Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/1 tsamba 23-28
  • ‘Odala Ali Onse Amene Amdikira Yehova’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Odala Ali Onse Amene Amdikira Yehova’
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbewu za Umishonale Zifesedwa
  • Mavuto m’Spanya
  • Kulalikira Pansi pa Ulamuliro Wankhanza Wachikatolika
  • Chizunzo ndi Kuthamangitsidwa
  • Gawo Lina, Chinenero China
  • Nthaŵi ya Mavuto Iyamba
  • Kulalikira m’Morocco Wachisilamu
  • Gawo la Kanthaŵi Kochepa?
  • Ziyeso ndi Madalitso
  • Kufutukuka mu El Salvador
  • Zochitika Zosayembekezeka Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuchokera ku Umphaŵi Wadzaoneni Kumka ku Chuma Chochuluka
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Mulungu Anatisonyeza Kukoma Mtima Kwakukulu M’njira Zambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Tinapatsidwa Ngale ya Mtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/1 tsamba 23-28

‘Odala Ali Onse Amene Amdikira Yehova’

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI DOMENICK PICCONE

Makolo anga anasamuka ku Italiya kupita ku United States m’zaka za ma 1920 ndipo pomalizira pake anakhazikika ku South Philadelphia, panthaŵiyo yodziŵika monga Italiya Wamng’ono. Pofika 1927 iwo anali kuyanjana ndi Ophunzira Baibulo, omwe pambuyo pake anadzadziŵika monga Mboni za Yehova.

NDINABADWA mu 1929 ndipo chotero ndakhala ndikuwona chowonadi cha Baibulo kuchokera ku ukhanda. Ndimakumbukira kuti Mboni zinali kusonkhana m’nyumba mwathu zisanapite kukalalikira m’matauni a Roma Katolika m’chigawo cha migodi ya malasha cha Pennsylvania, kumene abale anali kugwidwa nthaŵi zambiri. Ndinabatizidwa mu 1941 pamsonkhano wa Mboni za Yehova mu St. Louis, Missouri. Ndiyeno zinthu zinayamba kuipa.

Ndinayamba kuyanjana ndi achichepere oipa m’mudzimo ndipo ndinayamba kusuta ndi kutchova njuga m’ngondya za makwalala. Mwamwaŵi, makolo anga anazindikira kuti anali kulephera kundilamulira ndipo anasankha kusamukira kudera lina la mzindawo. Sindinakondwere, chifukwa chakuti ndinataikiridwa mabwenzi anga a m’khwalala. Komabe, lerolino ndimayang’ana m’mbuyo ndikukhala woyamikira kwenikweni kwa atate ŵanga. Iwo anapereka nsembe yeniyeni yazachuma kuti andiwonjole m’malo amenewo. Pamene kuli kwakuti kalelo anali kuyenda pansi kupita kuntchito, tsopano anafunikira kukwera sitima kwa ulendo wautali. Koma kachitidwe kameneka kanandibwezera m’malo ateokratiki.

Mbewu za Umishonale Zifesedwa

Pafupifupi chaka chirichonse, tinali kupita ku South Lansing, New York, kukapezekapo pa kumaliza maphunziro kwa Sukulu ya Baibulo ya Watchtower ya Gileadi. Kuwona amishonalewo akutumizidwa padziko lonse kunafesa chikhumbo cha utumiki waumishonale mumtima mwanga. Chotero, pambuyo pakumaliza maphunziro ku sekondale, ndinalembetsa monga minisitala wachipainiya wokhazikika, kuyambira May 1947.

Mpainiya wina wachichepere mumpingo wathu anali Elsa Schwarz, ndipo anali wachangu m’ntchito yolalikira. Nthaŵi zonse makolo ake anali kumlimbikitsa kukhala mishonale, chotero mungalote chotulukapo chake. Tinakwatirana mu 1951. Pamene tinali kutumikira pamodzi monga apainiya mu Pennsylvania, tinafunsira kukapezekapo pa sukulu ya Gileadi ya amishonale. Mu 1953 tinaitanidwa ku kalasi ya 23 ya Gileadi. Pambuyo pa miyezi isanu yamaphunziro osamalitsa ndi kukonzekera ku Gileadi, tinamaliza maphunziro pa msonkhano mu Toronto, Canada, ndipo tinalandira gawo lathu​—Spanya!

Mavuto m’Spanya

Pamene tinali kukonzekera kupita ku gawo lathu laumishonale mu 1955, Elsa ndi ine tinali ndi mafunso ambiri. Spanya! Kodi kukakhala bwanji? Dzikolo linali pansi pa ulamuliro wa wolamulira wankhanza wa Chikatolika Generalissimo Francisco Franco, ndipo ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa. Kodi tikakhoza motani pansi pa mikhalidwe yoteroyo?

Tinauzidwa ndi abale pa malikulu a Sosaite ku Brooklyn kuti Frederick Franz, yemwe panthaŵiyo anali wachiŵiri kwa presidenti wa Watch Tower Society, ndi Alvaro Berecochea, mishonale wa ku Argentina, anagwidwa, limodzi ndi abale ena ambiri. Msonkhano wachinsinsi unalinganizidwa m’nkhalango pafupi ndi Barcelona. Komabe, apolisi anadziŵa za malo osonkhanira achinsinsiwa ndipo anagwira ambiri a awo omwe anafikapo.a

Tinauzidwa kuti mwinamwake sipadzakhala aliyense wokhoza kudzatichingamira tikafika ku Barcelona. Tinalangizidwa kuti: “Mukafune malo okhala m’hotela, ndiyeno mukadziŵitse Sosaite ku New York za keyala ya hotelayo.” Tinakumbukira mawu awa a Yesaya: ‘Odala ali onse amene amdikira [Yehova]. Ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.’ (Yesaya 30:18, 21) Tinangofunikira kumdikira Yehova ndikutsatira chitsogozo cha gulu lake.

Tinatsazikana ndi makolo athu ndi mabwenzi omwe anabwera ku New York kudzatitsazika, ndipo posakhalitsa chombo chathu, Saturnia, chinayamba kuyandama pa Mtsinje wa Hudson kulinga ku Atlantic. Imeneyo inali nthaŵi yomalizira imene ndinawona bambo ŵanga. Zaka ziŵiri pambuyo pake, pamene ndinali kudziko lakunja, anamwalira pambuyo pa kudwala kwa nthaŵi yaitali.

Pomalizira pake tinafika ku gawo lathu, mzinda wapadoko wa Barcelona. Linali tsiku lamdima, lamvula, koma pamene tinali kudutsa akuluakulu owona za oloŵa ndi kutuluka m’dziko, tinawona nkhope “zowala” ndi chimwemwe. Alvaro Berecochea, limodzi ndi abale ena Achispanya, anafika kudzatichingamira. Tinalidi achimwemwe kudziŵa kuti abale athu anamasulidwa.

Tsopano tinafunikira kuphunzira Chispanya. M’masiku amenewo amishonale anayenera kuphunzira zinenero movuta​—popanda mabuku ophunzirira kapena aphunzitsi. Panthaŵiyo padalibe maphunziro ophunzitsa chinenero. Tinayenera kufikiritsa muyeso wofunikira wa maola m’ntchito yolalikira ndipo panthaŵi imodzimodziyo kuphunzira chinenerocho​—pantchito.

Kulalikira Pansi pa Ulamuliro Wankhanza Wachikatolika

Panthaŵiyo gulu la Yehova lina lidakali khanda m’Spanya. Mu 1955 panali chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 366 m’dziko lokhala ndi anthu okwanira 28 miliyoni. Munali mipingo khumi yokha m’dziko lonselo. Kodi likakhala choncho kwa nthaŵi yaitali? Mwamsanga pamene mkazi wanga ndi ine tinayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba, tinapeza kuti Spanya anali ngati paradaiso kwa ofalitsa mbiri yabwino. Inde, anthuwo anali ndi njala ya chowonadi.

Koma kodi ntchito yolalikirayo inali kuchitidwa motani, popeza kuti inali yoletsedwa? Kaŵirikaŵiri sitinali kuchezera nyumba iriyonse pakhwalala, osatinso chipinda chirichonse pa nyumba yosanja. Barcelona uli mzinda wokhala ndi nyumba zambiri zokhala ndi zipinda zosanja zisanu ndi zisanu ndi chimodzi, ndipo tinalangizidwa kuyambira pamwamba kumatsika pansi. Mwinamwake tinali kungofikira nyumba imodzi pa chipinda chosanja chirichonse kapena ngakhale kudumpha zipinda zingapo. Njira imeneyi inakupangitsa kukhala kovuta kuti apolisi atigwire ngati mwininyumba wotengeka maganizo anatineneza.

Misonkhano yampingo inali kuchitidwira m’nyumba, mipingo inali kupangidwa ndi magulu atatu kapena anayi a phunziro labukhu. Ichi chinatheketsa mtumiki wa mpingo kuchezera lirilonse la magulu a maphunziro abukhu ameneŵa kamodzi pamwezi. Wochititsa phunziro labukhu anali ndi thayo lakuchititsa misonkhano yonse, yochitidwa usiku uŵiri wosiyana pamlungu kwa gulu laling’ono la anthu kuchokera pa 10 mpaka 20.

Tinayenera kuphunzira njira yamoyo yatsopano. Panthaŵiyo kudalibe makonzedwe a nyumba ya amishonale m’Spanya. Pamene kunali kotheka, tinakhala m’nyumba za abalewo. Kuphunzira kuphikira pa mbaula kunali chitokoso chenicheni kwa Elsa! M’kupita kwanthaŵi tinali okhoza kugula chitofu cha parafini, chomwe chinapeputsako zinthu ndithu.

Chizunzo ndi Kuthamangitsidwa

Patapita kanthaŵi tinalandira uthenga wakuti chizunzo chinayambika ku Andalusia, kumene mpainiya wapadera anagwidwa. Mwatsokalanji, anali ndi kabukhu komwe kanali ndi maina ndi makeyala a abale a m’mbali zonse za dzikolo. Tinapitiriza kulandira malipoti akuti abale athu anali kugwidwa mumzinda umodzi pambuyo pa unzake. Kuloŵererako kunali kuyandikira pang’onopang’ono ku Barcelona. Pomalizira pake, chizunzo chinakantha Barcelona.

Miyezi ingapo kuchiyambi, apolisi ananditengera ku malikulu awo kukandifunsa. Pambuyo pa maola angapo ndinamasulidwa, ndipo ndinaganiza kuti zinthu zathera pompo. Ndiyeno ofesi ya Kazembe wa Amereka inandipatsa lingaliro lakuti kuti ndipeŵe kuchititsidwa manyazi mwakuthamangitsidwa, ndiyenera kuchoka ndekha m’dzikomo. Mwamsanga pambuyo pake, apolisi anatiuza kuti kunangotsala masiku khumi kuti tituluke m’dzikomo. Popeza kuti padalibe nthaŵi yakuti tilembere Watch Tower Society, kodi tikanachitanji? Mikhalidwe inawonekera kutisonyeza kuti tiyenera kupita kumunda waumishonale wapafupi kunja kwa Spanya​—Portugal, kumadzulo.

Gawo Lina, Chinenero China

Pamene tinangofika mu Lisbon, Portugal, mu July 1957, tinagaŵiridwa monga amishonale ku Porto, mzinda wokhala kumpoto kwenikweni kwa Lisbon. Unalingaliridwa kukhala likulu lachiŵiri la dzikolo ndipo unali m’chigawo chodziŵika chifukwa cha vinyo wake wokoma. Mpingo womakulakula unali kuchitira misonkhano yake pansi pa nyumba yokhala kunsi kwa tauni. Ntchito yolalikira inalinso yoletsedwa mu Portugal, popeza kuti dzikolo linali pansi pa ulamuliro wankhanza wa Salazar. Komabe, mikhalidwe inali yosiyana kotheratu ndi ija ya ku Spanya. Misonkhano inali kuchitidwa m’nyumba za abale, ndipo magulu a anthu ochokera pa 40 mpaka 60 anafikapo. Panalibe zisonyezo zakuti nyumbazo zinali malo osonkhanira a Mboni za Yehova. Ngakhale kuti sindinali kulankhula Chipwitikizi, ndinaikidwa kukhala mtumiki wa mpingo. Kachiŵirinso, tinaphunzira chinenero chatsopano mwanjira yovuta.

Pafupifupi chaka chimodzi pambuyo pake, tinagaŵiridwa ku Lisbon. Kunoko, kwanthaŵi yoyamba, tinali ndi nyumba yathuyathu, chipinda choyang’ana ku mzinda wa Lisbon. Tinagaŵiridwa kusamalira dera​—dziko lonse la Ripabuliki la Portugal. Pamene tinafika ku Portugal, kunali ofalitsa 305 okha ndi mipingo isanu.

Nthaŵi ya Mavuto Iyamba

Pamapu ena osonyeza Portugal ndi timaiko take, panali mawu onena kuti: “Dzuŵa silimaloŵa konse m’gawo la Apwitikizi.” Izitu zinali zowona, popeza kuti Portugal anali ndi maiko m’mbali zambiri za dziko, aŵiri aakulu kwambiri akumakhala Mozambique ndi Angola mu Afirika. Mu 1961 kunawonekera kuti panali mavuto omwe anabuka m’maiko ameneŵa, ndipo Portugal anawona kufunika kwakuwonjezera magulu ake ankhondo.

Tsopano, kodi abale achichepere akachitanji pamene iwo analembedwa kaamba ka utumiki wankhondo? Ena anali okhoza kupatulidwa chifukwa cha kudwala, koma ambiri anachirimika mu uchete Wachikristu. Posakhalitsa mkuntho wa chizunzo unayamba. Nthambi inalandira malipoti akuti apainiya apadera anali kugwidwa ndi kumenyedwa modetsa nkhaŵa ndi apolisi achinsinsi, ma P.I.D.E. (Polícia Internacional e Defesa do Estado) ambiri yoipawo. Ena a amishonalefe tinaitanidwa ku malikulu a apolisi kukafunsidwa. Ndiyeno, mabanja atatu anapatsidwa masiku 30 kuti achoke m’dzikomo. Tonsefe tinapempha ulamuliro kuti usinthe chosankhacho.

Mmodzi ndi mmodzi amishonale okwatiranawo anaitanidwa kumalikulu a apolisi kukafunsidwa ndi mtsogoleri wa P.I.D.E. Poyamba, mtumiki wa nthambi, Eric Britten, ndi mkazi wake, Christina, anafunsidwa. Ndiyeno, Eric Beveridge ndi mkazi wake, Hazel, ndipo pomalizira pake Elsa ndi ine tinafunsidwa. Mkulu wa apolisiyo mwachinyengo anatipatsa mlandu wakugwiritsiridwa ntchito ndi Akomyunisiti kunyalanyaza dziko la Kumadzulo ndi chiphunzitso chathu cha uchete. Kuchonderera kwathu sikunaphule kanthu.

Kunali komvetsa chisoni chotani nanga kusiya abale ndi alongo 1,200 omwe anali kupyola nthaŵi zovuta chifukwa cha ulamuliro wankhalwe wa wolamulira wankhanza wosalingalira! Pamene kuli kwakuti a Beveridge anapita ku Spanya ndipo a Britten anabwerera ku Mangalande, kodi gawo lathu lotsatira likakhala kuti? Morocco Wachisilamu!

Kulalikira m’Morocco Wachisilamu

Kachiŵirinso, tinali kumdikira Yehova. Gawo latsopano, miyambo yatsopano, ndi zinenero zatsopano! Chiluya, Chifalansa, ndi Chispanya ndizo zinali zinenero zalamulo mu Ufumu wa Morocco, kumene kunali Mboni 234 m’mipingo isanu ndi itatu. Chipembedzo chalamulo cha dzikolo chinali Chisilamu, ndipo kupanga ophunzira pakati pa Asilamu kunali koletsedwa mwalamulo. Chotero tinali kungolalikira makamaka kwa anthu ochokera ku Ulaya omwe sanali Asilamu.

Pamene amishonale anayamba kufika kumapeto kwa ma 1950, ziwonjezeko zinayamba kuwonekera. Koma boma la Morocco linayamba kuika chitsenderezo pa anthu a ku Ulaya, ndipo alendo ambiri anatuluka, kuphatikizapo abale ambiri.

Pamene gulu lathu la anthu osakhala Asilamu linayamba kuchepa, tinakakamizika kupeza njira zaluso zolankhulira ndi Asilamu, ndipo ichi chinapangitsa anthu kudandaula kwa apolisi. Pamene madandaulowo anayamba kuchuluka ku Tangier ndi mizinda ina, pomalizira pake tinauzidwa kuti kunangotsala masiku 30 okha kuti tituluke m’dzikomo. Mu May 1969, Elsa ndi ine tinathamangitsidwanso m’gawo lina.

Gawo la Kanthaŵi Kochepa?

Tinauzidwa kuti tibwerere ku Brooklyn, ndipo ndinaitanidwa kukapezekapo pa msonkhano wa atumiki a nthambi womwe unachitidwa chilimwe chimenecho. Pamene ndinali kumeneko, ndinauzidwa kuti gawo lathu latsopano likakhala El Salvador, Central Amereka, ndikuti ndikatumikira kumeneko monga mtumiki wa nthambi. Ndinauzidwa kuti kunali kothekera kwenikweni kuti ndikakhalako pafupifupi zaka zisanu, mlingo waukulu umene amishonale analoledwa kukhala m’dzikolo, popeza kuti ntchito yathu inali isanazindikiridwe mwalamulo kumeneko.

El Salvador​—linali gawo labwino lotani nanga! Kunali ofalitsa 1,290, kuphatikizapo apainiya 114 omwe ankachitira lipoti pa avareji mwezi uliwonse. Anthuwo anali owopa Mulungu, okonda Baibulo, ndipo ochereza. Pafupifupi pakhomo lirilonse, anatiitana kuloŵa m’nyumba ndi kukambitsirana nawo. M’kanthaŵi kochepa, tinali ndi maphunziro Abaibulo ambiri omwe tikanakhoza.

Pamene tinawona chiwonjezeko ndi kusoŵa kwakukulu kumeneko, tinali achisoni kuti tikakhalako kwa zaka zisanu zokha. Chotero kunagamulidwa kuti tiyeseyese kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya Mboni za Yehova. Tinapereka zikalata ku boma mu December 1971, ndipo pa April 26, 1972, tinasangalala kuŵerenga m’nyuzipepala yaboma, Diario Oficial, kuti pempho lathu linavomerezedwa. Amishonale sakafunikiranso kuchoka pambuyo pa zaka zisanu koma akhoza kupeza zikalata zokhaliratu m’dzikomo.

Ziyeso ndi Madalitso

M’zaka zonsezi m’magawo athu osiyanasiyana, tapanga mabwenzi ambiri ndikuwona zipatso za uminisitala wathu. Elsa anali ndi chokumana nacho chabwino mu San Salvador ndi mphunzitsi wapasukulu ndi mwamuna wake yemwe anali msirikali. Mmodzi wa mabwenzi a mphunzitsiyo anakondweretsedwanso ndi chowonadi. Poyamba mwamunayo sanasonyeze chikondwerero m’Baibulo; komabe, tinamuchezera pamene anali m’chipatala, ndipo anali waubwenzi. Potsirizira pake anaphunzira Baibulo, analeka ntchito yake yankhondo, nayamba kulalikira pamodzi nafe.

Panthaŵi imodzimodziyo, dona wina anafika pa Nyumba Yaufumu ndikufunsa ngati Elsa anali kuphunzira ndi yemwe kale anali msirikaliyo. Zinangochitika kuti iye anali chibwenzi chake! Nayenso anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pamsonkhano wachigawo, mwamuna yemwe adali wankhondoyo, mkazi wake, bwenzi lamkaziyo, ndi yemwe kale anali chibwenzi cha mwamunayo onse anabatizidwa!

Kufutukuka mu El Salvador

Chifukwa cha chiwonjezeko chachikulu, Nyumba Zaufumu zambiri zamangidwa, ndipo dzikolo tsopano liri ndi Mboni zokangalika zoposa 18,000. Komabe, kupita patsogolo kumeneku sikunachitike kopanda ziyeso. Kwa zaka khumi, abalewo anafunikira kuchita chifuniro cha Yehova mkati mwa nkhondo yachiweniweni. Koma anasungabe uchete wawo ndipo anakhalabe okhulupirika ku Ufumu wa Yehova.

Pakati pa aŵirife, Elsa ndi ine takhala mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka 85. Tapeza kuti pamene timdikira Yehova ndikumvetsera ‘mawu kumbuyo [kwathu] akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo,’ sitimagwiritsidwa mwala konse. Tasangalaladi ndi moyo wokhutiritsa wopatsa mphotho monga atumiki anthaŵi zonse a Yehova.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka tsatanetsatane wokwanira, onani 1978 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 177-9.

[Chithunzi patsamba 24]

Msonkhano m’nkhalango mu Spanya, 1956

[Chithunzi patsamba 25]

Tinkalalikira kwa anthu osakhala Asilamu m’Morocco

[Chithunzi patsamba 26]

Nthambi ya ku El Salvador, gawo lathu lapanthaŵi ino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena