Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/1 tsamba 25-29
  • Nkosangalatsa Chotani Nanga Kukhala Pagome la Yehova!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkosangalatsa Chotani Nanga Kukhala Pagome la Yehova!
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyesedwa
  • Chakudya Chauzimu m’Msasamo
  • Kukhulupirika Mpaka Imfa
  • Zogaŵira Zauzimu m’Neuengamme
  • Madalitso Auzimu Ochuluka
  • Yehova Anatipulumutsa ku Ulamuliro Wankhanza
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kulibe Chinthu Chabwino Choposa Choonadi
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mulungu Ndiye Pothaŵira Panga ndi Mphamvu Yanga
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Ndine Wamphamvu Ngakhale Ndili Wofooka
    Nsanja ya Olonda—2005
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/1 tsamba 25-29

Nkosangalatsa Chotani Nanga Kukhala Pagome la Yehova!

Monga momwe yasimbidwira ndi Ernst Wauer

Lerolino kuli kosavuta kwenikweni kwa ine kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova, kuphunzira Baibulo, ndi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Komabe, zimenezo sizinakhale tero nthaŵi zonse muno m’Jeremani. Pamene Adolf Hitler anali wolamulira wotsendereza ufulu, kuchokera 1933 mpaka 1945, kutenga mbali m’ntchito Zachikristu zoterozo kunatanthauza kuika moyo wamunthuwe pachiswe.

CHAKA chimodzi Hitler asanakhale paulamuliro, pamene ndinali wazaka 30 zakubadwa, ndinakumana ndi Mboni za Yehova kwanthaŵi yoyamba ku Dresden. Mu January 1935, ndinadzipatulira kwa Yehova ndi kusonyeza chikhumbo changa cha kubatizidwa. Ntchito yathu inali italetsedwa kale mu 1933, chotero ndinafunsidwa kuti: “Kodi ukuzindikira chimene chosankha chako chikutanthauza? Ukuika pachiswe banja lako, thanzi, ntchito, ufulu, ndipo ngakhale moyo wako weniweniwo!”

“Ndaŵerengera mtengo, ndipo ndine wofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kuchifera,” ndinayankha motero.

Ngakhale pamene ndinali ndisanabatizidwe, ndinayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba. Pakhomo lina, ndinakumana ndi mtsogoleri wa mayusi wa SS (Alonda a Hitler Ovala Zakuda) wovala yunifomu, yemwe anafuula kuti: “Kodi sudziŵa kuti zimenezi nzoletsedwa? Ndidzaitana apolisi!”

“Aitaneni. Ine ndikulankhula za Baibulo basi, ndipo palibe lamulo lotsutsa zimenezo,” ndinayankha mokhazika mtima. Ndiyeno ndinapita panyumba yotsatirapo ndipo ndinaloŵetsedwa m’nyumba ndi mwamuna waubwenzi. Palibe zimene zinandichitikira.

Posapita nthaŵi ndinapatsidwa thayo lakuyang’anira gulu la phunziro la Mboni zisanu kapena zisanu ndi ziŵiri zomwe zinkakumana mlungu uliwonse. Tinkaphunzira makope a Nsanja ya Olonda amene analoŵetsedwa mwakabisira m’Jeremani kuchokera ku maiko apafupi. Chotero, mosasamala kanthu za chiletso, tinakhala pa “gome la [Yehova, NW]” nthaŵi zonse kuti tilimbikitsidwe mwauzimu.​—1 Akorinto 10:21.

Kuyesedwa

Mu 1936, J. F. Rutherford, pulezidenti wa Watch Tower Society, anachezera msonkhano ku Lucerne, Switzerland, naitanira abale amene anali ndi udindo wauyang’aniro wateokratiki m’Jeremani kukapezekako. Popeza kuti abale ambiri analandidwa mapasipoti awo ndipo abale angapo ankayang’aniridwa mosamalitsa ndi apolisi, oŵerengeka okha anakhoza kupezekako. Mbale woyang’anira ntchito ku Dresden anandipempha kukamuimira ku Lucerne.

“Koma kodi sindine wamng’ono kwambiri ndi wosazoloŵera?” ndinafunsa motero.

“Chomwe chiri nkanthu tsopano,” iye ananditsimikiziritsa motero, “ndicho kukhala wokhulupirika. Ndicho chinthu chachikulu.”

Mwamsanga pambuyo pobwera kuchokera ku Lucerne, ndinagwidwa ndi kulekanitsidwa mwadzidzidzi ndi mkazi wanga, Eva, ndi ana athu aang’ono aŵiri. Popita ku malikulu apolisi ku Dresden, ndinayesayesa zolimba kukumbukira lemba lomwe likanditsogoza. Ndinakumbukira Miyambo 3:5, 6 lomwe limati: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendendwe ako.’ Kukumbukira lembali kunandilimbitsa kaamba ka mafunso oyambirira. Pambuyo pake ndinatsekeredwa m’kachipinda kakang’ono, ndipo ndinali ndi lingaliro lakunyanyalidwa mwakanthaŵi. Koma kupemphera mosalekeza kwa Yehova kunandidzaza ndi mtendere.

Khoti linandiweruzira kupika ndende kwa miyezi 27. Ndinabindikiritsidwa ndekha kwa chaka chimodzi ku ndende yokhaulitsira m’Bautzen. Nthaŵi ina, nduna yazachiweruzo yoleka ntchito​—yomwe inkagwirizira malo a wina​—inatsegula chitseko cha chipinda changa ndikunena mwachisoni kuti: “Ndidziŵa kuti suloledwa kuŵerenga chirichonse, koma mwina ufunikira kanthu kena kokuiŵalitsa mkhalidwewu.” Atatero anandipatsa mobisa magazini akale abanja nati: “Ndidzawatenga usiku.”

Kwenikwenidi sindinafunikira kanthu kalikonse kuti ‘ndiuiŵale mkhalidwewo.’ Pamene ndinali wobindikiritsidwa ndekha, ndinakumbukira malemba Abaibulo kuchokera m’mutu ndi kupanga nkhani ndi kuzipereka mofuula. Koma ndinayang’ana m’magaziniwo kuwona ngati anali ndi Malemba alionse​—ndipo ndinapezadi angapo! Lemba lina linali Afilipi 1:6, limene limati m’mbali yake: ‘Pokhulupirira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza.’ Ndinayamikira Yehova kaamba ka chilimbikitso chimenechi.

Pambuyo pake ndinasamutsidwira ku msasa wachibalo. Ndiyeno, m’ngululu ya 1939, pamene kubindikiritsidwa kwanga kunali pafupi kutha, woyang’anira msasawo anandifunsa ngati ndinasintha malingaliro anga. “Ndifuna kukhala wokhulupirika ku chikhulupiriro changa,” ndilo linali yankho langa. Pamenepo iye anandiuza kuti ndikasamutsidwira ku msasa wachibalo wa ku Sachsenhausen.

Kumeneko ndinapereka zovala zanga, ndinasamba, ndinametedwa tsitsi lonse lapathupi, ndipo ndinapatsidwa zovala zam’ndende. Ndiyeno ndinapititsidwa kukasamba kachiŵirinso, panthaŵiyi ndiri m’zovala​—kachitidwe kamene a SS anakatcha “ubatizo.” Pambuyo pake ndinakakamizidwa kuimirira pabwalo, ndiri wonyoweratu, mpaka madzulo.

M’misasayo Mboni za Yehova zinachitiridwa nkhanza yapadera ndi a SS. Nthaŵi zambiri tinkaimirira pabwalo laperete kwa maola ambirimbiri. Nthaŵi zina mmodzi wa ife ankadandaula kuti: “Kodi sikukakhala kwabwino kudya chakudya chabwino kwenikweni?” Wina ankayankha kuti: “Osasumika maganizo ako pa zinthu zotero. Tangolingalira mmene kuliri kwaulemerero kuchirikiza dzina la Yehova ndi Ufumu wake.” Ndipo winanso akawonjezera kuti: “Yehova adzatilimbitsa!” Mwanjirayi tinalimbikitsana. Nthaŵi zina kungopukusa mutu kwaubwenzi kunali kokwanira kunena kuti: “Ndifuna kukhala wokhulupirika; nawenso ukutero!”

Chakudya Chauzimu m’Msasamo

Ena anatsogolera m’kudyetsa abale mwauzimu, ndipo ndinasankhidwa kuŵathandiza. Tinali kokha ndi Baibulo la Luther lalikulu. Ndithudi, kukhala nalo kunali koletsedwa. Chotero chuma chamtengo wake chimenechi chinabisidwa, ndipo m’chigawo chazipinda chirichonse mbale mmodzi yekha woikidwa ndiye anali kuliŵerenga mwakanthaŵi. Pamene inali nthaŵi yanga, ndinkakwaŵira kunsi kwa kama ndi muni ndi kuliŵerenga kwa pafupifupi mphindi 15. Ndinaloŵeza malemba amene pambuyo pake ndikakambitsirana ndi abale m’chigawo chazipinda chathu. Chotero, kugaŵiridwa kwa chakudya chauzimu kunali kolinganizidwa kumlingo wakutiwakuti.

Abale onse analimbikitsidwa kupempha chakudya chauzimu chowonjezereka kwa Yehova m’pemphero, ndipo iye anamva mapembedzero athu. M’nyengo yachisanu ya 1939/​40 mbale womangidwa chatsopano anakhoza kuloŵetsa mwakabisira makope angapo a Nsanja ya Olonda mumsasa mwakuwaika mkati mwa mwendo wake wathabwa. Chimenechi chinawoneka ngati chozizwitsa, popeza kuti anthu onse ankafufuzidwa mosamalitsa.

Kaamba ka chisungiko, magaziniwa anapatsidwa kwa abale osankhidwawo kwa tsiku limodzi pa nthaŵi imodzi. Tsiku lina, pamene garaji inali kumangidwa, ndinabisala m’dzenje ndi kuŵerenga pamene mbale ankalonda kubwalo. Panthaŵi ina ndinaika Nsanja ya Olonda pa miyendo mkati mwa “ola [lathu] lakusoka” (m’madzulo tinkakhala m’misasa tikukonza maglovu ndi ziŵiya zina), pamene abale anakhala pambali monga alonda. Pamene mlonda wa SS anabwera, ndinabisa Nsanja ya Olonda mofulumira. Kugwidwa kukanatanthauza kutaya moyo wanga!

Yehova anatithandiza modabwitsa kuloŵeza pamtima mfundo zolimbitsa za nkhanizo. Kaŵirikaŵiri kutopa kwadzawoneni kunkandigonetsa tulo tofa nato usiku. Koma usiku umene ndinaŵerenga Nsanja ya Olonda, ndinkagalamuka nthaŵi zingapo ndi kukumbukira mfundozo mosavuta kwenikweni. Abale osankhidwa m’zigawo zina zazipinda anali ndi zokumana nazo zofananazo. Motero Yehova anapangitsa chikumbukiro chathu kukhala chakuthwa kotero kuti tikakhoza kugaŵira chakudya chauzimu. Tinkachita zimenezi mwakufikira mbale payekha ndi kumlimbitsa.

Kukhulupirika Mpaka Imfa

Pa September 15, 1939, gulu lathu logwira ntchito linabwerera ku msasa mofulumira koposa nthaŵi zonse. Kodi inali nthaŵi ya chiyani? August Dickmann, mmodzi wa abale athu achichepere, akanyongedwa poyera. Anazi anali ndi chidaliro kuti chimenechi chikachititsa unyinji waukulu wa Mboni kukana chikhulupiriro chawo. Pambuyo pa kunyongako, akaidi ena onse anachotsedwapo. Koma ife Mboni za Yehova tinakankhidwira chauku ndi chauko pabwalo laperete, kupondedwa chidyali ndi kukwapulidwa kufikira pamene sitikakhoza kuyenda. Tinalamulidwa kusaina chikalata chokanira chikhulupiriro chathu; apo phuluzi, tikawomberedwa mfuti nafenso.

Podzafika tsiku lotsatira, palibe yemwe anasaina. Ndipotu, mkaidi watsopano, yemwe anasaina pofika, anafafaniza saini yake tsopano. Anasankha kumwalira pamodzi ndi abale ake mmalo mwakusiya msasawo monga mdyera kuŵiri. Miyezi yotsatirapo, tinalangidwa ndi ntchito yachibalo, kuchitiridwa moipa kosalekeza, ndi kumanidwa chakudya. Abale athu oposa zana limodzi anamwalira mkati mwa nyengo yachisanu ya 1939/​40. Iwo anasunga umphumphu wawo kwa Yehova ndi Ufumu wake mpaka mapeto enieni.

Ndiyeno Yehova anapereka chithandizo. Abale ambiri anasamutsidwira kukagwira ntchito m’misasa yopangidwa chatsopano, kumene analandira chakudya chowonjezereka. Ndiponso, kuchitiridwa nkhanza kunacheperapo. M’ngululu ya 1940, ndinasamutsidwira ku msasa wachibalo wa Neuengamme.

Zogaŵira Zauzimu m’Neuengamme

Pamene ndinafika, panali gulu la Mboni pafupifupi 20, opanda Baibulo kapena mabuku ena alionse. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kugwiritsira ntchito zinthu zimene ndinaziphunzira ku Sachsenhausen kulimbitsa abale mu Neuengamme. Monga sitepe loyamba, ndinakumbukira malemba ndi kuwasankha kaamba ka malemba atsiku ndi tsiku. Ndiyeno makonzedwe anapangidwa kaamba ka misonkhano mmene ndikafotokoza mfundo zochokera m’nkhani zophunziridwa mu Nsanja ya Olonda zimene ndinaŵerenga ku Sachsenhausen. Pamene abale atsopano anafika, anasimba zimene anaphunzira mu Nsanja za Olonda zaposachedwa.

Podzafika mu 1943 chiŵerengero cha Mboni za Yehova m’Neuengamme chinakwera kufika pa 70. Mboni za Yehova zinasankhidwa kukagwira ntchito kunja kwa msasawo, monga ngati kuyeretsa pambuyo pa kuukira kwa ndege zankhondo. Monga chotulukapo, tinali okhoza kubweretsa mwakabisira Mabaibulo, makope a Nsanja ya Olonda, ndi mabuku ena ndi mabrosha a Sosaite m’msasawo. Tinalandiranso mitokoma yokhala ndi mabuku owonjezereka ndi vinyo ndi mkate wopanda chotupitsa kaamba ka Chikumbutso chapachaka papositi. Mwachiwonekere Yehova anachititsa khungu omwe anafufuza mitokomayo.

Popeza kuti tinali omwazikana m’misasa yosiyanasiyana, tinapanga magulu asanu ndi aŵiri a Phunziro la Nsanja ya Olonda, lirilonse lokhala ndi wochititsa ndi wothandiza. Makope a Nsanja ya Olonda ankapangidwa mwakabisira m’ofesi ya kazembe wamsasawo, mmene ndinkagwira ntchito mwakanthaŵi. Chotero, gulu lirilonse linalandira kope limodzi lathunthu kaamba ka phunziro lamlungu ndi mlungu. Panalibe msonkhano ndi umodzi womwe unalephereka. Kuwonjezerapo, maguluwo analandira kope la lemba latsiku ndi tsiku m’mawa mulimonse pabwalo laperete, kuphatikizapo ndi ndemanga zochokera mu Nsanja ya Olonda.

Nthaŵi ina a SS anali patchuthi, chotero tinakhoza kuchita msonkhano kwa theka latsiku ndi kukambitsirana mmene tingalalikirire m’msasamo. Tinagaŵa msasawo m’magawo ndipo mwaluso tinafikira akaidi anzathu ndi “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Popeza kuti akaidiwo anachokera ku maiko osiyanasiyana, tinapanga makadi a zinenero zambiri ochitira umboni amene anafotokoza ntchito yathu ndi Ufumu. Tinalalikira mokangalika kwambiri kotero kuti akaidi azandale anadandaula kuti: “Kulikonse kumene upita, ukumva nkhani yonena za Yehova basi!” Lipoti la utumiki wakumunda la ntchito yathu linafikadi ku ofesi yanthambi ku Bern, Switzerland.

Zonse zinayenda bwino kufikira pamene a Gestapo anafufuza misasa yachibalo yonse mu 1944. Depo yathu ya mabuku m’Neuengamme sinapezedwe, koma zinthu zingapo zinapezedwa kwa Karl Schwarzer ndi ine. Tinafunsidwa mafunso ndi kumenyedwa kwamasiku atatu. Pamene kuzunzidwa kumeneko kunatha, tonse aŵirife tinali mikwingwirima thupi lonse. Komabe, ndi chithandizo cha Yehova, tinachira.

Madalitso Auzimu Ochuluka

Ndinamasulidwa ndi asirikali Ogwirizana mu May 1945. Patsiku lotsatira kumasulidwako, ndinayamba kuyenda limodzi ndi gulu laling’ono la abale ndi anthu okondwerera. Titatopa, tinakhala pansi pachitsime m’mudzi woyamba umene tinaloŵamo ndipo tinamwa madzi. Nditapezanso mphamvu, ndinapita kunyumba ndi nyumba nditakwapatira Baibulo langa. Mkazi wina wachichepere anakhudzidwa kwambiri kudziŵa kuti ifeyo Mboni za Yehova tinali m’misasa yachibalo chifukwa cha chikhulupiriro chathu. Iye anathamangira m’kitchini, nabwera ndi mkaka ndi mkate kudzapatsa gulu lathulo.

Pambuyo pake, tidakali chivalire zovala zathu za m’msasa, tinalengeza uthenga Waufumu m’mudzi wonsewo. Munthu wina wapamudzipo anatiitanira ku phwando lalikulu la chakudya. Iyeyo anatipatsa zinthu zimene tinkasoŵa kwazaka zambiri. Ha, zinali zotsekemera chotani nanga! Komabe, sitinangogwidiza chakudyacho. Tinapemphera ndi kudya mokhazikika, ndipo mumkhalidwe wabwino. Zimenezi zinawakondweretsa kwambiri openyerera kwakuti pamene tinayamba msonkhano pambuyo pake, anamvetsera ku nkhani Yabaibulo. Mkazi wina analandira uthengawo ndipo ndimlongo wathu wauzimu lerolino.

Tinapitirizabe kuyenda ndi kusangalala ndi chisamaliro cha Yehova m’njira zambiri zodabwitsa. Ha, kwakhala kosangalatsa chotani nanga kupitirizabe muufulu tsopano, kusangalala ndi chakudya chonse chofalitsidwa ndi gulu la Yehova ndi kugaŵana chakudyacho ndi ena! M’zaka zomwe zatsatirapo, kukhulupirira kwathu Yehova kotheratu kwafupidwa mobwerezabwereza.

Kuchokera mu 1945 mpaka 1950, ndinali ndi mwaŵi wotumikira pa Beteli ya ku Magdeburg ndiyeno, pa ofesi ya Watch Tower Society m’Berlin kudzafika mu 1955. Pambuyo pake, ndinatumikira monga woyang’anira woyendayenda kufikira mu 1963, pamene mkazi wanga Hilde, anandiuza kuti anali ndi pathupi. (Eva, mkazi wanga woyamba, anamwalira ine ndiri m’ndende, ndipo ndinakwatiranso mu 1958.) Mwana wathu wamkazi anakhala Mboni yokangalika pambuyo pake.

Bwanji ponena za ana a muukwati wanga woyamba? Mwatsokalanji, mwana wanga wamwamuna sanasonyeze chikondwerero m’chowonadi. Koma mwana wanga wamkazi Gisela anatero, ndipo analoŵa sukulu ya Gileadi yaumishonale mu 1953. Tsopano, iye limodzi ndi mwamuna wake, amatumikira pa imodzi ya Maholo Osonkhanira m’Jeremani. Ndi chithandizo cha Yehova, ndakhoza kukhalabe muutumiki waupainiya wokhazikika chiyambire 1963 ndi kutumikira kumene chithandizo chinafunikira, choyamba ku Frankfurt ndiyeno ku Tübingen.

Kufikira lero ndimasangalalabe ndi chakudya choperekedwa ndi gulu la Yehova kaamba ka banja lake la chikhulupiriro. (1 Timoteo 3:15) Masiku ano, sikovuta kupeza chakudya chauzimu, koma kodi ifeyo nthaŵi zonse timachiyamikira? Ndiri wachidaliro kuti Yehova ali ndi madalitso ochuluka osungidwira omwe amamkhulupirira, omwe amakhalabe okhulupirika, ndipo amadya pagome lake.

[Chithunzi pamasamba 26, 27]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MSASA WACHIBALO WA KU SACHSENHAUSEN

A. Misasa ya a SS

B. Bwalo loitanira maina

C. Nyumba yazipinda

D. Kobindikiritsira

E. Malo ochosera nsabwe

F. Malo onyongerako

G. Chipinda cha gas

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena