Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 6/1 tsamba 22-24
  • Kalasi ya 84 ya Gileadi—Kukhalira Moyo ku Ziyembekezo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalasi ya 84 ya Gileadi—Kukhalira Moyo ku Ziyembekezo!
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Nyumba Yatsopano Kaamba ka Sukulu ya Mishonale ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi—“Amishonale Enieni!”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 6/1 tsamba 22-24

Kalasi ya 84 ya Gileadi​—Kukhalira Moyo ku Ziyembekezo!

MIYAMBO 10:28 imanena kuti: “Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe.” Mmenemo ndi mmene zinaliri pa mmawa wa March 6, 1988. Chinali chachidziŵikire kwa wopenyerera aliyense kuti ziyembekezo zinali kuwonjezereka pakati pa 4,360 osonkhana pa Jersey City Assembly Hall ya Mboni za Yehova.

Chenicheni chakuti banja lonse la Beteli la pa Brooklyn ndi Watchtower Farms linakhoza kukhala pamodzi m’makhazikitsidwe okongola oterowo chinali mwa icho chokha chopangitsa cha chimwemwe ndi chikondwerero chachikulu! Ngakhale kuli tero, awo omwe analipo anabwera m’chiyembekezo cha zowonjezereka kuposa kugwirizana kwa banja kwakukulu. Choyambirira kwenikweni m’malingaliro awo chinali chimene iwo anadziŵa kuti chidzakhala chochitika chopanga mbiri: kumaliza maphunziro kwa kalasi ya 84 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower.

Yoikidwa tsopano pa malikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova mu Brooklyn, New York, Gileadi inakhazikitsidwa mu 1943 kuti ipititse patsogolo ntchito yoikidwa ndi Mulungu ya ‘kupanga ophunzira.’ (Mateyu 28:19, 20) Pambuyo pa kumaliza kuphunzira kwa miyezi isanu kwa maphunziro a Baibulo, omaliza maphunziro a Gileadi amatumizidwa, osati ku ntchito zobweretsa phindu, koma m’munda wa dziko lonse monga amishonale. (Mateyu 13:38) Momvekera, chotero, aliyense wokhala ndi mwaŵi wopezeka pa Gileadi ali ndi ziyembekezo zapamwamba.​—Yerekezani ndi Luka 12:48.

Programu ya kumaliza maphunziroyo mwamphamvu inabweretsa ziyembekezo zimenezi pa malo owonekera bwino. Inatsegulidwa ndi pemphero lachangu ndi George Gangas, chiwalo cha Bungwe Lolamulira. C. W. Barber, nayenso wa Bungwe Lolamulira, anatumikira monga tcheyamani tsiku limenelo. ‘Tikudziloŵetsa m’ndawala yokulira koposa ya maphunziro m’mbiri,’ anatero Barber. Akumatenga mawu kuchokera ku Yesaya mutu 6, iye analongosola kuti kaŵirikaŵiri tiyenera kulalikira pansi pa mikhalidwe yaukali. Ndipo mofanana ndi tsiku la Yesaya, kokha chiŵerengero chophiphiritsira cha “chikhumi,” kapena “otsalira,” angavomereze ku uthenga wathu. (Yesaya 6:13; Aroma 9:27) Sitiyenera nkomwe, ngakhale kuli tero, kudzimva kuti zoyesayesa zathu za kulalikira ziri zosaphula kanthu!

Ndemanga zolimbikitsa zimenezi zinadzutsa chiyembekezo kaamba ka chomwe chikatsatira: mpambo wa nkhani zachidule, koma zamphamvu, zolunjikitsidwa kwa omaliza maphunzirowo. Calvin Chyke wa Komiti ya Fakitale anayamba mwa kufunsa funso lakuti, ‘Kodi mudzatsimikizira kukhala dalitso kwa ena?’ Iwo alandira madalitso ambiri pa Gileadi. Tsopano iwo ayenera kupereka madalitso, kupereka ‘mphatso zauzimu’ kwa ena. (Aroma 1:11, 12) Ngakhale pamene mikhalidwe yoyesa ibuka, monga ngati kukhala opanda ndalama zokwanira, amishonale ayenera kupitiriza “kupatsa” mwauzimu. (Luka 6:38) Kenaka mawu a Masalmo 84:6 adzakwaniritsidwa kwa iwo: “Ngakhale ndi madalitso mlangizi amadzikuta iyemwini” (NW).

David Olson wa mu Komiti ya Service Department potsatira anakumbutsa amishonale za ubale wathu wa dziko lonse. Kwa miyezi isanu iwo anasangalala ndi chikondi ndi chirikizo la anzawo a m’kalasi imodzi​—kokha kuti abalalitsidwe pa dziko lonse. Olson anatsimikizira iwo kuti adzasangalala ndi kukwaniritsidwa kwa Marko 10:29, 30, amene amawalonjeza iwo mabwenzi atsopano ndi ‘mabanja.’

Daniel Sydlik wa Bungwe Lolamulira anagogomezera kufunika kwa omaliza maphunzirowo ‘Kukulitsa Ziyembekezo Zazikulu ndi Zoposa.’ Yehova anatilenga ife ndi kuthekera kwa kukhala ndi ziyang’aniro, ziyembekezo, ndi maloto. Chotero, kodi amishonale sayenera kukhala ndi ziyang’aniro zapamwamba kaamba ka iwo eni? ‘Ikani chonulirapo, pangani zilamuliro pa inu eni!’ anachenjeza tero Sydlik. ‘Dziwani chinenero cha dziko limene mwagawiridwako. Sungilirani makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’chinenero cha makolo anu kuti musungilire uzimu wanu. Pamene mukuphunzitsa ena,’ anapitiriza tero Sydlik, ‘ikani ziyang’aniro zapamwamba kaamba ka iwonso. Aloleni iwo kudziŵa kuti chikuyembekezedwa kuti iwo adzapezeka pa misonkhano ndi kukonzekera maphunziro pasadakhale.’

Alankhuli otsatira anapitiriza m’dongosolo limeneli. Lyman Swingle, nayenso wa Bungwe Lolamulira, anakumbutsa ophunzirawo: ‘Yesu Kristu ndi mmodzi amene akukutumizani inu. Ndipo iyeyu iyemwini anali mmodzi amene anatumizidwa m’munda wachilendo pano pa dziko lapansi.’ Mofanana ndi Yesu, amishonale ayenera kutenga thayo lawo mosamalitsa. Ngakhale kuli tero, iwo sayenera kudzitenga iwo eni mosamalitsa koposa. ‘Khalani ndi kuthekera kwa kudziseka inu eni pamene muchita chinachake chopusa,’ anatero Swingle. ‘Mlaliki 3:4 amatikumbutsa ife kuti pali nthaŵi ya “kuseka.”’

Alangizi aŵiri oyambirira a sukuluyo tsopano anali ndi mwaŵi wa kupereka kwa ophunzira awo chenjezo lomalizira. Mutu wa Jack Redford unali wakuti ‘Musaiwale Ntchito Yanu!’ Atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko ataya lingaliro la ntchito yawo, ambiri akumakhala odziloŵetsa m’ndale zadziko. Yesu Kristu, ngakhale kuli tero, anakwaniritsa ntchito yake yolalikira, sanasokeretsedwe nkomwe ndi zimene dziko la Satana linali nazo zopereka. Amishonale chotero nthaŵi zonse ayenera kukumbukira chifukwa chimene iwo anatumizidwira​—kudyetsa mtundu wa anthu wa njala mwauzimu. (Yerekezani ndi Mateyu 9:36.) Iwo chotero ayenera kupewa misampha ya kukondetsa zinthu zakuthupi ndi mkhalidwe wa chisembwere. Mwa kulunjika chidwi pa ntchito yawo yolalikira, iwo ali ndi chiyembekezo cha kusangalala ndi zokumana nazo zabwino zambiri m’munda!

U. V. Glass anatsatira ndi fanizo lokhudza chikho cha madzi ndi chingwe cha miyala ya mtengo wapatali. M’maiko ambiri kuyera kwa chikho cha madzi kuli kokaikirika. Mofananako kungakhalenso kuwona kwa chingwe cha miyala ya mtengo wapatali. ‘Bwanji ponena za kukhulupirika kwanu?’ anafunsa tero Glass. ‘Kusoweka kwa kukhulupirika kwatchedwa “wowononga wachete wa maunansi.”’ Ndimotani mmene omaliza maphunziro angakhazikitsire kukhulupirika kwawo? ‘Lankhulani chowonadi,’ anatero Glass, ‘osati kuchidetsa icho kapena kuchikhotetsa. Umphumphu uli maziko a kukhulupirika.’​—Aefeso 4:25.

Mfundo yaikulu ya mmawamo inali nkhani yomalizira ndi prezidenti wa zaka 94 zakubadwa wa Watch Tower Society, F. W. Franz. Mu liwu lomwe lidakali lolimba ndi lamphamvu, Franz anabwereramo mu mbiri ya Gileadi. Mkati mwa nkhondo ya dziko yachiŵiri, Bungwe Lolamulira linafikira pa kuzindikira kuti ‘Nkhondo ya Dziko II sikatsogolera ku Armagedon. Ikatha ndipo nyengo ya mtendere ikatsatira.’ Gileadi inakhazikitsidwa kuti itenge mwaŵi wa nyengo yampumulo imeneyi​—ndipo yakhala ikupitabe patsogolo mwamphamvu kuyambira nthaŵiyo! ‘Tikukhala m’nthaŵi yoyanjika ya nthaŵi zonse!’ anafuula tero prezidenti wa Sosaite. Gulu linasonyeza chiyamikiro chake kaamba ka chenjezo limeneli loperekedwa ndi mtumiki wa nthaŵi yaitali wa Yehova mwa kuwomba m’manja!

Nsalu zochinga tsopano zinatsegulidwa, kuvumbulutsa ophunzira 24 a kalasi ya 84 ya Gileadi atakhala pa pulatiformu. Ngakhale kuti iwo ali ndi avereji ya zaka zakubadwa 31.6, iwo sali alaliki atsopano. Nkulekelanji, popeza iwo ali ndi avereji ya zaka 11.3 za kulengeza kwa nthaŵi yonse! Ndipo iwo ali gulu la mitundu yonse, akumalengeza kuchokera ku Netherlands, Australia, Finland, Sweden, Germany, ndi United States. Ndi thandizo la A. D. Schroeder, yemwe anali mmodzi wa alangizi oyambirira a Gileadi, C. W. Barber anapereka kwa iwo madipuloma awo. Gulu linakondweretsedwa kudziŵa kuti omaliza maphunzirowo adzatumizidwa ku maiko asanu ndi anayi Philippines, Sierra Leone, Western Samoa, Taiwan, Tanzania, Papua New Guinea, Bolivia, Guam, ndi Colombia! Kenaka kalata yabwino ya chiyamikiro inaŵerengedwa ndi mmodzi wa ophunzirawo m’malo mwa kalasiyo.

Pambuyo pa kupumula kwa pa chakudya chamasana kwachidule, khamulo linasonkhananso kaamba ka Phunziro la Nsanja ya Olonda lofupikitsidwa, lotsogozedwa ndi Robert Wallen wa Komiti ya Beteli. Pambuyo pa kumaliza phunzirolo, kuwala kwa magetsi kunachepetsedwako. Tcheyamani wa programu anafulumiza gulu kuti: ‘Pumulani ndipo sangalalani ndi mphatso ya ophunzirawo kwa inu, programu ya ophunzira ya kalasi ya 84, yokhala ndi mutu wakuti “Lemekezani Utumiki Wathu.”’

Kupyolera m’nyimbo, zokumana nazo, ndi zisudzo, ophunzirawo tsopano anapereka kayang’anidwe ka mkati ka ophunzira ndi moyo wa umishonale. Chinasonyezedwa, mwachitsanzo, mmene gawo lalikulu lolalikira la Mzinda wa New York limagwiritsiridwa ntchito monga maziko ophunzitsira a umishonale. Chisudzo chimodzi choseketsa, chozikidwa pa zokumana nazo zenizeni za ophunzira a ku Gileadi, chinasonyeza mmene ophunzira amaphunzirira kupereka umboni wa mwamwaŵi wokhutiritsa pa timisewu ta mzindawo. Ndiponso zochitiridwa chitsanzo m’njira yosangalatsa, koma yeniyeni, zinali zochitika za amishonalewo akumapanga masinthidwe ovuta ku kakhalidwe ka anthu ndi miyambo ya ku malo achilendo.

M’mishonale mmodzi womaliza maphunziro anafupikitsa programuyo bwino lomwe, mwa kunena kuti: ‘Ndi njira yabwinopo yotani ya kulemekeza utumiki wathu yoposa kuthandiza ena kuika chidaliro chawo chotheratu pa Mawu a Yehova?’ Mosakaikira kwa onse opezekapo anasonkhezeredwa kulingalira mmene iwo angakhalire ndi kugawanamo kokulira kwaumwini mu ntchito yolalikira. Monga chotsirizira, ophunzirawo kenaka anapereka chitsanzo chamakono chogogomezera kufunika kwa ife kudzigonjetsera ife eni kwa Mulungu. Chochitika china chopanga mbiri chinafika kumapeto ndi pemphero loyamikira la J. E. Barr wa Bungwe Lolamulira.

Mosakaikira, programu ya kumaliza maphunziro a Gileadi inakhalira moyo ku ziyembekezo. Bwanji, ngakhale kuli tero, ponena za kalasi lomaliza maphunzirolo? Tiri ndi chidaliro kuti, mofanana ndi anzawo a patsogolo, gulu laposachedwa limeneli la omaliza maphunziro a umishonale lidzakhalira moyo kuposa ku chimene chikuyembekezeredwa, inde, kulamulidwa kuchokera kwa iwo, ndi Yehova​—kuti alemekeze utumiki wawo m’magawo awo achilendo!

[Chithunzi patsamba 24]

Kalasi Yomaliza Maphunziro ya 84 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizere yaŵerengedwa kuchokera kutsogolo kupita kumbuyo ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kumanzere kupita kulamanja mu mzere uliwonse.

(1) Norberg, C.; Holmes, T.; Holland, J.; Vehlen, B.; Rector, D.; Thomas, K. (2) Rajalehto, T.; Rajalehto, T.; Hoefnagels, J.; Moonen, A.; Summers, C.; Wahl, H. (3) Holland, J.; Holmes, F.; Hoefnagels, H.; Koivula, V.; Moonen, M.; Thomas, B. (4) Wahl, M.; Rector, W.; Summers, G.; Keighley, P.; Vehlen, P.; Norberg, O.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena