Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 11/1 tsamba 25-29
  • ‘Yehova Ndiye Mulungu Wanga, Amene Ndimkhulupirira’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Yehova Ndiye Mulungu Wanga, Amene Ndimkhulupirira’
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Changu Chopereka Chitsanzo cha Makolo Anga
  • Uphungu Wanzeru wa Atate
  • Uthenga Wochokera Kumwamba!
  • Kuyamikira Mwaŵi Uliwonse Wautumiki
  • Kukhalabe Wokangalika m’Nthaŵi ya Nkhondo
  • Kucheza Kokhala ndi Zotulukapo Zosayembekezeredwa
  • Kupirira Mosasamala Kanthu za Zovuta
  • Mbale Knorr Abweranso
  • Zodabwitsa Zina Zatsopano
  • Kuyang’ana m’Mbuyo
  • Moyo Umene Sindinadandaulepo Nawo
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Madalitso Amene Ndapeza mu Utumiki wa Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Moyo Wanga m’Gulu Lotsogozedwa ndi Mzimu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 11/1 tsamba 25-29

‘Yehova Ndiye Mulungu Wanga, Amene Ndimkhulupirira’

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI WILLI DIEHL

“Kodi nchifukwa ninji ukufuna kupita ku Beteli?” Ili linali funso la bambo ŵanga m’ngululu ya 1931 pamene ndinawauza za chikhumbo changa chakuyamba utumiki wa pa Beteli. Makolo anga, omwe ankakhala ku Saarland, anakhala m’chowonadi kwa pafupifupi zaka khumi, ndipo anakhazikitsira anyamata atatufe chitsanzo chabwino. Chowonadi chinali njira ya moyo wawo wonse, ndipo ndinafuna kuchipanga kukhalanso njira ya moyo wanga wonse.

KOMA kodi makolo anga anaphunzira bwanji ponena za Yehova ndi chifuniro chake chopatulika? Pokhala osakhutiritsidwa ndi chipembedzo cholinganizidwa, iwo anafunafuna chowonadi kwanthaŵi yaitali. Iwo anayesa matchalitchi ndi mipatuko yosiyanasiyana, namapeza kuti zonse sizinali zowona.

Tsiku lina handibilu yolengeza nkhani ya zithunzithunzi ndi kanema yonena za chifuno cha Mulungu yotchedwa “Photo-Drama of Creation” inasiyidwa pakhomo pathu. Atate anafunikira kupita kuntchito pamene “Photo-Drama” inayenera kusonyezedwa, koma anawalimbikitsa Amayi kupita. Iwo anati: “Mwinamwake kungakhale chinachake chopindulitsa.” Pambuyo poiwona madzulo amenewo, Amayi anali otenthedwa maganizo. Iwo anati: “Ndachipeza chowonadi pomalizira pake! Mubwere m’mawa madzulo mudzadziwonere nokha. Ndichowonadi chimene takhala tikuchifunafuna kwa nthaŵi yaitali.” M’menemo munali mu 1921.

Monga Akristu odzozedwa ndi mzimu, makolo anga anakhala okhulupirika kufikira pamene anamwalira, Atate anamwalira mu 1944, pambuyo pakuponyedwa m’ndende ndi Anazi kwa nthaŵi zingapo, ndipo Amayi anamwalira mu 1970. Nawonso anakhala nthaŵi yaitali m’ndende pansi pa ulamuliro wa Nazi.

Changu Chopereka Chitsanzo cha Makolo Anga

Asanamwalire, makolo anga anali okangalika kwambiri muutumiki wakumunda. Amayi anali achangu kwenikweni m’kugaŵira zigamulo za pamsonkhano zotulutsidwa kuyambira 1922 mpaka 1928. Trakiti ya Ecclesiastics Indicted, yokhala ndi chigamulo chotengedwa mu 1924 inasuliza mwamphamvu atsogoleri achipembedzo. Kunafunikira kulimba mtima kuti igaŵiridwe. Ofalitsa anauka 4 koloko m’maŵa, kuika matrakitiwo pansi pa zitseko. Ngakhale kuti ndinali ndi zaka 12 zokha, makolo anga anandilola kukhala ndi phande. Kaŵirikaŵiri tinayamba 5 koloko m’maŵa, kutchova njinga kwa maola atatu kufika ku anayi kupita kugawo lakutali. Tinabisa njingazo m’thengo, ndipo ndinali kuzilonda pamene enawo anali kugwira ntchito m’mudzimo. Masana tinabwerera kunyumba panjingazo, ndipo madzulo tinayenda pansi kwa ola limodzi kupita kumsonkhano.

Pambuyo pake, winawake wocheperako anasiyidwa kulonda njingazo, ndipo ine ndinapita limodzi ndi ofalitsawo. Koma palibe aliyense analingalira zondiphunzitsa. Anangondiuza khwalala logwiriramo ntchito! Mwamantha ndinapita kunyumba yoyamba, ndikumayembekeza kuti pasakhale aliyense panyumba. Mwatsoka, mwamuna anatsegula chitseko. Ndinasoŵa mawu. Nditapapasa, ndinaloza ku bukhu lomwe linali m’chola changa. Iye anafunsa kuti: “Kodi ndi la Judge Rutherford?” Ndinayankha mododoma. Iye anatinso: “Kodi ndilatsopano, lomwe ndiribe?” “Inde, ndilatsopano,” ndinatsimikizira motero. “Pamenepo ndiyenera kulitenga. Kodi ndilandalama zingati?” Ichi chinandilimbikitsa kupitiriza.

Mu 1924 akuluakulu anali kulankhula kaŵirikaŵiri za 1925. Nthaŵi ina tinachezera banja la Ophunzira Baibulo, ndipo ndinamva mbale wina akufunsa kuti: “Ngati Ambuye atitenga kunka nawo, kodi nchiyani chimene chidzachitikira ana athu?” Amayi, akumayankha motsimikiza mwanthaŵi zonse, anati: “Ambuye adzadziŵa mowasamalirira.” Nkhaniyo inandisangalatsa. Kodi zinali kutanthauzanji? Chaka cha 1925 chinafika ndikutha, ndipo palibe chimene chinachitika. Komabe, makolo anga sanataye changu chawo.

Uphungu Wanzeru wa Atate

Pomalizira pake, mu 1931, ndinawauza atate zimene ndinafuna kuchita m’moyo. “Kodi nchifukwa ninji ukufuna kupita ku Beteli?” atate anafunsa motero pondiyankha. “Chifukwa chakuti ndikufuna kutumikira Yehova,” ndinayankha motero. Iwo anapitiriza kuti: “Bwanji ngati waitanidwa ku Beteli, kodi ukudziŵa kuti abale kumeneko sali angelo? Iwo ali opanda ungwiro ndipo amapanga zophophonya. Ndikudera nkhaŵa kuti ichi chingakupangitse kuthaŵa ndikutaya chikhulupiriro chako. Uzilingalirenso mosamalitsa.”

Ndinadabwa kumva zoterozo, koma pambuyo posanthula nkhaniyo kwa masiku angapo, ndinabwereza chikhumbo changa chakufunsira kaamba ka Beteli. Iwo anati: “Tandiuzanso chifukwa chimene ukufuna kupitira kumeneko.” Ndinabwereza kuti: “Chifukwa ndikufuna kutumikira Yehova.” “Mwananga, usadzaiwale konse chimenecho. Ngati waitanidwa, kumbukira chifukwa chimene ukupitira. Ngati uwona chinachake cholakwika, osadera nacho nkhaŵa mopambanitsa. Ngakhale ngati wachitiridwa moipa, osathaŵa. Osaiwala konse chifukwa chimene uliri pa Beteli​—chifukwa chakuti ukufuna kutumikira Yehova! Udzingochita ntchito yako ndi kukhulupirira mwa iye.”

Chotero masana a pa November 17, 1931, ndinafika pa Beteli m’Bern, Switzerland. Ndinali kukhala m’chipinda chimodzi ndi ena atatu ndipo ndinali kugwira ntchito m’chipinda chosindikizira, ndikuphunzira kuyendetsa makina aang’ono osindikizira ogwiritsira ntchito manja. Chinthu choyambirira chimene ndinagaŵiridwa kusindikiza inali Nsanja ya Olonda m’chinenero cha ku Romania.

Uthenga Wochokera Kumwamba!

Mu 1933 Sosaite inafalitsa kabukhu kakuti The Crisis, kokhala ndi nkhani zitatu zapawailesi zimene Mbale Rutherford anapereka mu United States. Mbale Harbeck, mtumiki wa nthambi, anadziŵitsa banja la Beteli pachakudya chakufisula m’maŵa wina kuti kabukhuko kanayenera kugaŵiridwa m’njira yapadera. Timapepala tolengezera tidzaponyedwa kuchokera m’ndege yaing’ono yobwerekedwa yomwe idzidzauluka pamwamba pa Bern, pamene ofalitsa adzaima m’makwalala kugaŵira kabukhuko kwa anthu. “Kodi ndani wa abale achicheperenu amene ali wokonzekera kupita m’mwamba pandege?” iye anafunsa motero. “Bweretsani maina anu mofulumira.” Ndinatero, ndipo pambuyo pake Mbale Harbeck analengeza kuti ndinasankhidwa.

Patsiku lalikululo, tinapita ku bwalo landege ndi makatoni a mapepalawo. Ndinakhala kumbuyo kwa woulutsa ndege ndipo ndinaunjika mapepalawo pampando wapafupi nane. Malangizo anga achindunji anali akuti: Ukulunge mahandibiluwo m’mipukutu ya zana limodzi uliwonse, ndipo uponyere pazenera mpukutu uliwonse ndi mphamvu zonse kumbali imodzi. Kusasamala kungachititse mapepalawo kugwidwa kumchira kwa ndegeyo, ndipo kungapangitse mavuto. Koma zonse zinayenda bwino. Pambuyo pake abale ananena kuti zinali zosangalatsa kuwona ‘uthenga wochokera kumwamba.’ Unali ndi chiyambukiro chomwe chinafunidwa, ndipo timabukhu tambiri tinagaŵiridwa, ngakhale kuti anthu ena anatumiza foni kudandaula kuti mabedi awo amaluŵa anakutidwa ndi mapepalawo.

Kuyamikira Mwaŵi Uliwonse Wautumiki

Ndinathokoza Yehova tsiku lirilonse chifukwa cha chimwemwe ndi chikhutiro cha utumiki wa Beteli. Mumpingo, ndinagaŵiridwa kutsegula Nyumba ya Ufumu, kukonza mipando mwadongosolo, ndikuika chikho cha madzi ozizira pa choikapo zinthu cha wokamba nkhani. Ndinalingalira zimenezi kukhala ulemu waukulu.

Pa Beteli, pomalizira pake ndinagwira ntchito pa makina aakulu osindikizira ogwiritsiridwa ntchito kusindikizira The Golden Age (tsopano Galamukani!) m’Chipolish. Mu 1934 tinayamba kugwiritsira ntchito makina oseŵerera uthenga wojambulidwa, ndipo ndinathandiza kuwapanga. Ndinapeza chisangalalo chachikulu kupita kunyumba ndi nyumba ndi nkhani Zabaibulo zojambulidwa. Eninyumba ambiri anali kuchita kaso ndi kachiŵiya kakang’onoka, ndipo kaŵirikaŵiri banja lonse linali kusonkhana kudzamvetsera, namachoka mmodzi mmodzi. Pamene banja lonse linachoka, ndinangopita kunyumba yotsatira.

Kukhalabe Wokangalika m’Nthaŵi ya Nkhondo

Pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya I, mudzi wanga wa Saarland unapatulidwa ku Jeremani ndipo unalamulidwa pansi pa zigwirizano za Mitundu Yogwirizana. Chotero, Saarland inapereka zikalata zakezake zachizindikiritso. Mu 1935 munachitika msonkhano wogamula kuti kaya nzika zake zinafuna kugwirizananso ndi Jeremani. Ndinatenga mwaŵiwo kuchezera banja langa, podziŵa kuti sindidzakhala wokhoza kuchita zimenezo pamene Saarland ikhala pansi pa ulamuliro wa Nazi. Ndipo zowonadi, kwa zaka zambiri pambuyo pake, sindinamve kalikonse kuchokera kwa makolo kapena abale anga.

Ngakhale kuti sanaloŵetsedwe mwachindunji m’Nkhondo Yadziko ya II, Switzerland anakhala wopatuka kotheratu pamene Jeremani analoŵerera maiko oyandikana nawo limodzi ndi limodzi. Tinkasindikiza mabuku a Yuropu yonse kupatulapo Jeremani, koma tsopano panalibe mabuku omwe akanatumizidwa. Mbale Zürcher, yemwe panthaŵiyo anali mtumiki wanthambi, anatiuza kuti panalibiretu ndalama zomwe zinatsala, ndipo anatiuza kupeza ntchito kunja kwa Beteli kufikira zinthu zitakhala bwino. Komabe, ndinaloledwa kukhala, popeza kuti panali zinthu zina zofunikira kusindikizidwa kaamba ka ofalitsa pafupifupi chikwi chimodzi a kumaloko.

Banja la Beteli silidzaiwala konse July 5, 1940. Titangomaliza chakudya chamasana chigalimoto cha asirikali chinafika. Asirikali anadumpha naloŵa m’Beteli. Tinalamulidwa kuima chiriri, ndipo aliyense wa ife analondedwa ndi msirikali wokhala ndi chida. Tinapititsidwa m’chipinda chodyera pamene nyumba yonseyo inafufuzidwa. Olamulira anatilingalira kuti tinali kuuza ena kukana utumiki wankhondo, koma analephera kupeza umboni uliwonse.

Mkati mwa zaka zankhondozo, ndinali mtumiki wampingo ponse paŵiri ku Thun ndi Frutigen. Izi zinatanthauza kuti ndandanda yanga ya kothera kwa mlungu inali yodzaza kwenikweni. Loŵeruka lirilonse, mwamsanga pambuyo pa chakudya chamasana, ndinatchova njinga yanga kwa mtunda wa makilomita 50 kupita ku Frutigen, kumene ndinachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda madzulo. Sande m’maŵa ndinatsagana ndi ofalitsa muutumiki wakumunda. Ndiyeno, masana ndinanyamuka, kupita ku Interlaken kukachititsa Phunziro Labukhu Lampingo ndipo pambuyo pake kuchititsa phunziro Labaibulo ndi banja lina ku Spiez. Pomaliza tsikulo, ndinachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ku Thun.

Usiku, nditamaliza ntchito zanga zonse, ndinaimba ndi kuliza mluzu pobwerera ku Bern, ndiri wokhutira kwabasi. Magalimoto anali ochepa ndipo sindinakumane ndi ambiri. Mapiri okutidwa ndi mdima chifukwa cha lamulo loletsa kuyatsa magetsi m’nthaŵi yankhondo, anali abata ndi osasokonezedwa, akumawala mwa apa ndi apo ndi kuunika kwa mwezi. Ha, masiku a kothera kwa mlungu oterowo analemeretsa motani nanga moyo wanga ndi kulimbitsa nyonga yanga!

Kucheza Kokhala ndi Zotulukapo Zosayembekezeredwa

M’chilimwe cha 1945, Mbale Knorr anatichezera. Tsiku lina analoŵa m’fakitale pamene ndinaimirira pamakina osindikizira. Iye anaitana nati: “Tsika pansi! Kodi ungakonde kupezekapo pa Sukulu ya Gileadi?” Ndinachita kakasi. Ndinayankha kuti: “Ngati mukuganiza kuti ndine wokhoza kutero, ndidzakondwera.” Ziitano za Mbale Fred Borys, Mlongo Alice Berner, ndi ine zinafika m’ngululu ya 1946. Koma popeza kuti ndinabadwira mu Saarland, ndinali wopanda boma ndipo chotero ndinafunikira kupempha chilolezo chapadera ku Washington, D.C., U.S.A.

Pamene kuli kwakuti enawo ananyamuka panthaŵi yake, ndinafunikira kudikirira yankho la pempho langa. Pamene sukulu inayamba pa September 4, ndinali ndidakali ku Switzerland, ndikumataya chiyembekezo pang’onopang’ono. Ndiyeno Kazembe wa United States anatumiza foni, kundidziŵitsa kuti chilolezo changa chinafika. Panthaŵi yomweyo ndinayesa kupanga makonzedwe aulendo ndipo pomalizira pake ndinapeza malo m’chombo chankhondo chochokera ku Marseilles kumka ku New York. Chinali chokumana nacho chotani nanga! Chombo cha Athos II chinali chodzaza. Ndinapatsidwa mpando m’chipinda chopanda kanthu. Patsiku lachiŵiri tiri panyanja, kuphulika kwa m’chipinda cha injini kunaimika chombocho. Okweramo ndi antchito omwe anachita mantha, kuwopa kuti mwina tingamire. Ichi chinandipatsa mwaŵi wabwino koposa wakuchitira umboni za chiyembekezo cha chiukiriro.

Kukonza chombocho kunatenga masiku aŵiri, pambuyo pake tinapitiriza ulendowo paliŵiro lochepa. Tinafika ku New York masiku 18 pambuyo pake, ndipo tinakakamizika kukhala m’chombocho chifukwa cha sitalaka ya anthu ogwira ntchito padoko. Pambuyo pakukambitsirana, pomalizira pake tinatsika chombocho. Ndinatumiza telegraph ku Sosaite kuidziŵitsa za mkhalidwewo, ndipo pamene ndinamaliza ndi owona za kutuluka ndi kuloŵa m’dziko, munthu wina anafunsa kuti: “Kodi ndinu Bambo Diehl?” Anali mmodzi wa othandiza a Mbale Knorr, ndipo anandikwezeka sitima yausiku kupita ku Ithaca, pafupi ndi Sukulu ya Gileadi, kumene ndinafika itangopitirira pang’ono 8 koloko m’maŵa wotsatira. Ndinali wosangalala chotani nanga pomalizira pake, kukhala wokhoza kupezekapo pa kalasi la mitunduyonse loyambirira la Gileadi!

Kupirira Mosasamala Kanthu za Zovuta

Kumaliza maphunziro kwa kalasi la Gileadi lachisanu ndi chitatu kunali pa February 9, 1947, ndipo aliyense mtima unali m’malere. Kodi tikatumizidwa kuti? Kwa ine, “zingwe zoyesera” zinagwera pa fakitale yosindikizira ya Sosaite yotsegulidwa chatsopano ku Wiesbaden, Jeremani. (Salmo 16:6, NW) Ndinabwerera ku Bern kukapempha zilolezo zoyenerera, koma magulu ankhondo a United States omwe anali ku Jeremani anali kulola anthu okha omwe anakhalako kale nkhondo isanayambe kuloŵa m’dzikolo. Popeza kuti sindinakhaleko, ndinafunikira gawo latsopano kuchokera ku malikulu ku Brooklyn. Linakhala ntchito yadera m’Switzerland, yomwe ndinailandira ndi chidaliro chotheratu mwa Yehova. Koma pamene ndinkadikirira gawo limeneli, tsiku lina ndinapemphedwa kusonyeza Beteli kwa alongo atatu odzacheza. Mmodzi wa iwo anali mpainiya wotchedwa Marthe Mehl.

Mu May 1949, ndinadziŵitsa malikulu a ku Bern kuti ndinakonzekera zakukwatira Marthe ndikuti tikukhumba kukhalabe muutumiki wanthaŵi zonse. Kodi yankho linali lotani? Kulibe mwaŵi wina uliwonse kusiyapo kokha upainiya wokhazikika. Tinauyamba mu Biel, pambuyo pa ukwati wathu mu June 1949. Sindinaloledwe kupereka nkhani, ndiponso sitikanafuna malo ogona a nthumwi zobwera ku msonkhano, ngakhale kuti tinavomerezedwa ndi woyang’anira dera wathu kaamba ka mwaŵi umenewu. Ambiri analeka kutipatsa moni, akumatichitira mofanana ndi anthu ochotsedwa, ngakhale kuti tinali apainiya.

Komabe, tinadziŵa kuti kukwatira sikunali kopanda malemba, chotero tinathaŵira m’pemphero ndikuika chidaliro chathu mwa Yehova. Kwenikweni, kachitidwe kameneka sikanasonyeze lingaliro la Sosaite. Kunali kungogwiritsira molakwa malangizo a gulu.

Mbale Knorr Abweranso

Mu 1951, Mbale Knorr anabweranso kudzacheza ku Switzerland. Pambuyo pakupereka nkhani, ndinauzidwa kuti anafuna kulankhula nane. Ngakhale kuti ndinachita mantha, ndinali wachimwemwe kuti anakondwera kundiwona. Anafunsa ngati tingakhale ofunitsitsa kulandira gawo pa nyumba ya amishonale yolingaliridwa m’Geneva. Mwachibadwa, tinasangalala, ngakhale kuti kuchoka ku Biel sikukachitidwa popanda zodandaula. Tsiku lotsatira tinalandira pempho lina kuchokera kwa Mbale Knorr. Kodi tikakhala ofunitsitsa kuyambanso ntchito yadera, popeza kuti inafunikira chisamaliro chowonjezereka m’Switzerland? Tinavomera nthaŵi yomweyo. Nthaŵi zonse mkhalidwe wanga wakhala wakulandira gawo lirilonse loperekedwa.

Ntchito yathu yadera kum’maŵa kwa Switzerland inadalitsidwa mokulira. Tinapita kumipingo pasitima, tikumanyamula katundu wathu yense m’masutikesi aŵiri. Kaŵirikaŵiri abale anatichingamira pasitesheni ndi njinga, popeza kuti oŵerengeka okha ndiwo anali ndi magalimoto nthaŵi imeneyo. Zaka zingapo pambuyo pake mbale wina anatipatsa galimoto yoti tidziyendera, imene inapeputsako utumiki wathu.

Zodabwitsa Zina Zatsopano

Chinali chosangalatsa chotani nanga pamene mu 1964 mkazi wanga ndi ine tinaitanidwa ku kalasi la 40 la Gileadi, kalasi lamaphunziro osamalitsa lomalizira, kosi ya miyezi khumi, yomwe tsopano inafupikitsidwa kukhala miyezi isanu ndi itatu. Marthe anafunikira kuphunzira Chingelezi mofulumira, koma anakhoza kuchita zimenezi modabwitsa. Maganizo anali m’malere ponena za kumene tidzatumizidwa. Kulingalira kwanga kunali kwakuti: ‘Sindisamala kumene ndagaŵiridwa, malinga ngati sintchito yokhala pa desiki!’

Koma zimenezo ndizo zimene zinachitika! Patsiku lakumaliza maphunziro, September 13, 1965, ndinaikidwa monga mtumiki wanthambi ya Switzerland. Beteli inayenera kukhala chokumana nacho chatsopano kwa Marthe. Kwa ine, kunatanthauza kubwerera ku “Nyumba ya Mulungu,” osati kosindikizira, kumene ndinatumikira kuyambira 1931 mpaka 1946, koma mu ofesi. Ndinafunikira kuphunzira zinthu zambiri zatsopano, koma ndi chithandizo cha Yehova ndinali wokhoza kutero.

Kuyang’ana m’Mbuyo

M’zaka 60 za utumiki wanthaŵi zonse, ndinadalira kotheratu mwa Yehova, monga momwe atate anandiuzira kuti ndiyenera kutero. Ndipo Yehova watsanula madalitso ochuluka. Marthe wakhala magwero a chilimbikitso chachikulu m’nthaŵi zogwiritsidwa mwala kapena pamene mathayo anawoneka kukhala aakulu kwambiri kwa ine, ndithudi ali bwenzi lokhala ndi chidaliro chotheratu mwa Yehova.

Atamandidwe Yehova chifukwa cha mwaŵi wautumiki wochuluka umene ndasangalala nawo! Ndikutumikirabe monga wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi mu Thun, ndipo nthaŵi zambiri ndinayenda monga woyang’anira woyendera nthambi. Mosasamala kanthu za zimene ndinapemphedwa kuchita, nthaŵi zonse ndinayang’ana kwa Yehova kaamba ka chitsogozo. Mosasamala kanthu za zolakwa ndi zophophonya zanga zambiri, ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova wandikhululukira kupyolera mwa Kristu. Ndipitirizetu kukhala wokondweretsa kwa iye. Ndipo iye apitirizetu kutsogoza mapazi anga, pamene ndikuyang’ana mosalekeza kwa iye monga “Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.”​—Salmo 91:2.

[Chithunzi patsamba 27]

Mbale Diehl kuchiyambi kwa ntchito yake ya Beteli

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena