Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Bwanji Ponena za Mtsogolo?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Mulungu Amasamalira Nyama?
    Galamukani!—2011
  • “Iwe Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Zinyama Zidzasangalatsa Anthu Mpaka Kalekale
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi nchifukwa ninji Yesaya 11:6 mu New World Translation of the Holy Scriptures amanena kuti “mmbulu udzakhaladi kwakanthaŵi ndi mwana wankhosa”? Kodi mtendere umenewo sudzakhala wokhalitsa?

Mtendere wosangalatsa pakati pa nyama woloseredwa pa Yesaya 11:6-9 udzakhala wokhalitsa. Koma kumasulira kosamalitsa kwa Yesaya 11:6 kumamveketsa bwino mfundo yakuti nyama zimenezo sizidzakhalira pamodzi nthaŵi zonse.

Mu New World Translation of the Holy Scriptures, Yesaya 11:6 amanena kuti: “Mmbulu udzakhaladi kwakanthaŵi ndi mwana wa nkhosa, ndipo mwana wambuzi adzagona pamodzi ndi nyalugwe weniweniyo, mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi nyama yonenepa zonse pamodzi; ndipo mnyamata wamng’ono adzakhala wozitsogolera.”

Matembenuzidwe ambiri Abaibulo amaŵerengedwa kuti: “Mmbulu nawonso udzakhala [kapena, “kukhala ndi moyo”] ndi mwana wa nkhosa.” Mamasuliridwe otero angapereke chithunzi cha mmbulu ndi mwana wa nkhosa zikukhala pamodzi kosalekeza, monga ngati kuti m’banja latsopano kapena makonzedwe atsopano akukhala ndi moyo.

Komabe, liwu Lachihebri lotembenuzidwa “kukhala” kapena “kukhala ndi moyo” ndilo gur. Malinga ndi kunena kwa William Gesenius, katswiri womasulira mawu, limatanthauza “kukhalitsa, kukhala kwakanthaŵi, kukhala osati monga panyumba, ndiko kuti monga mlendo, mlendo wa dziko lina, mlendo wocheza naye.” (A Hebrew and English Lexicon of the Old Testament, lotembenuzidwa ndi Edward Robinson) Bukhu lomasulira mawu lolembedwa ndi F. Brown, S. Driver, ndi C. Briggs limapereka tanthauzo la “kukhalitsa, kukhala kwanthaŵi (yodziŵika kapena yosa[dziŵika]), kukhala monga mlendo . . . wopanda zoyenerera zoyambirira.”

Mulungu anagwiritsira ntchito gur pouza Abrahamu ‘kukhala mlendo’ m’Kanani. Kholo limenelo silikanakhala ndi kadziko kakekake, koma likakhala nzika yotetezeredwa kumeneko. (Genesis 26:3; Eksodo 6:2-4; Ahebri 11:9, 13) Mofananamo, Yakobo ananena kuti anali ‘kukhala monga mlendo’ m’dera la Harana, popeza akabwerera ku Kanani.​—Genesis 29:4; 32:4, NW.

Mu Paradaiso amene Mulungu adzakhazikitsa posachedwapa, nyama ndi anthu zidzakhala pamtendere. Mwana wa nkhosa sadzakhala paupandau mwakukhala ndi mmbulu kapena mwana wang’ombe ndi nyalugwe. Monga ngati kusonyeza kusiyana ndi nthaŵi yamakono, chinenero chikulola ngakhale lingaliro lakuti mmbulu ukakhala nzika yotetezeredwa ndi mwana wa nkhosa.​—Yesaya 35:9; 65:25.a

Komabe, nyamazo zikakhalabe ndi malo awo okhala osiyana. Nyama zina nzamoyo wa ku nkhalango, zina ku zidikha, ndipo zinanso ku madera a ku gombe kapena ku mapiri. Ngakhale panthaŵi ya Paradaiso woyambirira, Mulungu ananena za ‘nyama zoŵeta ndi zakuthengo.’ (Genesis 1:24, NW) Mwachiwonekere nyama zoŵeta zinali zija zomwe mwachisawawa zingakhale pafupi ndi anthu ndi malo awo okhala. Zakuthengo, ngakhale kuti sizinali zolusa, mwachiwonekere zinakonda kukhala kutali ndi anthu. Choncho, monga momwe ulosi wa Yesaya umaneneratu, mmbulu “udzakhaladi kwakanthaŵi ndi mwana wa nkhosa,” koma sudzakhalirira pafupi ndi nyama zoŵeta zoterozo.

[Mawu a M’munsi]

a The Bible in Living English imanena motere pa Yesaya 11:6: “Ndipo mmbulu udzakhala kwa mwana wa nkhosa.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Zoological Research Center, Tel-Aviv Hebrew University

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena