Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/1 tsamba 2-4
  • Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Wakhala Woleza Mtima Motero?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Wakhala Woleza Mtima Motero?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Amasamaladi!
  • Mungu N’ngofunika Kwambiri Pamoyo
    Galamukani!—2007
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/1 tsamba 2-4

Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Wakhala Woleza Mtima Motero?

PENYANI nkhope yochititsa chisoni ya mwana wanjala. Onani thupi lake lowonda ndi mimba yake yotupa. Talingalirani ponena za kusoŵa kwake chakudya kothetsa nzeru, ndipo onani mbale yopanda kanthu imene wanyamula. Mwinamwake amayi ŵake akuyang’ana ndi maso ofooka, nkhope yawo yeniyeniyo ikupereka chithunzi cha kupanda chochita. Ndiyeno yesani kupondereza chisoni chanu​—inde, gwirani misozi yanu.

Mkhalidwe woterewu umakhalapo kwa nthaŵi mamiliyoni ambiri m’chigawo chokanthidwa ndi njala chokuta makilomita 6 miliyoni m’mbali zonse zinayi chotchedwa Sahel. Icho chimafutukuka kwa makilomita oposa 4,800 kudutsa Afirika kum’mwera kwa Chipululu cha Sahara, kuchokera ku Senegal ku Gombe la Atlantic mpaka ku Ethiopia ku Nyanja Yofiira. Ndithudi, njala ikuwopsezanso anthu ambiri m’maiko ena. Bungwe la World Health Organization likusimba kuti pafupifupi anthu mamiliyoni zikwi 1.1 kuzungulira dziko lapansi ali odwala mowopsa kapena opereŵera chakudya kwa dzawoneni.

Ndithudi, njala yangokhala mbali imodzi ya kuvutika kwa anthu. Munthu akuipitsa dziko lapansi, ndipo tonsefe tikuyambukiridwa. Madongosolo andale zadziko amavomereza chisalungamo ndi nkhondo zimene zimabweretsa chisoni ndi imfa kwa ambiri. Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola zinthu zoterozo? Kodi iye amasamala ponena za ife?

Mulungu Amasamaladi!

Mlengi wathu amasamala ponena za ife. Pali umboni wambiri wa izi ndi wa kukhoza kwake kupangitsa zinthu kugwirira ntchito pamodzi kaamba ka ubwino wathu ndi kaamba ka chigwirizano m’chilengedwe chake chonse. Mwachitsanzo, tayang’anani pa chithunzichi cha njuchi yomwe yapita pa duŵa pa mtengo wa zipatso. Njuchiyi imadalira pa duŵa kaamba ka madzi a m’maluŵa omwe nchakudya chake. Mtengowu nawonso, umadalira pa pollen imene imakangamira ku thupi la njuchi yochokera ku mtengo wofanana. Mwanjirayi, duŵalo limalandira pollen imene imakulitsa chipatso. Simitengo yonse ya zipatso imene imalandira pollen mwa njira imeneyi, koma Mulungu motsimikizirika anapanga makonzedwe a kugwirizana kodabwitsa m’nkhani imeneyi. Ndipo ubwino wake umatulukapo chipatso chimene tikhoza kudya ndi chisangalalo ndi kupindula.

Njuchiyi iri mbali ya nthenje ya njuchi zoposa 30,000. Zina zimalonda muoma, pamene zina zimayeretsa kapena kuomberamo mpweya wabwino. Zinanso zimasonkhanitsira ku nkhokwe madzi a m’maluŵa ndi pollen, kudyetsa ana awo, kapena kukafunafuna kopeza madzi a m’maluŵa kwatsopano. Mulungu iyemwini analinganiza zinthu kuti tipindule pamene njuchi zotanganitsidwa zoterozo zipanga uchi wokoma ndi wopatsa nyonga.

Chozizwitsa cha kugwirizana kwa pakati pa njuchi ndi zomera ndi pakati pa tizilombo tokhatokha chiri umodzi wa maumboni ambiri akuti Mlengi ali wokhoza kotheratu kupangitsa zinthu zamoyo kugwirizana. Chifukwa cha chimenecho, ‘Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.’ (1 Akorinto 14:33) Pamenepo, kodi nchifukwa ninji iye walola anthu kukhala osagwirizana chotero, zotulukapo masoka kwa ambiri? Ngati Mulungu amatisamala, kodi nchifukwa ninji iye wayembekeza kwa nthaŵi yaitali chotero anasawongolere mkhalidwe? Ndithudi, kodi nchifukwa ninji Mulungu wakhala woleza mtima motero?

Mawu a Mulungu, Baibulo, amayankha mafunso oterowo. Bukhu lapadera limeneli limatiuza kuti Yehova Mulungu wakhala woleza mtima kaamba ka chifukwa chabwino. Kodi nchifukwa chiti chimenecho? Ndipo kodi kuleza mtima kwa Mulungu kudzapitirizabe kwa utali wina wotani?

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Cover photo: Frilet/​Sipa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena