Chimwemwe Chosatha Chikuyembekezera Opatsa Opembedza
‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike koma akhale nawo moyo wosatha.’—YOHANE 3:16.
1, 2. (a) Kodi Mpatsi wamkulu koposa ndani, ndipo mphatso yake yaikulu koposa kwa anthu njotani? (b) Popereka mphatso yake yaikuluyo, kodi ndimkhalidwe wotani umene Mulungu anasonyeza?
YEHOVA MULUNGU ndiye Mpatsi wamkulu koposa onse. Mtumwi Wachikristu Yakobo analemba za iye, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi kuti: ‘Mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho chirichonse changwiro zichokera kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.’ (Yakobo 1:17) Yehova alinso Mpatsi wa mphatso yaikulu koposa imene inaperekedwa. Ponena za mphatso yake yaikulu koposa kwa anthu, kunanenedwa kuti: ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike koma akhale nawo moyo wosatha.’—Yohane 3:16.
2 Wokamba mawuwo sanali wina aliyense koma Mwana wobadwa yekhayo wa Mulungu mwini. Mwana wobadwa yekha wa tate mwachibadwa akayamikira ndi kukonda tate woteroyo monga magwero a moyo ndi zinthu zonse zabwino zoperekedwa kuti mwanayo asangalale ndi moyo. Koma chikondi cha Mulungu sichinali pa Mwana ameneyu yekha. Kugaŵiranso mphatso yotero kwa zolengedwa zake zina kukasonyeza chikondi cha Mulungu kumlingo wapadera. (Yerekezerani ndi Aroma 5:8-10.) Ichi chimawonekera bwino lomwe pamene tipenda tanthauzo lenileni la liwulo “anapatsa” m’nkhaniyi.
Mphatso ya Mulungu ya ‘Mwana wa Chikondi Chake’
3. Kuwonjezera pa ‘Mwana wa chikondi chake,’ kodi ndani ena amene anasangalala ndi chikondi cha Atate wakumwamba?
3 Kwa nyengo yosatchulidwa, Mulungu anasangalala ndi unansi waumwini ndi Mwana wake wobadwa yekha ameneyu—‘Mwana wa chikondi chake’—kumwamba. (Akolose 1:13) Kwa nthaŵi yonseyo, Atate ndi Mwanayo anakulitsa chikondi ndi chiyanjo pa wina ndi mnzake moti panalibenso kukondana kofanana ndi kwawo. Zolengedwa zina zimene Mulungu anachititsa kukhalako kupyolera mwa Mwana wake wobadwa yekha zinakondedwanso monga ziŵalo za banja laumulungu la Yehova. Chotero, chikondi chinafunga pabanja lonse la Mulungu. Malemba opatulika amanena molondola kuti ‘Mulungu ndiye chikondi.’ (1 Yohane 4:8) Chotero banja laumulungu likapangidwa ndi awo okondedwa ndi Atate, Yehova Mulungu.
4. Kodi kupatsa kwa Mulungu Mwana wake kunaposa motani pakutaikiridwa unansi waumwini wokha, ndipo kaamba ka ayani?
4 Unansi pakati pa Yehova ndi Mwana wake woyamba kubadwa unali wathithithi moti kudzimana iwo eni kuyanjana kwapamtima koteroko kukakhala kutaikiridwa kwakukulu. (Akolose 1:15) Koma ‘kupatsa’ kwake Mwana wobadwa yekha ameneyu kunapambana pa kudzimana kwake Mulungu kwa unansi waumwini ndi ‘Mwana wa chikondi chake.’ Kunafikadi pamlingo wakuti Yehova alole Mwana wake kuloŵa mu imfa ndipo motero kuchotsedwa mwakanthaŵi m’banja lachilengedwe chonse la Mulungu. Imeneyi inali imfa yofera amene sanakhalepo ziŵalo za banja la Mulungu. Yehova sakanapereka mphatso yoposa pa Mwana wake wobadwa yekha mmalo mwa anthu ovutika, yemwe Malembanso amamdziŵikitsa monga ‘woyamba wa chilengo cha Mulungu.’—Chivumbulutso 3:14.
5. (a) Kodi mkhalidwe wa ana a Adamu unali wotani, ndipo kodi nchiyani chimene chiweruzo cholungama cha Mulungu chinafunikiritsa kwa mmodzi wa ana Ake okhulupirika? (b) Kodi mphatso ya Mulungu yaikulu koposayo inamfunikiritsa iye kuchitanji?
5 Anthu okwatirana oyambirira, Adamu ndi Hava, analephera kusunga malo awo monga ziŵalo za banja la Mulungu. Umenewo ndiwo mkhalidwe umene anadzipezamo atathamangitsidwira kunja kwa munda wa Edene chifukwa cha kuchimwira Mulungu. Kuwonjezera pa kusakhalanso ziŵalo za banja la Mulungu anakhalanso pansi pa chilango cha imfa. Chotero, vuto silinali chabe lakubwezeretsa ana awo m’chiyanjo cha Mulungu monga ziŵalo za banja lake komanso lakuwachotsera chilango cha imfa chaumulungu. Malinga ndi kugwira ntchito kwa chiweruzo cholungama cha Mulungu, zimenezi zikafunikiritsa kuti mmodzi wa ana okhulupirika a Yehova Mulungu afe monga mloŵa mmalo, kapena dipo. Chifukwa chake, funso lalikulu linali lakuti: Kodi amene adzasankhidwa akakhala wofunitsitsa kufa imfa yoteroyo yoloŵa mmalo mwa anthu ochimwa? Ndiponso, kudzetsa zimenezi kukafunikiritsa kuti Mulungu Wamphamvuyonse achite chozizwitsa. Kukafunikiritsanso kusonyezedwa kwa chikondi chaumulungu kumlingo wosayerekezereka.—Aroma 8:32.
6. Kodi Mwana wa Mulungu anali wokhoza motani kukwaniritsa zosoŵa za mkhalidwe wa anthu ochimwa, ndipo kodi iye ananenanji za nkhaniyo?
6 Mwana woyamba kubadwa wa Yehova ndiye yekhayo amene akakhoza kukwaniritsa zosoŵa zapadera za mkhalidwe wokhalamo anthu ochimwa. Ndiye chifanefane cha Atate wake wakumwamba m’kusonyeza chikondi paziŵalo za banja loberekedwa mwaumulungu kwakuti alibe wofanana naye pakati pa ana a Mulungu. Popeza kuti zolengedwa zina zonse zaluntha zinalengedwa kupyolera mwa iye, chikondi chake pa iwo chikhaladi chochuluka. Ndiponso, chikondi ndicho mkhalidwe waukulu wa Mwana wobadwa yekha wa Yehova, Yesu Kristu, chifukwa ‘ali chinyezimiro cha ulemerero wa [Mulungu], ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.’ (Ahebri 1:3) Akumasonyeza kufunitsitsa kwake kusonyeza chikondi chimenechi kumlingo waukulu koposa mwakupereka moyo wake mmalo mwa anthu ochimwa, Yesu anauza atumwi ake 12 kuti: ‘Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.’—Marko 10:45; onaninso Yohane 15:13.
7, 8. (a) Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yehova kutumiza Yesu Kristu m’dziko la anthu? (b) Kodi ndintchito yotani imene Mulungu anatumizira Mwana wake wobadwa yekha?
7 Yehova Mulungu anali ndi chifukwa chapadera chotumizira Yesu ku dziko la anthu lovutikali. Chikondi chaumulungu ndicho chinasonkhezera chimenechi, pakuti Yesu mwiniyo anati: ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.’—Yohane 3:16, 17.
8 Inali ntchito yakupulumutsa imene Yehova mwachikondi anatumizira Mwana wake wobadwa yekha. Mulungu sanatumize Mwana wake kunoko kudzaweruza dziko. Ngati Mwana wa Mulungu anatumizidwira ntchito yoweruza yotero, mtsogolo mwa anthu onse mukanakhala mopanda chiyembekezo. Chilango cha chiweruzo chowopsa chimene chikanaperekedwa ndi Yesu Kristu pabanja la anthu chikanakhala cha imfa. (Aroma 5:12) Chotero, mwakusonyezedwa kwapadera kumeneku kwa chikondi chake, Mulungu anachinjiriza chilango cha imfa chimene chiweruzo cholungama chikanafunikiritsa.
9. Kodi wamasalmo Davide anakulingalira motani kupatsa kwa Yehova?
9 M’zinthu zonse, Yehova Mulungu amasonyeza ndi kuzindikiritsa chikondi monga mbali yoposa ya umunthu wake. Ndipo kuli kowona kunena kuti Mulungu mwachikondi amapatsa olambira ake okhulupirika padziko lapansi zinthu zabwino koposadi. Wamasalmo Davide anailingalira motero nkhaniyo pamene anati kwa Mulungu: ‘Ha! kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuwopa inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira inu, pamaso pa ana a anthu!’ (Salmo 31:19) Mkati mwa ufumu wa Davide pamtundu wa Israyeli—inde, m’moyo wake wonse monga chiŵalo cha mtundu wosankhidwa mwapadera ndi Mulungu—iye kaŵirikaŵiri analandira ubwino wa Yehova. Ndipo Davide anaupeza kukhala wochulukadi.
Israyeli Ataikiridwa Mphatso Yaikulu Yochokera kwa Mulungu
10. Kodi nchifukwa ninji mtundu wa Israyeli unali wosafanana ndi mtundu wina uliwonse padziko lapansi?
10 Pokhala ndi Yehova monga Mulungu wake, Israyeli wamakedzana anali wosafanana ndi mtundu wina uliwonse padziko lapansi. Kupyolera mwa mneneri Mose monga nkhoswe, Yehova analoŵetsa mbadwa za Abrahamu, Isake, ndi Yakobo muunansi wapangano ndi iye. Sanachite ndi mtundu wina uliwonse mwanjirayi. Chotero, wamasalmo wouziridwa anakhoza kufuula kuti: ‘Awonetsa mawu ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israyeli. Sanatero nawo anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanawadziŵa. Haleluya.’—Salmo 147:19, 20.
11. Kodi ndikufikira liti pamene Israyeli anakhala ndi mkhalidwe woyanjidwa ndi Mulungu, ndipo kodi Yesu anasonyeza motani kusintha kwa unansi wawo?
11 Mtundu wa Israyeli wakuthupi unapitirizabe muunansi umenewu woyanjidwa ndi Mulungu kufikira unakana Yesu Kristu monga Mesiya m’chaka cha 33 cha Nyengo yathu Ino. Linalidi tsiku lomvetsa chisoni pa Israyeli pamene Yesu anadzuma molira kuti: ‘Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani nyumba yanu yasiidwa kwa inu yabwinja.’ (Mateyu 23:37, 38) Mawu a Yesu anasonyeza kuti, mosasamala kanthu kuti unali woyanjidwa ndi Yehova poyambapo, mtundu wa Israyeli unataikiridwa mphatso yapadera yochokera kwa Mulungu. Motani?
12. Kodi ndani anali ‘ana a Yerusalemu,’ ndipo kodi kuwasonkhanitsa pamodzi kwa Yesu kukanatanthauzanji?
12 Mwakugwiritsira ntchito liwu lakuti “ana,” Yesu analoza kokha kwa Ayuda akuthupi odulidwa amene anakhala m’Yerusalemu ndi kuimira mtundu wonse Wachiyuda. Kusonkhanitsa pamodzi ‘ana a Yerusalemu’ kwa Yesu kukanatanthauza kuwaloŵetsa “ana” ameneŵa m’pangano latsopano ndi Mulungu, iyemwiniyo akutumikira monga Nkhoswe pakati pa Yehova ndi Ayuda akuthupi ameneŵa. (Yeremiya 31:31-34) Zimenezi zikanapangitsa kukhululukidwa machimo, pakuti umenewo ndiwo unali ukulu wa chikondi cha Mulungu. (Yerekezerani ndi Malaki 1:2.) Chimenechi chikanakhaladi mphatso yaikulu.
13. Kodi kukana Mwana wa Mulungu kwa Israyeli kunachititsa kutaikiridwa chiyani, koma nchifukwa ninji chimwemwe cha Yehova sichinalepheretsedwe?
13 Momvana ndi Mawu ake aulosi, Yehova anayembekezera moyenerera asanafutukulire kwa osakhala Ayuda mphatso ya kukhala otenga mbali m’pangano latsopano. Koma mwakukana Mwana wa Mulungu, Mesiyayo, mtundu wa Israyeli unataikiridwa mphatso yaikulu imeneyi. Chotero Yehova anawonjola kukanidwa kwa Mwana wake mwakufutukulira mphatso imeneyi kwa anthu a kunja kwa mtundu Wachiyuda. Mwanjira imeneyo, chimwemwe cha Yehova monga Mpatsi Wamkulu chinapitirizabe mosalepheretsedwa.
Chimwemwe m’Kupatsa
14. Kodi nchifukwa ninji Yesu Kristu ali cholengedwa chachimwemwe koposa m’chilengedwe chonse?
14 Yehova ndiye “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Chimodzi cha zinthu zimene zimampangitsa kukhala wachimwemwe ndicho kupatsa ena zinthu. Ndipo m’zaka za zana loyamba C.E., Mwana wake wobadwa yekha anati: “Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa ndi chimene chiri m’kulandira.” (Machitidwe 20:35, NW) Momvana ndi lamulo lamakhalidwe abwino limeneli, Yesu anakhala cholengedwa chachimwemwe koposa cha Mlengi wa chilengedwe chonse. Motani? Eya, pokhala wachiŵiri kwa Yehova Mulungu mwiniyo, Yesu Kristu anapatsa mphatso yaikulu koposa mwakupereka moyo wake kuti anthu apindule. Kwenikweni, iye ndiye ‘Mwini Mphamvu wodala.’ (1 Timoteo 6:15) Motero Yesu wapereka chitsanzo cha chimwemwe chambiri chokhala m’kupatsa chimene ananena.
15. Kodi Yehova sadzaleka kukhala chitsanzo chotani, ndipo kodi zolengedwa zake zaluntha zingakhale motani ndi mlingo winawake wa chimwemwe chake?
15 Kupyolera mwa Yesu Kristu, Yehova Mulungu sadzalephera konse kukhala Mpatsi wooloŵa manja kwa zolengedwa zake zonse zaluntha ndipo nthaŵi zonse adzakhala chitsanzo chawo chabwino koposa m’kupatsa. Monga momwedi Mulungu amapezera chisangalalo m’kupatsa mphatso zabwino kwa ena, chotero waika mzimu wa kuoloŵa manja m’mitima ya zolengedwa zake zaluntha padziko lapansi. Mwanjirayo zimasonyeza ndi kutsanzira umunthu wake nizikhala ndi mlingo wakutiwakuti wa chimwemwe chake. (Genesis 1:26; Aefeso 5:1) Yesu anauza otsatira ake moyenerera kuti: ‘Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m’manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.’—Luka 6:38.
16. Kodi Yesu ananena zakupatsa kotani pa Luka 6:38?
16 Yesu anapereka kwa ophunzira ake chitsanzo chabwino koposa chakusonyeza njira yoilondola. Iye ananena kuti olandira akayamikira kwambiri kupatsa koteroko. Pa Luka 6:38, Yesu sanali kunena zakupatsa mphatso zakuthupi zokha. Sanali kuuza ophunzira ake kulondola njira imene ikawachititsa umphaŵi wakuthupi. Mmalomwake, anali kuwasonyeza njira imene ikawapatsa lingaliro lakukhutiritsidwa mwauzimu.
Chimwemwe Chosatha Nchotsimikizirika
17. Kodi ndimphatso yodabwitsa yotani imene Mulungu wapatsa Mboni zake m’masiku ano otsiriza?
17 Ha, ndimphatso yodabwitsa chotani nanga imene Yehova, Mutu wa chilengedwe chonse, wapatsa Mboni zake m’masiku ano otsiriza! Watipatsa mbiri yabwino ya Ufumu wake. Tiri ndi mwaŵi waukulu wakukhala olengeza Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu umene uli m’manja mwa Mwana wake wolamulirayo, Yesu Kristu. (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Kupangidwa kukhala Mboni zolankhulira Mulungu Wam’mwambamwamba ndiko mphatso yosayerekezereka, ndipo njira yabwino koposa imene tingatsanzirire Mulungu m’kupatsa ndiyo kugaŵana uthenga Waufumu ndi ena mapeto a dongosolo ili loipa la zinthu asanadze.
18. Monga Mboni za Yehova, kodi nchiyani chimene tiyenera kupatsa kwa ena?
18 Mtumwi Paulo anatchula mavuto amene anayang’anizana nawo pamene ankalengeza uthenga Waufumu kwa ena. (2 Akorinto 11:23-27) Mboni zamakono za Yehova nazonso zimayang’anizana ndi mavuto ndipo zimaika padera zofuna zaumwini poyesayesa kupatsa ena chiyembekezo Chaufumu. Mwina tingakhale amphwayi kupita kumakomo a anthu, makamaka ngati ndife amanyazi. Koma monga otsatira a Kristu, sitingapeŵe, kapena kunyalanyaza, mwaŵi wakupatsa zinthu zauzimu kwa ena mwakulalikira “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Tifunikira kukhala ndi kaimidwe kamaganizo kamene Yesu anali nako. Atayang’anizana ndi imfa, anapemphera kuti: ‘Atate, . . . simonga ndifuna ine, koma inu.’ (Mateyu 26:39) Ponena za kupatsa ena mbiri yabwino ya Ufumu, atumiki a Yehova ayenera kuchita chifuniro cha Mulungu, osati chawo—zimene iye afuna, osati zimene iwo angafune.
19. Kodi Eni ‘mahema osatha’ ndani, ndipo ndimotani mmene tingapalanire nawo ubwenzi?
19 Kupatsa koteroko kudzaloŵetsamo nthaŵi yathu ndi chuma, koma mwakukhala opatsa opembedza, timatsimikizira kuti chimwemwe chathu chidzakhala chosatha. Chifukwa ninji? Chifukwa Yesu anati: ‘[Palanani ubwenzi inu eni, NW] ndi chuma chosalungama [“chuma chaudziko,” New International Version], kuti pamene chikusoŵani, iwo akalandire inu m’mahema osatha.’ (Luka 16:9) Chiyenera kukhala cholinga chathu kugwiritsira ntchito ‘chuma chosalungama’ kupalana ubwenzi ndi Eni ‘mahema osatha.’ Pokhala Mlengi, Yehova ndiye mwini zonse, ndipo Mwana wake woyamba kubadwa ali ndi mbali muumwiniwo monga Woloŵa zinthu zonse. (Salmo 50:10-12; Ahebri 1:1, 2) Kuti tipalane nawo ubwenzi, tiyenera kugwiritsira ntchito chuma chathu m’njira imene imadzetsa chivomerezo chawo. Zimenezi zimaphatikizapo kukhala ndi kaimidwe kabwino kamaganizo pogwiritsira ntchito zinthu zakuthupi kuti ena apindule. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:3, 4; 2 Akorinto 9:7.) Tingagwiritsire ntchito ndalama m’njira yoyenera kulimbitsa unansi wathu ndi Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Mwachitsanzo, timachita zimenezi mwakugwiritsira ntchito mokondwera zimene tiri nazo kuthandiza anthu okhala m’kusoŵa kwenikweni ndi kugwiritsira ntchito chuma chathu kupititsa patsogolo zabwino za Ufumu wa Mulungu.—Miyambo 19:17; Mateyu 6:33.
20. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova ndi Yesu akhoza kutiloŵetsa “m’mahema osatha,” ndipo nkuti kumene malo ameneŵa angakhale? (b) Kodi tidzakhala ndi mwaŵi wotani kuumuyaya wonse?
20 Chifukwa cha kusakhoza kufa kwawo, Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu angakhale Mabwenzi athu kosatha ndipo angatiloŵetse “m’mahema osatha.” Zimenezi ziri choncho kaya tidzakhala kumwamba pamodzi ndi angelo oyera kapena padziko lino lapansi m’Paradaiso wobwezeretsedwa. (Luka 23:43) Yesu Kristu monga mphatso yochokera kwa Mulungu wachikondi anatheketsa zonsezi. (Yohane 3:16) Ndipo Yehova Mulungu adzagwiritsira ntchito Yesu kupitirizabe kupatsa kwa zolengedwa zonse, kumene kumampatsa Iye chimwemwe chapadera. Kwenikweni, ife tidzakhala ndi mwaŵi wa kupatsa kuumuyaya wonse pansi pa ulamuliro wachilengedwe chonse wa Yehova Mulungu ndi ufumu wa Mwana wake wobadwa yekha, Ambuye wathu ndi Mpulumutsi, Yesu Kristu. Chimenechi chidzachititsa chimwemwe chosatha kwa opatsa opembedza onse.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi mphatso yaikulu koposa ya Mulungu ikamfunikiritsa kuchitanji?
◻ Kodi ndintchito yotani imene Mulungu anatumizira Mwana wake?
◻ Kodi cholengedwa chachimwemwe koposa m’chilengedwe chonse ndani, ndipo chifukwa ninji?
◻ Kodi opatsa opembedza adzakhala motani ndi chimwemwe chosatha?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi mumayamikira mphatso ya Mulungu ya Mwana wake monga nsembe yadipo?
[Zithunzi patsamba 12]
Kodi mumafuna Ufumu wa Mulungu choyamba mwakulalikira mbiri yabwino ndi kuchirikiza ntchitoyo ndi chuma chanu?