Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/1 tsamba 18-20
  • Madalitso a Maphunziro a Gileadi Afalikira Padziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madalitso a Maphunziro a Gileadi Afalikira Padziko Lonse
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Alangizi Apereka Uphungu
  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Maphunziro a Gileadi m’Chikhulupiriro Choyeretsetsa
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuchoka pa Ophunzira Okhoza Bwino Kukhala Amishonale Okhoza Bwino
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/1 tsamba 18-20

Madalitso a Maphunziro a Gileadi Afalikira Padziko Lonse

MAPHUNZIRO m’dziko lakale lino ali ndi phindu lochepa chabe. Popeza kuti kwakukulukulu ngozikidwa pa malingaliro a anthu mmalo mwa kuzikidwa pa chowonadi cha Mulungu, iwo sangathe kupereka chifuno chowona m’moyo. Koma Sukulu ya Gileadi njosiyana. M’mawu ake oyamba pa mwambo wa kumaliza maphunziro a kalasi la Gileadi la 93, Theodore Jaracz wa Bungwe Lolamulira anasonyeza kuti sukulu imeneyi imapereka maphunziro okhala ndi phindu lowona. Monga momwe Salmo 119:160 limanenera, “chiŵerengero cha mawu a [Mulungu] ndicho chowonadi.” Chotero kunali mwa chidwi chachikulu kuti omvetsera pafupifupi 6,000 anatchera khutu ku programu ya mwambo wa omaliza sukulu pa September 13, 1992.

Nkhani yoyamba ya mmaŵa, yokambidwa ndi Lon Schilling chiŵalo cha Komiti ya Watchtower Farms, inali ya mutu wakuti “Pitirizani Kugonjetsa Dziko ndi Wolamulira Wake.” Mbale Schilling anasumika nkhaniyo pa Chivumbulutso 12:11 ndipo anasonyeza kuti vesilo limasonyeza njira zitatu zakugonjetsa nazo: (1) mwa mwazi wa Mwanawankhosa, (2) mwa kuchitira umboni, ndi (3) mwa kukhala ndi mzimu wakudzimana. Iye anakumbutsa ophunzirawo kuti ambiri a atumiki a Yehova asonyeza mzimu wotero ndipo ayang’anizana ngakhale ndi imfa mofunitsitsa kuti asunge kukhulupirika kwawo ndi umphumphu.

“Tetezerani Choikiziridwa Chanu Chabwino Kwambiricho” unali mutu wankhani wokambidwa ndi John E. Barr wa Bungwe Lolamulira. Mwa liwu lake lozoloŵereka laubwenzi, anayerekezera kudalirana pakati pa Yehova ndi atumiki ake ndi kudalirana kokhala mu ukwati wabwino. Mogwiritsira ntchito mfundo za 2 Timoteo 1:12, 13, (NW), anachichiza ophunzirawo kutetezera choikiziridwa chawo mwakugwiritsitsa “chitsanzo cha mawu amoyo” amtengo wapataliwo m’Baibulo. Iye anagogomezera kuchita phunziro laumwini kukhala mbali yofunika ya programu ya tsiku ndi tsiku ndipo analangiza ophunzirawo mokoma mtima kusalola konse ndemanga zawo pa misonkhano kukhala zochitidwira kuti zindichoke, koma nthaŵi zonse kuzipangitsa kukhala zopereka tanthauzo.

William Van De Wall, chiŵalo cha Komiti ya Dipatimenti Yautumiki anakamba nkhani yotsatira yakuti, “Sonyezani Kudera Nkhaŵa Kwachikondi Anthu Onga Nkhosa.” Iye anafunsa ophunzirawo zimene akafunafuna mwa dokotala wa banja ndipo anawachichiza kukulitsa kudera nkhaŵa komweko, kukoma mtima, ndi chifundo zimene iwo akakonda.

Daniel Sydlik, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira analankhula motenthedwa maganizo pa mutu wankhani wakuti “Zinthu Zonse Nzotheka kwa Mulungu.” Anakumbutsa ophunzirawo kuti Abrahamu ndi Sara anaseka atauzidwa chiyembekezo chowonekera kukhala chosatheka cha kukhala ndi mwana wamwamuna mu ukalamba wawo. Malonjezo ambiri a Mulungu amawonekera kukhala osatheka m’lingaliro la anthu; koma monga momwe mngelo anafunsira Abrahamu, “kodi chilipo chinthu chomlaka Yehova?” (Genesis 18:14) Mbale Sydlik anadandaulira ophunzirawo kusonyeza chikhulupiriro m’mphamvu ya Mulungu yakuchita zosatheka, posalola konse chikhulupiriro chimenecho kufwifwa kapena kugwedezeka, mosasamala kanthu za mayeso amene angakumane nawo.

Alangizi Apereka Uphungu

Alangizi aŵiri a Gileadi anatsatira kulankhula. Choyamba, Jack D. Redford anakamba nkhani pamutu wakuti “Kupanga Dzina Labwino ndi Mulungu.” Chimene chimapangitsa dzina kukhala labwino kapena kukhala loipa, iye anatero, ndiye munthu amene ali nalo. Iye anayerekezera maina onga akuti Adamu, Nimrodi, Yezebele, Sauli, ndi Yudasi ndi maina onga akuti Nowa, Abrahamu, Rute, Paulo, ndi Timoteo. Dzina lirilonse liri ndi ziganizo zambirimbiri zogwirizanitsidwa ndi njira yamoyo ya mwiniwake. Iye anafunsa ophunzirawo mtundu wa dzina limene akakhala nalo pambuyo pa zaka 10, 100, kapena ngakhale 1,000​—lawolepa kapena la wodandaula kaya la m’mishonale wokhulupirika? Iye anawapatsa uphungu wakusumika maganizo pa njira zothetsera mavuto ndi zonulirapo mmalo mwa kusumika pa mavuto.

“Kodi Mukutetezera Chikhulupiriro Chanu Bwino Motani?” unali mutu wankhani wosonkhezera maganizo wokambidwa ndi Ulysses V. Glass. Iye anayerekezera chikhulupiriro champhamvu ndi kampasi yabwino imene nthaŵi zonse imasonya kumalo olondola. Kampasi ya m’galimoto ingayambukiridwe ndi mphamvu yokoka yochokera ku zinthu zina kuwonjezera pa yochokera ku dziko lapansi, ndipo mphamvu zoterozo zifunikira kusulutsidwa. Mofananamo, dziko lakale lino limatulutsa zisonkhezero zambiri zimene zingagwedeze kapena kufooketsa chikhulupiriro chathu ngati tizilola. Pamene anachenjeza ophunzirawo za zisonkhezero zotero, Mbale Glass anawayamikiranso chifukwa cha luntha lakuzindikira kaimidwe ka maganizo ka ena ndi malingaliro.

Nkhani yomalizira ya m’mawawo inakambidwa ndi Albert D. Schroeder, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira. Iye analimbikitsa ophunzirawo “Kusunga Mzimu Waumishonale,” akumawayamikira chifukwa cha kusonyeza mzimu waumishonale umodzimodziwo wosonyezedwa ndi kalasi loyamba kalelo mu 1943, pamene iye anali kutumikira monga wolemba maina a ophunzira m’sukuluyo. Iye ananena kuti iwo anali okondwerera ubwino wa anthu, alaliki mwachibadwa, amene amakonda kutsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu. Pitirizani kukulitsa mkhalidwe womwewo, mukumagwiritsira ntchito mokwanira New World Translation m’phunziro laumwini, iye anachichiza motero. Anamaliza mwakukambitsirana vesi ndi vesi la Salmo 24 monga chitsanzo.

Kenako, ophunzira a Gileadi anasintha nakhala omaliza maphunziro a Gileadi! Anapatsidwa madiploma awo pamene magawo awo aumishonale analengezedwa mofuula, zotsagana ndi kuwombera m’manja waa waa waa kwa omvetsera.

Madzulo, Calvin Chyke, chiŵalo cha Komiti ya Fakitale anachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Programu yokondweretsa ya ophunzira inatsatira, imene inasimba zokumana nazo za ophunzira m’munda mkati mwa kosi ya miyezi isanuyo ndiponso anasonyeza masilaidi amaiko ena kumene iwo anali kutumizidwa. Ndiponso, aŵiri okwatirana achikulirepo anafunsidwa, ndipo anapereka zina za chidziŵitso ndi nzeru zimene anapeza kuchokera m’zaka zambiri monga amishonale. Madzulowo anamalizidwa ndi drama la panthaŵi yake lamutu wakuti Musanyengedwe Kapena Kupusitsa Mulungu.

Omvetserawo anachoka atakondweretsedwa, atasangalala kuwona zimene maphunziro a chowonadi cha Mulungu angachite ndipo anakondwera kudziŵa kuti mapindu amaphunziro otero adzapitirizabe kumvedwa padziko lonse. Pamene amishonale 48 amenewa akupita kumagawo awo, mapemphero ambiri akuwatsatira, osonyeza chiyembekezo chochokera pansi pamtima ndi chidaliro chakuti okhulupirika amenewa adzakhala dalitso kwa anthu a Mulungu kulikonse amkako.

[Bokosi patsamba 19]

Ziŵerengero za Kalasi

Chiŵerengero cha maiko oimiridwa: 7

Chiŵerengero cha maiko kumene agaŵiridwa: 18

Chiwonkhetso cha ophunzira: 48

Chiŵerengero cha okwatirana: 24

Avareji ya msinkhu: 32.8

Avareji ya zaka m’chowonadi: 15.3

Avareji ya zaka muuminisitala wa nthaŵi yonse: 10.4

[Bokosi patsamba 20]

OMALIZA MAPHUNZIRO A KALASI LA GILEADI LOWONJEZERA

Pa June 21, 1992, kagulu ka amishonale 24 kanamaliza maphunziro pa kalasi lachinayi la Sukulu Yowonjezera ya Gileadi mu Selters/​Taunus, M’Jeremani. Kalasilo, lopangidwa ndi okwatirana 11 ndi alongo 2 osakwatiwa ochokera ku maiko asanu ndi aŵiri, anachita avareji ya zaka 32 zakubadwa, 14 zapambuyo paubatizo, ndi 8.5 zautumiki wa nthaŵi yonse m’ntchito yolalikira. Oposa 2,000 anafika pa mwambo womaliza maphunziro.

Mbale Jaracz anayamba programu ndi kukambitsirana Miyambo 11:24, imene imati: “Alipo ogaŵira, nangolemerabe.” Iye ananena kuti ophunzirawo anali pafupi kutumizidwa ndipo akasonkhezera chiwonjezeko.

Nkhani zochokera m’malemba zolimbikitsa zinakambidwa ndi Richard Kelsey, wogwirizanitsa wa Komiti Yanthambi ya Jeremani; Wolfgang Gruppe wa Dipatimenti Yautumiki; Werner Rudtke ndi Edmund Anstadt, amenenso ali ziŵalo za Komiti Yanthambi; ndi alangizi aŵiri, Dietrich Förster ndi Lothar Kaemmer. Albert Schroeder, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yaikulu yokondweretsa ya mutu wakuti “Pitirizani Kukhala Ofunafuna Ngale Zauzimu.” Mapeto a programuyo anali kuperekedwa kwa magawo ku maiko 11 mu Afirika, Central America, ndi Kummaŵa kwa Yuropu, pambuyo pake mmodzi wa omaliza maphunzirowo anaŵerenga kalata yochokera ku kalasilo yomka ku Bungwe Lolamulira yosonyeza chiyamikiro chochokera pansi pa mtima.

[Chithunzi patsamba 18]

Kalasi la chi 93 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda inoyi, manambala a mizera akuchokera kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.

(1) Hitesman, C.; West, P.; Evans, D.; Hipps, M.; Simonelli, N.; Wood, S.; Corkle, M.; Flores, C.; Thomas, J. (2) Jones, M.; Nissinen, J.; Sponenberg, M.; Zachary, K.; Ravn, G.; Backman, M.; Wettergren, A.; Evans, D.; Flores, R.; Caporale, G. (3) Simonelli, N.; Rechsteiner, M.; Rechsteiner, M.; Ruiz-Esparza, L.; Gerbig, B.; Simpson, C.; Zanewich, C.; Zachary, B.; Ricketts, L.; (4) Simpson, J.; Backman, J.; Corkle, G.; Gerbig, M.; Ricketts, B.; Bagger-Hansen, L.; Jones, A.; Zanewich, K.; Ravn, J.; Hipps, C. (5) Sponenberg, S.; Hitesman, A.; Caporale, L.; Ruiz-Esparza, S.; Thomas, R.; Bagger-Hansen, B.; Wood, M.; West, M.; Wettergren, C.; Nissinen, E.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena