Moyo Umene Sindinadandaulepo Nawo
YOSIMBIDWA NDI PAUL OBRIST
Mu 1912, ndili ndi zaka zisanu nchimodzi, Amayi anamwalira akubala mwana wawo wachisanu. Patapita ngati zaka ziŵiri, wantchito wosamalira panyumba, Berta Weibel, anayamba kusamalira banja lathu. Pamene Bambo anamkwatira chaka chotsatira, anafe tinasangalala kuti takhalanso ndi mayi.
TINKAKHALA ku Brugg, tauni yaing’ono m’chigawo cholankhula Chijeremani ku Switzerland. Berta analidi munthu wachikristu, ndipo ndimamkonda kwambiri. Anali atayamba kuŵerenga mabuku a Ophunzira Baibulo (Mboni za Yehova) mu 1908, ndipo amauzako ena zomwe anali kuphunzira.
Mu 1915, pasanapite nthaŵi yaikulu Berta ndi Bambo atakwatirana, ndinapita naye limodzi kumene amaonetsa kanema ya “Photo-Drama of Creation.” Silaidi ndi filimu imeneyi ya International Association of Earnest Bible Students inandikondweretsa kwambiri. Ena omwe anaiona nawonso inawakondweretsa kwambiri. Nyumbayo mu Brugg inadzaza mwakuti apolisi anatseka zitseko ndi kubweza onse obwera mochedwa. Kenaka ambiri anayesayesa kuloŵera pa zenera lotseguka mwakukwera ndi makwerero, ndipo ena oŵerengeka analowadi.
Chitsanzo Chabwino cha Amayi
Nkhondo Yadziko I inali mkati mu Ulaya, ndipo anthu anali ndi mantha ponena za mtsogolo. Motero, kulalikira kukhomo ndi khomo kuwauza uthenga wotonthoza wa Ufumu wa Mulungu, monga momwe Amayi ankachitira, pamafunikira kulimba mtima. Nthaŵi zina amanditenga, zimene ndimasangalala nazo kwambiri. Mu 1918, Amayi anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova Mulungu mu ubatizo wa m’madzi.
Atate samanena chilichonse pa kulambira kwa Amayi mpaka ubatizo wawo, koma atabatizidwa anayamba kuwatsutsa. Tsiku lina analanda mabuku awo onena za m’Baibulo ndi kuwaponya m’chitofu. Amayi anangotha kulanditsako Baibulo lawo lokha pa moto. Koma chimene anachita pambuyo pake chinali chodabwitsa. Anapita nawakumbatira Atate. Sanawasungire chakukhosi.
Atadabwa kwambiri, Atate anatsitsa mtima pansi. Komabe, nthaŵi ndi nthaŵi, mosayembekezereka amayambiranso kutsutsa, ndipo timakhalira kupirira mkwiyo wawo.
Ntchito ndi Kupita Patsogolo Mwauzimu
Mu 1924, nditagwira nawo ntchito kwa zaka zitatu monga wometa tsitsi, ndinachoka panyumba ndi kukapeza ntchito kudera lolankhula Chifrenchi mu Switzerland. Unakhala mwaŵi woti ndidziŵe bwino chilankhulo cha Chifrenchi. Ngakhale kuti kusamukako kunasokoneza kupita kwanga patsogolo mwauzimu mwanjira ina, kukonda kwanga choonadi cha Baibulo sikunathe. Nditabwerera kwathu zaka zisanu nchimodzi pambuyo pake, ndinayamba kumasonkhana nawo mumpingo wachikristu wa ku Brugg.
Posapita nthaŵi ndinasamukira ku Rheinfelden, tauni yaing’ono yokhala pa mtunda wokwana makilomita 40. Kumeneko ndimagwira ntchito mu shopu yokonza tsitsi ya mlongo wanga ndipo ndinapitiriza kupita patsogolo mwauzimu mwakumasonkhana ndi kagulu kochepa ka Ophunzira Baibulo. Tsiku lina potsiriza phunziro lathu la Baibulo la pakati pa mlungu, Mbale Soder, mkulu woyang’anira, anafunsa kuti: “Ndani wakonzeka kupita mu utumiki wakumunda pa Lamlungu?” Ndinadzipereka, ndikumaganiza kuti ndidzapita ndi wina yemwe adzandisonyeza momwe ndingachitire.
Lamlungu litafika ndipo titafika ku gawo lathu, Mbale Soder anati, “A Obrist adzalalikira dera ilo.” Ngakhale kuti mtima wanga unagunda momwe sunachitirepo, ndinayamba kukumana ndi anthu m’nyumba zawo ndikulankhula nawo za Ufumu wa Mulungu. (Machitidwe 20:20) Kuyambira nthaŵi imeneyi, sindinadodomepo kuchita ntchito yolalikira imene Yesu anati iyenera kuchitika mapeto a dongosolo ili la zinthu asanafike. (Mateyu 24:14) Pa March 4, 1934, ndili ndi zaka 28, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi.
Zaka ziŵiri pambuyo pake ndinapeza ntchito monga wokonza tsitsi ku Lugano, mzinda womwe uli m’dera lolankhula Chitaliyana m’Switzerland. Ngakhale kuti sindimachidziŵa bwino Chitaliyana ndinayamba kulalikira uthenga wabwino kumeneko nthaŵi yomweyo. Ngakhale zinali tero, Lamlungu loyamba lomwelo ndinagaŵira timabuku 20 timene ndinatenga. Patapita nthaŵi, ndinakwanitsa kusonkhanitsa anthu angapo omwe amasonyeza chidwi ndi kupanga gulu kuti tiziphunzira Nsanja ya Olonda. M’kupita kwa nthaŵi ena mwa ameneŵa anabatizidwa, ndipo mu February 1937 tinapanga mpingo wa Mboni za Yehova mu Lugano.
Patatha miyezi iŵiri, mu April 1937, ndinalandira kalata imene inasintha moyo wanga mwadzidzidzi. Kunali kuitanidwa kukatumikira pa Beteli, monga momwe maofesi a nthambi a Mboni za Yehova m’dziko lililonse amatchulidwira. Ndinalola kukatumikira nthaŵi yomweyo—ganizo limene silinandimvetsepo chisoni. Motero ndinayamba ntchito ya utumiki wa nthaŵi zonse yomwe ndaigwira kwa zaka 60.
Utumiki pa Beteli mu Nthaŵi za Mavuto
Panthaŵi imeneyo Beteli ya ku Switzerland inali mumzinda wa Bern, likulu la Switzerland. Kumeneko timasindikiza mabuku, timabuku, ndi magazini m’zilankhulo 14, ndipo zimenezi zimatumizidwa m’maiko onse a ku Ulaya. Nthaŵi zina, ndinali kutengera mabuku osindikizidwawo pa wilibala kupita nawo ku siteshoni ya treni, chifukwa masiku amenewo kaŵirikaŵiri sitimakhala ndi galimoto. Ntchito yanga yoyamba ku Beteli inali ya ku Dipatimenti ya Kompozishoni, kumene timasonkhanitsa zitsulo za lead zomwe timagwiritsira ntchito posindikiza mabuku. Posapita nthaŵi ndinayamba kutumikira m’chipinda cholandirira alendo, ndiponso ndimatumikira monga wometa tsitsi wa banja la Beteli.
Mu September 1939, Nkhondo Yadziko II inaulika, ndipo mantha anagwira aliyense mu Ulaya chifukwa cha mmene Anazi anali kuphera anthu. Dziko la Switzerland linali labata pakati pa maiko omwe anali kumenyana. Poyamba tinapitiriza ntchito yathu yachikristu popanda kudodometsedwa. Kenaka, pa July 5, 1940, 2 koloko masana ndili pa desiki langa molandirira alendo, panafika munthu ndi msilikali yemwe ananyamula mfuti yokhala ndi mpeni kutsogolo.
“Zürcher ali kuti?” anazaza motero munthuyo. Panthaŵiyo Franz Zürcher ndiye anali woyang’anira nthambi pantchito yathu yolalikira mu Switzerland.
“Kodi ndimuuze kuti ndani akumuitana?” Ndinafunsa. Mwamsanga anandigwira nkundikoka kundikweza pa masitepesi uku akunena kuti ndiwasonyeze ku ofesi ya Zürcher.
Banja lonse la Beteli—pafupifupi 40 pa nthaŵiyo—linalamulidwa kusonkhana m’chipinda chodyera. Kunja kwa holoyo kunali asilikali onyamula mfuti za machine gun zinayi kuopseza kuti aliyense asathawe. Mkatimo, asilikali okwana 50 anayamba kusecha m’nyumbayo. Mosemphana ndi zimene amaganiza, sanapeze umboni uliwonse wakuti Mboni za Yehova zimalimbikitsa anthu kukana kuloŵa usilikali. Komabe, mabuku ambiri analandidwa ndipo anatengedwa pamagalimoto asanu a asilikali.
Titakana kuti antchito a boma ndiwo azivomereza kapena kukana zomwe tikufuna kulemba mu Nsanja ya Olonda, kufalitsidwa kwake kunaima mu Switzerland. Izi zinapangitsa kuti pasafunikirenso anthu ambiri ogwira ntchito pa Beteli, ndipo achinyamata analimbikitsidwa kuchoka ndi kukakhala apainiya, momwe Mboni za Yehova zomwe zimachita ntchito ya ulaliki wa nthaŵi zonse zimatchedwera.
Kuchita Upainiya m’Nthaŵi ya Nkhondo
Mu July 1940, ndinabwerera kudera lolankhula Chitaliyana pafupi ndi Lugano mu Switzerland, kumene ndimakhala ndisanabwere pa Beteli. Dera limeneli lodzala ndi Akatolika, ndiponso kumene panthaŵiyo Chifasizimu chinali chitatenga malo, ndilo linali dera langa lochitirako upainiya.
Pafupifupi masiku onse apolisi ankandiimitsa ndi kundiuza kuti ndisiye ntchito yanga yolalikira. Tsiku lina pamene ndinali kulankhula ndi mkazi wina pachipata cha munda, munthu wina anandigwira kumbuyo, nandikokera ku galimoto ya asilikali olonda, ndi kupita nane ku Lugano. Kumeneko anandipereka kwa apolisi. Atandifunsa, ndinawauza kuti Yehova Mulungu anatilamulira kuti tilalikire.
“Pansi pano, timalamulira ndife,” anayankha tero ofesalayo modzikuza. “Mulungu akhoza kulamulira kumwamba!”
Panthaŵi yankhondo, kunali kofunika kwambiri kumvera uphungu wa Yesu wakuti “khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.” (Mateyu 10:16) Motero, ndimabisa mabuku anga ambiri m’matumba a mkati mwa shati yanga. Ndipo kuti nditsimikizire kuti sindinataye kalikonse, ndimavala kabudula wotakata kumwambaku koma wothina m’maondomu.
Patapita nthaŵi, ndinalandira malangizo kuti ndipite ku chigwa cha Engadine, kumene ndinakapitiriza kuzembanazembana ndi apolisi. Ichi ndi chigwa chokongola kummaŵa kwa mapiri a Swiss Alps, kumene nthaŵi yozizira chipale chofeŵa chimakwiririratu nthaka, choncho ananditumizira ma ski (zoyendera pa chipale chofeŵa) kuti ndizitha kuyendera deralo.
Magolovesi ofundira ngofunika pamene ukuyenda ndi ma ski m’nthaŵi yozizira. Anga anayamba kutha chifukwa chowagwiritsira ntchito kaŵirikaŵiri. Tsiku lina ndinasangalala chotani kulandira paselo mosayembekezereka pa positi momwe munali juzi ndiponso magolovesi ofundira zolukidwa pamanja! Mlongo wachikristu mumpingo wanga wapoyamba ku Bern ndiye adandilukira. Mpaka tsopano ndimati ndikakumbukira, ndimathokoza.
Mautumiki Ambiri Osangalatsa
Mu 1943, mu Switzerland munayamba kukhala bata, ndipo ndinaitanidwanso kukatumikira pa Beteli. Chifukwa cha mavuto ena mumpingo wa Chifrenchi ku Lausanne pa mtunda wa makilomita ngati 100, ndinagaŵiridwa kuti ndizipita ku mzinda umenewo kaŵirikaŵiri kukathandiza ofalitsa kuti alidziŵe bwino gulu la Mulungu.
Kenaka kwakanthaŵi ndinatumikira monga woyang’anira dera m’mipingo yonse yolankhula Chifrenchi mu Switzerland. Kumayambiriro kwa mlungu, ndimagwira ntchito pa Beteli, koma Lachisanu, Loŵeruka, ndi Lamlungu, ndimakachezera mipingo yosiyanasiyana mlungu ndi mlungu ncholinga choithandiza mwauzimu. Kuphatikiza apo, pamene mpingo wachifrenchi unapangidwa mu Bern mu 1960, ndinakhala woyang’anira wotsogoza wake. Ndinatumikira motero kufikira mu 1970, pamene Beteli inasamutsidwa kuchokera ku Bern kupita kumalo okongola kumene ili tsopano m’tauni ya Thun.
Ndinali wokondwa kupeza kagulu kochepa ka Mboni zolankhula Chitaliyana mu Thun, ndipo ndinayamba kugwira nawo ntchito limodzi. Patapita nthaŵi mpingo unapangidwa, ndipo ndinatumikira monga woyang’anira wotsogoza wake kwa zaka zochulukirapo kufikira pamene abale achinyamata anakwanitsa ziyeneretso kuti asenze udindo umenewo.
Chomwe ndachiona kukhala monga mwaŵi wapadera wosangalatsa ndi kupita ku misonkhano yamitundu yonse ya anthu a Yehova. Mwachitsanzo, mu 1950 kunali Msonkhano wa Chiwonjezeko cha Teocrase wosaiŵalika ku Yankee Stadium, New York. Kukacheza kumalikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York kunandipatsa chimwemwe chosatha. Ndiponso sindidzaiŵala nkhani ya Mbale Milton G. Henschel chaka chotsatira pamsonkhano wa Kulambira Koyera ku London, ku England, imene inafotokoza mawu a Yesu akuti, “Ndinena ndi inu, ngati awa akhala chete miyala idzafuula.” (Luka 19:40) Mbale Henschel anafunsa, “Kodi mukulingalira kuti miyala iyenera kulankhula?” Mpaka lero ndimamvabe m’makutu mwanga kukuwa kuti, “Ayi!” kumene kunachokera mkamwa mwa anthu zikwizikwi.
Pamene ndinapita ku Beteli kalelo mu 1937, atate, omwe anamva kuti timalandira alawansi yochepa, anandifunsa modera nkhaŵa kuti, “Mwana wanga, udzakhala bwanji utakalamba?” Ndinawayankha mogwira mawu a wamasalmo Davide kuti: “Sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” (Salmo 37:25) Kwa ine mawu ameneŵa akwaniritsidwadi.
Ndine wokondwa chotani nanga kuti zaka 80 kalelo, Berta Weibel anakwatirana ndi Atate ndi kutinso kupyolera mwa chitsanzo ndi chitsogozo chake ndinadziŵa Yehova ndi makhalidwe ake! Ngakhale kuti ena m’banjamo amamunyoza, anatumikirabe Yehova mokhulupirika kufikira imfa yake mu 1983. Sanadandaulepo chifukwa chotumikira Mulungu wake Yehova; inenso sindinadandaulepo chifukwa chokhala mbeta ndiponso kupereka moyo wanga wonse pa utumiki wa Yehova.
[Chithunzi patsamba 25]
Kugwira ntchito pa Beteli