Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/1 tsamba 29-31
  • Ophunzira Mawu a Mulungu Atsiriza Sukulu Yawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ophunzira Mawu a Mulungu Atsiriza Sukulu Yawo
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chilimbikitso Chapanthaŵi Yake kwa Amishonale Atsopano
  • Kufunsa
  • Kuchoka pa Ophunzira Okhoza Bwino Kukhala Amishonale Okhoza Bwino
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi—“Amishonale Enieni!”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Gileadi Itumiza Amishonale “Kufikira Malekezero Ake a Dziko”
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/1 tsamba 29-31

Ophunzira Mawu a Mulungu Atsiriza Sukulu Yawo

POTSANZIRA Akristu a m’zaka za zana loyamba, Mboni za Yehova zimadziŵika padziko lonse chifukwa cha kulalikira kwawo khomo ndi khomo. Ntchito imeneyi anaigogomezera m’mawu oyamba pa programu yomaliza ya kalasi ya 102 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower.

Pa March 1, 1997, Albert Schroeder, wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ananena za nkhani ina m’magazini ya ku France yotchedwa Le Point. Inalongosola makonzedwe a Aroma Katolika oyamba kulalikira kukhomo ndi khomo mu Italy. “Kuti [amishonale a ku Vatican] asafike chimanjamanja popikisana m’gawo la Mboni za Yehova,” inatero nkhaniyo, “a Vatican asindikiza makope a Uthenga Wabwino wa Marko Woyera Mtima mpaka miliyoni imodzi, kuti amithenga awowo azinyamula poyang’anizana ndi akatswiri [Mbonizo] ‘pogaŵira’ mawu abwino khomo ndi khomo.”

Omaliza maphunziro 48 amenewo ali pakati pa aja omwe amatsanzira Yesu panjira zaukatswiri zolalikira nazo pofalitsa Mawu a Mulungu. Anachokera m’maiko asanu ndi atatu kubwera ku Malikulu Amaphunziro a Watchtower ku Patterson, New York. Pamiyezi yawo isanu ya sukulu, anaphunzira Baibulo kuyambira kuchikuto mpaka kuchikuto. Maphunziro awo anaphatikizapo mbiri ya gulu la Mulungu, mbali zofunika za moyo waumishonale, ndiponso zipatso za mzimu wa Mulungu. Zonsezi zinali ncholinga chimodzi​—kuwakonzekeretsa utumiki waumishonale m’maiko 17 akutali kumene anali kutumizidwa. Paprogramu yawo yomaliza maphunziro imeneyi, panali omvetsera okwanira 5,015 ochokera ku maiko osiyanasiyana omwe anakondwera nawo paphwandolo. Nangano a sukulu ya Gileadiwo analandira uphungu wothandiza wotani kumapeto kwake?

Chilimbikitso Chapanthaŵi Yake kwa Amishonale Atsopano

Pambuyo pa mawu oyamba a tcheyamani, Ralph Walls, wothandiza mu Komiti ya Antchito ya Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yoyamba yaifupi yauphungu wabwino kwa amishonale atsopanowo. Mutu wake unali wakuti “Kumbukirani Kukonda.” Anatero kuti Baibulo, pa 2 Timoteo chaputala 3, linaneneratu kuti dziko lidzakhala lopanda chikondi. Anapereka uphungu wapanthaŵi yake kwa amishonale atsopanowo, mogwirizana ndi mmene 1 Akorinto 13:1-7 yalongosolera chikondi, kuti: “Inuyo, monga amishonale, mungapyole mlingo wa maola anu. Mungakhale ndi chuma cha chidziŵitso chimene mwapeza m’maphunziro a Gileadi. Kapena tingaonjezere maola a kugwira ntchito mwachangu panthambi. Koma khama lathu ndi kudzipereka kwathu kungakhale chabe ngati tiiŵala kukonda.”

Wotsatira paprogramuyo anali Carey Barber, wa Bungwe Lolamulira, yemwe anakamba nkhani yakuti “Yehova Akutitsogolera ku Chilakiko.” Kungoyambira pamene anali oŵerengeka, pambuyo pa Nkhondo Yadziko I, Yehova Mulungu watsogolera atumiki ake okhulupirika ku chilakiko polalikira uthenga wabwino wa Ufumu, mosasamala kanthu za chizunzo. Mu 1931 Ophunzira Baibulo, monga momwe kalelo anali kudziŵikira, anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova, ndiye atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anangovala manyazi. “Kalasi ya 102 ya amishonale ophunzitsidwa pa Gileadi tsopano ili ndi mwaŵi waukulu wochita mbali yaikulu pantchito yaulemerero yopatsa ambiri mpata wolidziŵa dzina limeneli,” anafotokoza choncho Mbale Barber. Aloŵa pamzera wautali wa amishonale 7,131 amene anaphunzira pa Sukulu ya Gileadi ndi amene anathandiza kufalitsa Mawu a Mulungu kuyambira pa maiko 54 mu 1943 mpaka maiko 233 lerolino.

Mlankhuli wotsatira, Lloyd Barry, nayenso wa Bungwe Lolamulira, anali womaliza maphunziro a kalasi ya 11 ya Gileadi ndipo anakhalapo mmishonale ku Japan kwa zaka zoposa 25. Anawalimbikitsa ndi nkhani yake yakuti ‘Muzikhala mu Izi.’ Anawauza ophunzirawo kuti “kupirira ndiko kudzakupatsani chimwemwe chachikulu.” Kodi kupirira pantchito yaumishonale kapena ina iliyonse yateokrase kuli ndi mapindu otani? “Koposa zonse, chipiriro chathu chimasangalatsa mtima wa Yehova . . . Timakhutira kwambiri ngati tikhulupirika pachiyeso . . . Pangani utumiki waumishonale kungokhala ntchito ya moyo wanu wonse . . . Mphoto yanu idzakhala kuyamikiridwa ndi mtima wonse kuti ‘wachita bwino.’” (Mateyu 25:21, NW; Miyambo 27:11) Potsiriza nkhani yake Mbale Barry anawalangiza mwachikondi amishonale atsopanowo kuti ‘azikhala mu izi’ mwa kutsimikiza kuti munda waumishonale udzangokhala moyo wawo.​—1 Timoteo 4:16.

“Kodi Mudzaona Chiyani?” linali funso limene anafunsa Karl Adams, yemwe anaphunzitsapo kwa zaka zambiri pa Gileadi. Ananena kuti zimene amishonale atsopanowo ati akaone sakaziona ndi maso enieni okhawa iyayi komanso ndi maso a mtima wawo. (Aefeso 1:18) Azondi achiisrayeli anasonyeza zimenezi pamene anakazonda Dziko Lolonjezedwa. Azondi onse 12 anaona ndi maso aumunthu zinthu zofananazo, koma aŵiri okha ndiwo anaona Dziko Lolonjezedwa monga mmene Mulungu analionera. Amishonalenso angaone zinthu mosiyanasiyana. Kumaiko ena kumene adzakhala akutumikira, angaone umphaŵi, kuvutika, ndi kupanda chiyembekezo. Koma sayenera kunyansidwa nazo ndi kuchokamo m’dzikomo iyayi. Mbale Adams anatchula za mmishonale wina wa m’kalasi yaposachedwapa amene anati: “Zokumana nazo zimenezi zimandipangitsa kuzindikira kuti ndiyenera kukhala konkuno. Anthu ameneŵa akufunikira chiyembekezo chamtsogolo. Ndikufuna ndiwongolere moyo wawo.” Mbale Adams anamaliza mwa kuwalimbikitsa amishonale atsopanowo kuti aziona maiko kumene atumizidwako monga madera amene Yehova akufuna kuwapanga mbali ya Paradaiso Wake wapadziko lonse ndi kumawaona anthu okhala kumeneko monga anthu oyembekezera kudzakhala m’dziko latsopano.

Nkhani yotsiriza pambali iyi ya programu inali ya Wallace Liverance, yemwe anali m’munda waumishonale kwa zaka zambiri asanakhale mlangizi wa Gileadi. “Chitani Mwanzeru Pozindikira Ntchito Zodabwitsa za Mulungu” ndiwo unali mutu wankhani yake. Kuchita mwanzeru ndiko kuchita mosamala, mochenjera, ndi mozindikira. Zimenezo nzimene Mfumu Sauli wa Israyeli analephera kuchita.​—1 Samueli 13:9-13; 15:1-22.

Njira ina yochitira mwanzeru ndiyo kuzoloŵera moyo watsopano, kuphatikizapo kuphunzira chinenero chatsopano ndi kuwadziŵa anthu. Zokumana nazo za amishonale polimbana ndi mavuto ndi kulaka zopinga zingawalimbikitse mwauzimu mofanana ndi mmene zinalimbikitsira Yoswa ndi Kalebi pamene analanda dziko limene Mulungu anawapatsa.

Kufunsa

Mbali yotsatira ya programuyo inali mpambo wa mafunso. Harold Jackson anafunsa Ulysses Glass, wosunga kaundula ndi mlangizi wanthaŵi yaitali wa Sukulu ya Gileadi, yemwe tsopano ngwa zaka 85 zakubadwa. Amishonale ambiri amene adakali m’munda amakumbukira zaka zake zophunzitsa mokhulupirika. Kenako panafika Mark Noumair, mlangizi wa Gileadi amene anatha zaka zambiri mu utumiki wam’dziko lachilendo mu Afirika asanakhale mphunzitsi pa Sukulu ya Gileadi. Anawafunsa ophunzirawo za utumiki wawo pamiyezi isanu yasukulu yawo. Zokumana nazo zawo zinasonyeza bwino kuti m’gawo la kumeneko muli anthu ofuna Mawu a Mulungu.

Ndiyeno Robert Ciranko ndi Charles Molohan analankhula ndi amuna ena achidziŵitso omwe anali kuloŵa sukulu ina pomwepo, sukulu ya antchito a panthambi. Uphungu umene anawapatsa omaliza maphunzirowo unaphatikizapo kufunika kwa kudzichepetsa ndi kuthandiza kusunga umodzi wampingo. Iwo ananena kuti omaliza maphunzirowo sayenera kuganizira zimene zidzawachitikira m’ntchito yaumishonale, koma akhale okonzekera mkhalidwe uliwonse. Ndithudi, kugwiritsira ntchito uphungu umenewu kudzawathandiza amishonale atsopanowo kuchita ntchito yawo monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu.

Potsirizira, Theodore Jaracz, wa Bungwe Lolamulira, analankhula ndi omvetsera m’nkhani yakuti “Kodi Ndani Akusonkhezera Wina?” Analongosola kuti pamene Akristufe tisonyeza zipatso za mzimu, timawasonkhezera ena kuchita zabwino. “Amishonale amene gulu la Yehova latumiza akhala ndi mbiri yabwino yosonkhezera anthu m’njira yabwino yauzimu,” anatero. Ndiyeno anatchula ndemanga za anthu ena amene anathandizidwa kutumikira Mulungu chifukwa cha zitsanzo zabwino zimene amishonale amasonyeza. “Sunganibe mbiri imene anthu a Yehova ali nayo ndipo gogodanibe pamakomo m’dera lanu lachilendo pofunafuna oyenera . . . Ndiponso, mwa khalidwe lanu labwino ndi loyera, tsutsani mzimu wadzikoli, ndipo sonkhezerani ena kuchita zabwino kuti atamande Yehova ndi kumpatsa ulemu,” anamaliza choncho.

Potsiriza programuyo, tcheyamani anapereka malonje ochokera kwa ena apafupi ndi kutali ndiyeno anapereka madiploma ndiponso nalengeza maiko kumene anatumizidwa. Pambuyo pa zimenezo, mmodzi wa omaliza maphunzirowo anaŵerenga kalata ya kalasiyo yoyamikira malangizo amene analandira. Mwachionekere, programu ya omaliza maphunziro a kalasi ya 102 inapangitsa onse amene analipo kukhala ofunitsitsa kulalikira Mawu a Mulungu.

[Chithunzi patsamba 31]

Kalasi ya 102 ya Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

Pampambo uli pansiwu, mizera taŵerenga kuyambira kumaso kumka kumbuyo, ndipo maina talemba kuyambira kulamanzere kumka kulamanja pamzera uliwonse.

(1) Duffy, C.; Alexis, D.; Harff, R.; Corey, J.; Nortum, T; Mora, N.; Mora, N.; Journet, F. (2) Djupvik, L.; Singh, K.; Hart, B.; Kirkoryan, M.; Lee, S.; Rastall, S.; Zoulin, K.; Kollat, K. (3) Singh, D.; Pitteloud, J.; Pitteloud, F.; Bokoch, N.; Torma, C.; Muxlow, A.; Richardson, C.; Nortum, D. (4) Harff, J.; Journet, K.; Barber, A.; Loberto, J.; Loberto, R.; Muxlow, M.; Mora, R.; Hart, M. (5) Torma, S.; Rastall, A.; Diaz, R.; Diaz, H.; Weiser, M.; Weiser, J.; Kirkoryan, G.; Zoulin, A. (6) Alexis, R.; Barber, D.; Djupvik, H.; Duffy, C.; Kollat, T.; Richardson, M.; Bokoch, S.; Corey, G.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena