‘Miliri M’malo Akuti Akuti’
MILIRI yosayerekezereka muukulu wake inali mbali yonenedweratu ya “chizindikiro cha kukhalapo kwa [Yesu Kristu] ndi cha chimaliziro cha dongosolo la zinthu.” (Mateyu 24:3, NW) Wolemba Uthenga Wabwino Luka akuwonjezera mfundo imeneyi yosatchulidwa m’zolembedwa za Mateyu ndi Marko. (Mateyu, mitu 24 ndi 25; Marko, mutu 13) Kubuka kwa miliri ndi matenda osakaza kukachitika ‘m’malo akuti akuti’ m’masiku otsiriza. (Luka 1:3; 21:11) Kodi matenda oterowo akachokera kuti?
“Asayansi amadziŵa tizirombo tamatenda tosiyanasiyana tokhala m’malo otentha—kuti ngati mphamvu zachilengedwe zitiyanja—tikhoza kusakaza miyoyo yambiri kuposa imene mwachiwonekere idzawonongedwa ndi mliri wa AIDS,” akutero magazini a Science News. “Ngakhale ngati magwero a tizirombo tamatenda angasungike osasintha, ofufuza amanena kuti, malo otentha ali kale ndi tizirombo tamatenda ‘tokwanira’ kufafaniza chigawo chachikulu cha chiŵerengero cha anthu onse Padziko.”
Chimene chimapangitsa nyengo yathu kukhala yowopsezedwa mowonjezereka ndichiŵerengero cha anthu chomakula kodetsa nkhaŵa ndi zosoŵa zazikulu za dziko lodzala ndi anthu. “Mbiri imasonyeza kuti kubuka kwa tizirombo tamatenda kowopseza moyo kaŵirikaŵiri kwatsatirapo pamene anthu asamukira kumalo osafufuzidwa kapena pamene mikhalidwe ya moyo m’tauni inyonyotsoka m’njira zimene zimaitana tizirombo tambiri tatsopano,” ikutero Science News. Pamene anthu akuloŵa m’madera okhala ndi tizirombo tamatenda amene kale sankafikidwa, kaŵirikaŵiri pamatsatira miliri yatsopano ya tizirombo tamatenda. Chinthu chofananacho chimachitika pamene tizirombo tichuluka kaamba ka kusintha kwa mkhalidwe wamphepo wadziko lonse. “Kuwonjezerapo,” akutero magaziniwo, “maluso a zamankhwala amakono monga ngati kuthira mwazi ndi kusintha ziŵalo za thupi kwapereka njira zatsopano zoyendera tizirombo tamatenda pakati pa anthu ambirimbiri. Kwateronso kusinthasintha kwa zamayanjano ndi makhalidwe, kuphatikizapo kuyendayenda m’maiko kwa anthu achuma ndi otchuka ndi kubwerekana nsingano zoloŵetsera mankhwala oledzeretsa m’thupi kwa omwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa.”
“Mbiri yaposachedwapa imapereka zitsanzo zowonekera bwino za zizindikiro m’malo akutali zimene zingaperekeretu chithunzi cha kubuka kwa miliri yaikulu mtsogolo,” inawonjezera tero nkhaniyo. Zitsanzo ndi izi: kachirombo kapapitapo kosadziŵika kotchedwa Marburg, kachirombo kakupha ka m’malo otentha kamene kanakantha asayansi ambiri mu Jeremani Yakumadzulo chakumapeto kwa ma 1960; kachirombo kochititsa malungo a mu Rift Valley kamene kanayambukira mamiliyoni ambiri ndikupha zikwi zambiri mu Igupto mu 1977; kachirombo koyambitsa matenda ka kumalo otentha kotchedwa Ebola kamene kanayambukira anthu oposa chikwi chimodzi mu Zaire ndi Sudan mu 1976 ndikupha pafupifupi anthu 500, ambiri a iwo adokotala ndi anamwino omathandiza kuchiritsa oyambukiridwa nako.
Kubuka kosakaza kwa tizirombo tamatenda sikumaloseredwa kaŵirikaŵiri. “Mwachitsanzo, mu 1918, mliri wachaola wa fuluwenza ya anthu unafalikira padziko lonse, ukumapha anthu pafupifupi 20 miliyoni,” ikutero Science News. “Posachedwapa, kubuka kwa kachirombo mwa anthu kamene mwinamwake panthaŵi ina kanali kokha mwa apusi a mu Afirika kanakanthanso dziko mosadziŵa. Kachirombo ka AIDS tsopano kayambukira anthu kuchokera pa 5 miliyoni kufika ku 10 miliyoni m’maiko 149, malinga ndi kupenda kongoyerekezera kwa World Health Organization. Koma mosasamala kanthu za nkhaŵa yonse yochititsidwa ndi mliri watsopano kwambiri umenewu, zinthu zina zowopsa kwambiri zikutidikirira, akatswiri a tizirombo tamatenda ambiri akuchita mantha.”
Miliri yovutitsa kwambiri imeneyi, iri mbali ya chizindikiro chachiungwe cha kukhalapo kwa Yesu muulemerero wa Ufumu, pamodzi ndi zinthu zonga nkhondo, njala, ndi zivomezi zazikulu. (Marko 13:8; Luka 21:10, 11) Mbali zimenezi zirinso chifukwa chotipatsa chisangalalo, popeza kuti Luka akuwonjezera mawu a Yesu kuti: ‘Koma poyamba kuchitika izi ŵeramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.’—Luka 21:28.