Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/1 tsamba 9-14
  • Kuchingamira Dziko Latsopano la Mulungu la Ufulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchingamira Dziko Latsopano la Mulungu la Ufulu
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumasula Anthu Ake
  • Ufulu Wowona M’dziko Latsopano la Mulungu
  • Kuphunzitsa Kwapadziko Lonse Kopezera Moyo
  • Maufulu Abwino Ngakhale Tsopano Lino
  • Kumasula Ena ku Zikhulupiriro Zonyenga
  • Mfuneni Yehova
  • Zimene Ufumu wa Mulungu Udzachita
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Dziko Lopanda Nkhondo Posachedwa
    Galamukani!—1996
  • Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/1 tsamba 9-14

Kuchingamira Dziko Latsopano la Mulungu la Ufulu

‘[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.’​—CHIVUMBULUTSO 21:4.

1, 2. Kodi ndani yekha amene angabweretse ufulu wowona, ndipo Baibulo limatiphunzitsanji ponena za Iye?

MBIRI yatsimikizira mawu a mneneri Yeremiya kukhala owona akuti: ‘Njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’ Kodi ndani yekha amene angalongosole mapazi a munthu moyenera? Yeremiya anapitiriza kunena kuti: “Yehova, mundilangize.” (Yeremiya 10:23, 24) Inde, Yehova yekha ndiye angabweretse ufulu wowona wakumasuka ku mavuto amene akantha banja la anthu.

2 Baibulo liri ndi zitsanzo zambiri za kukhoza kwa Yehova kupereka ufulu kwa amene amamtumikira. ‘Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwachipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.’ (Aroma 15:4) Ziweruzo za Yehova motsutsana ndi kulambira konyenga nazonso zinalembedwa, ndipo zimakhala ‘zotichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.’​—1 Akorinto 10:11.

Kumasula Anthu Ake

3. Kodi Yehova anasonyeza motani kukhoza kwake kumasula anthu ake mu Igupto?

3 Chitsanzo cha kukhoza kwa Mulungu kupereka chiweruzo pakulambira konyenga ndi kumasula awo ochita chifuniro chake chinaperekedwa pamene anthu ake a m’nthaŵi zamakedzana anali muukapolo ku Igupto. Eksodo 2:23-25 amati: ‘Kulira kwawo kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo. Ndipo Mulungu anamva kubuula kwawo.’ M’chisonyezero chochititsa mantha cha ukulu wake pa milungu yonama ya Igupto, Mulungu Wamphamvuyonse anakantha mtunduwo ndi miliri khumi. Uliwonse wa miliriyo unalinganizidwira kuchititsa manyazi mulungu wosiyana wa Igupto, kusonyeza poyera kuti inali yonyenga ndi yosakhoza kuwathandiza Aigupto omwe anailambira. Motero Mulungu anamasula anthu ake ndi kuwononga Farao ndi magulu ake ankhondo pa Nyanja Yofiira.​—Eksodo, mitu 7 mpaka 14.

4. Kodi nchifukwa ninji sikunali kupanda chilungamo pamene Mulungu anawononga Akanani?

4 Pamene Mulungu analoŵetsa Aisrayeli m’Kanani, nzika zake zolambira ziŵanda zinawonongedwa ndipo dzikolo linapatsidwa kwa anthu a Mulungu. Monga Mfumu ya Chilengedwe Chonse, Yehova ali nako kuyenera kwakupereka ziweruzo zake pa zipembedzo zoluluzika. (Genesis 15:16) Ndipo ponena za chipembedzo cha Akanani, Bible Handbook la Halley limati: “Kulambiridwa . . . kwa milungu Yachikanani kunaphatikizapo mapwando akumwa onkitsa; akachisi awo anali nyumba zochitiramo uhule. . . . Akanani analambira, mwakudziloŵetsa m’chisembwere, monga dzoma lachipembedzo, pamaso pa milungu yawo; ndiyeno, mwakupha ana awo achisamba, monga nsembe kwa milungu yonama imeneyi. Kukuwonekera kuti, pamlingo waukulu, dziko la Kanani lidafikira kukhala monga Sodomu ndi Gomora pamlingo wa mtunduwo.” Iye akuwonjezera kuti: “Kodi chitaganya chauve chonyansa motero ndi nkhanza zake chirinso ndi kuyenera kulikonse kwakukhalapo? . . . Ofukula m’mabwinja amene amakumba m’mabwinja a mizinda ya Kanani amadabwa chifukwa chake Mulungu sanawawononge mwamsanga koposa ndi mmene anachitira.”

5. Kodi ndimotani mmene kumasula anthu ake akale kwa Mulungu kuliri chitsanzo cha nthaŵi yathu?

5 Nkhani zimenezi za kuwononga kwa Mulungu olambira onyenga, kupulumutsa anthu ake achipangano, ndi kuwapatsa dziko lolonjezedwa zimapereka chitsanzo cha zinthu zirinkudza. Zimasonya mtsogolo pafupipa pamene Mulungu adzaphwanya zipembedzo zonyenga za dziko lino ndi ozichirikiza ake ndipo adzaloŵetsa atumiki ake amakono m’dziko latsopano lachilungamo.​—Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14; 2 Petro 3:10-13.

Ufulu Wowona M’dziko Latsopano la Mulungu

6. Kodi ndimaufulu abwino koposa otani amene Mulungu adzapereka m’dziko latsopano?

6 M’dziko latsopano, Mulungu adzadalitsa anthu ake ndi mbali zonse zokongola za ufulu umene iye analinganizira banja la anthu. Padzakhala ufulu womasuka ku chitsenderezo cha magulu a ndale zadziko, azamalonda, ndi achipembedzo chonyenga. Padzakhala ufulu womasuka ku uchimo ndi imfa, ndipo anthu adzakhala ndi chiyembekezo chakukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29; Mateyu 5:5.

7, 8. Kodi kudzachitika zotani pobwezeretsa thanzi langwiro m’dziko latsopano?

7 Dziko latsopanolo litabwera, mwamsanga nzika zake zidzabwezeretsedwa mozizwitsa ku thanzi langwiro. Yobu 33:25 amati: ‘Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana, adzabwerera ku masiku aubwana wake.’ Yesaya 35:5, 6 amalonjeza kuti: ‘Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lirime la wosalankhula lidzaimba.’

8 Inu amene muli ndi matenda akuthupi chifukwa cha ukalamba kapena thanzi lofooka, tadziyerekezerani muli m’dziko latsopano m’limene mudzuka m’maŵa uliwonse muli wathanzi ndi wamphamvu. Makwinya anu asiira malo khungu losalala lathanzi​—simufunikiranso mafuta akhungu. Maso anu omwe ankawona mwachimbuuzi kapena akhungu akuwona bwino moti ngwee​—simufunikiranso mandala. Makutu anu atsegulidwa​—tayani zipangizo zothandiza kumvera. Miyendo yopuŵala yalimbitsidwa ndi kuumbika bwino​—tayani ndodo zoyenderazo, ndi mipando yamagudumu. Palibenso kudwala​—atayeni mankhwala onsewo. Chifukwa chake, Yesaya 33:24 akuneneratu kuti: ‘Ndipo wokhalamo sadzanena ine ndidwala.’ Akunenanso kuti: ‘Adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.’​—Yesaya 35:10.

9. Kodi ndimotani mmene nkhondo idzaletsedwera kunthaŵi zonse?

9 Palibe aliyense amene adzaperekedwa nsembe ku nkhondo. ‘[Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; Atentha magareta ndi moto.’ (Salmo 46:9) Zida za nkhondo sizidzaloledwanso ndi Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, Kristu Yesu, amene Yesaya 9:6 amamutcha ‘Kalonga wa Mtendere.’ Vesi 7 limawonjezera kuti: ‘Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.’

10, 11. Kodi mtendere wotheratu udzatanthauzanji ku dziko lapansi?

10 Lidzakhala dalitso lotani nanga kwa mtundu wa anthu, ndi dziko lapansi lino, kumasuka ku zida zankhondo! Eya, kufikira nthaŵi ino, zida zimene zinagwiritsiridwa ntchito m’nkhondo zapitazo zikuwonongabe anthu. M’dziko limodzi lokha, Falansa, akatswiri oposa 600 owononga mabomba aphedwa chiyambire 1945 pamene ankayesa kuwononga zophulika zotsalira m’nkhondo zapapitazo. Mkulu wa gulu lowononga mabomba la kumeneko anati: “Tidakapezabe mizinga yokhoza kuphulika ya m’nthaŵi ya Nkhondo ya Falansa ndi Prussia ya 1870. Pali nyanja zodzazidwa ndi mabomba oponya akupha a m’nthaŵi ya Nkhondo Yadziko ya I. Kaŵirikaŵiri, mlimi polima ndi talakita amaponda bomba lokumbiridwa pansi la m’Nkhondo Yadziko ya II ndipo kalanga ine, amathero pamenepo. Zinthu zimenezi ziri ponseponse.” Zaka ziŵiri zapitazo The New York Times inawonjezera ndemanga iyi: “M’zaka 45 chiyambire kutha kwa Nkhondo Yadziko ya II [timagulu towononga mabomba] tachotsa m’nthaka [ya Falansa] makombola a mfuti zazikulu okwanira mamiliyoni 16, mabomba 490,000 ndi mabomba okumbiridwa pansi pa madzi 600,000. . . . Malo aukulu wa [mahekitala] mamiliyoni ambiri adakali otchingidwa, okhala ndi zida zankhondo kufikira m’mawondo ndi ozingidwa ndi zikwangwani zimene zimachenjeza kuti: ‘Musagwire. Zimapha!’”

11 Ha, dziko latsopano lidzakhala losiyana chotani nanga! Aliyense adzakhala ndi nyumba yabwino, chakudya chochuluka, ndi ntchito yatanthauzo ndi yopindulitsa yosanduliza dziko lonse lapansi kukhala paradaiso. (Salmo 72:16; Yesaya 25:6; 65:17-25) Anthu kapena dziko lapansi, sadzaphulitsidwanso ndi mamiliyoni a zipangizo zophulika. Dziko latsopano loterolo nlimene Yesu anali nalo m’maganizo pamene ananena kwa mwamuna amene anasonyeza chikhulupiriro mwa iye kuti: “Udzakhala nane m’Paradaiso.”​—Luka 23:43, NW.

Kuphunzitsa Kwapadziko Lonse Kopezera Moyo

12, 13. Kodi ndintchito yophunzitsa yapadziko lonse yotani imene Yesu ndi Yesaya ananenera kuti idzachitika m’nthaŵi yathu?

12 Pamene munthu aphunzira ponena za dziko latsopano la Mulungu, amaphunziranso kuti m’tsiku lathu, Yehova wapanga mpingo wapadziko lonse wolinganizidwira kulambira kowona. Udzakhala chitima cha dziko latsopano, ndipo Mulungu akuugwiritsira ntchito tsopano kuphunzitsa ena zifuniro zake. Gulu Lachikristu limeneli likuchita ntchito yakuphunzitsa yapadziko lonse yamtundu ndi ukulu umene sunakhalepo ndi kalelonse. Yesu ananeneratu kuti zimenezi zikachitika. Iye anati: “Mbiri yabwino imeneyi yaufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14, NW.

13 Yesaya nayenso ananena za ntchito yophunzitsa yapadziko lonse imeneyi kuti: ‘Ndipo padzakhala masiku otsiriza [m’nthaŵi yathu], kuti phiri la nyumba ya Yehova [kulambiridwa kwake kokwezedwa] lidzakhazikika . . . mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, . . . ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.’​—Yesaya 2:2, 3.

14. Kodi anthu a Mulungu tingawazindikire motani lerolino?

14 Motero, ntchito yapadziko lonse ya kulalikira za Ufumu wa Mulungu iri umboni wamphamvu wakuti tiri pafupi ndi mapeto a dongosolo la zinthu liripoli ndikuti ufulu wowona wayandikira. Amene amafikira anthu ndi uthenga wopereka chiyembekezo wonena za dziko latsopano la Mulungu amalongosoledwa pa Machitidwe 15:14 monga “anthu a dzina la [Mulungu].” Kodi ndani amene akutchedwa ndi dzina la Yehova ndi kupereka umboni wapadziko lonse ponena za Yehova ndi Ufumu wake? Mbiri ya m’zaka za zana la 20 ikuyankha: Mboni za Yehova zokha. Lerolino izo zafika chiŵerengero choposa mamiliyoni anayi m’mipingo yoposa 66,000 kuzungulira dziko lonse.​—Yesaya 43:10-12; Machitidwe 2:21.

15. Ponena za ndale zadziko, kodi ndimotani mmene tingazindikirire atumiki owona a Mulungu?

15 Umboni wina wakuti Mboni za Yehova zikukwaniritsa maulosi onena za ntchito yolalikira Ufumu ukuwonedwa pa Yesaya 2:4 pamene pamati: ‘Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.’ Chotero amene akuchita ntchito yapadziko lonse yolalikira ponena za ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu ayenera ‘kusaphunziranso nkhondo.’ Yesu ananena kuti iwo sayenera kukhala “a dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Izi zitanthauza kuti iwo sayenera kuloŵa m’ndale zadziko, kusakhala kumbali iriyonse m’mikangano ndi nkhondo za mitundu. Kodi ndani amene sali mbali ya dziko amene samaphunziranso nkhondo? Apanso, mbiri ya m’zaka za zana la 20 ikuchitira umboni: Mboni za Yehova zokha.

16. Kodi ntchito ya Mulungu yakuphunzitsa yapadziko lonse idzachitidwa bwino kotheratu motani?

16 Ntchito yakuphunzitsa yapadziko lonse yochitidwa ndi Mboni za Yehova idzapitirizabe ngakhale pambuyo pakuwonongedwa kwa dziko loipa liripoli ndi Mulungu. Yesaya 54:13 amati: “Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.” Chotero kuphunzitsa kumeneku kudzachitidwa bwino kotheratu monga momwe Yesaya 11:9 amanenera kuti: “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” Maphunzirowo adzapitirizabe osati kokha kwa amene adzapulumuka mapeto a dziko lakale lino, ndi ana amene angabadwe m’dziko latsopano, komanso kwa mabiliyoni amene adzabwezeretsedwa ku moyo m’chiukiriro. Pomalizira pake, munthu aliyense wokhala padziko lapansi adzaphunzitsidwa kugwiritsira ntchito ufulu wake wa kusankha m’njira yabwino mkati mwa malire a malamulo a Mulungu. Chotulukapo? ‘Ofatsa adzalandira dziko lapansi, nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.’​—Salmo 37:11.

Maufulu Abwino Ngakhale Tsopano Lino

17. Kodi Mose anauza anthu a Mulungu akale kuchitanji?

17 Pamene Aisrayeli akale anali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose analankhula kwa iwo nati: ‘Tawonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati pa dziko limene mumkako kulilandira likhale lanulanu. Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziŵitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira. Pakuti mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pawo monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene paliponse timaitanira Iye?’​—Deuteronomo 4:5-7.

18. Kodi ndimaufulu abwino otani amene atumiki a Mulungu amawapeza ngakhale tsopano lino?

18 Lerolino mamiliyoni amene amalambira Yehova alinso pafupi kuloŵa m’dziko lolonjezedwa​—dziko latsopano. Chifukwa chakuti amamvera malamulo a Mulungu, iye amakhala pafupi nawo ndipo ali olekana ndi anthu ena onse. Mulungu wawamasula kale ku malingaliro achipembedzo chonyenga, kusankhana fuko, kugwiritsira ntchito mankhwala oletsedwa, kusankhana mtundu, nkhondo, ndi mliri wa matenda opatsirana mwakugonana. Ndiponso, iye wawagwirizanitsa m’gulu la abale lapadziko lonse la chikondi chosasweka. (Yohane 13:35) Iwo samawopa mtsogolo koma ‘amaimba ndi mtima wosangalala.’ (Yesaya 65:14) Ndimaufulu abwino chotani nanga amene iwo amasangalala nawo ngakhale tsopano lino mwakutumikira Mulungu monga Wolamulira!​—Machitidwe 5:29, 32; 2 Akorinto 4:7; 1 Yohane 5:3.

Kumasula Ena ku Zikhulupiriro Zonyenga

19, 20. Kodi anthu amamasulidwa motani ndi zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za mkhalidwe wa akufa?

19 Anthu ambiri amene Mboni za Yehova zimalalikirako nawonso amafikira pakuwapeza maufulu ameneŵa. Mwachitsanzo, m’maiko kumene anthu amalambira makolo akufa, Mboni za Yehova zimadziŵitsa ena kuti akufa samakhala ndi moyo kwina kulikonse ndipo sangavulaze amoyo. Mbonizo zimasonyeza Mlaliki 9:5, pamene pamati ‘amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.’ Amasonyezanso Salmo 146:4, pamene pamati munthu atafa ‘amabwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitaika.’ Choncho Baibulo limasonyeza kuti kulibe chimzukwa chamzimu kapena moyo wosakhoza kufa umene umachiritsa kapena kuwopseza amoyo. Chifukwa chake, palibe kufunikira kwakuwononga ndalama zopezedwa movutikira kugulira mautumiki a asing’anga kapena ansembe.

20 Chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo choterocho chimamasula anthu ku ziphunzitso zonyenga za moto wa helo ndi purigatoriyo. Pamene anthu aphunzira chowonadi cha Baibulo chakuti akufa samadziŵa kanthu, monga ngati kuti ali m’tulo tatikulu, iwo samavutikanso ndi zimene zinachitika kwa okondedwa awo akufa. Mmalomwake, amayang’ana mtsogolo kunthaŵi yodabwitsa imene mtumwi Paulo ananena pamene anati: ‘Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.’​—Machitidwe 24:15.

21. Mosakaikira konse, kodi ndani amene adzaphatikizidwa mwa oukitsidwawo, ndipo mwachiwonekere kodi iwo adzachita motani?

21 M’chiukiriro chimenecho akufa adzabwezeretsedwa ku moyo padziko lapansi atamasulidwa kosatha ku imfa yacholoŵa ya kwa Adamu. Mosakaikira oukitsidwawo adzaphatikizapo ana operekedwa nsembe kwa milungu Yachikanani, monga Moleki, anyamata operekedwa nsembe kwa milungu ya Aaztec, ndi mamiliyoni osaŵerengeka operekedwa nsembe kwa mulungu wankhondo. Ha, adzazizwa nadzasangalala chotani nanga awo amene adali mikole ya zikhulupiriro za chipembedzo chonyenga! Panthaŵiyo, oukitsidwawo akhoza kufuula mokondwera kuti: ‘Imfa, miliri yako irikuti? Chiwonongeko chako chirikuti?’​—Hoseya 13:14.

Mfuneni Yehova

22. Ngati tifuna kukhala m’dziko latsopano la Mulungu, kodi tiyenera kumakumbukiranji?

22 Kodi mumafuna kukhalamo m’dziko latsopano lolungama la Mulungu, m’mene mudzakhala ufulu wowona? Ngati nditero, labadirani mawu a pa 2 Mbiri 15:2 akuti: ‘Yehova ali nanu, mukakhala ndi iye, mukamfuna iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.’ Ndipo kumbukirani kuti zoyesayesa zanu zowona mtima zakuphunzira ponena za Mulungu ndi kumkondweretsa sizidzanyalanyazidwa. Ahebri 11:6 amanena kuti Mulungu ali ‘wobwezera mphotho kwa iwo akumfuna iye.’ Ndipo Aroma 10:11 amati: ‘Palibe aliyense amene akhulupirira iye, adzachita manyazi.’

23. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchingamira dziko latsopano la Mulungu la ufulu?

23 Dziko latsopano la Mulungu la ufulu wowona layandikira ndithu likuwonekera m’chizimezime. M’menemo ‘cholengedwa chomwe chidzamasulidwa kuukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’ Ndipo ‘[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.’ (Aroma 8:21; Chivumbulutso 21:4) Pamenepo atumiki a Yehova onse adzatukula mitu yawo ndipo mwachisangalalo adzachingamira dziko latsopano la Mulungu la ufulu mwakudzuma kuti, ‘Zikomo, Yehova, kaamba kakuti wadza ufulu wowona potsirizira pake!’

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi Yehova anasonyeza motani kukhoza kwake kumasula anthu ake?

◻ Kodi ndimaufulu abwino koposa otani amene adzakhalapo m’dziko latsopano la Mulungu?

◻ Kodi ndimotani mmene Yehova akuphunzitsira anthu kuti akapeze moyo?

◻ Kodi ndimaufulu otani amene anthu a Mulungu akusangalala nawo ngakhale tsopano lino mwakutumikira Yehova?

[Chithunzi patsamba 10]

Yehova anasonyeza ukulu wake pa milungu yonyenga ya Igupto, namasula alambiri ake

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Lerolino, atumiki owona a Mulungu amazindikiridwa mwakuchita ntchito yake yophunzitsa yapadziko lonse ndi mwakutchedwa ndi dzina lake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena