Lipoti la Olengeza Ufumu
Kufola Gawo Lakutali m’Paraguay Kukubala Zipatso
NTHAMBI ya Watch Tower Society ya ku Paraguay imazindikira bwino lomwe kufunika kwakulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu m’mbali zonse za gawo lake. (Machitidwe 1:8) Ino ndinthaŵi yakuti anthu onse aphunzire ponena za Ufumu ndi kutumikira Yehova asanawononge dongosolo loipa liripoli mu ‘chisautso chachikulu’ chikudzacho. (Mateyu 24:21, 22) Zokumana nazo zotsatirazi zimasonyeza zimene zikuchitidwa kuthandiza anthu okhala m’magawo osagaŵiridwa. Nthambiyo ikusimba motere:
Makonzedwe anapangidwa akufola magawo onse osagaŵiridwa mwakutumako apainiya apadera apakanthaŵi. M’miyezi ya November mpaka January ya chaka chautumiki cha 1990, abale ndi alongo 39 anafola mizinda ndi matauni aang’ono zana limodzi kumene sikunakhalebe ofalitsa Aufumu. Iwo anakhoza kugaŵira mabuku 6,119, timabuku 4,262, ndi magazini 5,144. Monga chotulukapo cha ntchito imeneyi, timagulu tatsopano ta ofalitsa tikukhazikitsidwa.
◻ Mkazi wina analandira kuchokera kwa mlongo yemwe ndimpainiya wogwira ntchito m’gawo losagaŵiridwa bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Mpainiyayo anapereka mwaŵi kwa mkaziyo wakuphunzira naye Baibulo, ndipo analola mokondwa. Pamene mpainiyayo anapitako kachiŵiri, anapeza kuti womuyembekezera sanali dona uja yekha, komanso mwamuna wake ndi ana awo khumi. Paulendo wotsatira, nkupeza kuti banjalo pamodzi ndi mabwenzi awo ndi anansi ankayembekezera phunziro Labaibulo! Mkaziyo anawamema, akunena kuti phunzirolo linali labwino ndikuti chiyembekezo ndi madalitso zimene Yehova akuzipereka nzodabwitsa. Palibe munthu aliyense amene anamuuzapo zimenezi, chotero analingalira kuti anansi ake nawonso ndi mabwenzi ake anayenera kumvako mbiri yabwino imeneyi.
Nthaŵi zonse pamene mpainiyayo ankachititsa phunziro, panali kupezeka anthu ambiri kotero kuti anawoneka ngati kampingo ndithu. Anthu okondwerera ameneŵa anafunsa mafunso ambiri ndipo ankayankhapo paphunzirolo. Pamene mpainiyayo anawauza kuti atalifola gawo lonselo, iye ndi anzake akapita kumalo atsopano, donayo anafunsa modera nkhaŵa kuti nanga iwo akachitanji paokha. Makonzedwe anapangidwa ndi abale ampingo wapafupi akupitiriza kuphunzira nawo. Tsopano apainiya apadera agaŵiridwa kukathandiza okondwerera onga nkhosa ameneŵa.
◻ Pamene ankafikira nyumba ndi nyumba m’gawo lina losagaŵiridwa, mlongo wina yemwe ndimpainiya anapeza mwamuna yemwe anali ndi bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya limene analigula zaka khumi zapitazo. Chichokere pamenepo sanawonane ndi Mboni ya Yehova iriyonse. Komabe, iye anadziŵa kuti Yehova, amene adamutcha Yehova wa makamu, ndiye Mulungu wowona yekha ndikuti Iye yekhayo ndiye ayenera kulambiridwa. Iye anadziyambira kulankhula ponena za Yehova kwa aliyense amene anadziŵa. Ndipotu, mlungu uliwonse anayenda mtunda wa makilomita atatu kukachezetsa okwatirana okondwerera kulankhula nawo ponena za Mulungu, chifukwa chakuti monga momwe iyemwini ananenera kuti, ‘Ngati ndileka kuwachezera, adzamuiŵala Yehova.’ Kuwonjezera pa okwatirana ameneŵa, panalinso ena khumi amene anafuna kuphunzira Baibulo—onsewo chifukwa chakuti munthu wokondwerera ameneyo anawalalikira.
Modabwitsa, patatsala masiku ochepa mpainiyayo asanamfikire, mwamuna mmodzimodziyu analetsa wansembe wakumaloko ndi anthu ake kuloŵa m’nyumba mwake ndi fano la namwali, nawauza kuti iye samakhulupirira mafano. Wansembeyo anakwiya kwambiri. Usikuwo mwamunayo anapemphera kwa Yehova kaamba ka chithandizo. Motero tangoyerekezerani mmene anakhalira wokondwa ndi wachimwemwe pamene mpainiyayo anamfikira! Mwamsanga makonzedwe anapangidwa aphunziro Labaibulo lokhazikika, ndipo mwamunayo akupitabe patsogolo m’mayanjano ake ndi gulu lateokratiki.
Ndithudi, Yehova akudalitsa ntchito yosonkhanitsa m’Paraguay pamene abale akuyesayesa zolimba kupereka umboni wokwanira m’magawo osagaŵiridwa ameneŵa.—Mateyu 24:14.