Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/1 tsamba 9
  • Iwo Anakhutiritsidwa mu Kathmandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Iwo Anakhutiritsidwa mu Kathmandu
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • “Chikondi Chimene Anatisonyeza Chinatikhudza Kwambiri”
    Galamukani!—2017
  • Mbiri Yateokratiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Tsopano Ndili pa Mtendere ndi Mulungu Komanso Amayi Anga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/1 tsamba 9

Lipoti la Olengeza Ufumu

Iwo Anakhutiritsidwa mu Kathmandu

M’MISIRI wolemba zithunzi wamkazi anayamba kufunafuna chowonadi m’Brittany, ku Falansa, mu 1980. Iye anakambitsirana ndi Apentekosito ndi kuphunzira zipembedzo za Kum’maŵa​—popanda kukhutiritsidwa. Ndiyeno anakambitsirana ndi mmodzi wa Mboni za Yehova koma posapita nthaŵi analeka. Iye anakumana ndi m’misiri wina wamwamuna nayamba kugwira naye ntchito ndi kukhala naye.

Posapita nthaŵi aŵiri osakwatirana ameneŵa anaganiza zokacheza ku Nepal. Iwo anasangalatsidwa kwambiri ndi kukongola ndi mtendere wa dzikolo koma anakhumudwa ndi mwambo wa kusankhana fuko, umene unawoneka kukhala wopanda chilungamo kwa iwo monga anthu Akumadzulo.

Atabwerera ku Falansa, mkaziyo anapereka lingaliro kwa mnzakeyo kuti adziphunzira Baibulo pamodzi, ndipo zinamdabwitsa kuti iye anavomera. Anamvana ndi Mboni imene mkaziyo anali kukambitsirana nayo zaka ziŵiri kalero. Poyamba anagwiritsira ntchito Baibulo lokha, koma m’kupita kwa nthaŵi, iwo anavomereza kugwiritsira ntchito bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndipo pambuyo pake bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. M’chaka chimodzi iwo analeka kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa.

Pambuyo pochezera Nepal kachiŵirinso kwa miyezi iŵiri, aŵiriwo anabwerera ku Falansa kumene anapitiriza kuphunzira. Analeka kusuta ndi kupita ku mabawa ndi ku makalabu ausiku nayamba kupezeka ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Komabe, pamene anamaliza bukhu la Kukhala ndi Moyo Kosatha, anaganiza zakuleka kuphunzira.

Anapitanso ku Nepal, nakakhala m’nyumba yaing’ono patsinde pa Mapiri a Himalaya. Tsiku lina mwamuna wokalamba, wovala suti ndi tayi, anagogoda pakhomo pawo. Mkaziyo adali yekha m’nyumbamo, ndipo anaganiza kuti anali wogula amene anabwera kudzawona zithunzithunzi zawo. Koma anadabwa kuwona kuti inali Mboni imene inabwera mmalo mwa munthu yemwe ankaphunzira nawo m’Falansa. Posapita nthaŵi mnzakeyo anabwera kunyumba, ndipo panakhala kukambitsirana kwa maola aŵiri.

Masiku oŵerengeka pambuyo pake, aŵiriwo anapezeka ku msonkhano wa Mboni za Yehova m’Kathmandu ndipo anakondweretsedwa kwabasi ndi kawonekedwe kaudongo ka opezekapo. Iwo anawona chikondi chaubale ndi chimwemwe zofanana ndi zimene adawona pamisonkhano m’Falansa. Anawonanso umodzi wa anthu a ku Nepal opezekapowo, ngakhale kuti anachokera ku magulu a miyambo yosiyanasiyana. Tsopano anakhutiritsidwa kuti ili liyenera kukhala gulu la Yehova.

Mwezi umodzi pambuyo pake anabwerera ku Falansa ndipo mwamsanga anayambanso phunziro lawo Labaibulo ndi kupezeka ku misonkhano. Anakwatirana, ndi kuyamba kukhala ndi phande m’ntchito yochitira umboni, ndipo pomalizira pake anabatizidwa. Mwamunayo tsopano ndimtumiki wotumikira, ndipo mkazi wake amakhala ndi phande mokhazikika muutumiki waupainiya wothandiza. Ndithudi, amene ali ndi mtima wabwino adzathandizidwa ndi mzimu wa Yehova kupita patsogolo ndi kukhala olambira ake.​—Chibvumbulutso 7:15-17.

[Bokosi/​Mapu patsamba 9]

NEPAL

Chiŵe. cha anthu - 17,712,221

Chiŵe. Chapamwa. cha Ofa. mu 1990 - 63

Kugaŵa, Wofa. 1 pa anthu - 281,146

Avar. ya Apai. Ofalitsa - 10

Chiŵe. cha Mipingo - 1

Avar. ya Maphu. Abaibulo - 107

Opezeka pa Chikumbutso - 220

[Mapu]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NEPAL

INDIA

[Chithunzi patsamba 9]

Pa nsika ku Kathmandu, Nepal

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena