Sekerani mwa Yehova Ndipo Kondwerani
NTHAŴI zonse pamakhala chisangalalo pamene ntchito yofunika kwambiri yamalizidwa bwino. Zomwe zinachitika pomaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower pa March 13, 1999, ku Likulu la Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York, zinalidi zosangalatsa kwa ophunzira 48 a kalasi ya 106 ya sukuluyo.
Mawu amalonje a Theodore Jaracz, wa mu Bungwe Lolamulira, amene anamaliza maphunziro mu kalasi yachisanu ndi chiŵiri ya Gileadi, ndiponso amene anali tcheyamani wa pologalamu yomaliza maphunziroyo, anagogomezera mawu a pa Salmo 32:11 akuti: “Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima.” Polongosola chifukwa chake kunali kofunika kuti aliyense asangalale pa chochitika chimenechi, iye anati: “Ndi chifukwa cha zimene Yehova akuchita ndi anthu amene ali owongoka mtima, kuphatikizapo ophunzira athu a Gileadi, kuti timasangalala panthaŵi zangati zimenezi.” Pamene kuli kwakuti ophunzirawo anakonzekera kupita ku Sukulu ya Gileadi ndipo mwakhama anayesetsa kuti ayenerere utumiki waumishonale, Yehova ndiye anatheketsa kuti chilichonse chichitike bwino lomwe. (Miyambo 21:5; 27:1) Mbale Jaracz ananenetsa kuti chimenecho ndicho chifukwa ‘chosekera mwa Yehova.’
Mwa anthu amene anali mu holo ya ku Patterson panali abale awo akuthupi ndi alendo a ophunzirawo amene anachokera m’mayiko 12 kudzaonerera chochitika chosangalatsachi. Pamene anthu 5,198 amene analipo—kuphatikizapo a banja la Beteli ku Brooklyn, Patterson, ndi Wallkill, omwe anali kumverera ndi kuonerera pa vidiyo—ankayembekezera kuti pologalamuyo iyambe, zinali kuonekeratu kuti panali mzimu wachimwemwe.
Analimbikitsidwa Kukhalabe ndi Mzimu Wachimwemwe
Mbale Jaracz atamaliza kupereka malonje, anaitana mlankhuli woyamba mwa alankhuli asanu amene anakonzekera kupereka malangizo a m’Malemba olimbikitsa osati kwa omaliza maphunziro a Gileadi okhawo komanso kwa aliyense amene analipo.
Amene anayamba kulankhula anali William Malenfant, yemwe anamaliza maphunziro a Gileadi mu kalasi ya 34, ndipo tsopano akutumikira monga wothandiza Komiti Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira. Mogwirizana ndi mutu wa nkhani yake wakuti “‘Zonse’ Si Zachabechabe!” wotengedwa pa Mlaliki 1:2, anafunsa funso lakuti: “Kodi Solomo anatanthauzadi kuti zilizonse, m’lingaliro lake lonse la liwulo, ndi zachabe?” Yankho: “Ayi. Iye anali kunena kuti zochita za anthu zimene zimanyalanyaza chifuno cha Mulungu, zokhumba zimene zili zosiyana ndi chifuno cha Mulungu—zinthu zonse zimenezi ndi zachabe.” Mosiyana ndi zimenezo, kulambira Mulungu woona, Yehova, si kwachabe; ngakhalenso kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kuwaphunzitsa kwa ena si kwachabe. Mulungu saiwala zoyesayesa zoterozo za atumiki ake. (Ahebri 6:10) Ndipotu, ngakhale ngati awo amene apeza chiyanjo ndi Mulungu atakumana ndi tsoka, iwo ‘adzamangika m’phukusi la amoyo lokhala ndi Yehova.’ (1 Samueli 25:29) Ndi lingaliro losangalatsa bwanji! Kukumbukira mfundo zimenezi kungathandize olambira a Yehova onse kukhalabe ndi mzimu wachimwemwe.
John Barr, wa mu Bungwe Lolamulira, analimbikitsa amene anali kumaliza maphunzirowo ndi nkhani yake yakuti “Pezani Chimwemwe mu Utumiki Wanu Waumishonale.” Iye anasonyeza kuti utumiki waumishonale ndi chinthu chimene nthaŵi zonse chakhala mumtima mwa Yehova Mulungu. “Ndi chinthu chimene chinamangidwa pamodzi ndi kusonyeza chikondi kwa Yehova ku dziko lapansi. Iye anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi pano. Yesu anali mmishonale wamkulu kuposa onse, mmishonale wofunika kwambiri.” Pamene omaliza maphunzirowo anali kulingalira za zimene Yesu anafunika kusintha kuti athe kuchita ntchito yake bwino padziko lapansi, mapindu a utumiki waumishonale wa Yesu akupezekabe kwa onse amene adzawagwiritsa ntchito. Izi zili choncho chifukwa, monga Mbale Barr anatchulira, Yesu anasangalala ndi kugwira ntchito ya Mulungu, ndiponso anakonda mtundu wa anthu. (Miyambo 8:30, 31) Mbale Barr analimbikitsa omaliza maphunzirowo kukamamatira ku ntchito yawo, osati kokha chifukwa chopirira, komanso chifukwa chakuti amasangalala poichita. “Dalirani Yehova; sadzakukhumudwitsani,” iye anachonderera ophunzirawo.—Salmo 55:22.
“Kuyenda m’Dzina la Yehova Nthaŵi Zonse” unali mutu umene anasankha mlankhuli wotsatira, Lloyd Barry, winanso wa mu Bungwe Lolamulira. Pokhala atatumikirapo monga mmishonale kwa zaka zoposa 25 ku Japan pambuyo pomaliza maphunziro m’kalasi ya 11 ya Gileadi, Mbale Barry anasimba zinthu zina zimene amishonale oyambirira anakumana nazo ndipo analongosolanso mavuto amene ankakumana nawo. Kodi iye anali ndi uphungu wothandiza wotani kwa amene anali kumaliza maphunzirowo? “Koposa zonse, pitirizani kukhala anthu auzimu. Ndiponso, phunzirani chinenero ndi chikhalidwe cha anthuwo. Khalanibe anthabwala. Ndipo mamatirani kuntchito yanu; musatope ndipo musafooke.” Mbale Barry anauza omaliza maphunzirowo kuti pantchito yawo ya m’dziko lina adzakumana ndi anthu amene amayenda m’dzina la milungu yosiyanasiyana, ndipo anawakumbutsa mawu a Mika akuti: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mlungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.” (Mika 4:5) Ndithudi chitsanzo cha amishonale akale chingasonkhezere mwamphamvu atumiki a Mulungu onse kuti apitirize kuyenda m’dzina la Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika.
Wotsatira kukamba nkhani anali mphunzitsi wa Gileadi Lawrence Bowen. Mutu wa nkhani yake unadzutsa funso lakuti, “Kodi Mudzakhala Otani?” Anasonyeza kuti kuchita bwino mu utumiki wa Mulungu kumadalira pa chikhulupiriro ndi kudalira Yehova. Kudalira Yehova ndi mtima wonse kunapangitsa Mfumu Asa kugonjetsa mwamtima bii gulu la ankhondo a adani ake la anthu zikwi chikwi chimodzi. Komabe anakumbutsidwa ndi mneneri Azariya kufunika kwa kupitiriza kudalira pa Mulungu: “Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye.” (2 Mbiri 14:9-12; 15:1, 2) Popeza kuti dzina la Mulungu, Yehova, limapereka lingaliro lakuti iye amakhala chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse chifuno chake—kaya zimenezi zikutanthauza kukhala Mgaŵiri, Mtetezi, kapena ngakhale Wakupha—amishonale amene amadalira pa Yehova ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuno chake adzatha kugwira bwino ntchito yawo. (Eksodo 3:14) “Osaiŵala,” anamaliza motero Mbale Bowen, “kuti ngati inu mupanga chifuno cha Yehova kukhala chifuno chanu, iye adzakupangani kukhala chilichonse chimene chikufunika kuti mukwaniritse ntchito yanu.”
Amene anakamba nkhani yomalizira pa mbali iyi ya pologalamuyi anali Wallace Liverance, amene kale anali mmishonale ndipo tsopano ndi wosunga kaundula wa sukuluyo. Nkhani yake, yamutu wakuti “Mawu a Mulungu Akhale Amoyo Ndipo Azigwira Ntchito mwa Inu,” inapangitsa anthu kulingalira za uthenga, kapena lonjezo, lotsimikizirika la Mulungu limene nthaŵi zonse likuyandikira kukwaniritsidwa kwake. (Ahebri 4:12) Limakhudza miyoyo ya awo amene amalilola kuwakhudza. (1 Atesalonika 2:13) Kodi mawu amenewo angakhale amoyo ndipo angamagwire ntchito bwanji m’miyoyo yathu? Mwa kuphunzira Baibulo mwakhama. Mbale Liverance anakumbutsa omaliza maphunzirowo za njira zophunzirira Baibulo zimene anaphunzira ku Gileadi zimene zinaphatikizapo kuŵerenga ndi kupeza tanthauzo lake ndi kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Iye anagwira mawu a Albert Schroeder, wa mu Bungwe Lolamulira amene anali tcheyamani wa komiti imene inakhazikitsa Sukulu ya Gileadi zaka zoposa 50 zapitazo, akuti: “Mwa kupenda nkhani yonse, munthu angapeze mphamvu yonse yauzimu ndiponso yolongosoka imene Mulungu amapereka m’Mawu ake.” Kuphunzira Baibulo mwanjira imeneyi kumapangitsa Mawu a Mulungu kukhala amoyo ndi kuti azigwira ntchito.
Zokumana Nazo Zosangalatsa Ndiponso Kufunsa
Nkhani zitatha, omvera anamvetsera zinthu zina zosangalatsa zimene ophunzirawo anakumana nazo. Motsogozedwa ndi Mark Noumair, yemwe kale anali mmishonale ndipo tsopano ndi mphunzitsi wa Gileadi, kagulu ka ophunzira kanalongosola ndi kuchitira chitsanzo mmene anali kuyesetsera kupereka umboni m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Ena anali okhoza kuyamba ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu a m’gawolo mwa kukhala tcheru pa mikhalidwe yawo ndi zimene anali kukamba ndiponso mwa kuchita nawo chidwi. Motero ophunzirawo anali ‘kudzipenyerera okha ndi chiphunzitsocho’ ndipo analidi osangalatsidwa kuthandiza anthu ena kupeza chipulumutso.—1 Timoteo 4:16.
Panaperekedwa malingaliro ambiri othandiza, ndipo kusangalatsa kwa utumiki waumishonale kunasonyezedwanso ndi abale angapo ozoloŵera amene anali pamaphunziro m’sukulu ya mamembala a komiti ya nthambi ochitikira ku Likulu la Maphunziro a Watchtower. Mbale Samuel Herd ndi Mbale Robert Johnson a kulikulu la Sosaite anapereka mafunso osangalatsa kwa oimira maofesi a nthambi za Sosaite ku Bolivia, Zimbabwe, Nicaragua, Central African Republic, Dominican Republic, Papua New Guinea, ndi Cameroon.
Zokumana nazo ndi mafunso zitatha, Gerrit Lösch, yemwe anamaliza maphunziro a kalasi ya 41 ya Gileadi ndipo tsopano ndi wa mu Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yomaliza pa mutu wochititsa chidwi wakuti “Kodi Ndinu ‘Munthu Wokondedwa’?” Poyamba Mbale Lösch anakumbutsa omaliza maphunzirowo kuti Yesu, Mwana wangwiro wa Mulungu, anthu sanamuone kuti anali wokondedwa, koma “iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu.” (Yesaya 53:3) Motero ndi posadabwitsa kuti lerolino m’mayiko ambiri, amishonale amaonedwa kukhala anthu osafunika, osayenera. Mosiyana ndi zimenezo, panthaŵi yaitali imene Danieli anatumikira ku Babulo, kupyolera mwa mngelo nthaŵi zitatu Mlengi anatchula Danieli kuti ‘wokondedwa.’ (Danieli 9:23; 10:11, 19) Kodi ndi chiyani chimene chinapangitsa Danieli kukhala wokondedwa? Pamene anali kuchita zinthu kuti agwirizane ndi chikhalidwe chachibabulo, iye sanaswe mapulinsipulo a Baibulo; anali woona mtima pa chilichonse, sanagwiritse ntchito udindo wake kuti apeze phindu laumwini; ndipo anali wophunzira wachangu wa Mawu a Mulungu. (Danieli 1:8, 9; 6:4; 9:2) Analinso kupemphera nthaŵi zonse kwa Yehova ndipo sanali kuzengereza kulemekeza Mulungu pa zochita zake. (Danieli 2:20) Mwa kutsatira chitsanzo cha Danieli, atumiki a Mulungu angakhale okondedwa, osati kwenikweni ndi anthu, koma ndi Yehova Mulungu.
Potsiriza pologalamu yolimbikitsa mwauzimuyo, tcheyamani anaŵerenga ena mwa mauthenga amene anachokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi. Ndiyeno, banja lililonse mwa mabanja 24 amenewo linalandira dipoloma, ndi kulengeza dziko limene anali kutumizidwako. Potsiriza penipeni, woimira kalasiyo anaŵerenga kalata imene analembera Bungwe Lolamulira ndiponso banja la Beteli, kuyamikira maphunziro amene kalasiyo inalandira ndiponso mmene anawakonzekeretsera m’miyezi isanu yapitayo.
Pamene pologalamuyo inali kutha, ‘kukondwera ndi mayamiko’ zinali kumveka pakati pa gulu limene linali kuchokalo.—Nehemiya 12:27.
[Bokosi patsamba 27]
Ziŵerengero za Kalasi
Chiŵerengero cha mayiko kumene anachokera: 10
Chiŵerengero cha mayiko kumene anatumizidwa: 19
Chiŵerengero cha ophunzira: 48
Chiŵerengero cha mabanja: 24
Avareji ya zaka zakubadwa: 33
Avareji ya zaka m’choonadi: 16
Avareji ya zaka mu utumiki wa nthaŵi zonse: 13
[Chithunzi patsamba 25]
Kalasi la 106 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.
(1) Deakin, D.; Puopolo, M.; Laguna, M.; Davault, S.; Dominguez, E.; Burke, J. (2) Gauter, S.; Vazquez, W.; Seabrook, A.; Mosca, A.; Helly, L.; Breward, L. (3) Brandon, T.; Olivares, N.; Coleman, D.; Scott, V.; Petersen, L.; McLeod, K. (4) McLeod, J.; Thompson, J.; Luberisse, F.; Speta, B.; Lehtimäki, M.; Laguna, J. (5) Gauter, U.; Dominguez, R.; Helly, F.; Smith, M.; Beyer, D.; Mosca, A. (6) Scott, K.; Seabrook, V.; Speta, R.; Coleman, R.; Breward, L.; Davault, W. (7) Smith, D.; Lehtimäki, T.; Petersen, P.; Thompson, G.; Vazquez, R.; Beyer, A. (8) Luberisse, M.; Deakin, C.; Brandon, D.; Puopolo, D.; Olivares, O.; Burke, S.