Tinapatsidwa Ngale ya Mtengo Wapatali
YOSIMBIDWA NDI RICHARD GUNTHER
Munali mu September 1959. Tinali mu sitima yapanyanja ya ku Italy yotchedwa Julio Caesar tikumayenda ulendo kudutsa Atlantic Ocean kuchokera ku New York kumka ku Cádiz, Spain. Watch Tower Society inali itatumiza ine, limodzi ndi mkazi wanga, Rita, ndi Paul ndi Evelyn Hundertmark, banja lina la amishonale, ku dziko limenelo la ku Iberia. Tinayembekezera kukakumana ndi zovuta zambiri. Koma kodi ndimotani mmene tinasankhira ntchito yaumishonale?
INE ndi Rita tinabatizidwa kukhala Mboni za Yehova mu 1950 ku New Jersey, U.S.A. Posapita nthaŵi, tinapanga chosankha chimene m’kupita kwa nthaŵi chinali kudzatipatsa ngale ya mtengo wapatali. Tinali mumpingo wokhala ndi abale ndi alongo okwanira kufola gawo lake. Chotero tinakakamizika kudzipereka kukatumikira kumene kusoŵa kwa alaliki kunali kokulira. Pa msonkhano wa mitundu yonse wa Mboni za Yehova ku New York City m’chilimwe cha 1958, tinafunsira utumiki waumishonale.
Posapita nthaŵi, tinaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, ndipo chaka chisanakwane tinali paulendo wathu wa ku Spain monga amishonale. Pokhala otanganitsidwa kwambiri ndi makonzedwe ambiri ndi chisangalalo chachikulu kwambiri, sitinadziŵe panthaŵiyo chimene tinapatsidwa. Yesu analakhula za ngale ya mtengo wapatali. (Mateyu 13:45, 46) Ngakhale kuti umishonale sunali mfundo yofotokozedwa m’fanizo lake, kwa ife mwaŵi wathu wa kutumikira monga amishonale unali wofanana ndi ngale yotero. Pamene tikumbukira za kumbuyoko, tsopano timazindikira kwambiri za mphatso ya mtengo wapatali imeneyi ya utumiki m’gulu la Yehova.
Chochitika Chosaiŵalika
Panthaŵiyo kosi yaumishonale wa Gileadi inachitidwira m’malo ena okongola ku chigawo cha Finger Lakes ku New York State. Kumeneko, tinakhalako miyezi isanu ndi umodzi yokondweretsa tili omwerekera kotheratu m’kuphunzira Baibulo ndi m’mayanjano enieni Achikristu, tili olekanitsidwa ndi zochitika za dzikoli ndi mavuto ake. Ophunzira anzathu anali ochokera ku mbali zambiri za dziko, zonga Australia, Bolivia, Britain, Greece, ndi New Zealand. Komabe, posapita nthaŵi, tsiku la kumaliza maphunziro linafika. Mu August 1959, tinatsazikana ndi ena misozi ili m’maso pamene tinanyamuka ulendo wa panyanja kumka ku magawo athu aumishonale. Patapita mwezi tinafika ku Spain.
Miyambo Yatsopano
Tinafika pa doko lakummwera la Algeciras, m’mphepete mwa Rock of Gibraltar wamkulukuluyo. Usikuwo anayife, ine ndi Rita pamodzi ndi banja la a Hundertmark, tinakwera sitima yapamtunda kumka ku Madrid. Tinafika ku Hotel Mercador, tinayembekezera kumeneko kufikira pamene tinaonana ndi ziŵalo za ofesi ya nthambi ya Sosaite yobisika. Spain anali pansi pa ulamuliro wotsendereza wa Generalissimo Francisco Franco. Zimenezi zinatanthauza kuti chipembedzo chokha chimene chinali chololedwa mwalamulo m’dzikolo chinali Tchalitchi cha Roma Katolika. Kudzisonyeza kukhala wa chipembedzo china poyera kunali kosaloledwa ndi lamulo, ndipo ntchito yolalikira kukhomo ndi khomo ya Mboni za Yehova inaletsedwa. Ngakhale misonkhano yachipembedzo inaletsedwa, kwakuti Mboni za Yehova, zimene panthaŵiyo mu Spain zinali pafupifupi 1,200 m’mipingo 30, sizinathe kusonkhana m’Nyumba Zaufumu monga m’maiko ena. Tinali kusonkhana mobisa m’nyumba za abale.
Kuphunzira Chispanya ndi Kuyamba Ntchito
Vuto lathu loyamba linali la kuphunzira chinenero. Mwezi woyamba tinathera maola 11 patsiku tikumaphunzira Chispanya—maola 4 mmaŵa uliwonse tili m’kalasi, ndiyeno maola 7 tikumaphunzira tokha. Mwezi wachiŵiri zinali chimodzimodzi mmaŵa, koma tinathera nthaŵi ya masana mu ulaliki wa kukhomo ndi khomo. Kodi mungayerekezere zimenezo? Tili osadziŵabe chinenero ndipo titanyamula chabe khadi lolembedwapo mawu oyamba oloŵezedwa pamtima, ine ndi Rita tinapita kuntchito ya kukhomo ndi khomo tili tokhatokha!
Ndikukumbukira ndikumagogoda pakhomo lina ku Vallecas, chigawo cha anthu opeza bwino cha Madrid. Nditagwiriza khadi langa, pochitira kuti zingavute, ndinalankhula m’Chispanya kuti: “Moni. Tikuchita ntchito Yachikristu. Baibulo limati (tinaŵerenga vesi). Tikufuna kukusiyirani kabukuka.” Tsono, mkaziyo anangoyang’ana, pamenepo anatenga kabukuko. Pamene tinabwereranso, anatipempha kuloŵa m’nyumba, ndipo pamene tinali kulankhula, anangoyang’ana. Tinayamba kuchita naye phunziro la Baibulo malinga ndi kukhoza kwathu, ndipo pophunzirapo, ankangomvetsera ndi kuyang’ana. Patapita nthaŵi anatiuza kuti sankamva zimene tinanena pa ulendo wathu woyamba koma anamva liwu lakuti Dios (Mulungu) ndi kuti limenelo linamkhutiritsa kudziŵa kuti zinali za kanthu kena kabwino. M’kupita kwa nthaŵi, anapeza chidziŵitso chambiri cha Baibulo ndipo anabatizidwa ndi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova.
Kuphunzira Chispanya kunali kondivuta kwambiri. Pamene ndinali kuyenda mu mzindawo, ndinkaloŵeza maverebu pamtima. Zimene ndinaloŵeza m’mlungu umodzi ndinkaziiŵala m’mlungu wotsatira! Zinali zogwiritsa mwala kwambiri. Ndinafuna kusiya kangapo konse. Popeza kuti ndinkalankhula Chispanya chosalongosoka nkomwe, abale Achispanya anali oleza mtima kwambiri pamene ndinali kuwatsogolera. Pamsonkhano wina wachigawo, mbale wina anandipatsa chilengezo cholembedwa pamanja kuti ndikaŵerenge pa pulatifomu. Povutika ndi malembedwe a mbaleyo, ndinalengeza kuti: “Bwerani ndi muletas (ndodo za m’khwapa) zanu kusitediyamu maŵa.” Ndinayenera kuŵerenga kuti, “Bwerani ndi maletas (katundu) wanu kusitediyamu maŵa.” Zoonadi, khamulo linaseka, ndipo ine mwachibadwa ndinachita manyazi.
Mayeso Oyambirira ku Madrid
Ine ndi Rita tinavutika mtima kwambiri ndi zaka zingapo zoyamba zimenezo ku Madrid. Tinkalakalaka kwambiri kwathu ndi mabwenzi athu. Nthaŵi iliyonse pamene tinalandira kalata yochokera ku United States, tinali kulakalaka kwambiri kumudzi. Nyengo zimenezo zolakalaka kwathu zinali zovuta kwambiri, komano zinapyola. Ndi iko komwe, tinali titasiya kwathu, achibale, ndi mabwenzi kuti m’malo mwawo tilandire ngale ya mtengo wapatali. Tinafunikira kuzoloŵera.
Pamene choyamba tinakhala mu Madrid, tinali kukhala m’nyumba yosalongosoka yofikiramo alendo. Tinali ndi chipinda chathu ndipo tinkapatsidwa chakudya katatu patsiku. Chinali chipinda chaching’ono chamdima, ndipo matiresi ake anali a udzu. Lendi ya pamwezi inali kudya alawansi yathu yochepa ya mwezi ndi mwezi. Kaŵirikaŵiri tinkadya pamenepo masana, ndipo mwini malowo amene anali mkazi ankatisiyira chakudya chamadzulo mu uvuni kuti chikhalebe chotentha kotero kuti usiku tidzakhale ndi chakudya. Komabe, poyenda m’misewu masana ndi madzulo, tinkamva njala kwambiri. Ngati tinalibe ndalama zotsala za alawansi, tinkagwiritsira ntchito ndalama zathu zapambali zochepa kugulira chokoleti chilichonse chotsika mtengo kwambiri chimene tinapeza. Komabe, posakhalitsa, woyang’anira woyendera nthambi wa Sosaite atafika mkhalidwe umenewu unasintha. Iye anaona mkhalidwe wathuwo nanena kuti tifunefune nyumba ina yaing’ono yoti tizigwiritsira ntchito monga nyumba ya amishonale. Motero, zimenezi zinali zabwino kwambiri kuposa kusambira m’khichini utaimirira m’bafa. Tsopano tinali ndi shawa, firiji yosungiramo chakudya, ndi sitovu ya magetsi yophikira chakudya chathu. Tinayamikira kwambiri pa kutilingalira kumeneku.
Zokumana Nazo Zokondweretsa ku Madrid
Ulaliki wa kunyumba ndi nyumba unali kuchitidwa mosamala kwambiri. Piringupiringu ndi phokoso la tsiku ndi tsiku la m’Madrid zinali zothandiza kwambiri, zikumatibisa kotero kuti tisadziŵike kwambiri. Tinayesera kuvala ndi kuchita zinthu mofanana ndi ena kotero kuti tisaonekere kukhala anthu achilendo. Njira yathu ya kulalikira kukhomo ndi khomo inali ya kuloŵa pa mdadada wa nyumba, kugogoda pakhomo, kulankhula ndi munthu, ndiyeno kuchoka panyumbayo, msewu wake, ndi deralo. Nthaŵi zonse panali kuthekera kwakuti mwininyumba akanatha kuitana apolisi, ndipo nchifukwa chake sikunali kwanzeru kukhalabe m’deralo. Kwenikweni, ngakhale Paul ndi Evelyn Hundertmark amene anali ochenjera kwambiri pogwiritsira ntchito njira imeneyi, anagwidwa ndi kuthamangitsidwa m’dzikolo mu 1960. Iwo anapita ku Portugal woyandikana naye, akumatumikira kumeneko kwa zaka zingapo, Paul akumayang’anira ofesi ya nthambi yobisika. Lerolino iye ndi woyang’anira mzinda wa San Diego, ku California.
Komabe, kwa ife kulinganiza kunachitidwa. Miyezi ingapo chabe pambuyo pake, amishonale asanu ndi mmodzi amene anatumizidwa ku Portugal anauzidwa kuchoka m’dzikolo! Zimenezi zinadzetsa zochitika zokondweretsa chifukwa chakuti Eric ndi Hazel Beveridge, amene analinso m’kalasi yathu ya Gileadi, tsopano anauzidwa kuchoka m’Portugal ndi kubwera ku Spain. Chotero, kachiŵirinso mu February 1962 tinali pa Hotel Mercador—panthaŵiyi kudzalandira Eric ndi Hazel pamene anafika.
Munali m’masiku oyambirira ameneŵa ku Madrid pamene ine ndi Rita tinadzionera chinyengo cha chipembedzo. Tinkaphunzira Baibulo ndi banja lina, Bernardo ndi Maria, amene ankakhala m’chithando chopangidwa ndi zinthu zomangira nyumba zotayidwa zimene Bernardo anapeza. Tinkaphunzira nawo usiku kwambiri, ndipo pambuyo pa phunzirolo, ankatipatsa buledi, vinyo, ndi tchizi kapena china chilichonse chimene anali nacho. Ndinaona kuti tchizicho chinali chofanana ndi cha ku America. Usiku wina titatsiriza kuphunzira, iwo anabweretsa chitini cha tchizicho. Chinalembedwa m’Chingelezi ndi zilembo zazikulu kuti, “Chochokera kwa anthu a ku America kaamba ka anthu a ku Spain—chosagulitsa.” Kodi banja losaukali linalandira motani tchizicho? Tchalitchi cha Katolika chinagwiritsiridwa ntchito ndi boma kuchigaŵira kwa osauka. Koma wansembe anali kuchigulitsa!
Utumiki Waphindu kwa Asilikali Ankhondo
Posapita nthaŵi kanthu kena kosangalatsa kanachitika kamene kanakhala dalitso lalikulu kwa ife ndi kwa ena ambiri. Tinalandira chidziŵitso kuchokera ku ofesi ya nthambi chotipempha kuti tikaonane ndi mnyamata wina wotchedwa Walter Kiedaisch, amene anali kumalikulu a Air Force ya United States ku Torrejón, okhala pamtunda wa makilomita oŵerengeka kunja kwa Madrid. Tinapita kukaonana naye iyeyo ndi mkazi wake, tinayamba kuchita nawo phunziro la Baibulo ndiponso ndi banja lina la pa Air Force pamenepo.
Panthaŵi imeneyo, ndinali kuchititsa maphunziro a Baibulo asanu ndi akuluakulu a Air Force ya United States, onsewo m’Chingelezi. Pakati pa ameneŵa, asanu ndi aŵiri anabatizidwa, ndipo atabwerera ku United States, anayi a amunawo anakhala akulu a mpingo.
Imeneyi inali nthaŵi pamene panali njira zochepa zoloŵetsera mabuku, magazini, ndi ma Baibulo m’dzikolo chifukwa cha chiletso choikidwa pa ntchito yathu. Komabe, mabuku ena anafika ndi alendo oona malo ndi anzathu a ku America. Ndinasankhidwa ndi nthambi kutsegula malo obisa ofikira mabuku. Anali m’chipinda chosungiramo katundu kuseri kwa sitolo yogulitsa ziŵiya za mu ofesi ku Vallecas. Mkazi wa mwini sitoloyo anali Mboni ya Yehova. Ngakhale kuti mwini sitoloyo sanali Mboni, anachitira ulemu ntchito yathu, ndipo ngakhaledi kudziika pangozi iye mwiniyo ndi bizinesi yake, anandilola kugwiritsira ntchito mbali imeneyi yakumbuyo kupangira mitokoma ya mabuku ofuna kutumizidwa kumizinda m’dziko lonselo. Popeza kuti chipindachi nthaŵi zonse chinafunikira kuoneka monga mmene chinalili—chipinda cha fumbi, chodzaza makatoni mbwe—ndinapanga benchi ndi mashelefu amene ndinkaimika ndi kukonzekera kugwira ntchito mofulumira ndiyeno kuwabisa m’nyengo yaifupi. Tsiku litatha, ndinkayembekezera kufikira munthu aliyense atatuluka m’sitoloyo ndi kutuluka mofulumira ndi mitokoma yangayo.
Unalidi mwaŵi weniweni kukhala ndi phande m’kupereka zinthu zauzimu, zonga ngati magazini a Nsanya ya Olonda ndi Galamukani! ndi mabuku ena, ku mipingo m’dziko lonselo. Zimenezo zinali nthaŵi zosangalatsa.
Rita anali ndi dalitso la kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 16, amene theka lawo anakhala Mboni za Yehova zobatizidwa. Dolores anali mkazi wachichepere wokwatiwa amene anathera nyengo yozizira pakama chifukwa cha nthenda ya mtima. M’ngululu iyeyo ankadzuka nakhala wokangalika ndithu. Chikhulupiriro cha Dolores chinali cholimba, chotero pamene nthaŵi ya msonkhano wathu wachigawo ku Toulouse, France inafika, anafuna kwambiri kupitako. Anachenjezedwa ndi dokotala kuti kuchita zimenezo kukakhala kupusa chifukwa cha vuto la mtima wake. Atavala diresi wamba ndi masilipasi ali wopanda katundu, anapita kusiteshoni ya sitima yapamtunda kukatsazikana ndi mwamuna wake, amake, ndi ena amene anali paulendowo. Misozi ili m’maso, zinamkanika kuwaona akumapita popanda iye, chotero anakwera sitimayo, ndipo anamka ku France! Rita sanadziŵe kuti zimenezi zachitika. Koma anadabwa chotani nanga pamene anaona Dolores, akumwetulira kwambiri kumsonkhanoko!
Phunziro la Baibulo Lachilendo
Sitingamalize nkhaniyi ya gawo lathu la ku Madrid popanda kutchulapo Don Benigno Franco, “el profesor.” Mboni ina ya kumaloko inamka nane kukaonana ndi mwamuna wina wokalamba wolemekezeka amene anali kukhala ndi mkazi wake m’nyumba ina ya mkhalidwe woipa kwambiri. Ndinayamba kuchita naye phunziro la Baibulo. Nditaphunzira naye kwapafupifupi chaka chimodzi ndi theka, anapempha kubatizidwa ndi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova.
Mwamuna wokalamba wolemekezeka ameneyu, Don Benigno Franco, anali mbale wake wa Francisco Franco, wolamulira wotsendereza wa Spain panthaŵiyo. Kukuonekera monga ngati kuti Don Benigno anali munthu wokonda ufulu nthaŵi zonse. Mkati mwa Spanish Civil War, iye anali wogwirizana ndi Republic ndipo anatsutsana ndi mbale wakeyo—kazembe wankhondo amene anapambana m’nkhondoyo ndi kukhazikitsa ulamuliro wotsendereza Wachikatolika. Chiyambire 1939, Don Benigno anamanidwa mwaŵi wa ntchito, ndipo anali ndi zinthu zochepa kwambiri zochirikizira moyo. Chotero kunachitika kuti mbale wa Generalissimo Francisco Franco, wolamulira wotsendereza wa Spain, anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova.
Pempho Lodabwitsa
Mu 1965 ofesi ya nthambi ya Spain inatipempha kuti tikayambe maulendo mu ntchito ya dera ku Barcelona. Zimenezi zinatanthauza kusiyana ndi abale onse achikondi amene tinakonda kwambiri mu Madrid. Tsopano chochitika china chatsopano chinali kudzayambika, chimene kwa ine chinalinso chiyeso. Chochitikacho chinali chochititsa mantha chifukwa chakuti nthaŵi zonse ndinali kuona kukhala wosakhoza kuchita zinthu. Ndikudziŵa bwino kwambiri kuti Yehova ndiye amene anandikhozetsa kukhala wogwira mtima m’mbali imeneyi ya utumiki.
Kuchezetsa mipingo mlungu uliwonse kunatanthauza kukhala m’nyumba za abale. Tinalibe nyumba yeniyeni, ndipo pafupifupi kamodzi pa milungu iŵiri iliyonse, tinali kupita kunyumba ina. Zimenezi nzovuta makamaka kwa mkazi. Koma posapita nthaŵi José ndi Roser Escudé, amene anali kukhala ku Barcelona, anatipempha kukakhala nawo kwa masiku angapo panthaŵi ndi nthaŵi. Chimenechi chinali chikondi chawo chachikulu, pakuti zinatanthauza kuti tinakhala ndi malo achikhalire osungirako zinthu zathu ndiponso panyumba pofikira nthaŵi zonse pa Sande madzulo.
Ine ndi Rita tinathera zaka zinayi zotsatira m’ntchito yadera m’chigawo cha Catalonia, chokhala ku Mediterranean Coast. Misonkhano yathu yonse ya Baibulo inkachitidwa mobisa m’nyumba za abale, ndipo ulaliki wathu wa kunyumba ndi nyumba unkachitidwanso mochenjera kuti anthu asanyumwe. Nthaŵi zina mpingo wonse unkasonkhana pamodzi pa Sande kudzachita “pikiniki” m’nkhalango, makamaka pochita msonkhano wadera.
Nthaŵi zonse timayamikira abale ambiri auzimu odzipereka amene anaika ntchito yawo ndi ufulu wawo pangozi, akumayesayesa kuchititsa mipingo kukhala yogwirizana ndi yokangalika. Ambiri a iwo anatsogolera m’kufutukulira ntchitoyo m’matauni ena a kunja kwa mzindawo. Zimenezi zinamanga maziko a chiwonjezeko chachikulu koposa ku Spain chiletsocho chitachotsedwa ndipo ufulu wachipembedzo utaperekedwa mu 1970.
Kufunika kwa Kusiya Gawo Lathu la ku Dziko Lachilendo
M’zaka zathu khumi ku Spain, chisangalalo chathu cha dalitso lapadera limeneli la kutumikira Yehova chinadodometsedwa ndi mkhalidwe wa makolo athu. Nthaŵi zambiri, tinatsala pang’ono kusiya gawo lathu ndi kumka kwathu kukasamalira amayi ndi atate wanga. Komabe, chifukwa cha abale ndi alongo achikondi a m’mipingo ya pafupi ndi makolo anga, tinali okhoza kupitirizabe kukhala ku Spain. Inde, mwaŵi wakutumikira m’zaka zimenezo mu ntchito yaumishonale mwapang’ono unatheka chifukwa cha ena amene anakhala ndi phande nafe m’kuika zinthu za Ufumu wa Mulungu poyamba.
Potsirizira pake, mu December 1968, tinapita kwathu kukasamalira amayi wanga. Mwezi womwewo atate wanga anamwalira, ndipo amayi wanga anali amasiye. Pokhalabe omasuka pang’ono kutumikira nthaŵi yonse, tinalandira gawo la kutumikira mu ntchito yadera, komano panthaŵiyi ku United States. Kwa zaka 20 zotsatira, tinatumikira m’madera a Chispanya. Ngakhale kuti ngale yathu ya mtengo wapatali ya umishonale inatayika, tinapatsidwanso ina.
Kulalikira Pakati pa Anamgoneka ndi Chiwawa
Tsopano tinali kugwira ntchito pamodzi ndi abale ndi alongo ambiri amene anali kukhala m’mbali za mizinda zodzala chiwawa. Tangoganizani, mlungu woyamba weniweniwo mu ntchito yadera ku Brooklyn, New York, Rita anamtsomphola chikwama chake.
Panthaŵi ina ine ndi Rita tinali ndi kagulu kena m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba m’chigawo china cha New York City. Pokhota pagulaye ina, tinaona anthu ena amene anaima pamzera patsogolo pa chiboo china cha pakhoma la nyumba yosakhalamo anthu. Pamene tinayenda pang’ono mu msewuwo, tinaona wachichepere wina ataima m’kanjira ka m’mbali mwa msewu namatiyang’ana. Panali winanso amene anaima cha pagulaye ina patali akumayang’a galimoto za apolisi. Tinali titaloŵa pakati pa anthu amalonda a anamgoneka! Mlonda woyambayo anazunguzika, komano anaona magazini a Nsanja ya Olonda ndipo anakhazika mtima pansi. Ndi iko komwe, mwina ndinali wapolisi, adziŵa bwanji! Ndiyeno m’Chispanya anatchula kuti, “¡Los Atalayas! ¡Los Atalayas!” (A Nsanja ya Olonda! A Nsanja ya Olonda!) Anadziŵa kuti tinali ayani, akumatidziŵa chifukwa cha magazini, ndipo zonse zinali bwino. Pamene ndinamdutsa pafupi, ndinati, “¿Buenos dias, como está?” (Mwadzuka bwanji?) Anandiyankha mwa kundipempha kuti ndimpempherere!
Chosankha Chovuta Kwambiri
Mu 1990 kunafikira kukhala kwachionekere kuti ndinafunikira kukhala ndi amayi tsiku lililonse. Tinali titayesa mwamphamvu kukhalabe mu ntchito yoyendayenda, koma tinaona kuti kunali kosatheka kuchita mathayo aŵiri onsewo. Tinafunadi kutsimikizira kuti Amayi akusamaliridwa mwachikondi. Koma kachiŵirinso tinali kusiya ngale ya mtengo wapatali, kanthu kena kamene kanali kofunika kwambiri kwa ife. Miyala yonse yeniyeni ya mtengo wapatali ya m’dziko ndi zonse zimene ingachitire munthu nzochepa kwambiri poiyerekezera ndi miyala ya mtengo wapatali ya kutumikira monga mmishonale kapena woyang’anira woyendayenda m’gulu la Yehova.
Tsopano ine ndi Rita tili m’zaka zathu za ma 60. Tili okhutira ndi osangalala kutumikira mumpingo wa kwathu kuno wolankhula Chispanya. Pamene tikukumbukira za m’zaka zathu zonse zakumbuyoku mu utumiki wa Yehova, timamthokoza chifukwa cha kutiikizira ngale za mtengo wapatali.
[Chithunzi patsamba 23]
Ine ndi Rita ndi Paul ndi Evelyn Hundertmark (kulamanja) kunja kwa bwalo la nkhunzi la Madrid
[Chithunzi patsamba 24]
Kuchezetsa mpingo pa “pikiniki” m’nkhalango