Kodi Kubwezera Nkolakwa?
Mumsewu waukulu umene magalimoto amathamanga kwambiri popanda malipiro mu United States, galimoto lina linachedwa kupatukira kumbali kupereka mpata ndikulola lina kudutsa. Woyendetsa galimoto lachiŵirilo analipsira mwakuwombera mfuti galimoto lolakwalo, napha wokweramo wopanda liŵongo.
Msungwana wazaka zapakati pa 13 ndi 19 analephera m’maseŵera kwa msungwana wina. Anamlipsira mwakuuza bwenzi lalimuna la msungwanayo kuti msungwanayo anali kuwonana ndi mnyamata wapasukulu ina. Chotero anawononga unansi wa msungwanayo ndi mnyamatayo.
ANTHU ambiri amadzimva kukhala olungamitsidwa kulipsira pamene aganiza kuti alakwiridwa. Mwanjira imodzi kapena ina, iwo amatsatira mawu ofala akuti: “Usakwiye, tangolipsira.” Lerolino, chikondi cha mnansi chacheperatu, ndipo mzimu wakubwezera ukuwonjezeka.—Mateyu 24:12.
Komabe, kodi ndimotani mmene inuyo mumawonera kubwezera? Ngati mumakhulupirira Baibulo, mwinamwake mumalingalira kuti kwakukulukulu kubwezera nkolakwa. Koma pokhala kuti tikukhala m’dziko losapembedza, mungaganize kuti kukhululukira, kosemphana kwenikweni ndi kubwezera, kaŵirikaŵiri kumakhala kosatheka. Kodi mungachite bwanji ngati mwanyengezedwa kapena kufwambidwa? Kodi mumalipsira ngati munthu wina akunyalanyazani kapena alankhula monyoza za inu kwa ena? Kodi ndinu wobwezera kapena wokhululukira?
Mkhalidwe Wolipsira Umavulaza
Ndithudi, kulakwa kumakhala kosiyanasiyana. Koma anthu ambiri amene amafuna kulipsira munthu wina samakhala atafwambidwa kapena kuukiridwa mwaupandu. “Zolakwa” zogwidwa mawu koyambirira kwa nkhani ino zinali zazing’ono, ngakhale kuti zinawonekera zazikulu m’maganizo mwa awo amene anasankha kulipsira.
Baibulo limanena kuti sitiyenera kukulitsa mkhalidwe wobwezera. Miyambo 24:29 imapatsa uphungu wakuti: ‘Usanene, Ndidzamchitira zomwezo anandichitira ine.’ Nkulekeranji? Choyamba, mkhalidwe woterowo umakhala wosakaza mwamaganizo ndi mwakuthupi. Malingaliro obwezera amachotsa mtendere wa maganizo ndikutsekereza kulingalira kwanzeru. Talingalirani lipoti lanyuzi ili: “Alimi aŵiri akumawombera mfuti ali m’magalimoto awo anaphana pamalo oimika magalimoto, kuthetsa mkangano wa zaka 40 womwe unayamba pamene anali ana.” Tangolingalirani, m’moyo wawo wonse kuganiza kwa amuna aŵiri ameneŵa kunali koipitsidwa ndi mzimu wotukusira, wobwezera!—Miyambo 14:29, 30.
Chifukwa china chosakulitsira mzimu wakubwezera nchakuti olakwawo—ngakhale olakwa kwambiri—angasinthe. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo panthaŵi ina ‘anavomereza kuphedwa’ kwa wophunzira Stefano ndipo ‘anapumira pa akuphunzira a Ambuye kuwopsa ndi kupha.’ Koma anasintha. Zaka zambiri pambuyo pake mtumwi Petro—amene moyo wake unali paupandu kwa Paulo m’nthaŵi zoyambirirazo—anamutcha “mbale wathu wokondedwa Paulo.” (Machitidwe 8:1; 9:1; 2 Petro 3:15) Akristu akanayesayesa kumbwezera Paulo, makamaka pamene anali kudikirira m’Damasiko, ali wakhungu. (Machitidwe 9:3-15) Chimenecho chikanakhala chophophonya changozi chotani nanga!
Chifukwa chake, Paulo anali wokhoza kupereka uphungu uwu, pa Aroma 12:20: ‘Ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse.’ Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ngati tibwezera mdani, timakhwimitsa mkhalidwe wake ndikulimbitsa udani pakati pathu. Koma ngati tichita zabwino kwa munthu amene atilakwira kapena kutivulaza, tingafeŵetse mkhalidwe wake ndikupanga yemwe anali mdaniyo kukhala bwenzi.
Kuzindikira zofooka zathu kumathandizanso m’kulaka mkwiyo womwe umatsogolera ku chikhumbo cha kubwezera. Wamasalmo anafunsa kuti: ‘Mukadasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?’ (Salmo 130:3) Tonsefe tinalakwirapo kapena kuwiyitsa ena. Kodi sitinakondwere ngati sanayeseyese kutibwezera? Pamenepo, kodi ifeyo sitiyenera kuchita modziletsa mofananamo? Yesu anapereka uphungu wakuti: ‘Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.’—Mateyu 7:12.
Zowonadi, Baibulo limanena kuti: ‘Danani nacho choipa.’ (Salmo 97:10; Amosi 5:15) Koma silimatiuza kudana ndi munthu wochita choipa. Kwenikweni, Yesu anatilamula kuti: ‘Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.’ (Mateyu 5:44) Ngati tibwezera choipa mosinthana ndi choipa, timatsanzira mzimu wa wochita choipayo. Mwambi wakale umati: “Usanene, Ndidzabwezera zoipa; Yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.” (Miyambo 20:22) Ha, ndi mkhalidwe wanzeru wotani nanga! Kuli kwabwino koposa kudzisonyeza kukhala opambana mwakupeŵa chiyeso chakutsanzira ochita zoipa.—Yohane 16:33; Aroma 12:17, 21.
Chilango—Choperekedwa ndi Yani?
Ndithudi, machitidwe ena ali oipitsitsa kuposa kukangana wamba kapena kuvulazidwa. Kodi bwanji ngati ndife mnkhole wa upandu? Mwachibadwa, timalingalira kuti mwachilungamo, payenera kuchitidwa chinachake. Koma chiyani? M’zitaganya zina sikunakhale kodabwitsa kudzichitira zinthu wekha ndi kubwezera. Koma kaŵirikaŵiri zitaganya zoterozo zimathera m’mikangano yowopsa yokhetsa mwazi. Lerolino, kaya malamulo a Mulungu kapena m’zochitika zambiri malamulo a anthu samalola anthu kubwezera okha maupandu, ndipo amachita zimenezo kaamba ka chifukwa chabwino. Chiwawa chaumwini choterocho chimangowonjezera chiwawa chochuluka.
Pamenepo, kodi mnkhole wa upandu ayenera kungokhala osachitapo kanthu ku nkhanzayo? Osati kwenikweni. Pamene ife eni kapena katundu wathu wasakazidwa, pali olamulira omwe tingatembenukireko. Mungafune kuitana apolisi. Kuntchito, pitani kwa wotsogolera wanu. Kusukulu, mungafune kuwuza mkulu wapasukulupo. Chimenecho ndicho chifukwa chimodzi chimene anthu oterowo amakhalirapo—kusungitsa chiweruzo cholungama. Baibulo limatiuza kuti maulamuliro aboma ali ‘mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.’ (Aroma 13:4) Chiweruzo cholungama chimafuna kuti boma lichite ulamuliro wake, kuletsa kuchita zoipa, ndi kulanga ochita zoipa.
Zowonadi, nthaŵi zina chiweruzo cholungama sichimafika mofulumira. Wolemba nkhani wosakondweretsedwa ndi zosangalatsa zadziko anati: “Chiweruzo cholungama chiri ngati sitima imene pafupifupi nthaŵi zonse imachedwa kufika.” Ndithudi, nthaŵi zina sitimayo simafika konse. Ochita zosalungama angakhale amphamvu kwakuti olamulira amalephera kuwaletsa. Komabe, njira yanzeru ndiyo kudziletsa. Baibulo limati: ‘Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.’—Miyambo 29:11.
Kubwezera—Kochitidwa ndi Yani?
Chotero kudziletsa kuti tisabwezere kudzatibweretsera mapindu, ndipo tingadikirire mwabata, tikudziŵa kuti ngati chiweruzo cholungama chiyenera kuperekedwa, Mulungu adzachita tero panthaŵi yake yoyenera. Yehova amadziŵa kuti kuchita zoipa kosalamuliridwa kumatsogolera ku kusakondweretsedwa. (Mlaliki 8:11) Iye sadzalola anthu oipitsitsa kutsendereza anthu kosatha. Chimenecho ndicho chifukwa chake mtumwi Paulo anatipatsa uphungu wakuti: ‘Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW].’ (Aroma 12:19) Ndithudi, Baibulo limalankhula za tsiku lakubwezera la Mlengi. Kodi tsiku lakubwezera limeneli lidzakhala lotani? Ndipo kodi ndani amene adzakhala chandamale cha kubwezera kwa Mulungu? Tidzakambitsirana zimenezi m’nkhani yotsatira.
[Bokosi patsamba 4]
Kuti mulamulire malingaliro akubwezera, kumbukirani kuti
□ Mulungu amalingalira za chiweruzo cholungama
□ kusunga mkhalidwe wamaganizo wolipsira kuli kovulaza
□ kaŵirikaŵiri kukhala wokoma mtima kumachepetsa mavuto ndi ena
□ zolakwa zathu zambiri zimanyalanyazidwa
□ ochimwawo angasinthe
□ timalaka dziko mwakupeŵa njira zake