Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 12/1 tsamba 21-24
  • Kuchoka pa Ophunzira Okhoza Bwino Kukhala Amishonale Okhoza Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchoka pa Ophunzira Okhoza Bwino Kukhala Amishonale Okhoza Bwino
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ophunzira Akhama Apeza Chimwemwe mu Utumiki
  • Amene Akhala Amishonale kwa Zaka Zambiri Afotokoza Chinsinsi cha Kukhoza
  • Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Sekerani mwa Yehova Ndipo Kondwerani
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Asonkhezeredwa Kutumikira
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Ophunzira Mawu a Mulungu Atsiriza Sukulu Yawo
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 12/1 tsamba 21-24

Kuchoka pa Ophunzira Okhoza Bwino Kukhala Amishonale Okhoza Bwino

“SINDITHABE kukhulupirira kuti takhala ndi mwaŵi umenewu!” anatero Will, ponena za maphunziro amene iyeyo ndi mkazi wake, Patsy, anali atangomaliza kumene monga ophunzira a kalasi la 103 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Zahid ndi Jeni anavomereza zimenezi. “Tikudzimva kukhala amwaŵi kwambiri kupezeka kuno,” iwo anatero. Ophunzira onse anali akhama pasukuluyo. Iwo tsopano anali ofunitsitsa kuyamba ntchito yawo monga amishonale. Koma choyamba, pa programu yokondwerera kumaliza maphunzirowo pa September 6, 1997, iwo analandira uphungu wachikondi umene udzawathandiza kupambana kumagawo awo aumishonale.

Tcheyamani wa programuyo anali Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira. Iye anafotokoza kuti mabwenzi ndi achibale ochokera ku Canada, Ulaya, Puerto Rico, ndi United States​—limodzi ndi banja la Beteli ndi oimira nthambi 48 mwa nthambi za Watch Tower Society​—analipo kudzatsimikizira ophunzira za chichirikizo ndi chikondi chawo. Mbale Jaracz anafotokoza kuti amishonale otumizidwa ndi matchalitchi a Dziko Lachikristu nthaŵi zambiri achenjenekedwa pantchito yawo yaumishonale ndipo ayamba kulondola zolinga zaukatswiri wamaphunziro kapena kuloŵanso m’ndale. Mosiyana ndi amenewo, omaliza maphunziro a Gileadi amachita zimene aphunzitsidwa kuchita. Iwo amaphunzitsa anthu Baibulo.

Kenako Robert Butler wa ku ofesi ya Sosaite ku Brooklyn anakamba nkhani yamutu wakuti “Pangani Njira Yanu Kukhala Yachipambano.” Iye anafotokoza kuti pamene kuli kwakuti anthu amapima chipambano malinga ndi ndalama kapena zinthu zina zaumwini zimene apeza, chofunika kwambiri ndicho mmene Mulungu amapimira chipambano. Utumiki wa Yesu unali wachipambano, osati chifukwa chakuti anatembenuza anthu ambiri, koma chifukwa chakuti anali wokhulupirika pantchito yake. Yesu anadzetsa ulemerero kwa Yehova, ndipo sanadetsedwe ndi dziko. (Yohane 16:33; 17:4) Zimenezi ndi zinthu zimene Mkristu aliyense angachite.

“Khalani Akapolo kwa Anthu Onse,” analangiza motero Robert Pevy, amene kale anali mmishonale ku maiko a kummaŵa. Mtumwi Paulo anali mmishonale wokhoza bwino. Kodi chinsinsi chake chinali chiyani? Iye anadzipanga kapolo kwa onse. (1 Akorinto 9:19-23) Mlankhuliyo anafotokoza kuti: “Womaliza maphunziro a Gileadi amene ali ndi mzimu umenewo sadzaona utumiki waumishonale monga kukwezedwa pantchito, njira yopezera malo apamwamba m’gulu. Mmishonale amapita kugawo lake ndi cholinga chimodzi basi​—kukatumikira, popeza zimenezo nzimene akapolo amachita.”

Mu uphungu wake wozikidwa kwenikweni pa 2 Akorinto machaputala 3 ndi 4, Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira analimbikitsa ophunzirawo ‘Kusonyeza Ulemerero wa Yehova Monga Akalilole.’ Iye anawakumbutsa kuti chidziŵitso cha Mulungu chili ngati nyali younikira Mkristu pamene achilandira ndi mtima wonse. Timasonyeza kuunika kumeneko mwa kulalikira uthenga wabwino ndiponso mwa kusunga khalidwe labwino. “Nthaŵi zina mungadzimve kukhala wopereŵera,” anavomereza motero. “Pamene mukhala ndi malingaliro otero, dalirani Yehova, ‘kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu.’” (2 Akorinto 4:7) Mwa kugwiritsira ntchito mawu a Paulo olembedwa pa 2 Akorinto 4:1, Mbale Lösch anachonderera ophunzirawo kuti: “Musasiye ntchito yanu yaumishonale. Walitsanibe akalilole anu!”

Karl Adams, mmodzi wa aphunzitsi a Gileadi, anakamba nkhani yosangalatsa yamutu wakuti “Kodi Yehova Ali Kuti?” Funsolo silikunena za malo enieni kumene Mulungu amakhala mumlengalenga, koma likunena za kufunika kwa kuzindikira lingaliro la Yehova ndi zinthu zosonyeza chitsogozo chake. “Ngakhale munthu amene watumikira Yehova kwa nthaŵi yaitali angaiŵale zimenezo atapsinjika maganizo,” iye anatero. (Yobu 35:10) Nanga m’tsiku lathu lamakonoli? Mu 1942, anthu a Mulungu anafunikira chitsogozo. Kodi ntchito yolalikira inali kumapeto, kapena kodi panali ntchito yaikulu yoti ichitidwe? Kodi chifuniro cha Yehova kwa anthu ake chinali chiyani? Pamene anapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu, yankho linaonekera poyera. “Chakacho chisanathe,” Mbale Adams anatero, “makonzedwe a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower anapangidwa.” Ndithudi Yehova wadalitsa ntchito ya amishonale otumizidwa ndi sukulu imeneyo.

Mark Noumair anali mphunzitsi wachiŵiri kulankhulapo. M’nkhani yake, yamutu wakuti “Kodi Luso Lanu Mudzaligwiritsira Ntchito Motani?,” iye analimbikitsa ophunzira kugwiritsira ntchito maphunziro amene analandira pa Gileadi atangofika kumagawo awo atsopano. “Yesetsani kudziŵana ndi ena,” iye anatero. “Zoloŵeranani nawo. Khalani wofunitsitsa kudziŵa mwambo wawo, mbiri yawo, ndi zinthu zimene zimaseketsa anthu a m’dzikolo. Mukaphunzira msanga chinenero simudzavutika kwambiri.”

Ophunzira Akhama Apeza Chimwemwe mu Utumiki

Kuwonjezera pa kuchita khama pamaphunziro awo pamene anali pa Gileadi, ophunzirawo anatumizidwa ku mipingo 11 yakomweko. Pakutha kwa mlungu, iwo anali kutengamo mbali m’ntchito yolalikira mwachangu. Wallace Liverance, mmodzi wa aphunzitsi a Gileadi, anaitana angapo kuti asimbire omvetsera zina za zokumana nazo zawo. Chimwemwe chawo chinaonekeratu pamene anali kusimba zimene anakumana nazo pochitira umboni kumasitolo, pamalo oimika magalimoto, m’magawo a malo amalonda, m’misewu, ndi kunyumba ndi nyumba. Ena a iwo anayesetsa kufikira anthu olankhula zinenero za kumaiko ena amene anali kukhala ndi kugwira ntchito m’gawo la mpingo wawo. Maphunziro a Baibulo apanyumba pafupifupi khumi anayambidwa ndi kuchititsidwa ndi a m’kalasi la 103 pamiyezi isanu yamaphunziro awo.

Amene Akhala Amishonale kwa Zaka Zambiri Afotokoza Chinsinsi cha Kukhoza

Mbali yosangalatsa imeneyi ya programu itatha, Patrick Lafranca ndi William Van de Wall anaitana asanu ndi aŵiri a m’ma Komiti a Nthambi kuti afotokoze maphunziro amene anaphunzirapo pantchito yawo yaumishonale kuti a m’kalasilo apindule. Iwo analangiza omaliza maphunzirowo kuti ayenera kuzindikira kuti ntchito yawo yaumishonale njochokera kwa Yehova ndi kutsimikiza mtima kuti adzapitirizabe kugwira ntchitoyo. Iwo analankhula za mmene amishonale ophunzitsidwa ku Gileadi athandizira ntchito ya m’maiko ena.

Kodi nchiyani chinathandiza a m’ma Komiti a Nthambi ameneŵa kutumikira zaka makumi ambiri monga amishonale achimwemwe ndi othandiza? Iwo anagwira ntchito mogwirizana kwambiri ndi abale a m’maikowo ndi kuphunzira kwa iwo. Iwo anayesetsa kuphunzira chinenero atangofika kumagawo awo. Anaphunzira kukhala ololera ndipo anayamba kutsatira mwambo wakomweko. Charles Eisenhower, amene anamaliza maphunziro a Gileadi m’kalasi loyamba ndipo amene wakhala mmishonale zaka 54, anatchula “zinsinsi” zisanu zimene amishonale okhoza bwino azindikira: (1) Phunzirani Baibulo nthaŵi zonse, (2) phunzirani chinenero, (3) khalani wachangu mu utumiki, (4) limbikani kupangitsa mtendere panyumba ya amishonale, ndiponso (5) pempherani kwa Yehova nthaŵi zonse. Ophunzirawo anachita chidwi osati chabe ndi uphungu wothandiza umene analandira komanso ndi chimwemwe choonekeratu chimene amishonale achidziŵitso ameneŵa ali nacho mu utumiki wa Yehova. Monga momwe Armando ndi Lupe ananenera, “iwo amasangalala pamene alankhula za miyoyo yawo.”

Kufunsako kutatha, panatsala nkhani imodzi. Albert Schroeder, wa m’Bungwe Lolamulira, anasankha mutu wa nkhani yake kukhala wakuti “Kukhala Mdindo Wokhulupirika wa Mawu a Mulungu Kumasonyeza Ngale za Choonadi.” Popeza kuti Baibulo ndilo buku lophunziramo lofunika kwambiri m’Sukulu ya Gileadi, ophunzirawo anatchera khutu kuti amvetsetse chimene adzanena. Mbale Schroeder anafotokoza kuti pamene ntchito ya New World Translation of the Holy Scriptures inayambika zaka 50 zapitazo, mamembala odzozedwa a m’Komiti Yotembenuza Baibulo la New World sanafune kukondweretsa munthu koma anadalira chitsogozo cha mzimu woyera. (Yeremiya 17:5-8) Komabe, posachedwapa akatswiri ena azindikira kuti New World Translation ili ndi matembenuzidwe apamwamba kwambiri. M’kalata imene analembera Sosaite, katswiri wina wamaphunziro analemba kuti: “Buku labwino kwambiri ndimalizindikira ndikaliona, ndipo komiti yanu yotchedwa ‘Komiti Yotembenuza Baibulo la New World’ inachita ntchito yake mwaluso.”

Nkhaniyi itatha, ophunzira analandira madiploma awo, ndipo magawo awo analengezedwa kwa omvetsera. Inali nthaŵi yokhudza mtima kwa a m’kalasilo. Pamene woimira kalasi anali kuŵerenga kalata yoyamikira, ambiri anakhudzidwa mtima ndipo anagwetsa misozi. Ophunzira ena anali kukonzekera ntchito yaumishonale kwa zaka zambiri. Podziŵa kuti kosi ya Gileadi idzachitidwa m’Chingelezi, angapo anasamukira kumipingo yolankhula Chingelezi kuti akachidziŵe bwino chinenerocho. Ena anasamukira kumene kunali kusoŵa kwakukulu kwa apainiya, kaya m’dziko lawo momwemo kapena kunja. Komanso ena anakonzekera mwa kuŵerenga zokumana nazo, kufufuza, kapena kupenyerera mobwerezabwereza vidiyo ya Sosaite yakuti To the Ends of the Earth [Kumalekezero a Dziko Lapansi].

Will ndi Patsy, otchulidwa poyamba, anachita chidwi kwambiri kuona mmene ena anasonyezera chikondi chawo kwa iwo. “Anthu amene sanali kutidziŵa nkomwe anatikupatira ndi kutijambula zithunzi. Wina wa m’Bungwe Lolamulira anatigwira chanza nanena kuti, ‘Tikunyadira chifukwa cha inu!’” Ndithudi, tikuwakonda kwambiri ophunzira a m’kalasi la 103. Iwo aphunzitsidwa bwino. Maphunziro amene alandira ku Gileadi adzawathandiza kusintha kuchoka pa ophunzira okhoza bwino kukhala amishonale okhoza bwino.

[Bokosi patsamba 22]

Ziŵerengero za Kalasi

Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 9

Chiŵerengero cha maiko kumene anatumizidwa: 18

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Chiŵerengero cha mabanja: 24

Avareji ya zaka zakubadwa: 33

Avareji ya zaka m’choonadi: 16

Avareji ya zaka mu utumiki wanthaŵi zonse: 12

[Chithunzi patsamba 23]

Kalasi la 103 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.

(1) Bunn, A.; Dahlstedt, M.; Campaña, Z.; Boyacioglu, R.; Ogando, G.; Nikonchuk, T.; Melvin, S. (2) May, M.; Mapula, M.; Lwin, J.; Hietamaa, D.; Hernandez, C.; Boyacioglu, N.; Sturm, A.; Melvin, K. (3) Thom, J.; Mapula, E.; Nault, M.; Teasdale, P.; Wright, P.; Pérez, L.; Shenefelt, M.; Pak, H. (4) Murphy, M.; Campaña, J.; Stewart, S.; Cereda, M.; Reed, M.; Pérez, A.; Teasdale, W.; Pak, J. (5) Stewart, D.; Wright, A.; Cereda, P.; Nikonchuk, F.; Reed, J.; Hietamaa, K.; Ogando, C.; Shenefelt, R. (6) Murphy, T.; Hernandez, J.; Nault, M.; Bunn, B.; Thom, R.; Dahlstedt, T.; Lwin, Z.; May, R.; Sturm, A.

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi tikupita kuti?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena