Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 12/1 tsamba 15-20
  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Liwu Lakuti “Chipembedzo” m’Baibulo
  • ‘Koyera ndi Kosadetsa’ Pamaso pa Mulungu
  • “Wosachitidwa Maŵanga ndi Dziko Lapansi”
  • Zizindikiro Zina za Chipembedzo Chowona
  • Chipembedzo Chowona​—Njira ya Moyo
  • Mphamvu Yabwino, Yogwirizanitsa
  • Chilakiko cha Chipembedzo Choyera
  • Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 12/1 tsamba 15-20

Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso

“Chipembedzo chimene chiri choyera ndi chenicheni pamaso pa Mulungu Atate chidzawonekera chokha mwa zinthu zonga . . . kudzisungira kwa munthu osadetsedwa ndi dziko.”​—YAKOBO 1:27, Phillips.

1. Kodi chipembedzo chamasuliridwa motani, ndipo kodi ndani mwanzeru yemwe ali ndi kuyenerera kwakuika malire pakati pa chipembedzo chonyenga ndi chowona?

CHIPEMBEDZO chamasuliridwa kukhala “chisonyezero cha chikhulupiriro cha munthu ndi mantha aulemu kwa mphamvu yoposa yaumunthu yozindikiridwa monga mlengi ndi wolamulira wa chilengedwe chonse.” Pamenepo, kodi ndani mwanzeru, amene ali ndi kuyenerera kwa kuika malire pakati pa chipembedzo chowona ndi chipembedzo chonyenga? Ndithudi ayenera kukhala Uyo amene amakhulupiriridwa ndi kuwopedwa mwaulemu, Mlengi. Yehova wasonyeza bwino lomwe m’Mawu ake lingaliro lake pa chipembedzo chowona ndi chonyenga.

Liwu Lakuti “Chipembedzo” m’Baibulo

2. Kodi ndimotani mmene madikishonale amalongosolera liwu loyambirira Lachigiriki lotembenuzidwa “mtundu wa kulambira” kapena “chipembedzo,” ndipo kodi ilo lingagwiritsiridwe ntchito ku mitundu ya kulambira yotani?

2 Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “mtundu wa kulambira,” kapena “chipembedzo,” nlakuti thre·skeiʹa. A Greek-English Lexicon of the New Testament imamasulira liwuli kukhala “kulambiridwa kwa Mulungu, chipembedzo, mak[amaka] pamene imanena za iyo yokha mu za utumiki wachipembedzo kapena dzoma.” Theological Dictionary of the New Testament imapereka tsatanetsatane wowonjezereka, ikumati: “Mbiri ya tanthauzo lake imatsutsidwa; . . . akatswiri amakono amayanja liwu logwirizanitsa lakuti therap- (‘kutumikira’). . . . Kusiyana kwa tanthauzo kungawonedwenso. Lingaliro labwino nlakuti ‘changu chachipembedzo’ . . . , ‘kulambiridwa kwa Mulungu,’ ‘chipembedzo.’ . . . Koma palinso lingaliro loipa, ndilo, ‘kupambanitsa kwachipembedzo,’ ‘kulambira kolakwa.’” Chotero, thre·skeiʹa lingatembenuzidwe kukhala kaya “chipembedzo” kapena “mtundu wa kulambira,” kwabwino kapena koipa.

3. Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anagwiritsirira ntchito liwu lotembenuzidwa “mtundu wa kulambira,” ndipo kodi ndi ndemanga yokondweretsa yotani imene inaperekedwa pa kutembenuzidwa kwa Akolose 2:18?

3 Liwuli limawonekera kanayi kokha m’Malemba Achikristu Achigiriki. Mtumwi Paulo analigwiritsira ntchito kaŵiri kutanthauza chipembedzo chonyenga. Pa Machitidwe 26:5, panalembedwa mawu ake akunena za nthaŵi yakumbuyo asanakhale Mkristu, ‘ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa [kulambira, NW] [“chipembedzo,” Phillips] kwathu.’ M’kalata yake kwa Akolose, iye anachenjeza kuti: ‘Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwiniwake, ndi [kulambira, NW] angelo.’ (Akolose 2:18) Mwachiwonekere, kulambira angelo koteroko kunali kofalikira m’Frugiya m’masikuwo, koma kunali mtundu wa chipembedzo chonyenga.a Mokondweretsa, pamene kuli kwakuti matembenuzidwe ena a Baibulo amamasulira thre·skeiʹa kukhala “chipembedzo,” pa Akolose 2:18, ambiri amagwiritsira ntchito liwu la “kulambira.” New World Translation mosasintha imatembenuza thre·skeiʹa monga “mtundu wa kulambira,” mawu am’tsinde mu Reference Bible nthaŵi zonse akumatchula liwu lina lolitembenuzira la “chipembedzo” logwiritsiridwa ntchito m’matembenuzidwe Achilatini.

‘Koyera ndi Kosadetsa’ Pamaso pa Mulungu

4, 5. (a) Malinga ndi Yakobo, kodi ndilingaliro layani la chipembedzo limene liri lofunika koposa? (b) Kodi nchiyani chimene chingapangitse mtundu wa kulambira kwa munthu kukhala wopanda pake, ndipo kodi liwu lotembenuzidwa ‘chopanda pake’ limatanthauzanji?

4 Malo ena aŵiri pamene liwu la thre·skeiʹa limapezeka ndi m’kalata yolembedwa ndi wophunzira Yakobo, chiŵalo cha bungwe lolamulira la mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba. Iye analemba kuti: “Ngati wina adziyesera ali wolambira [“kukhala ‘wachipembedzo,’” Phillips] komabe samanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, mtundu wa kulambira [“chipembedzo,” Phillips] wa munthuyu ngwopanda pake. Mtundu wa kulambira [“chipembedzo,” Phillips] koyera ndi kosadetsa pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate ndiwo: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.”​—Yakobo 1:26, 27, NW.

5 Inde, kusunga lingaliro la Yehova la chipembedzo nkofunika ngati tifuna kukhala ndi chivomerezo chake ndi kupulumuka kuloŵa m’dziko latsopano limene iye walonjeza. (2 Petro 3:13) Yakobo akusonyeza kuti munthu angadziwone kukhala wachipembedzo kwenikweni komabe mtundu wa kulambira kwake ungakhale wopanda pake. Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa panopa ‘chopanda pake’ limatanthauzanso “chachabe, chopanda kanthu, chosaphula kanthu, chopanda ntchito, chopanda mphamvu, chopanda chowonadi.” Zingakhale tero ngati wina wodzitcha kukhala Mkristu sanamange lilime lake kuligwiritsira ntchito kutamanda Mulungu ndi kumangirira Akristu anzake. Iye akakhala ‘akudzinyenga mtima wake’ ndi kusalondola “chipembedzo chimene chiri choyera ndi chenicheni pamaso pa Mulungu.” (Phillips) Lingaliro la Yehova ndilo liri kanthu.

6. (a) Kodi kalata yolembedwa ndi Yakobo iri ndi mutu wanji? (b) Kodi nchiyeneretso chotani cha kulambira koyera chimene Yakobo anagogomezera, ndipo kodi Bungwe Lolamulira lamakono lanenanji pambali imeneyi?

6 Yakobo sakundandalitsa zinthu zonse zimene Yehova amafuna ponena za kulambira koyera. Mogwirizana ndi mutu waukulu wa kalata yake, umene ndiwo chikhulupiriro chotsimikiziridwa ndi ntchito zake ndi kufunika kwa kusakhala paubwenzi ndi dziko la Satana, iye akugogomezera ziyeneretso ziŵiri zokha. Chimodzi ndicho “kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” Ichi chimaphatikizapo chikondi chowona Chachikristu. Yehova nthaŵi zonse wasonyeza nkhaŵa yachikondi kwa ana amasiye ndi akazi amasiye. (Deuteronomo 10:17, 18; Malaki 3:5) Chimodzi cha zochita zoyambirira za bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba la mpingo Wachikristu chinali chokomera akazi amasiye Achikristu. (Machitidwe 6:1-6) Mtumwi Paulo anapereka malangizo atsatanetsatane akupereka chisamaliro chachikondi kwa akazi amasiye okalamba osoŵa chithandizo omwe anatsimikizira kukhala okhulupirika kwa zaka zambiri ndi omwe analibe banja lowathandiza. (1 Timoteo 5:3-16) Bungwe Lolamulira lamakono la Mboni za Yehova mofananamo lapereka malangizo oyenerera a “Kusamalira Osauka,” likumati: “Kulambira kowona kumaphatikizapo kusamalira okhulupirika ndi odalirika amene angakhale osoŵa chithandizo chakuthupi.” (Onani bukhu la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 122-3.) Mabungwe a akulu kapena Akristu pa okha omwe amanyalanyaza mbali imeneyi amaphonya mbali yofunika kwambiri ya mtundu wa kulambira kumene kuli koyera ndi kosadetsa pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.

“Wosachitidwa Maŵanga ndi Dziko Lapansi”

7, 8. (a) Kodi nchiyeneretso chachiŵiri chotani cha chipembedzo chowona chimene Yakobo anatchula? (b) Kodi atsogoleri achipembedzo ndi ansembe amachikwaniritsa chofunika chimenechi? (c) Kodi nchiyani chimene chinganenedwe kwa Mboni za Yehova?

7 Chiyeneretso chachiŵiri cha chipembedzo chowona chotchulidwa ndi Yakobo chinali “kudzisungira mwini wosachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.” Yesu ananena kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi”; mosasiyana, otsatira ake owona ‘sakakhala a dziko lapansi.’ (Yohane 15:19; 18:36) Kodi zimenezi zinganenedwe kwa atsogoleri achipembedzo ndi ansembe a zipembedzo zirizonse za dziko lino? Iwo amavomereza Mitundu Yogwirizana. Ambiri a atsogoleri awo analandira chiitano cha papa chokakumana ku Assisi, Italiya, mu October 1986 kuti akagwirizanitse mapemphero awo kaamba ka chipambano cha “Chaka cha Mtendere cha Mitundu Yonse” chochirikizidwa ndi Mitundu Yogwirizana. Komabe, kuphedwa kwa mamiliyoni m’nkhondo za chaka chimenecho ndi zaka zotsatira kufikira leroli, kumasonyeza kuti zoyesayesa zawo zinali zopanda pake. Atsogoleri achipembedzo kaŵirikaŵiri amachita chibwenzi ndi chipani cholamulira, pamene kuli kwakuti mwamachenjera amachitanso zamtseri ndi otsutsa kotero kuti aliyense amene adzalamulira adzawawone kukhala ‘mabwenzi.’​—Yakobo 4:4.

8 Mboni za Yehova zadzipangira dzina labwino monga Akristu amene amasunga uchete m’nkhani za ndale zadziko ndi mikangano ya dziko lino. Iwo amasunga kaimidwe kameneka m’maiko onse ndi mitundu, monga momwe amachitiridwa umboni ndi malipoti a nkhani za panyuzindi zolembedwa zamakono za mbiri m’mbali zonse za dziko. Iwo alidi “osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.” Chawo chiri “chipembedzo chimene chiri choyera ndi chenicheni pamaso pa Mulungu.”​—Yakobo 1:27, Phillips.

Zizindikiro Zina za Chipembedzo Chowona

9. Kodi chiyeneretso chachitatu cha chipembedzo chowona nchotani, ndipo chifukwa ninji?

9 Ngati chipembedzo ndicho “mantha aulemu kwa mphamvu yoposa yaumunthu yozindikiridwa monga mlengi ndi wolamulira wa chilengedwe chonse,” ndithudi chipembedzo chowona chiyenera kupereka kulambira kwake kwa Mulungu wowona yekha, Yehova. Sichiyenera kuphimba anthu kumvetsetsa kwawo Mulungu mwakuwaphunzitsa malingaliro achikunja onga mulungu wautatu amene Atate amagaŵana ukulu wake, ulemerero, ndi umuyaya ndi anthu ena aŵiri mu Utatu wachinsinsi. (Deuteronomo 6:4; 1 Akorinto 8:6) Chiyeneranso kudziŵikitsa dzina losayerekezereka la Mulungu, Yehova, ndi kulemekeza dzinalo, ndithudi kutenga dzina la Mulungu monga anthu olinganizidwa. (Salmo 83:18; Machitidwe 15:14) Ochilondola ayenera kutsatira chitsanzo cha Kristu Yesu m’zimenezi. (Yohane 17:6) Kodi ndianthu ati lerolino omwe amachikwaniritsa chiyeneretso chimenechi kusiyapo Mboni za Yehova Zachikristu?

10. Kuti chipembedzo chipereke chipulumutso kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu, kodi chiyenera kuchitanji, ndipo chifukwa ninji?

10 Mtumwi Petro ananena kuti: ‘Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina [Yesu Kristu] pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.’ (Machitidwe 4:8-12) Motero, chipembedzo choyera chimene chidzapereka chipulumutso kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu chiyenera kusonkhezera chikhulupiriro mwa Kristu ndi mtengo wa nsembe yadipo. (Yohane 3:16, 36; 17:3; Aefeso 1:7) Ndiponso, chiyenera kuthandiza olambira owona kugonjera kwa Kristu monga Mfumu yolamulira ya Yehova ndi Mkulu Wansembe wodzozedwa.​—Salmo 2:6-8; Afilipi 2:9-11; Ahebri 4:14, 15.

11. Kodi chipembedzo chowona chiyenera kuzikidwa pachiyani, ndipo kodi Mboni za Yehova zikuchita motani m’mbali imeneyi?

11 Chipembedzo choyera chiyenera kuzikidwa pa chifuniro chovumbulidwa cha Mulungu yekha wowona ndipo osati pa miyambo kapena nthanthi zopangidwa ndi anthu. Popanda Baibulo, sitikadadziŵa chirichonse ponena za Yehova ndi zifuno zake zodabwitsa, osati ngakhale Yesu ndi nsembe yadipo. Mboni za Yehova zimakhomereza mwa anthu chidaliro chosagwedezeka m’Baibulo. Izo zimasonyezanso m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku kuti zimagwirizanadi ndi ndemanga ya mtumwi Paulo yakuti: ‘Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, . . . kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.’​—2 Timoteo 3:16, 17.

Chipembedzo Chowona​—Njira ya Moyo

12. Kuwonjezera pa chikhulupiriro, kodi chofunikanso nchiyani kuti kulambira kukhale kowona, ndipo kodi chipembedzo chiri njira ya moyo m’mbali zotani?

12 Yesu analengeza kuti: ‘Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:24) Chotero, chipembedzo chowona, kapena mtundu wa kulambira, sichisonyezero chakunja cha umulungu, chamwambo kapena dzoma. Kulambira koyera kuli kwauzimu, kozikidwa pa chikhulupiriro. (Ahebri 11:6) Komabe, chikhulupiriro chimenecho chiyenera kuchirikizidwa ndi ntchito. (Yakobo 2:17) Chipembedzo chowona chimakana zizoloŵezi zofala. Chimamamatira ku miyezo ya Baibulo ya makhalidwe ndi kulankhula mawu abwino. (1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 5:3-5) Amene amachilondola amayesayesa mowona mtima kubala zipatso za mzimu wa Mulungu m’banja lawo, kuntchito yawo yakuthupi, pasukulu, ndipo ngakhale m’zosangulutsa zawo. (Agalatiya 5:22, 23) Mboni za Yehova zimayesayesa kusaiŵala konse uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: ‘Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.’ (1 Akorinto 10:31) Chipembedzo chawo sichiri chizoloŵezi wamba; chiri njira ya moyo.

13. Kodi kulambira kowona kumaloŵetsamo chiyani, ndipo kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Mboni za Yehova ziridi anthu opembedza?

13 Ndithudi, chipembedzo chowona chimaloŵetsamo zochita zauzimu. Izi zimaphatikizapo pemphero laumwini ndi labanja, phunziro lokhazikika la Mawu a Mulungu ndi zothandizira kuphunzira Baibulo, ndi kupezeka pamisonkhano yampingo ya Chikristu chowona. Zotsirizirazi zimatsegulidwa ndi kutsekedwa ndi nyimbo zotamanda Yehova ndi mapemphero. (Mateyu 26:30; Aefeso 5:19) Nkhani zauzimu zomangirira zimapendedwa mwa nkhani zoperekedwa ndi kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho kwa zinthu zosindikizidwa zopezeka kwa onse. Misonkhano yoteroyo kaŵirikaŵiri imachitidwa m’Nyumba Zaufumu zaudongo koma zosakongoletsedwa mopambanitsa, zimene zimagwiritsiridwa ntchito kokha kaamba ka zifuno zachipembedzo: misonkhano yanthaŵi zonse, maukwati, mautumiki achikumbutso. Mboni za Yehova zimalemekeza Nyumba zawo Zaufumu ndi Maholo Osonkhanira aakulu monga malo operekedwa ku kulambiridwa kwa Yehova. Mosiyana ndi matchalitchi ambiri a Chikristu Chadziko, Nyumba Zaufumu siziri makalabu amayanjano.

14. Kodi kulambira kunatanthauzanji kwa anthu olankhula Chihebri, ndipo kodi nzochita zotani zimene zimazindikiritsa Mboni za Yehova lerolino?

14 Tawona poyamba kuti akatswiri amagwirizanitsa liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “mtundu wa chipembedzo” kapena “chipembedzo” ndi mneni wakuti “kutumikira.” Mokondweretsa, liwu lofanana Lachihebri, ‛avo·dhahʹ, lingatembenuzidwe kukhala “utumiki” kapena “kulambira.” (Yerekezerani ndi mawu am’tsinde pa Eksodo 3:12 ndi 10:26, NW.) Kwa Ahebri, kulambira kunatanthauza utumiki. Ndipo nzimene kumatanthauzanso kwa olambira owona lerolino. Chizindikiro chosiyanitsa, chofunika kwambiri cha chipembedzo chowona nchakuti onse ochilondola amakhala ndi phande muutumiki waumulungu wakulalikira “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu . . . m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse.” (Mateyu 24:14, NW; Machitidwe 1:8; 5:42) Kodi nchipembedzo chiti chimene chiri chodziŵika padziko lonse kaamba ka kuchitira umboni poyera Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokha cha anthu?

Mphamvu Yabwino, Yogwirizanitsa

15. Kodi chipembedzo chowona chimadziŵika ndi chinthu chapadera chotani?

15 Chipembedzo chonyenga chimadzetsa magaŵano. Chinachititsa, ndipo chikuchititsabe chidani ndi kukhetsa mwazi. Mosiyana, chipembedzo chowona chimagwirizanitsa. Yesu ananena kuti: ‘Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:35) Chikondi chimene chimagwirizanitsa Mboni za Yehova sichimawona malire autundu, mayanjano, chuma, ndi fuko amene amagaŵagaŵa anthu onse. Mbonizo ‘zikuchirimika mumzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha [mbiri yabwino, NW].’​—Afilipi 1:27.

16. (a) Kodi ndi “mbiri yabwino” yotani imene Mboni za Yehova zimalalikira? (b) Kodi ndimaulosi otani amene akukwaniritsidwa pa anthu a Yehova, ndipo kodi ndimadalitso otani amene atsatirapo?

16 “Mbiri yabwino” imene amailalikira njakuti posachedwapa chifuno cha Mulungu chosasintha chidzakwaniritsidwa. Chifuniro chake chidzachitidwa, ‘monga kumwamba chomwecho pansi pano.’ (Mateyu 6:10) Dzina laulemerero la Yehova lidzayeretsedwa, ndipo dziko lapansi lidzakhala paradaiso, m’mene olambira owona adzakhoza kukhala ndi moyo kosatha. (Salmo 37:29) M’lingaliro lenileni, mamiliyoni a anthu m’maiko onse akugwirizana ndi Mboni za Yehova, akumati, m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Yehova akudalitsa anthu ake. ‘Wochepa’ wakhaladi “mtundu wamphamvu,” ndiwo mpingo wadziko lonse wogwirizana kotheratu m’mbali zonse​—m’lingaliro, m’ntchito, m’kulambira. (Yesaya 60:22) Ichi ndichinthu chimene chipembedzo chonyenga chakhala chosakhoza konse kuchikwaniritsa.

Chilakiko cha Chipembedzo Choyera

17. Kodi nchiyani chimene chikuyembekezera Babulo Wamkulu, ndipo kodi ndimotani mmene chimenechi chidzachitikira?

17 Mawu a Mulungu ananeneratu chiwonongeko cha ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga, mophiphiritsira wotchedwa ‘Babulo Wamkulu.’ Baibulo limaphiphiritsanso “mafumu,” kapena olamulira andale zadziko, a dziko lapansi ndi chizindikiro cha nyanga za chirombo cholusa. Limatiuza kuti Mulungu adzaika m’mitima mwa olamulira ameneŵa chifuno cha kugubuduza ndi kuwononga kotheratu chiungwe chonga mkazi wachigololo chimenechi cha Satana Mdyerekezi.​—Onani Chibvumbulutso 17:1, 2, 5, 6, 12, 13, 15-18.b

18. Kodi nchifukwa chachikulu chotani chimene Baibulo limapereka chakumuwonongera Babulo Wamkulu, ndipo kodi ndiliti pamene chipembedzo chonyenga chinayamba njira yake yowopsa?

18 Kodi nchifukwa ninji Babulo Wamkulu ali woyenerera chiwonongeko? Baibulo limayankha kuti: ‘[Mwa iye, NW] munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.’ (Chibvumbulutso 18:24) Posonyeza kuti liŵongo lamwazili la chipembedzo chonyenga limabwerera kumbuyo ngakhale kupyola pamene Babulo anayamba, Yesu anatsutsa atsogoleri achipembedzo a Chiyuda, chimene chinadziphatika ku Babulo Wamkulu, pamene anati: ‘Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthaŵa kulanga kwake kwa gehena? . . . Udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira ku mwazi wa Abele wolungamayo.’ (Mateyu 23:33-35) Inde, chipembedzo chonyenga, chimene chinayamba padziko lapansi panthaŵi ya chipanduko m’Edene, chiyenera kuyankha liŵongo lake lamwazi lowopsalo.

19, 20. (a) Kodi olambira owona adzachitanji pambuyo pakuperekedwa kwa chiweruzo pa Babulo Wamkulu? (b) Ndiyeno kodi nchiyani chimene chidzachitika, ndipo kodi nchiyembekezo chotani chimene chidzatseguka kwa olambira owona?

19 Pambuyo pa kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, olambira owona padziko lapansi adzathirira mang’ombe pamodzi ndi gulu lakumwamba limene likuimba kuti: ‘Aleluya . . . pakuti . . . waweruzidwa mkazi wachigololo wamkulu . . . ndipo wabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo. . . . Ndipo utsi wake ukwera ku nthaŵi za nthaŵi.’​—Chibvumbulutso 19:1-3.

20 Ndiyeno mbali zina zopanga gulu lowoneka la Satana zidzawonongedwa. (Chibvumbulutso 19:17-21) Pambuyo pa zimenezi, Satana, woyambitsa wa chipembedzo chonyenga chonse, ndi ziŵanda zake adzaponyedwa mphompho. Sadzakhalanso omasuka kuzunza olambira owona a Yehova. (Chibvumbulutso 20:1-3) Chipembedzo choyera chidzakhala chitalakika pa chonyengacho. Amuna ndi akazi okhulupirika omwe akulabadira chenjezo laumulungu lakuthaŵa tsopano kuchoka m’Babulo Wamkulu adzakhala ndi mwaŵi wakupulumuka ndi kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. M’menemo, adzakhala okhoza kulondola chipembedzo chowona ndi kutumikira Yehova mwakumlambira kosatha.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze malongosoledwe a kulambira angelo kotchulidwa pa Akolose 2:18, onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 1986, masamba 12-13.

b Kuti mupeze malongosoledwe okwanira a ulosi umenewu, onani bukhu la Revelation​—Its Grand Climax At Hand! lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., mitu 33-6.

Yesani Chikumbukiro Chanu

◻ Kodi ndilingaliro layani la chipembedzo limene liri lofunika koposa, ndipo chifukwa ninji?

◻ Kodi nziyeneretso ziŵiri zotani za chipembedzo chowona zimene Yakobo anagogomezera?

◻ Kodi zofunika zina za kulambira koyera nzotani?

◻ Kodi ndi “mbiri yabwino” yotani imene Mboni za Yehova zikulalikira?

◻ Kodi chipembedzo chowona chidzalakika motani pa chipembedzo chonyenga?

[Chithunzi patsamba 17]

Atsogoleri achipembedzo anasonkhana ku Assisi, Italiya, mu October 1986

[Chithunzi patsamba 19]

Chipembedzo chowona chimaloŵetsamo kusonkhana pamodzi kaamba ka kulambira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena