Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 3/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nchifukwa Chiyani Yesu Anavutika Mpaka Kufa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Funso Lachiwiri: Kodi Chidzandichitikire N’chiyani Ndikadzamwalira?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa—Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 3/1 tsamba 16
Anthu akusangalala m’mbali mwa nyanja m’dziko laparadaiso ndipo ana akusambira

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi imfa ya Yesu imatipindulitsa bwanji?

Mulungu analenga anthu n’cholinga choti akhale ndi moyo kwamuyaya padziko lapansi. Sanafune kuti anthu azivutika ndi matenda komanso imfa. Komabe, munthu woyambirira, Adamu, sanamvere Mulungu. Zimenezi zinapangitsa kuti asakhalenso ndi moyo kwamuyaya. Popeza anthufe tinachokera kwa Adamu, nafenso timafa. (Aroma 5:8, 12; 6:23) Choncho, Yehova Mulungu anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzafe ndi kuwombola anthu kuti adzakhalenso ndi moyo wosatha umene Adamu anataya.—Werengani Yohane 3:16.

Yesu anafa n’cholinga choti anthu adzapeze moyo wosatha. Taganizirani mmene anthu adzasangalalire padzikoli imfa ikadzatha

Imfa ya Yesu inapangitsa kuti Mulungu azitikhululukira machimo komanso kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Baibulo limafotokoza mmene moyo udzakhalire wosangalatsa, ukalamba, matenda ndiponso imfa zikadzatha.—Werengani Yesaya 25:8; 33:24; Chivumbulutso 21:4, 5.

Kodi tizikumbukira bwanji imfa ya Yesu?

Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu analamula ophunzira ake kuti azikumbukira imfa yake pochita mwambo wachidule. Kukumbukira imfa ya Yesu pochita mwambo umenewu, kumatithandiza kuganizira kwambiri mmene Yehova ndi Yesu amatikondera anthufe.—Werengani Luka 22:19, 20; 1 Yohane 4:9, 10.

Chaka chino, mwambo wokumbukira imfa ya Yesu, udzachitika Lolemba pa April 14, dzuwa litalowa. Tikukuitanani kuti mudzapezeke pa mwambo umene a Mboni za Yehova adzachite kudera lanulo.—Werengani Aroma 1:11, 12.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 4 ndi 5 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Mungapangenso dawunilodi bukuli pa webusaiti yathu ya www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena