Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/15 tsamba 19-20
  • Bukhu Latsopano Lisangalatsa Mamiliyoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bukhu Latsopano Lisangalatsa Mamiliyoni
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magwero a Bukhulo
  • Limalimbitsa Chikhulupiriro
  • Kuligwiritsira Ntchito Mosiyanasiyana
  • Mbali Zophindulitsa
  • Chivomerezo cha Oŵerenga Bukhu la Young People Ask
    Galamukani!—1990
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • ‘Moto wa m’Mtima ndi m’Maganizo Wolakalaka Kudziŵa Zambiri’
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Itanirani Ena Kudzatsatira Munthu Wamkulu Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/15 tsamba 19-20

Bukhu Latsopano Lisangalatsa Mamiliyoni

YAPADERA pa Misonkhano ya “Okonda Ufulu” imene inayamba m’June wapita inali nkhani yakuti “Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.” Mfundo yake yaikulu inali kumasulidwa kwa bukhu lokhala ndi mutu wakuti “The Greatest Man Who Ever Lived.” Anthu oposa mamiliyoni asanu ndi imodzi padziko lonse apezeka kale pamisonkhano imeneyi ndi kumva nkhaniyo, imene irinso m’nkhani ziŵiri zapitazo m’magazini ano koma yosinthidwako pang’ono.

Makope oposa 12 miliyoni a bukhu la The Greatest Man Who Ever Lived asindikizidwa m’zinenero 60. Lipezekanso ngakhale m’zinenero za Kum’maŵa kwa Yuropu za Albanian, Croatian, Hungarian, Macedonian, Polish, Russian, Serbian, ndi Slovenian. Makamaka oposa 74,000 omwe anapezeka pamisonkhano isanu ndi iŵiri mu Soviet Union anasangalala kwabasi kulilandira m’chinenero cha Russian.

Magwero a Bukhulo

Nkhani za m’bukhulo choyamba zinatuluka monga mpambo m’makope otsatizana okwanira 149 a Nsanja ya Olonda, kuyambira ndi kope la September 15, 1985. Oŵerenga ambiri ananena kuti sanakondwere pamene mpambowo unatha m’kope la June 1, 1991. Melissa, wazaka 12 wa ku Italiya, ananjerama misozi m’maso pamene anaŵerenga nkhani yomalizira mu Nsanja ya Olonda. “Usiku wochera patsiku la msonkhano,” iye anatero, “ndinapemphera kwa Yehova kupempha bukhu losimba moyo wa Yesu. Pamene bukhulo linasonyezedwa, ndinawomba m’manja kwa nthaŵi yaitali mosalekeza.”

Nkhani zoperekedwa mumpambo mu Nsanja ya Olonda zinasonkhanitsidwa ndi kupangidwa bukhu lokhala ndi zithunzithunzi zokongola, lamasamba 448 ndi mitu 133. Panali chisamaliro chachikulu chakupereka nkhani iriyonse imene Yesu anaikamba ndi chochitika chirichonse m’moyo wake wapadziko lapansi, kuphatikizapo mafanizo ake onse ndi zozizwitsa. Kumlingo wothekera, chirichonse chikusimbidwa motsatira dongosolo la kuchitika kwake. Kumapeto kwa mutu uliwonse, mudzapeza ndandanda ya malemba a Baibulo amene mutuwo wazikidwapo.

Wina angalingalire kuti, ‘Eya, ine ndinaliŵerenga kale bukhulo popeza kuti ndinaŵerenga mpambowo mu Nsanja ya Olonda.’ Komabe oŵerenga Nsanja ya Olonda analandira nkhani ya moyo wa Yesu m’zigawo zazing’ono zoperekedwa pambuyo pa milungu iŵiri iriyonse kwa nyengo yoposa zaka zisanu ndi chimodzi. Ngakhale kuti nkhanizo zinali zopereka chidziŵitso mumpambo wakewo, talingalirani nthumanzi yakuŵerenga nkhani yonse m’nthaŵi yaifupi ndi kuwona chithunzi chonse cha munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako!

Limalimbitsa Chikhulupiriro

“Ndinamaliza kuliŵerenga bukhulo m’milungu iŵiri,” akutero mkazi wa ku Washington, D.C., U.S.A. “Ndinalikugwetsa misozi poliŵerenga. Ndinkalekeza kuŵerenga ndi kuyamba kupemphera ndi kulira. Linandipangitsa kumva ngati kuti ndinali naye Yesu, kuvutika naye pamodzi. Ngakhale patapita mlungu umodzi pambuyo pakuliŵerenga bukhulo, misozi inali kunjeramabe m’maso pamene ndinalingalira zimene ndidaŵerenga. Ndimadzimva kukhala womyandikiradi Yehova kaamba ka kupereka Mwana wake.”

“Ndamaliza lero bukhulo lonena za Yesu,” analemba tero mkazi wa ku Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A. “Linali logwira mtima kwabasi. Ndinali kugwetsa misozi poŵerenga mitu ingapo yomalizira. Kuŵerenga bukhu lonselo panthaŵi imodzi nkosangalatsa zedi. Ndasoŵa mawu onenera mmene ndinamverera​—ndidzangoti ndinalikonda zedi!”

Zithunzithunzi zake zokongola zimawonjezera kukhudzidwa kwa maganizo a munthu, monga momwe woŵerenga woyamikira wina ananenera kuti: “Ndimamva ngati kuti ndidzawamva akulira mwana wakufayo (mutu 47) kapena monga tikudziŵa zimene Yesu anali kuganiza pamene mkazi wodwala nthenda yamwazi anamgwira ndi kuchira (mutu 46). Nkhope zawo zimasonyeza mkhalidwe wawo weniweni womvetsa chisoni. . . . Mmalo mwakuti kuŵerenga kukhale kotopetsa, bukhuli limakhala ngati chosangulutsa kapena kaseŵero kosangalatsa pakutha kwa tsiku. Njira yogwira mtima imene bukhuli linalembedwera siimangosonyeza zimene Yesu anachita koma imapereka lingaliro la mmene anaganizira ndi kumverera.”

Kuligwiritsira Ntchito Mosiyanasiyana

Ambiri ayamba kugwiritsira ntchito bukhuli paphunziro lawo labanja Labaibulo. “Tiri ndi ana aang’ono atatu,” analemba tero makolo a ku Silverton, Oregon, U.S.A., “ndipo bukhuli nloyenerera kaamba ka ‘phunziro lathu labanja la usiku uliwonse.’ Ndithudi, nkoyenera chotani nanga kuti tikuphunzira kakulidwe ka Mfumu yathu yachikondi, Kristu Yesu.”

Msungwana wa ku Japan anafotokoza kuti: “Abambo akhala akuliŵerenga kwa ife titakhala pansi pambuyo pa chakudya chamadzulo. Monga banja, timaŵerenga kuchokera kuchiyambi, koma ndinasankha kumaŵerenga mutu umodzi usiku uliwonse ndisanagone kuchokera kothera kwa bukhulo. Komabe, bukhulo nlotenga maganizo kwakuti kaŵirikaŵiri nthaŵi imafika 1 koloko ine osadziŵa.”

Ambiri amadabwa ndi kuchuluka kwa tsatanetsatane wophatikizidwa m’nkhanizo. “Ndinaphunzira zinthu zambiri zimene sindinadziŵe,” inalemba tero Mboni ina. Kalata yochokera ku California, U.S.A., inati: “Mkazi wanga ndi ine takhala m’chowonadi kwa zaka zoposa 35, ndipo kunena zowona, sitinakhalepo ndi bukhu losangalatsa ngati ili.”

Bukhuli liyenera kuthandiza kugwetsa bodza lamkunkhuniza lakuti Mboni za Yehova sizimakhulupirira Yesu. Woŵerenga wina woyamikira anathirira ndemanga motere: “Sindinathe kulitula pansi, popeza kuti linavumbula mwamphamvu umbuli wa awo onena kuti anthu a Yehova samakhulupirira kapena samalemekeza Yesu Kristu. Chimene tingofunikira kuchita tsopano ndicho kuika m’dzanja lawo yankho limeneli la umbuli wawo.”

Ndithudi bukhuli lidzachita mbali yaikulu muuminisitala wa Mboni za Yehova. “Ndinapatsa kope mkazi wina amene ndimaphunzira naye Baibulo,” inalemba tero Mboni ina, “ndipo lamyambukira mozizwitsa. Iye wakhala akuphunzira kwa chaka chimodzi, ndipo ndakhala ndi vuto lakumpangitsa kubwera kumisonkhano.” Pamene wophunzirayo anaŵerenga mitu 45 ya bukhu latsopanoli, Mboniyo inafotokoza tero, “anandiuza kuti akapezeka pamsonkhano pa Sande chifukwa chakuti inafika nthaŵi yakuti atenge kaimidwe kake.”

Mbali Zophindulitsa

Kwenikweni, bukhu la The Greatest Man Who Ever Lived limapereka ndemanga pa Mauthenga Abwino. Mulinso malongosoledwe ambiri a zinthu zimene Yesu ananena ndi kuphunzitsa, choncho bukhulo lingagwiritsiridwe ntchito monga chiŵiya chothandiza m’kufufuza, popeza kuti limamamatira mosamalitsa ku nkhani za Baibulo.

Mbali yabwino makamaka njakuti chochitika chirichonse chimasimbidwa m’dongosolo lotsatira nthaŵi ya kuchitika kwake. Kungosanthula masamba muli ndi mfundo imeneyi m’maganizo kungakhale kothandiza kudziŵa ndiliti, muuminisitala wa Yesu, pamene zinthu zakutizakuti zinachitika. Oŵerenga Mauthenga Abwino kaŵirikaŵiri amapeza zimene zimawoneka kukhala ngati zotsutsana. Bukhu latsopanolo, popanda kufotokoza zimenezi kwenikweni, limazigwirizanitsa bwino lomwe.

Monga Akristu, sitiyenera konse kunyalanyaza phunziro losamalitsa la moyo wa Chitsanzo chathu chokhulupirika, Yesu Kristu. Chifukwa chake, tiyeni tipendetu mosamalitsa nkhani za Mauthenga Abwino mothandizidwa ndi bukhu latsopanoli The Greatest Man Who Ever Lived.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena