Lipoti la Olengeza Ufumu
Iwo Anakhulupirira Yehova
MBONI ZA YEHOVA zinalamulidwa ndi Yehova kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu m’dziko lonse kotero kuti anthu a mitundu yonse akhale ndi mwaŵi wakudziŵa za dziko latsopano la Mulungu. M’maiko ena, kaŵirikaŵiri pansi pa chisonkhezero cha atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko, ntchito yathu imaletsedwa. Umenewo ndiwo mkhalidwe m’dziko linalake mu Afirika. Komatu Mboni za Yehova kumeneko zimachita mofanana ndi Mfumu Davide. Iye adati: “Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa.” (Salmo 56:11) Zokumana nazo za abale athu m’dziko limenelo zimasonyeza kuti iwo amakhulupirira Yehova ndi kupitirizabe ndi ntchito yake yofunika kwambiri.
Mboni yogwira ntchito monga hedimasitala pasukulu inaumirira pa “kumvera Mulungu koposa anthu,” ikulengeza uchete wake m’nkhani za Boma. (Machitidwe 5:29) Iyo inamenyedwa mowopsa ndipo inayembekezeredwa kupatsidwa mlandu wakukhala wopereka boma. Aliyense analingalira kuti iyo ikaphedwa. Komabe, Mboniyo inakhulupirira Yehova. Iyo inakhalabe yokhulupirika ndipo inalongosola zifukwa zake zachikumbumtima kaamba ka kaimidwe kake. Zotulukapo? Inamasulidwa ndi kubwezedwa ku tauni lakwawo, kumene nthumwi za Boma zomwe zidaimenyazo zinapepesa. Mboni yokhulupirika imeneyi inabwezedwa pantchito yake yauphunzitsi ndi kukwezedwa kuudindo wa woyang’anira masukulu!
Mgwirizanitsi wa sukulu ina anachotsa ntchito mphunzitsi wamwamuna yemwe anali Mboni. Pambuyo pa mwezi umodzi mgwirizanitsi ameneyu analandira bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kuchokera kwa mpainiya wapadera nalola phunziro Labaibulo. Pambuyo pomaliza mutu 6, iye anatula pansi udindo wake monga mgwirizanitsi wa sukuluyo, ndipo iye ndi mkazi wake anayamba kupezeka pamisonkhano yonse ya Mboni za Yehova. Sande ina m’mawa mphunzitsi wochotsedwa ntchitoyo anadabwa mokondwa kukumana ndi mwamuna yemwe adamchotsa ntchito ndi kupeza kuti anali panjira yakukhala mbale wauzimu.
Chokumana nacho china chochokera m’dziko limodzimodzilo chimasonyeza mmene Mboni za Yehova zimaperekera ulemu ku makonzedwe a Yehova ndi kugwira ntchito kusungitsa gulu kukhala loyera. Mpainiya wapadera winawake wogwirira ntchito m’gawo lakutali ankakumana ndi chitsutso chachikulu. Popeza kuti iye anali wochokera ku fuko lina ndi chigawo, adani a chowonadi anafuna kumpitikitsa pamudzipo. Komabe, mfumu yapamudzipo inatchula za mayendedwe ake abwino ndi zotulukapo zokoma za uminisitala wake ndipo sinalole kuti apitikitsidwe. Mfumuyo inawona kuti chibwerere mpainiya wapaderayo, anthu anali kulemekeza akuluakulu olamulira mwakukhoma misonkho yawo ndi kuchita ntchito yam’mudzi yokonza msewu kamodzi pamlungu.—Aroma 13:1, 7.
Kenaka, usiku wina Mboni inayake inagwidwa ikuchita chigololo ndi mkazi yemwe sanali Mboni. Panali zamanyazi, ndipo mpainiya wapaderayo anaitanidwa kwa mfumu, yomwe inamtonza, ikumati: “Suyu mbale wako wagwidwa akuchita chigololo. Inu Mboni za Yehova simusiyana konse ndi zipembedzo zina.” Komabe, mpainiya wapaderayo anafotokoza kuti: “Chinkana kuti ndife opanda ungwiro, ndife osiyana ndithu ndi zipembedzo zina chifukwa chakuti sitimalekerera zochita za awo ochita machimo aakulu.”
Mboniyo imene inachita chigololo inatumikira chilango m’ndende ndipo inalipira faindi. Ndiponso, iyo inachotsedwa mumpingo monga wochita zoipa wosalapa. Kachitidweka kanakondweretsa mfumuyo ndipo kanaleketsa manenanena a awo ojeda Mboni za Yehova. Mfumuyo inathirira ndemanga kuti: “Musamakamba zoipa ponena za Mboni za Yehova. Izo zirinacho chowonadi. Zipembedzo zina sizimakatenga kachitidwe koteroko.”
Mboni zokhulupirika m’dzikolo zimatsatira chilangizo cha Salmo 37:3 chakuti: ‘Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m’dziko, ndipo tsata chowonadi.’ Kodi ifeyo tidzakhulupirira Yehova monga momwe Akristuŵa akuchitira?