Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 12/1 tsamba 21-23
  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Nyumba Yatsopano Kaamba ka Sukulu ya Mishonale ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Madalitso a Maphunziro a Gileadi Afalikira Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Maphunziro a Gileadi m’Chikhulupiriro Choyeretsetsa
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 12/1 tsamba 21-23

Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse

MWEZI wa September uli nthaŵi yotuta kwa alimi, koma ntchito yotuta yofunika koposa inakopa khamu lalikulu kupita ku Holo Yosonkhanira ya Mboni za Yehova ku Jersey City, kutsidya lina la Mtsinje wa Hudson kuchokera ku mzinda wa New York, pa September 8, 1991. Kalasi la 91 la Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower linali kumaliza maphunziro. Ziŵalo za banja la Beteli zokwanira 4,263 ndi alendo oitanidwa anali kumeneko, ndi ena okwanira 1,151 olunzanitsidwa ndi nsambo za telefoni ku malikulu ku Brooklyn ndi ku famu ku Wallkill ndi ku Patterson.

Prezidenti wa Sukulu ya Gileadi, Frederick W. Franz, wazaka zakubadwa pafupifupi 98, anatsegula programuyo ndi pemphero laulemu logwira mtima. Albert D. Schroeder, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira ndi yemwe kale anali wolembetsa ndi mlangizi wa sukuluyo, anatumikira monga tcheyamani wa programu ya kumaliza maphunziroyo. Anakumbutsa gululo za Salmo 2:1, 2 ndi maulosi ena omwe amaneneratu za nthaŵi ino ya kugwedeza ndi kupokosera pakati pa amitundu. Mkhalidwe wosokonezeka umenewu watanthauza kutsegulidwa kwa minda yambiri yatsopano kaamba ka ntchito yotuta.

Nkhani yoyambirira patsikulo inaperekedwa ndi George M. Couch, chiŵalo cha Komiti ya Beteli. Mutu wa nkhani yake unali wakuti “Ŵerengerani Madalitso Anu.” Iye anakumbutsa ophunzira a Gileadiwo kuti sikungakhale kufulumira kwenikweni kuyamba chizoloŵezichi. Iye anathirira ndemanga kuti ophunzira enieniwo anadalitsidwadi koma kuti madalitso amenewo anafika kokha pambuyo pa ntchito yovuta yaikulu. Mofananamo, Yakobo wazaka 97 zakubadwa analimbana usiku wonse ndi mngelo​—zonsezo kuti alandire dalitso. (Genesis 32:24-32) Mbale Couch anafulumiza ophunzirawo kusaganizira pa malingaliro oipa koma kukhala dalitso kwa ena mwakukulitsa mtendere wa maganizo kupyolera mwa pemphero ndi kutsimikiza mtima.

John E. Barr wa Bungwe Lolamulira analankhula pa mutu wotsatira wakuti “Khalani Nacho Chikondano mwa Inu Nokha.” Otsatira a Yesu anali ofunitsitsa kuferana. “Kodi mumachimva chikondi choterocho m’mitima yanu?” iye anawafunsa ophunzirawo. Iye anati: ‘Popanda chikondi chimenechi, sitiri kanthu. Chimenechi ndicho chowonadi chenicheni cha nkhaniyo.’ (1 Akorinto 13:3) Mbale Barr anandandalitsa njira zina zothandiza zosonyezera chikondi. Iye analimbikitsa ophunzirawo kuchitira amishonale anzawo mwaulemu, nthaŵi zonse kufuna njira yochenjera yonenera zinthu. ‘Nyalanyazani kusamvana kwakung’ono,’ iye anawalangiza motero, akumagwira mawu 1 Petro 4:8. Iye anadziŵitsa kuti ngakhale masiku ophika a amishonalewo akhoza kukhala zochitika zosonyeza chikondi mwakuwona ntchitoyo kukhala yofunika osati utumiki wamba. Iye anawakumbutsa ophunzirawo kuti: “Sitimaleka konse kukhala ndi mangawa a chikondi kwa abale ndi alongo athu.”​—Aroma 13:8.

“Kodi Ndinu Achidaliro Motani?” ndiwo unali mutu wankhani yosangalatsa yokambidwa ndi David A. Olson wa Dipatimenti ya Komiti Yautumiki. Iye anagogomezera mbali ziŵiri zachidaliro: mwa Yehova ndi gulu lake, ndipo tiri ndi zifukwa zambiri zokhalira ndi chidaliro mwa iye ndi gululo (Miyambo 14:6; Yeremiya 17:8); ndi mwa ife eni. Amishonale ali ndi chifukwa chokhalira ndi mlingo wakutiwakuti wa chidaliro chaumwini, monga ngati makulidwe awo monga aminisitala ndi chidaliro chimene Yehova ndi gulu lake aika pa iwo. Mtumwi Paulo anasonyeza chidaliro choterocho kaamba ka zifukwa zofananazo. (1 Akorinto 16:13; Afilipi 4:13) Komabe, Mbale Olson anachenjeza za chidaliro chopambanitsa chimene dziko limachilikiza, monga momwe kwachitiridwa chitsanzo ndi wolemba nkhani wotchuka amene akusimbidwa kuti anati: “Kaŵirikaŵiri ndimadzigwira mawu. Kumakometsera kakambidwe kanga.” Komabe, chidaliro cholinganizidwa ndi kudzichepetsa chingapangitse chidaliro mwa ena. Izi zinalidi zowona m’nkhani ya Paulo.​—Afilipi 1:12-14.

Lyman A. Swingle wa Bungwe Lolamulira analangiza ophunzirawo kuti: “Omaliza Maphunziro a Gileadi Inu, Pitani Kuminda Yofunikira Kututa!” Iye anati ili nditsiku lotuta la Sukulu ya Gileadi ndi ubale wapadziko lonse, popeza kuti omaliza maphunzirowo adzapita kukagwirizana ndi zikwi za omaliza maphunziro akale amene adakali m’ntchito yaumishonale​—ena ochokera ku kalasi loyamba, lachiŵiri, ndi lachitatu a m’ma 1940! Mbale Swingle anathirira ndemanga kuti kalelo palibe aliyense anadziŵa kuti ntchito yaumishonale ikapitiriza kwa zaka zina 50, kapena kuti Chinazi, Chifasizimu, ndi zotsekereza zina zaboma za ntchito yolalikira zikagwa. Iye anafunsa kuti: “Ngati tikudabwitsidwa ndi zimene Yehova anachita kalelo, kodi mtsogolo mudzabweretsanji?” Iye anamaliza ndi chiitano chodzutsa maganizo kwa ophunzirawo kuti: “Pitani kumunda!”

Ndiyeno alangizi aakulu aŵiri a Sukulu ya Gileadi analankhula ndi kalasi la 91 kwa nthaŵi yomaliza. Jack D. Redford analankhula pa mutu wakuti “Tengani Nzeru.” Iye anauza ophunzirawo kuti Sukulu ya Gileadi imaphunzitsa chidziŵitso ndi luntha, koma ayenera kutenga nzeru, luso lakugwiritsira ntchito chidziŵitso chawo m’njira yolondola. Iye anafulumiza ophunzirawo kutaya lingaliro lakuti anaphunzira zonse zofunikira pa Gileadi. “Ziri zimene mumaphunzira pambuyo pa sukulu zimene ziri nkanthu.” Pakati pa zinthu zimene adzayenera kuphunzirabe pali: kuchita mwamtendere ndi anthu, kukhala okhoza kunena kuti “Pepani” kwa mnzawo wamuukwati, amishonale anzawo, ndi abale ndi alongo akumaloko; khalani ochenjera kusakhulupirira mawonekedwe oyambirira ndi kuzindikirani kuti vuto lirilonse liri locholoŵana, lofunikira kumvetsetsa kozama kwa mikhalidwe musanapereke uphungu wanzeru; ndi kulemekeza abale akumaloko chifukwa cha luso lawo lakulaka mikhalidwe yovuta.​—Miyambo 15:28; 16:23; Yakobo 1:19.

Ulysses V. Glass, wolembetsa wa Sukulu ya Gileadi, anatenga Afilipi 3:16 kukhala mutu wa nkhani yake. Iye anayamikira kalasilo chifukwa cha kupita patsogolo kumene linapanga ndikuwalimbikitsa kupitiriza mogwirizana ndi lemba limenelo. Pamene kuli kwakuti ophunzirawo ayenera kupitiriza kupeza chidziŵitso cholongosoka, iye anadziŵitsa kuti sadzadziŵa konse zonse. Iye anafotokoza mwafanizo mfundoyo ndi watchi ya manambala. Mwini wake angadziŵe kuigwiritsira ntchito popanda kudziŵa mmene imagwiriradi ntchito. Mofananamo, amishonale sayenera kunyoza awo amene kuya kwa chidziŵitso chawo sikungafanane ndi kwawo komabe amadziŵa chofunika koposa​—mmene angawopere Yehova. (Miyambo 1:7) Iye anakumbutsa kalasilo za kufunika kwa kukhala ndi ‘diso labwino.’ (Mateyu 6:22, NW) Diso lauzimu lingalepheretsedwe kuwona monga momwe lingachitire diso lenileni. Mwachitsanzo, ena ali ndi kawonedwe kolunjika​—kusumika maganizo mopambanitsa pa tsatanetsatane wochepa kuti awone chithunzi chonse​—pamene ena, mosiyana, amangowona pamwamba pa nkhanizo ndipo amalephera kufika pa nkhani zenizeni zimene amafunikira kukambapo.

Nkhani yomalizira ya m’maŵa inali ndi mutu wakuti “Kuzindikira ndi Kugwira Ntchito Limodzi ndi Gulu la Yehova,” yoperekedwa ndi Theodore Jaracz wa Bungwe Lolamulira. Mbale Jaracz anathirira ndemanga kuti pamene kuli kwakuti pali magulu ndi zitaganya zikwi zambiri m’dziko, gulu limodzi lokha pa onsewa silichokera ku dziko. Kodi mungazindikire motani limene limaimira Yehova? Mawu a Mulungu amapereka zizindikiro. Baibulo limasonyeza kuti zolengedwa zakumwamba ziri zolinganizidwa bwino koposa. (Salmo 103:20, 21; Yesaya 40:26) Gulu lapadziko lapansi la Yehova limazindikiridwanso ndi dongosolo lake limodzi ndi kupatuka kwake ku dziko, kumamatira kwake zolimba ku miyezo yamakhalidwe abwino a Baibulo, ndi muyeso wake wapamwamba wa makhalidwe abwino, ndi chikondi pakati pa ziŵalo zake. Mbale Jaracz anafulumiza ophunzira a Gileadi kuthandiza ambiri monga momwe angathere m’magawo awo kuzindikira gulu la Yehova Mwamalemba. Mogwirizana ndi zimenezo, anapanga chilengezo chodzutsa maganizo ichi: Posachedwapa Sukulu ya Gileadi idzaŵirikiza kaŵiri mu ukulu wake, kufika ku ophunzira pafupifupi 50 m’kalasi la 93! Ndiponso, makalasi Owonjezera a Sukulu ya Gileadi adzayamba pafupifupi panthaŵi imodzimodziyo mu Jeremani. Anthu anawomba m’manja kwa nthaŵi yaitali ndipo mokweza!

Pachimake pa programu ya m’maŵayo, ophunzira 24 onse a Gileadi analandira madipuloma. Posachedwa akanyamuka ulendo wawo wopita ku maiko 12 osiyanasiyana kuzungulira padziko. Kalasilo linapereka chigamulo chogwira mtima, kuthokoza Bungwe Lolamulira ndi banja la Beteli. Pambuyo pa chakudya chamasana, Mbale Charles J. Rice wa ku Komiti ya Watchtower Farms anachititsa Phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda. Ndiyeno omaliza maphunzirowo anaikapo programu yokondweretsa, akumachitira chitsanzo zina za zokumana nazo zomwe anali nazo muutumiki wakumunda mkati mwa kosi yawo ya miyezi isanu mu Wallkill, New York. Pambuyo pa chimenecho, ofalitsa oimira mipingo ingapo yakumaloko anasonyeza drama yokhala ndi mutu wakuti Achichepere Amene Amakumbukira Mlengi Wawo Tsopano.

Pomaliza programuyo, Mbale George Gangas, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira cha zaka 95 zakubadwa, anapereka pemphero laumoyo kwa Yehova. Gululo linachoka ndi chisangalalo, mosakaikira aliyense anasonkhezeredwa kukachita zochuluka m’ntchito yotuta yapadziko lonse.

[Bokosi patsamba 22]

Chiŵerengero cha Kalasilo

Chiŵerengero cha maiko oimiridwa: 6

Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwa: 12

Chiŵerengero cha ophunzira: 24

Chiŵerengero cha okwatirana: 12

Avereji ya zaka zakubadwa: 33.4

Avereji ya zaka m’chowonadi: 16.13

Avereji ya zaka muuminisitala wanthaŵi zonse: 11.3

[Chithunzi patsamba 23]

Kalasi Lomaliza Maphunziro la 91 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

Mu ndandanda iri pansipa, mizera yaŵerengedwa kuchokera kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kumanzere kupita kulamanja mu mzera uliwonse.

(1) McDowell, A.; Youngquist, L.; Skokan, B.; Wargnier, N.; Miller, Y.; Muñoz, M. (2) Bales, M.; Perez, D.; Attick, E.; Vainikainen, A.; Mostberg, K. (3) DePriest, D.; DePriest, T.; Perez, R.; Wargnier, J.; Muñoz, J.; Miller, J. (4) McDowell, S.; Bales, D.; Skokan, M.; Attick, C.; Youngquist, W.; Vainikainen, J.; Mostberg, S.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena