Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/1 tsamba 24
  • “Kunyumba ndi Nyumba”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kunyumba ndi Nyumba”
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Phunzitsani Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba
    Nsanja ya Olonda—1991
  • “New World Translation”—Yaukatswiri ndi Yowona
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Chochitika Chosaiŵalika kwa Okonda Mawu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/1 tsamba 24

“Kunyumba ndi Nyumba”

“TSIKU lirilonse m’kachisi ndi kunyumba ndi nyumba iwo anapitirizabe mosalekeza kumaphunzitsa ndi kulengeza mbiri yabwino yonena za Kristu, Yesu.” (Machitidwe 5:42, NW) Kaŵirikaŵiri Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito lemba limeneli ndi la Machitidwe 20:20 kutsimikiziritsa maziko a Malemba a ntchito yawo yakulalikira kukhomo ndi khomo. Komabe, osuliza Mboni za Yehova ku Jeremani atsutsa njira imene New World Translation imamasulirira mavesi ameneŵa, akumanena kuti imanamizira Chigiriki choyambirira.

Kodi kunena koteroko kuli kwamaziko? Kutalitali. Chenicheni nchakuti, osachepera pa matembenuzidwe Abaibulo Achijeremani asanu ndi amodzi amamasulira mavesiŵa mofananamo. Ena a amenewo ndiwo Zürcher Bibel yokonzedwanso ndiponso “Zipangano Zatsopano” zotembenuzidwa ndi Rupert Storr, Franz Sigge, ndi Jakob Schäfer (yokonzedwanso ndi N. Adler). Matembenuzidwe ambiri Achingelezi amagwirizana nawo.

Katswiri Wachijeremani Hans Bruns amapereka chifukwa cha kutembenuza kwake kwakuti, “kunyumba ndi nyumba,” pa Machitidwe 5:42, kumati: “Malinga ndi lemba loyambirira, kukuwonekera kuti iwo anapita kunyumba ndi nyumba.” Inde, katʼ oiʹkon, mawu oyambirira m’lembali, samagwiritsiridwa ntchito m’lingaliro lofotokoza mneni (“panyumba”) koma m’lingaliro lakugaŵira, m’lingaliro lenileni kutanthauza, “malinga ndi nyumba.” (Mpangidwe wochulukitsa wa, katʼ oiʹkous, kutanthauza “malinga ndi nyumba zambiri,” umapezeka pa Machitidwe 20:20.) Akatswiri ena, monga ngati Heinz Schürmann, amatsimikiziritsa matembenuzidwe akugaŵira a mawu ameneŵa. Horst Balz ndi Gerhard Schneider, ofalitsa a bukhu lomasulira mosamalitsa mawu a Chipangano Chatsopano, amanena kuti mawuwo angamasuliridwe kukhala “nyumba pambuyo pa nyumba.” Mabuku ambiri azilozero Achingelezi amafotokoza vesi limeneli mofananamo.

Kachiŵirinso, New World Translation yapirira ziukiro za osuliza. Chofunika koposa nchakuti, kuli kowonekera bwino kuti pali maziko olimba Abaibulo kaamba ka uminisitala wa kunyumba ndi nyumba. (Yerekezerani ndi Mateyu 10:11-14; 24:14.) Mboni za Yehova ziri ndi mwaŵi wakutsanzira anzawo a m’zaka za zana loyamba m’nkhaniyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena