Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 6/15 tsamba 5-7
  • Posachedwapa Sikudzakhalanso Matenda Kapena Imfa!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Posachedwapa Sikudzakhalanso Matenda Kapena Imfa!
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambi cha Matenda ndi Imfa
  • Padziko Lapansi Kapena Kumwamba?
  • Nchifukwa Ninji Zidzachitika Posachedwapa?
  • Thanzi Labwino kwa Onse—Lifika Posachedwapa!
    Galamukani!—2001
  • Matenda Onse Adzatha!
    Galamukani!—2007
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 6/15 tsamba 5-7

Posachedwapa Sikudzakhalanso Matenda Kapena Imfa!

PALIBE amene amasangalala ndi kudwala, ndiponso anthu samafuna kufa. Profesa wamwamuna wa maphunziro a zitaganya zamankhwala akutsimikiza kuti: “Kufunafuna moyo wautali kukuwoneka kukhala kwapadziko lonse m’mbiri yonse ndi m’zitaganya zambiri. Nkogwirizana ndi chikhumbo chachikulu cha kudzitetezera . . . Ponce de Leon ndi munthu mmodzi yekha wotchuka pa anthu ambiri amene anathera moyo wawo wonse akufunafuna moyo wautali. Mbali yaikulu ya sayansi ya zamankhwala njodzipereka ku kusunga moyo wautali kupyolera m’kuthetsa matenda ndi imfa.”

Imfa imaswa ndi kupweteka chibadwa chathu kwakuti pamene igonjetsa mabwenzi kapena ziŵalo zabanja, mwachibadwa timayesayesa kuchepetsa mphamvu yake. Bukhu lakuti Funeral Customs the World Over linafotokoza kuti: “Palibe gulu la anthu, kaya likhale losatsungula kapena lotsungula motani, lomwe litalekereredwa lokha ndi kuthekera kwake limene silimataya mitembo ya anthu ake ndi mwambo. . . . Limakhutiritsa zikhumbo zakuya zapadziko lonse. Kuchita zimenezo kumawoneka kukhala ‘kolondola,’ ndipo kusachita zimenezo, makamaka kwa awo amene ali ogwirizana thithithi mwa banja, malingaliro, kukhalira pamodzi, zokumana nazo zofala kapena maunansi ena, kumawoneka kukhala ‘kulakwa,’ chophophonya chosakhala chachibadwa, chinthu chofunikira kupempha chikhululukiro kapena kuchita nacho manyazi. . . . [Munthu] ndi chamoyo chimene chimakwirira akufa ake mwamwambo.”

Chiyambi cha Matenda ndi Imfa

Chotero, lingaliro lakuti tsiku lina matenda ndi imfa zidzachotsedwa liri ndi chisonkhezero champhamvu, koma kodi pali maziko kaamba ka chikhulupiriro choterocho? Ndithudi alipo, ndipo ali ponse paŵiri oyenerera, odalirika, ndi osalakwika. Ndiwo Mawu ouziridwa a Mlengi wathu​—Baibulo Lopatulika.

Bukhu limenelo limalongosola momvekera bwino lomwe chiyambi cha mavuto a anthu. Limatiuza kuti munthu woyamba, Adamu, analengedwa ndi Mulungu ndi kuikidwa m’mudzi wa munda waparadaiso womwe unali cha ku Middle East. Adamu analengedwa wangwiro; iye sanadziŵe matenda ndi imfa. Posakhalitsa iye anagwirizana ndi mkazi yemwe analinso wangwiro monga iye, ndipo onse pamodzi anasangalala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya padziko lapansi.​—Genesis 2:15-17, 21-24.

Mkhalidwe wabwino umenewu sunakhalitse. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mwadyera Adamu anasankha njira yamoyo yodziimira payekha osadalira pa Mulungu. Ntchito yakalavula gaga, kupweteka, matenda, ndipo pomalizira pake imfa ndizo zinatulukapo. (Genesis 3:17-19) Ana ake anapeza choloŵa cha moyo wopanda chimwemwe umene Adamu anasankha. Aroma 5:12 akulongosola kuti: ‘Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.’ Aroma 8:22 akuwonjezera kuti: ‘Pakuti tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.’

Padziko Lapansi Kapena Kumwamba?

Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu adzabwezeretsa posachedwapa anthu omvera ku mkhalidwe wachimwemwe umene Adamu ndi Hava anautaya. Chibvumbulutso 21:3, 4 chimati: ‘Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.’ Mofananamo mneneri wakale anawoneratu nthaŵi imene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—Yesaya 33:24.

Kodi mungalingalire dziko lopanda zipatala, mamotchale, ndi manda? Kodi mungalingalire kukhala ndi moyo kosatha, popanda chiwopsezo cha kuvutika ndi imfa? Inde, malonjezo a Mulungu amakhudza malingaliro a mkati mwathu tonsefe. Komabe, kodi tingakhale otsimikiza motani kuti chiyembekezo chosangalatsa chimenechi chidzachitika papulaneti lathu la Dziko Lapansi​—osati kumwamba? Tamverani mawu apatsogolo ndi apambuyo pa Malemba otchulidwawo. Mavesi oyambirira a Chibvumbulutso mutu 21 akulankhula za “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano.” Ndemanga yomvekera bwino yanenedwa yakuti Mulungu adzakhala ndi anthu ndikuti iwo adzakhala anthu ake. Lonjezo la m’bukhu la Yesaya lakuti wokhalamo sadzadwala latsatiridwa ndi chilozero kwa ‘anthu okhala mmenemo,’ amene ‘akhululukidwa mphulupulu zawo.’

Choncho malonjezo olimbikitsa ameneŵa akusonya ku dziko lapansi! Ndipo amagwirizana ndi pemphero la Yesu kwa Atate wake ili: ‘Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’​—Mateyu 6:10.

Nchifukwa Ninji Zidzachitika Posachedwapa?

Mboni za Yehova zathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuzindikira kuti malonjezo ameneŵa adzakwaniritsidwa mtsogolo posachedwapa. Komabe, kodi izo zimakhala zotsimikiza motero pa maziko otani? Pamaziko a umboni wochuluka koposa wakuti tikukhala ndi moyo “m’masiku otsiriza” a dongosolo liripoli, kapena makonzedwe, a zinthu padziko lapansi. (2 Timoteo 3:1-5) Ophunzira a Yesu anafunsa ponena za chizindikiro cha nthaŵi imene mapeto a dongosolo la zinthu akafika. Poyankha Yesu ananeneratu mwatsatanetsatane zochitika zadziko zomwe zachitika chiyambire Nkhondo Yadziko ya I mu 1914.a Kenaka iye anawonjezera kuti: ‘Chomwechonso inu, pamene mudzawona zimenezo, zindikirani kuti iye ali pafupi, inde pakhomo. Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.’ Choncho anthu ena a mbadwo umene unali ndimoyo mu 1914 adzakhala ndi moyo kudzawona mapeto a dongosolo ladziko liripoli.​—Mateyu 24:33, 34.

Panthaŵiyo Yehova Mulungu adzatuma Mwana wake, Kristu Yesu, kunka ndi kuwononga zochititsa kuvutika ndi chisoni zonse kuzichotsa pankhope ya pulaneti yokongola ya Dziko Lapansi. Baibulo limalankhula za kuchotsedwa kwa kuipa monga ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ pa Armagedo.​—Chibvumbulutso 16:14, 16.

Anthu ambiri owopa Mulungu adzapulumuka chochitika chowopsa chimenechi ndikukhala ndi moyo kudzawona kuyambika kwa ulamuliro wamtendere wa Kristu Yesu. (Chibvumbulutso 7:9, 14; 20:4) Chinkana kuti ulamuliro wake udzakhala wochokera kumwamba, zotulukapo zake zopindulitsa zidzasangalalidwa ndi onse okhala padziko lapansi​—ponse paŵiri opulumuka nkhondo ya Armagedo ndi mamiliyoni ambiri amene adzaukitsidwa kwa akufa. Pamenepo lonjezo ili lidzakwaniritsidwa: ‘[Kristu] ayenera kuchita ufumu kufikira [Mulungu, NW] ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.’​—1 Akorinto 15:25, 26.

Chotero mwachidaliro tingafuule kuti: “Posachedwapa sikudzakhalanso matenda kapena imfa!” Ilitu siloto wamba, kapena chilakolako. Ndi lonjezo lotsimikizirika la Yehova Mulungu, “wosanamayo.” Kodi mudzaika chidaliro chanu m’chiyembekezo chimenechi? Kungakupindulitseni kosatha!​—Tito 1:2.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka umboni wowonjezereka wakuti anthu akukhala ndi moyo m’masiku otsiriza, onani mutu 18 wa bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 7]

Posachedwapa matenda ndi imfa zidzaloŵedwa mmalo ndi thanzi labwino ndi moyo wamuyaya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena