Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 11/1 tsamba 30-31
  • Kodi Mumayamikira Gulu Lapadziko Lapansi la Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayamikira Gulu Lapadziko Lapansi la Yehova?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Peŵani Kuyang’ana Ena ndi Diso Losuliza
  • “Ogwirizana Bwino Lomwe m’Maganizo Amodzimodzi”
  • ‘Ndakhwimitsa Nkhope Yako Ngati Diamondi’
  • ‘Atumiki Anga Adzasangalala’
  • Mungapite Patsogolo Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Khalani Otetezereka m’Gulu Lolinganizidwa la Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mukuyenda Limodzi ndi Gulu la Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 11/1 tsamba 30-31

Kodi Mumayamikira Gulu Lapadziko Lapansi la Yehova?

YANG’ANANI diamondi yodulidwa bwino lomwe, yonyezimira zedi, ndipo kodi mukuwonanji? Mwala wamtengo wapatali wokongola kwabasi. Tsopano iyang’anitsitseni diamondiyo kupyolera m’maikolosikopu, ndipo kodi mukuwonanji? Mwachiwonekere imakhala yokalaukakalauka, ya ming’alu, yokhala ndi zinthu zina zokangamiramo, kapena zoipa zina.

Kodi mukaiwononga kapena kuitaya diamondiyo kokha chifukwa cha mmene ikuwonekera pamaikolosikopu? Ndithudi ayi! Tangochokanipo pamaikolosikopuyo, ndipo mudzakondabe kukongola ndi kunyezimira kodabwitsa kumene kumaipangitsa kusiyana ndi miyala ina yamtengo wapatali.

Mofanana ndi diamondi, gulu lapadziko lapansi la Yehova liri lapadera m’njira zambiri. Palibe gulu lina padziko lapansi limene limasangalala ndi unansi wathithithi ndi Mlengi. M’kalata yake kwa Akristu odzozedwa a m’zaka za zana loyamba, omwe anasangalala ndi chiyembekezo chakumwamba, mtumwi Petro anasonyeza unansi wapadera umenewu. Iye anati: ‘Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwiniwake.’ (1 Petro 2:9) Lerolino khamu lalikulu la “nkhosa zina,” lokhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi, lagwirizana ndi otsalira a ‘mtundu woyera’ umenewo m’kulambira Mulungu. (Yohane 10:16) Pamodzi magulu aŵiri ameneŵa amapanga gulu limene limaima palokha mofanana ndi mwala wamtengo wapatali wokongola ndi wonyezimira modabwitsa.

Peŵani Kuyang’ana Ena ndi Diso Losuliza

Koma tiyenera kuzindikira kuti gulu lapadziko lonse limeneli limapangidwa ndi anthu opanda ungwiro. Chotero, kodi nchiyani chimene chikachitika ngati tiliyang’ana kupyolera m’maikolosikopu yophiphiritsira? Inde, tikapeza mikhalidwe yauchimo ndi zifooko zaumunthu mwa anthu amene ali mbali yake.​—Aroma 3:23.

Mtumwi Paulo anavomereza kuti iye anali nazo zifooko zoterozo. Iye anati: ‘Pamene ndifuna chabwino, choipa chiriko.’ (Aroma 7:21) Mkristu aliyense amakhala ndi vuto lofananalo. Tonsefe timapanga zolakwa. Ndiponso, kaŵirikaŵiri ambiri amavutika chifukwa cha zolakwa za munthu winawake. Kodi tiyenera kulefulidwa kapena kukhwethemulidwa pamene tiwona zifooko ndi kupanda ungwiro kwa Akristu anzathu? Kodi zimenezo ziyenera kuzilalitsa chiyamikiro chathu cha gulu la Yehova? Ndithudi ayi! Mmalo mwake, tiyenera kuchokapo pamaikolosikopuyo, titero kunena kwake, ndi kuleka kusumika maganizo pa kupanda ungwiro kwa anthu.

Malemba amandandalitsa mikhalidwe ingapo imene ikazindikiritsa awo amene mzimu woyera umagwira ntchito pa iwo. Ina ya iyo ndi ‘chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.’ (Agalatiya 5:22, 23) Mosiyana, magulu achipembedzo, andale zadziko, ndi amalonda a dziko lino kaŵirikaŵiri amasonyeza zimene Baibulo limazitcha ntchito za thupi: ‘madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko, njiru, kuledzera, michezo, ndi zina zotere.’ (Agalatiya 5:20, 21) Chifukwa chake, mofanana ndi diamondi yonyezimira pakati pa miyala wamba, anthu a Yehova amapatulika pakati pa dziko lovunda mwauzimu.​—Mateyu 5:14-16.

“Ogwirizana Bwino Lomwe m’Maganizo Amodzimodzi”

Chinthu chapadera ponena za diamondi ndicho kapangidwe kake ka kumangika zolimba kwa ma atomu ake. Mofananamo, gulu lapadziko lapansi la Yehova limasonyeza umodzi wosayerekezereka m’chiphunzitso ndi ubale. Awo amene ali mbali ya gululo amagwiritsira ntchito chilangizo chopezeka m’Baibulo pa 1 Akorinto 1:10, (NW) pamene pamati: “Tsopano ndikupemphani, abale, kupyolera m’dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu kuti muyenera nonse kulankhula mogwirizana, ndikuti pasakhale magaŵano pakati panu, koma kuti mukakhale ogwirizana bwino lomwe m’maganizo amodzimodzi ndi mumzera umodzimodzi wa ganizo.”

Mboni za Yehova nzopatulikanso m’kupanda tsankho lafuko ndi kunyada kwautundu. Pokhala ndi ‘nzeru yochokera kumwamba,’ izo zimakhala ‘zopanda tsankhu lodzikometsera.’ (Yakobo 3:17) Tikupereka ulemerero kwa Yehova kaamba ka chimene wakwaniritsa m’zimenezi m’gulu lopangidwa ndi anthu opanda ungwiro.

Mosiyana, magazini akuti The Christian Century, ponena za chaka cha 1990, ananena kuti “dziko linawoneka kukhala logaŵikana kuposa ndi kalelonse m’magulu achipembedzo ndi m’malingaliro autundu ndi amwambo okhudza kwenikweni zikhulupiriro za chipembedzo. Kuchokera ku Indiya mpaka ku Ulaya ndi kuchokera ku Middle East mpaka ku Pacific, chipembedzo chinayanjana ndi zigwirizano za mwambo ndi zautundu​—kaŵirikaŵiri ndi zotulukapo zosakhwima za ndale zadziko.” Mwachiwonekere, awo amene amakhumba kutumikira Mulungu angatembenukire ku gulu limodzi lokha limene limasangalala ndi mzimu wa Yehova ndi dalitso.

‘Ndakhwimitsa Nkhope Yako Ngati Diamondi’

Diamondi ndichinthu cholimba koposa mwachibadwa chodziŵika kwa munthu. Baibulo limatchula kugwiritsiridwa ntchito kwa madiamondi m’kupala kapena kuzokota zinthu zolimba. (Yeremiya 17:1) Onaninso, mawu a Yehova kwa Ezekieli akuti: ‘Tawona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zawo; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yawo. Ndalimbitsa mutu wako [ngati diamondi, NW] woposa mwala wolimbitsitsa.’ (Ezekieli 3:8, 9) Yehova anapatsa Ezekieli cholinga chotsimikiza mtima cholimba ngati diamondi chimene chinamkhozetsa kunenera kwa anthu ouma khosi.​—Ezekieli 2:6.

Mofananamo lerolino, Yehova wapatsa anthu ake kulimba konga kwa diamondi poyang’anizana ndi chitsutso chachikulu. Mboni za Yehova zapirira ziletso zalamulo, chiwawa cha gulu loukira, kuphedwa kopanda lamulo, kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende kosalungama, kuzunzidwa, ngakhale kunyongedwa. Komabe, izo zasonyeza chikhulupiriro chawo kukhala chosasweka.

‘Atumiki Anga Adzasangalala’

Baibulo linalosera nthaŵi pamene anthu akakhala ndi ‘mawonekedwe achipembedzo’ koma ‘mphamvu yake akaikana.’ (2 Timoteo 3:1, 5) Nyuzipepala ina ikusimba kuti “Aprotesitanti, Aroma Katolika ndi Ayuda onse ali odera nkhaŵa ndi kuchepekera kwa anthu” m’matchalitchi ndi m’masunagoge awo. Kumbali ina, Mboni za Yehova ziri ophunzira osamalitsa a Baibulo. M’ziŵerengero zomakulakula, achichepere ndi okalamba, amuna ndi akazi, onsewo amapezeka pamisonkhano yambiri ya mlungu ndi mlungu. Kalata yopita ku nyuzipepala ponena za iwo inanena kuti “chipembedzo chawo ndicho chinthu chamtengo wapatali koposa chimene ali nacho, ndipo nkhaŵa yawo yokha ndiyo kugaŵana nacho ndi ena.”

Kaimidwe ka maganizo koteroko kamapangitsa gulu la Yehova kupatulika monga diamondi ya mtengo wapatali. Ndipo chitamando chimamka kwa Uyo amene amalimbitsa ndi kutsogolera anthu opanda ungwiro mwa mzimu wake woyera.

Mneneri Yesaya ananeneratu kuti: ‘Atero [Mfumu, NW] Ambuye Yehova, Tawonani atumiki anga adzadya, . . . tawonani, atumiki anga adzamwa, . . . tawonani, atumiki anga adzasangalala, . . . tawonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala.’​—Yesaya 65:13, 14.

Lerolino tikuwona kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu. Mulungu akusamalira anthu ake mwanjira yodabwitsa! Chifukwa chake, ngati mumayanjana nawo, musalole maganizo oipidwa aliwonse kukulandani chisangalalo chanu. Yang’anani chithunzi chonse ndipo kumbukirani kuti: Palibe gulu lina lirilonse padziko lapansi limene limasangalala ndi chisamaliro chapadera ndi chitetezo cha Mulungu. Musaleke konse kuusamalira mochititsa kaso mwaŵi wanu wakukhala mbali yake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena