Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 6/15 tsamba 25-26
  • ‘Moto wa m’Mtima ndi m’Maganizo Wolakalaka Kudziŵa Zambiri’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Moto wa m’Mtima ndi m’Maganizo Wolakalaka Kudziŵa Zambiri’
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sayansi Yomveka
  • Kum’dziŵa Bwino Mlengi
  • Bukhu Latsopano Lisangalatsa Mamiliyoni
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Dziŵani Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Chivomerezo cha Oŵerenga Bukhu la Young People Ask
    Galamukani!—1990
  • Mlengi Angawonjezere Tanthauzo la Moyo Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 6/15 tsamba 25-26

‘Moto wa m’Mtima ndi m’Maganizo Wolakalaka Kudziŵa Zambiri’

“Mawu akundisoŵa oti ndithokoze kaamba ka chimwemwe ndi chisangalalo chimene chikuŵirikizabe pamene ndikumwerekera poŵerenga buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Bukuli limangodzutsa chilakolako mwa munthu​—ayi, koma nditi moto wolakalaka kudziŵa zochuluka. Zikomo kwambiri pokoleza moto umenewo mumtima ndi m’maganizo mwanga.”

UMO NDI mmene wina wa Mboni za Yehova wa ku North Carolina, U.S.A., ananenera za buku limene Watch Tower Society inatulutsa pa Misonkhano Yachigawo yakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu” m’zaka za 1998/99. Ngakhale ngati mulibe bukulo, tamverani zimene enanso ananena.

Mwamuna wina, patapita masiku angapo chilandirire bukulo pamsonkhano wachigawo wa ku San Diego, California, U.S.A., analemba kuti: “Bukuli likundilimbitsa chikhulupiriro kwambiri. Likuchititsa mtima wanga kusefukira ndi chiyamikiro kwa Yehova kaamba ka zinthu zimene analenga. Ndafika patsamba 98, ndipo ndikuda nkhaŵa za tsiku limene ndidzalimaliza! Likundipatsa chimwemwe chachikulu kwabasi.”

Mkazi wina wa Kum’maŵa analemba kuti: “Wokamba nkhani pamsonkhano wachigawo ananena kuti ‘ndi buku lapadera,’ ndipo mawuwo akuyeneradi nkhani zolembedwa mmenemo. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti bukulo siliumiriza woŵerenga kuvomereza kuti Mulungu aliko, koma limapereka mfundo zenizeni.”

Mfundo zenizenizo zimaphatikizapo zimene asayansi azitulukira ponena za thambo lathuli, moyo, ndi ife tomwe. Zimenezi zinapatsa chidwi ambiri. Mkazi wina ku California analemba kuti: “Ndikusoŵa kuti nditi chiyani za mmene kabukuka kandikhudzira ineyo. Ndimalephera kukatula pansi poona kuti tsamba lililonse limafotokoza zochulukirapo zimene azitulukira ponena za thambo lathu ndi moyo wathu weniweniwo. Ndinaphunzira zambiri kwabasi! Kabukuka ndidzakaŵerenga bwino lomwe ndi kuuzako anthu ambiri nkhani za mmenemo.”

Mbali imene inasangalatsa ambiri ndiyo mmene bukulo limafotokozera za Baibulo, pomveketsa bwino lomwe umunthu wa Mlengi. Ambiri anena kuti: “Chithunzi chimene bukulo limapereka ponena za Baibulo, chakumapeto kwake, n’chimodzi mwa zabwino koposa zimene ndaŵerengapo.” Pamsonkhano wina woyambirira ku New York, U.S.A., munthu wina analemba kuti: “Buku latsopano limene latulutsidwali liyenera kukhala lokopa maganizo koposa onse amene mwalembapo. Ndinachita chidwi ndi umboni wake wasayansi wakuti Mlengi aliko. Mawu oyenera ochokera m’Baibulo amenewo n’ngokwanira kufotokozera mfundo zoperekedwa ndi kudzutsa chilakolako chofuna kuliŵerenganso kwambiri.”

Sayansi Yomveka

Mfundo za sayansi m’mitu yoyambirira zingaoneke ngati zovuta kumva, koma tamverani zimene ambiri anena.

Mwamuna wina ku Canada analemba kuti: “Likusiyana kwambiri ndi mabuku ena amene olemba ake amangofuna kutichititsa chidwi ndi mawu ovuta kumva. Luso lanu n’lapadera pofotokoza momveketsa bwino nkhani za physics, chemistry, DNA, ndi za ma chromosome. Mukanakhala ndinu amene munalemba mabuku ophunzira a payunivesite amene ndinaphunzira zaka zingapo zapitazo!”

Polofesa wa physics wa payunivesite analemba kuti: “[Bukulo] limafotokoza momveka bwino nkhani zake popanda kusokoneza munthu ndi mfundo zocholoŵana zochuluka. Limathandiza woŵerenga kulingalira ndipo limagwira mawu asayansi otchuka ambiri. Buku limeneli ndi ‘loyenera kuŵerenga’ aliyense wofuna kudziŵa za thambo ndi moyo, kaya wasayansi kapena munthu wamba.”

Mtsikana wina wophunzira zachipatala anathirira ndemanga kuti: “Sindinathe kukhulupirira pamene ndinatsegula mutu 4 ndi kuŵerenga mawu ogwidwa kuchokera m’buku limene tikuphunzira m’kalasi! Ndinapatsa polofesa wathu buku limeneli ndi kumuuza kuti adzapezamo chidziŵitso chosangalatsa. Ndinam’sonyeza tsamba 54 lonena za ubongo. Ataŵerenga anati, ‘Izi n’zosangalatsa kwabasi! Ndiliŵerenga ndione.’”

Phungu wa m’nyumba ya malamulo ku Belgium analemba kuti: “Chimene chinandikopa ndi kundisangalatsa anali mafotokozedwe a sayansi oonetsa kuti sayansi yamakono siitsutsa lingaliro la Baibulo lonena za Mulungu mmodzi, m’malo mwake limagwirizana nalo. Zimenezi n’zomveka bwino kwambiri.”

Kum’dziŵa Bwino Mlengi

Bukulo linathandiza anthu m’mayiko osiyanasiyana kuti am’dziŵe bwino Mulungu ndi kuti am’yandikire kwambiri. Woŵerenga wina mu mzinda wa Fukuoka, ku Japan, anati: “Zili ngati kuti magalasi analunjika pa Yehova kwa nthaŵi yoyamba. Bukulo limakhutiritsa maganizo modabwitsa. Ndinatha kum’dziŵa Yehova m’njira imene sindinaganizepo ndi kale lonse.” Munthu wina wa ku El Salvador analemba kuti: “Inu mumafotokoza momveka bwino mmene Mulungu alili wachifundo, wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wochuluka m’kukoma mtima. Kunena zoona, bukuli n’limene tiyenera kukhala nalo kuti tiyandikire kwa Mwana wake. Ndi buku loyamba limene limafotokoza mawu a Yehova ndi malingaliro a Mwana wake, Yesu, ponena za anthu.” Ndipo woŵerenga wina ku Zambia ananena kuti: “Yehova tsopano ndam’dziŵa m’njira yatsopano kotheratu.”

M’posadabwitsa kuti Mboni za Yehova zimasangalala kugaŵira ena buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Munthu wina anati: “Pamene ndinamaliza kuŵerenga mutu 10 [“Ngati Mlengi Amasamala, N’chifukwa Chiyani Pali Mavuto Choncho?”], ndinangoti, ‘Ili ndilo buku limene tikulifuna m’Japan!’ Ndikufuna kuti nkhani ya m’mutu umenewu ndiimvetsetse bwino lomwe kuti ndikaigwiritse ntchito kwambiri mu utumiki wakumunda.” Mkazi wina akuphunzitsa Baibulo mtsikana wina amene wakulira m’kachisi kumene bambo wake ndi wansembe. “Zinam’vuta kuti akhulupirire kuti Mlengi aliko. Mafotokozedwe a m’bukuli saumiriza munthu, koma mmenemo muli mfundo zenizeni, choncho ndikuganiza kuti ngakhale Abuda atha kuliŵerenga mosanyinyirika. Limatipangitsanso kuona kuti Yehova amatikonda.”

Munthu wina ku Mangalande anati: “Ndangolimaliza kumene buku la Creator ndipo ndikufuna kuyambiranso kuliŵerenga. Ndi buku losangalatsa bwanji! Munthu akaliŵerenga amangom’konda Yehova. Wina woyandikana naye nyumba ndam’patsa kale limodzi, ndipo atangoŵerenga mitu iŵiri anati, ‘Sinditha kulitula pansi, n’losangalatsa kwabasi.’ Ndikhulupirira kuti lidzathandiza anthu kum’dziŵa Mlengi wathu Wamkulu, ndi kum’konda.”

Mwamuna wina ku Maryland, U.S.A., anati: “Lakhaladi lolimbitsa mafupa anga auzimu! Ndikuganiza zogaŵira buku limeneli kwa onse amene ndimachita nawo malonda. Nthaŵi zina zimandivuta kuyamba ulaliki kwa anthu otanganidwa, ndi ophunzira otero. Koma ndi buku limeneli tsopano ndidzapeza njira yabwino ndi yogwira mtima.”

Mwachionekere, buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? lidzathandiza kwambiri anthu padziko lonse lapansi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Chithunzi chapachikuto, Eagle Nebula: J. Hester and P. Scowen (AZ State Univ.), NASA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena