Nyumba Yatsopano Kaamba ka Sukulu ya Mishonale ya Gileadi
PA FEBRUARY 1, 1943, Nathan H. Knorr, yemwe kale anali prezidenti wa Watchtower Bible and Tract Society, anapereka nkhani yotsegulira ku kalasi yoyamba ya sukulu yatsopano. Iye analongosola kwa ophunzira zana limodzi amenewo kuti “sichiri cholinga cha [sukulu] imeneyi kukonzekeretsa inu kukhala atumiki oikidwa. Inu muli kale atumiki ndipo mwakhala okangalika mu utumiki kwa zaka zingapo. . . . Kosi ya kuphunzira imeneyi . . . iri kaamba ka chifuno chotheratu chokukonzekeretsani inu kukhala atumiki okhoza mowonjezereka.” Kufikira tsiku lino Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ikupitirizabe kuphunzitsa atumiki kaamba ka ntchito ya umishonale ku maiko achilendo.
Kubwerera mu 1943, Sukulu ya Gileadi inali pa gawo la Finger Lakes mu New York State. Gileadi inakhalabe kumeneko kwa zaka 17. Kenaka, mu 1961, iyo inaikidwanso mu Brooklyn. Kaamba ka chifuno chotani? Dongosolo la maphunziro a Gileadi nthaŵi zonse lakonzedwa kufikira zosoŵa za gulu. Chifuno cha kukulitsa ndi kulinganiza kwabwino kwa ziwiya za nthambi kuzungulira pa dziko lonse lapansi chaitanira kaamba ka chilangizo chokulira kwa ophunzirawo choperekedwa ndi ziŵalo zogwira ntchito pa malikulu a Mboni za Yehova, okhala mu Brooklyn. Chotero kwa zaka zingapo, chigogomezero chinali pa kuphunzitsa ogwira ntchito pa nthambi. Pambuyo pa chimenecho, chisamaliro chinasumikidwanso pa ntchito ya umishonale.
Kwa zaka 27 zotsatira, mu 1961 mpaka 1988, ophunzira a Sukulu ya Gileadi asangalala ndi mwaŵi wa kukhala ndi kuphunzira pakati penipeni pa ogwira ntchito pa malikulu mu Brooklyn. Kumeneko ophunzirawo anapindula kuchokera ku kuyanjana kwathithithi ndi ziŵalo za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi atumiki ena ozoloŵera. Kodi ndi m’njira yabwinopo yotani yophunzirira mmene nthambi ya Watch Tower Society imagwirira ntchito? Ophunzirawo anapindula osati kokha kuchokera m’kuphunzira m’kalasi komanso kuchokera m’kuwona ogwira ntchito pa malikulu akugwira ntchito tsiku lirilonse.
Kodi ndi chiyambukiro chotani chimene Sukulu ya Gileadi yakhala nacho pa ntchito ya kulalikira ya mitundu yonse? Pa agwirizanitsi a komiti ya nthambi 93 otumikira kusunga ntchito yolinganizika dziko lonse, 74 ali omaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi. Ichi chimalankhula bwino kaamba ka kuphunzitsidwa kwabwino koposa kumene amuna amenewa amalandira kaamba ka kusamalira thayo lolemera la kuŵeta anthu a Mulungu lerolino. Oyang’anira oyendayenda osaŵerengeka omwe tsopano akutumikira zosoŵa za gulu alinso omaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi. Inde, programu yophunzitsa pa Sukulu ya Gileadi yayenda pa liŵiro lofanana ndi zosoŵa za gulu.
Gileadi Isamuka kuchoka mu Brooklyn
Kachiŵirinso, ngakhale kuli tero, chigamulo chinapangidwa cha kusamutsa Sukulu ya Gileadi. Chotero mu chirimwe cha 1988, magalimoto anayi odzaza ndi mipando ndi ziŵiya zina za ofesi anafika panyumba yachitatu ya Gileadi—Watchtower Farms, yokhala mu Wallkill, New York. Mkati mwa kokha miyezi iŵiri, ogwira ntchito okonza zinthu pa Watchtower Farms anakonza zipinda zophunziriramo zabwino, laibulale, ndi maofesi kaamba ka sukuluyo. Ena anagwira ntchito usana ndi usiku kukonzekeretsa ziwiya za sukulu pa nthaŵi yake kaamba ka kalasi yotsatira yodzayamba kuphunzira kwawo.
Pa October 17, 1988, kalasi ya 86 ya Gileadi inayamba. Popanda kuphonya kulikonse, sukuluyo inapitiriza chifuno chake cha ‘kuphunzitsa amuna ndi akazi kukhala atumiki okhoza mowonjezereka.’ M’malo ake atsopano okongola pa Watchtower Farms, zina za zokometsera za sukulu yoyambirira m’chigawo cha Finger Lakes zinabwezeretsedwa.
Kalasi ya 86 Imaliza Maphunziro
Pa March 5, 1989, ogwira ntchito onse pa malikulu a Watchtower mu Brooklyn ndi Watchtower Farms anakumana pamodzi mu Jersey City Assembly Hall kugawanamo m’kumaliza maphunziro kwa kalasi ya 86. Daniel Sydlik, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, anatsegula programu ndi pemphero. Karl Klein wa Bungwe Lolamulira anatumikira monga tcheyamani. M’mawu ake oyamba, iye anasonyeza kusiyana pakati pa amishonale ogwira ntchito m’maiko achilendo a Chikristu cha Dziko ndi aja a Mboni za Yehova. Ndi mwachipambano chotani nanga mmene amishonale ophunzitsidwa pa Gileadi akhalira m’kuphunzitsa chowonadi cha Mawu a Mulungu m’maiko onga Japan, kumene kuli tsopano Mboni zoposa 131,000 zogawanamo mokangalika mu utumiki wa m’munda!
Ndi mutu wakuti “Lolani Ntchito Zabwino Zikhale Chizindikiritso Chanu,” Donald Krebs analongosola mbali yokulira imene amishonale a Gileadi aichita m’kuwonjezeka kwa dziko lonse kwa gulu la Yehova. “Ntchito zanu zabwino m’munda wa umishonale monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu zidzakhala . . . chizindikiritso chanu chosiyanitsa. Tikukulimbikitsani inu kugwira ntchito mwamphamvu. Yehova adzadalitsa molemerera zoyesayesa zanu.”
George Gangas, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, anapereka nkhani yodzetsa nthumanzi pa mutu wakuti “Baibulo Liri Bukhu Labwino Koposa Pansi pa Nthambo.” Iye anachenjeza omaliza maphunzirowo kuti: “Musaiwale kuphunzira Baibulo. Baibulo liri lodzaza ndi miyala ya mtengo wake yauzimu . . . yomwe imawala ndi kung’anima. Wina amene amayamikira iyo amafuna kuyang’ana iyo mobwerezabwereza ndi kusangalala ndi mikhalidwe yake yong’anima.”
Mutu wa Richard Eldred unali wakuti “Inu Mungapange Kusiyana.” Pamene amishonale atsopano akukhudza miyoyo ya anthu ena, iwo angapange kusiyana kwabwino. Amuna ndi akazi m’nthaŵi zakale onga ngati Davide, Nehemiya, Debora, ndi Abigayeli anali ndi chisonkhezero chabwino pa ena mwa kusamalira mozama kaamba ka iwo, kusungirira chikhulupiriro chawo cholimba mtima, ndi kusonyeza mkhalidwe wofatsa, wauzimu.
“Ŵerengerani Madalitso Anu” anali mawu a Lyman Swingle, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, ku kalasi yomaliza maphunziroyo. Pambuyo pa kuŵerengeranso madalitso oŵerengeka amene kalasiyo inakhala nawo, onga ngati kukhala okhoza kuthera miyezi isanu m’kuphunzira Baibulo kosumika maganizo, iye anawalimbikitsa iwo kuti: “Pamene mapeto akuyandikira, mungapeze liŵirolo likufulumira, msewu ukukhala woipirako, ndipo njira ikutsetserekerako. Koma tsimikizirani kuti simutopa, kuti simuleka, kuti simukhala oimira panjira.”
Mmodzi wa alangiziwo, Jack Redford, anakulitsa mutu wakuti “Musalole Mphamvu Yanu Kukhala Chifooko.” Wozikidwa pa uphungu wa Solomo, “Usapambanitse kukhala wolungama,” iye anachenjeza za kudalira mopambanitsa pa maluso aumwini m’malo mwa kuyedzamira pa Yehova. (Mlaliki 7:16, 17) “Zikhoterero zabwino zomwe zikuchitidwa mopambanitsa zingakhale phompho.” Mwachitsanzo, wina amene mphamvu yake iri lamulo ndi dongosolo angatenge chikhoterero choterocho monkitsa mwa kukhala wowuma mutu. Mwakutero, iye anapereka uphungu uwu kwa kalasiyo: “Tonsefe tiyenera kukhala ozindikira za zofooka zathu, koma tiyeneranso kukhala ozindikira za nyonga zathu. Khalani olungama koma osati odzilungamitsa. Yedzamirani pa Yehova. Pangani Yehova kukhala nyonga yanu.”
Ulysses Glass, mlangizi ndi wolembetsa wa sukuluyo, analongosola mawu a Yesu, “Senzani goli langa.” (Mateyu 11:29, 30) Pano Yesu anali kuitana ophunzira ake ‘kutenga goli lake’ limodzi naye. Iye sanafune kuwalemetsa iwo. Iye anali ndi zosoŵa za ena choyambirira m’maganizo ake. Iye anasonyeza kudzichepetsa. Iye sanazunze ophunzira ake. Yesu ananena kuti, “Phunzira kwa iye.” M’mishonale ayenera kukhala ndi maganizo a Kristu. Mlankhuli ameneyu anayamikira kalasiyo kaamba ka mzimu wawo wa kupatsa ndi kuwalimbikitsa iwo kupitirizabe kusonyeza mzimu umodzimodziwo m’magawo awo achilendo.
Pamene gawo la m’mawa linayandikira kumapeto, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira Carey Barber anapereka nkhani yodzutsa maganizo pa mutu wakuti “Kututa Kuli Mapeto a Dongosolo la Kachitidwe ka Zinthu.” Iye anakokera chisamaliro ku kukwaniritsidwa kwamakono kwa fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole. (Mateyu, mutu 13) Choyamba, odzozedwa a Kristu akusonkhanitsidwa. Kenaka, makamaka chiyambire chaka cha 1935, nkhosa zina zagwirizana nawo ‘m’kututidwa.’ Sukulu ya Gileadi yakwaniritsa ntchito yozizwitsa m’kuthandiza kututa ophunzira a Kristu.
Pambuyo pakuti omaliza maphunziro anapatsidwa madipuloma awo, mmodzi wa chiŵerengero chawo anaŵerenga kalata yabwino yolongosola kudzimva kwawo ponena za kuphunzira ndi chisamaliro chimene analandira kuchokera kwa alangizi ndi banja la Beteli. Mbali yake, kalatayo inanena kuti: “Chikondwerero chanu mwa ife osati kokha monga kalasi ya Gileadi koma monga munthu aliyense payekha chatikondweretsa ndipo chiri njira yoyenera kutsanzira. Tiri ndi malingaliro osakanizika kuti tikulekana—achisoni kuchoka chifukwa tidzasowa kukhalapo kwanu koma achimwemwe ndi osangalatsidwa ponena za gawo lathu latsopano.”
Kaamba ka programu ya masana, omaliza maphunzirowo anatengamo mbali m’Phunziro la Nsanja ya Olonda lotsogozedwa ndi Ralph Walls. Kenaka kalasiyo inachitira chitsanzo nsonga zazikulu zina za zokumana nazo zomwe anakhala nazo mu utumiki wa m’munda mkati mwa kukhala kwawo pa Watchtower Farms. Komiti Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira inapereka programu ya zisonyezero yokhala ndi mutu wakuti “Ulemu kaamba ka Ulamuliro Umapititsa Patsogolo Umodzi” ndi kuperekedwa kwa zithunzithunzi kosonyeza chimwemwe chimene amishonele m’maiko ena agawanamo mkati mwa zaka. Programuyo inatha ndi pemphero lokhudza mtima ndi Frederick Franz, prezidenti wa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower wa zaka 95 zakubadwa.
Ndi chivomerezo chawo chotenthedwa maganizo ku programuyo, awo opezekapo anasonyeza kuchirikiza kwawo oyembekezera kukhala amishonalewo ndi chiyamikiro kaamba ka programuyo. Nchosakaikiritsa kuti omaliza maphunziro 24 a kalasi ya 86 ya Gileadi ali ogamulapo kupanga Yehova nyonga yawo pamene akupita ku magawo awo a mwaŵi m’munda wa umishonale.
[Bokosi patsamba 21]
KUIMIRIDWA KWA OPHUNZIRA
Chiŵerengero cha okwatirana: 12
Chiŵerengero cha ophunzira: 24
Chiŵerengero cha maiko amene ophunzira anachokerako: 6
Chiŵerengero cha maiko ogawiridwako: 12
Avereji ya zaka zakubadwa: 32.3
Avereji ya zaka m’chowonadi: 14.1
Avereji ya zaka mu utumiki wa nthaŵi zonse: 9.1
[Chithunzi patsamba 23]
Kalasi Yomaliza Maphunziro ya 86 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
Mu ndandanda iri pansipa, mizera yaŵerengedwa kuchokera kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kumanzere kupita ku lamanja mu mzera uliwonse.
(1) Parrott, R.; Imig, E.; Benig, G.; Bengtsson, E.; Baart, W.; Ihander, K. (2) Lewis, J.; Hilario, L.; Lindmark, A.; Antoncich, C.; Agurs, C. (3) Bengtsson, R.; Parrott, J.; Benig, J.; Imig, J.; Baart, A.; Rissell, S. (4) Rissell, M.; Lewis, L.; Antoncich, M.; Hilario, R.; Agurs, H.; Lindmark, L.; Ihander, J.