Chenjerani ndi Aneneri Onyenga!
OKWATIRANA aŵiri a ku Brazil anali gone usiku pamene anamva mbala zikuthyola nyumba yawo. Okwatirana ochita manthawo anakhoza kuthaŵira pazenera lakuchipinda chogona ndi kuitana apolisi. Koma pambuyo pake mkaziyo anachita mantha ndi chochitikachi kwakuti analephera kugona m’nyumbamo ndipo anapita kwa amayi ŵake.
Munthu aliyense amene nyumba yake inathyoledwapo kapena kuberedwa mwanjira ina angamverere chifundo mkaziyo. Chokumana nacho choterocho chingakhale cholobodola, ndipo, momvetsa chisoni, anthu ochulukirachulukira akuvutika mwanjira imeneyi. Komabe, pali mtundu wina wakuba umene uli ndi zotulukapo zowopsa kwambiri.
Kodi mtundu wowopsa kwambiri umenewu wakuba ngwotani, ndipo kodi mbalazo ndani? Yesu Kristu anatidziŵitsa za kumeneko pamene, polankhula za m’tsiku lathu, ananena kuti: “Aneneri [onyenga, NW] ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri.” (Mateyu 24:11) Aneneri onyenga ndimbala. Motani? Kodi amaba chiyani? Kuba kwawo kumachita ndi kulosera kwawo. Choncho kuti timvetsetse nkhaniyi mokwanira, choyamba tiyenera kudziŵa chimene kulosera kuli malinga ndi kunena kwa Baibulo.
Chimene Kulosera Kumatanthauza
Pamene mulingalira za kulosera, mwinamwake chinthu choyamba chomwe chimabwera m’maganizo mwanu ndicho kunenera zamtsogolo. Iyi inalidi mbali ina ya ntchito ya aneneri akale a Mulungu, koma sindiyo inali ntchito yawo yaikulu. Mwachitsanzo, pamene mneneri Ezekieli anauzidwa m’masomphenya ‘kunenera kwa mpweya,’ iye anangoyenera kupereka lamulo lochokera kwa Mulungu. (Ezekieli 37:9, 10) Pamene Yesu anali kuzengedwa mlandu pamaso pa ansembe, analavuliridwa ndi kubwanyulidwa, ndipo omzunzawo moseka anati: “Nenera kwa ife, Kristu iwe. Kodi ndani wakumenya?” Iwo sanali kumpempha Yesu kunenera zamtsogolo. Anali kupereka chitokoso kwa iye kuti azindikire ndi mphamvu ya Mulungu awo amene anammenya.—Mateyu 26:67, 68, NW.
Kwenikwenidi, lingaliro lenileni loperekedwa ndi mawu a chinenero choyambirira cha Baibulo otembenuzidwa “ulosi” kapena “kunenera” kwakukulukulu amatanthauza kunena maganizo a Mulungu pa nkhani ina kapena, monga momwe bukhu la Machitidwe limafotokozera, kunena ‘zazikulu za Mulungu.’ (Machitidwe 2:11) Anthu ambiri amaberedwa mwanjira imeneyi ndi aneneri onyenga.
Komabe, kodi ndani omwe ali aneneri onyenga, ndipo kodi amaba chiyani? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tiyang’ane kumbuyo m’mbiri ya mtundu wa Israyeli m’nthaŵi ya Yeremiya.