kaamba ka anthu, mitima yowona idzavomereza. Mudzakhala achipambano muutumiki wanu, ndipo mudzadziŵa kuti Yehova akugwira dzanja lanu.’

Mlankhuli womalizira pa programu yam’maŵa anali Carey W. Barber wa Bungwe Lolamulira, yemwe anasankha mutu wakuti “Loŵani Pakhomo Lopapatiza.” Akuthirira ndemanga pa Luka 13:23, 24, iye anati: ‘Ambiri amafuna madalitso a moyo, koma ngochepa amene afunitsitsa kuyesetsa mwamphamvu kuti awapeze.’ Nanga bwanji ponena za ife? ‘Nkwabwino kwa ife kudzifunsa kuti, “Kodi chithunzithunzi ichi cha khomo lopapatiza chimatanthauzanji kwa ine pandekha?”’ Awo amene amalephera kuloŵa pakhomo lopapatiza amalephera, osati chifukwa chakuti nkosatheka, koma chifukwa chakuti iwo okha sali ofunitsitsa kuyesetsa mwamphamvu. ‘Yehova sakufuna zopambanitsa kwa ife,’ mlankhuliyo anafotokoza motero. ‘Ndi chithandizo cha Yehova,’ iye anamaliza motero, ‘tatiyeni tonsefe mokondwa tikankhe ndi nyonga yokwana kudzipanikiza kupyola pakhomo lopapatiza kuloŵa m’dziko latsopano la moyo wosatha, lamtendere, chimwemwe, ndi chisangalalo, kuulemerero wamuyaya wa Yehova!’

Kutsatira ndemangazi, tcheyamani anapereka moni wolandiridwa kuchokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi. Nthaŵi inali itafika tsopano yakuti omaliza maphunzirowo alandire madipuloma awo. Ophunzirawo anachokera ku maiko asanu ndi limodzi​—Canada, Finland, Jeremani, Great Britain, Switzerland, ndi United States. Komabe, ntchito yawo idzaŵapereka ku maiko onga Argentina, Benin, Bolivia, Dominican Republic, Papua New Guinea, Peru, St. Lucia, ndi Taiwan. Ndipo kodi omaliza maphunzirowo anadzimva motani patsiku lawo lomaliza maphunziro? M’kalata yochititsa nthumanzi yolembedwera Bungwe Lolamulira ndi banja la Beteli, iwo anati m’mbali yake: “Tiri achidaliro cha chichirikizo cha Bungwe Lolamulira, banja la Beteli, ndi gulu lonse la Yehova. Pamene tidzayang’anizana ndi ziyeso mtsogolo, chichirikizocho nchinthu chomwe tidzakhala nacho. Tiridi oyamikira kaamba ka chimenechi.”

Pambuyo popuma, programu yamasana inayamba ndi Phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda, lotsogozedwa ndi Karl A. Adams. Pambuyo pake, ophunzirawo anachita zitsanzo za zokumana nazo zenizeni za kufikira mtima m’kuphunzitsa Mawu a Mulungu. Pomalizira pake, onse opezekapo, kuphatikizapo omaliza maphunziro a kalasi ya 90, anasangalala ndi drama yapanthaŵi yake yamutu wakuti Peŵani Nkhaŵa za Moyo, yochitidwa ndi ofalitsa akumaloko.

Tcheyamani, Karl Klein, analankhulirako onse pamene ananena motere m’ndemanga zake zomalizira: “Ndithudi kwakhala kwabwino kwa ife kupezeka pano patsiku iri lachitatu la March 1991!” Ndiyeno programu yosangalatsa inatha ndi nyimbo yothera, yotsatiridwa ndi pemphero loperekedwa ndi Harold J. Dies.

[Bokosi patsamba 27]

Chiŵerengero cha Kalasi

Chiŵerengero cha maiko oimiridwa: 6

Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 10

Chiwonkhetso cha ophunzira: 24

Avareji ya msinkhu: 31.2

Avareji ya zaka m’chowonadi: 15

Avareji ya zaka muuminisitala wanthaŵi zonse: 11

[Chithunzi patsamba 26]

Kalasi ya Omaliza Maphunziro ya 90 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera yaŵerengedwa kuyambira kutsogolo kunka kumbuyo ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kulamanzere kunka kulamanja mu mzera uliwonse. (1) Miller, M.; Helenius, S.; Marsh, L.; Kleeman, A.; Loosli, Y.; Nizan, H. (2) Skogen, R.; Nutter, D.; Noack, E.; Diehl, L.; Hair, J. (3) Marsh, C.; Helenius, H.; Loosli, M.; Danio, A.; Danio, A.; Nizan, D. (4) Miller, L.; Noack, J.; Hair, L.; Kleeman, W.; Skogen, D.; Diehl, S.; Nutter, W.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena