Omaliza Maphunziro a Gileadi Alimbikitsidwa Kukulitsa Maluso Abwino a Kulankhulana
PA SANDE, March 4, 1990, anthu oposa 4,100 anadzaza Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ya Mzinda wa Jersey kaamba ka chochitika cha kumaliza maphunziro kwa kalasi ya 88 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Omaliza maphunziro 24 awa anachokera m’maiko 6 ndipo tsopano ankatumizidwa ku maiko okwanira 13.
Programu inayamba pa 10:00 mmawa. Pambuyo pa nyimbo, George Gangas, yemwe tsopano ngwazaka zoposa 90 zakubadwa ndipo ali chiwalo cha Bungwe Lolamulira, anatsegulira ndi pemphero lapamtima kwa Yehova. Kutsatira iri, tcheyamani, C. W. Barber, yemwe alinso chiwalo cha Bungwe Lolamulira ndipo womalizanso maphunziro a Gileadi a kalasi ya 26, anafotokoza mwachidule masinthidwe ena a mwamsanga padziko lapansi. Iye anamaliza mwakunena kuti: “Sipanakhalepo mwaŵi wabwino kwambiri chotere nkalelonse wa kukhala mboni za ukulu ndi chilungamo cha Yehova.” Atatha kutero anayamba kuitana alankhuli osiyanasiyana a programu yammawayo.
Vernon Wisegarver, chiwalo cha Komiti ya Fakitale ya ku Brooklyn, anasankha mutu wakuti “Khalani Aluso m’Ntchito Yanu.” Pofotokoza fanizo la wosula zitsulo wapamudzi yemwe anapanga unyolo wolimba kwambiri umene, ataumangirira ku nangula, unapulumutsa miyoyo ya okwera ngalawa onse m’nthaŵi ya namondwe, iye anafanizira omaliza maphunziro a Gileadi ndi munthu wosula zitsuloyo. Mwakuwaphunzitsa anthu Baibulo, adzawathandiza kupanga unyolo wa mikhalidwe yaumulungu wopulumutsa miyoyo, mwa kugwiritsira ntchito maluso omwe anapata m’maphunziro awo a Gileadi. Iye analimbikitsa omaliza maphunzirowo kupitirizabe kufutukula maluso awo ophunzitsa ndikuima pamaso pa Mfumu yaikulu koposa onse monga “antchito aluso.”
Mlankhuli wotsatira, John Barr, chiwalo cha Bungwe Lolamulira, analankhula pamutu wakuti “Lawani Ndipo wonani Kuti Yehova Ndiye Wabwino.” Mawu ake anazikidwa pa Salmo 34:8, pomwe pamati: “Talawani ndipo wonani kuti Yehova ndiye wabwino; Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.” Iye anawalangiza kuti: “Lawani chirichonse m’ntchito yanu yaumishonale. Chiyeseni. Musachiwope. Pamenepo mudzakhala okhoza kukumana ndi ubwino wa Yehova m’njira imene simunakumanepo nawo ndi kale lonse. Musakhale osankha. Musanenepo kuti, ‘Ichi sindichikonda.’ Chilaweni.”
Charles Woody, chiwalo cha Komiti ya Dipatimenti Yautumiki ya Brooklyn, anasankha kukamba pankhani yakuti “Kudzisungira Kapenyedwe Kokhazikika Ife Eni.” Iye anati: “Timasangalala kukhala ndi amene ali ndi kapenyedwe kawo kokhazikika, amene samafuna njira zawo zokha nthaŵi zonse, omwe ali ofulumira kuyamikira ndi kumangirira ena, ndi omwe, ngakhale kuti ali ndi chidziŵitso, samachititsa ena kulingalira kuti iwo alibe.” Iye analongosola mowonjezera kuti: “Monga amishonale inu mudzafunikira kukopera anthu ku chowonadi, osati kuŵakhumudwitsa. Mkhalidwe wanu wodzichepetsa udzakhala wamtengo kwenikweni pothandizira kukwaniritsa izi.”
Lyman Swingle, chiwalo cha Bungwe Lolamulira, potsatira analankhula pamutu wakuti “Machaputala Otsatira, Kodi Adzatiuzanji?” Iye anayamba mwakunena kuti: “Lalero mwayamba chaputala chatsopano mmoyo wanu. Kodi mudzalembanji m’machaputala ameneŵa kuyambira tsopano kunka mtsogolo?” Iye anawakumbutsa kuti: “Chirichonse chimene muchita chiyenera kubweretsa ulemu ndi ulemerero kwa Yehova,” ndipo iye anawonjezera kuti: “Tsimikizirani kuti zosankha zanu zazikidwa pa Mawu a Mulungu. Kumbukirani Miyambo 3:7, imene imati: “Usadziyese wekha wanzeru.” Khalani wokhulupirika pochita ntchito yanu.” Iye anamaliza mwakuti: “Tikhulupirira kuti simudzamaliza kulemba mbiri yanu, kuti mudzakhala kosatha.”
Wotsatira, Jack Redford, mmodzi wa alangizi a sukuluyo, anachonderera omaliza maphunzirowo kukhala: “Nsembe Zamoyo.” Iye anatsegula mwakunena kuti: “Utumiki waumishonale ndiwo moyo wodzipereka nsembe. . . . Timakukondani chifukwa cha mzimu wanu wa kudzipereka nsembe.” Pogwira mawu Afilipi 2:17, pamene mtumwi Paulo anati anathiridwa ngati nsembe, kutanthauza kuti anali wofunitsitsa kudzikhuthula yekha monga nsembe yamoyo, iye anafunsa kuti: “Koma kodi amishonale kaŵirikaŵiri amafanana bwanji ndi nsembe yothiridwa?” Pamenepo iye anasimba zokumana nazo ziŵiri zonena za amishonale amene anadzikhuthula okha kuposa pa zomwe zinafunikira. Mmodzi anaumba njerwa 16,000 yekha ndipo anamanga Nyumba Yaufumu yoyamba m’dziko lake logaŵiridwalo. Chokumana nacho china chinakhudza mlongo amene anapita ndi mwamuna wake kunkhalango, kumene kakhalidwe kaumoyo kanali kachikale kwambiri. Alongo onse a komweko anamuyamikira chifukwa chakuti anazindikira kuti iye anadzikhuthula yekha monga ‘nsembe yamoyo.’ Komano mlankhuliyo anawakumbutsa ophunzirawo kuti nsembe imakhala yopanda mtengo itakhala yopanda chimvero. Pogwiritsira ntchito chochitika cha Mfumu Solomo ndi Amaleki, iye anachenjeza kuti: “Kumbukirani nthaŵi zonse kuti chimvero nchabwino kwambiri koposa nsembe. Musayese kupandirana malire ndi Yehova. Nthaŵi zonse chitani chomwe akuuzani kuchita.”
Pambuyo pake tcheyamani anaitana mlangizi wina wa sukuluyo, Ulysses Glass. Mbale Glass anayamba mwakuti: “Kalasi ya 88 inali ndipo njachimwemwe. Makalasi ena analinso achimwemwe. Nangano, kodi nchifukwa ninji chimwemwe chanu chiri chapadera?” Iye anasonyeza kuti chimwemwe “sichiri chonulirapo koma chotulukapo cha ntchito zabwino. Njira yofikira apa njomwe imabweretsa mfupo.” Iye anagwira mawu mlembi wina amene moyo wake unasinthidwa pamene anawona mawu olembedwa motere: “Chipambano ndiulendo, osati komwe ukumukako.” Mlembiyo anawinda kuti akaleka kuganizira kuti chimwemwe chimapezeka pamaziko a kufika kwa munthu komwe akumukako mmalo mowona moyo wake wonse kukhala ulendo wopanda kogomera. “Palibe njira yonkira kuchimwemwe,” anatero. “Chimwemwe ndicho njira.” Pamenepo Mbale Glass anathirira ndemanga kuti kalasiyo inazindikira tanthauzo la mawuwo. Iye anamaliza ndi mawu a pa Salmo 84 ndikuti: “Pitirizani kuyenda mmalo othiriridwa bwino. Mavuto aliwonse amene mungakumane nawo, lolani kuti chimwemwe chimene chiri kwa anthu okonda ndi kuwopa Yehova chipitirizebe kukhala nanu.”
Kenaka panabwera nkhani yaikulu ya mmawamo, imene inaperekedwa ndi chiwalo china cha Bungwe Lolamulira, Karl Klein, amene anasankha mutu wakuti “Kukulitsa Kulankhulana Kwachikristu.” Iye anayamba mwakukumbutsa onse kuti Yehova ndi mlankhuli wabwino kuposa onse. Mwana wake wobadwa yekha, Logosi, anagwiritsiridwa ntchito monga Wolankhulira Wamkulu wa Yehova, ndipo anafotokoza chifuniro cha Mulungu ndi malangizo ake kwa zolengedwa za padziko lapansi. Pamene Yesu anali padziko lapansi, makamu anazizwa ndi njira yake yophunzitsira. Iwo sanamvepo munthu yemwe analankhula ngati iye. Pa Mateyu 28:19, 20, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kukhala alankhuli abwino mwakupita m’dziko, kukaphunzitsa malamulo ake kwa ena ndi kuwapanga ophunzira.
Kenaka, polankhula mwachindunji kwa amishonale amtsogolowo, Mbale Klein anati pali njira zinayi zimene amishonale ayenera kudera nazo nkhawa pokulitsa maluso awo abwino a kulankhulana: pakati pa mwamuna ndi mkazi, ndi ena m’nyumba ya amishonale, ndi okhala pa ofesi ya nthambi kumene iwo agaŵiridwa, ndi awo amene amapeza muutumiki wakumunda. “Mumayamba kulankhulana musanatsegule pakamwa panu,” anatero Mbale Klein. “Umboni wanu ndi kapesedwe zimakulankhulirani kwa mwininyumba.” Pamenepo iye anapereka mafanizo ambiri kutsimikizira mfundo yake ndipo anamaliza ndi kuchonderera uku: “Khalani ofatsa maganizo. Sungani njira zanu zolankhulana kukhala zotseguka. Kalamirani kukhala alankhuli abwino.”
Pamene miyoni yotumizidwa inaŵerengedwa, tcheyamani anapereka madipuloma a ziyeneretso kwa aliyense wa omaliza maphunzirowo. Kenaka kalasiyo inapereka chitsimikizo cholembedwera Bungwe Lolamulira ndi banja la Beteli, chinaŵerengedwa ndi Paul Angerville wa ku Guadeloupe.
Chigawo chamasana chinayamba ndi phunziro la Nsanja ya Olonda. Pambuyo pake, ophunzirawo anachita programu imene inapatsa opezekapo mwaŵi wakuwona chinachake cha kalasi lawolo, kuwona mayanjano a mzipinda zawo, ndikumva zokumana nazo zawo zambiri zakumunda chiyambire kubwera kwawo ku Gileadi miyezi isanu yapitayo. Pomalizira pake, panali drama yabwino kwambiri yokhala ndi mutu wakuti Doing What Is Right in Jehovah’s Eyes (Kuchita Zoyenera Pamaso pa Yehova) Dramayo inachitidwa ndi ofalitsa a Mpingo wa Lyndhurst, New Jersey. Zochitika patsikulo zinamalizidwa ndi nyimbo yothera, yotsatiridwa ndi pemphero loperekedwa ndi Fred Franz, prezidenti wa Sosaite wa zaka 96 zakubadwa.
[Bokosi patsamba 27]
CHIŴERENGERO CHA KALASI
Chiŵerengero cha maiko oimiridwa: 6
Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 13
Chiŵerengero cha abale osakwatira: 2
Chiŵerengero cha okwatirana: 11
Chiŵerengero cha ophunzira: 24
Avereji ya msinkhu: 32.7
Avereji ya zaka m’chowonadi: 14
Avereji ya zaka muuminisitala wa nthaŵi zonse: 9
[Chithunzi patsamba 26]
Kalasi ya Omaliza Maphunziro ya 88 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera yaŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kulamanzere kumka kulamanja mum’mzera uliwonse. (1) Magney, D.; Rogers, L.; Foster, S.; Foley, R.; Untch, L.; Jonasson, G. (2) Buri, H.; Buri, B.; Krammer, M.; Hudson, D.; Underkoffler, J. (3) Angerville, P.; Olsson, M.; Jones, A.; Untch, R.; Krammer, A.; Hudson, C. (4) Foley, L.; Magney, J.; Jones, A.; Jonasson, H.; Foster, M.; Rogers, M.; Underkoffler, R.