Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/15 tsamba 31
  • Chilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilengezo
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chithandizo ku Makomiti a Bungwe Lolamulira
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Ntchito Zake
    Nsanja ya Olonda—2008
  • ‘Opatsidwa’ Ali Mphatso ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Ndi Ndani Akutsogolera Anthu a Mulungu Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/15 tsamba 31

Chilengezo

Chithandizo ku Makomiti a Bungwe Lolamulira

Ziŵalo za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, pakali pano zokwanira 12, zikupitiriza kutumikira mokhulupirika m’magawo awo. Izo nthaŵi zonse zimayamikira kwambiri ziŵalo zokhulupirika za “khamu lalikulu” lomakulakulabe kaamba ka chichirikizo chawo chachangu. (Chivumbulutso 7:9, 15) Polingalira za kuwonjezereka kwakukulu kwa padziko lonse, ino ikuwonekera kukhala nthaŵi yake yakupereka chithandizo chowonjezereka ku Bungwe Lolamulira. Chifukwa chake kwalingaliridwa kuitanitsa othandiza ochulukirapo, kwenikweni akhamu lalikulu, kukhala ndi phande m’misonkhano ya iriyonse ya Makomiti a Bungwe Lolamulira, ndiko kuti, Komiti ya Ogwira Ntchito, Yofalitsa, Yautumiki, Yophunzitsa, ndi Yolemba. Chotero, chiŵerengero cha opezeka m’misonkano ya iriyonse ya makomiti ameneŵa chidzawonjezeka kufika pa asanu ndi aŵiri kapena asanu ndi atatu. Pansi pa chitsogozo cha ziŵalo za Bungwe Lolamulira za makomiti, othandizira ameneŵa adzakhala ndi phande m’zokambitsirana ndipo adzachita maasainimenti osiyanasiyana omwe komiti idzaŵagaŵira. Makonzedwe atsopano ameneŵa adzayamba pa May 1, 1992.

Kwa zaka zambiri tsopano, chiŵerengero cha otsalira a Mboni zodzozedwa chakhala chikutsika, pamene chiŵerengero cha khamu lalikulu chawonjezereka kuposeratu pazimene tidayembekezera. (Yesaya 60:22) Timamthokoza chotani nanga Yehova kaamba ka kufutukuka kodabwitsa kumeneku! Pamene dzina latsopano, Mboni za Yehova, linalandiridwa ndi chimwemwe mu 1931, chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu chinali 39,372, ndipo ambiri a iwoŵa anadzisonyeza kukhala abale odzozedwa a Kristu. (Yesaya 43:10-12; Ahebri 2:11) Pambuyo pa zaka makumi asanu ndi limodzi, mu 1991, chiŵerengero chapamwamba cha dziko lonse cha ofalitsa chinali 4,278,820, mwa amene 8,850 okha ndiwo anadzisonyeza kukhala otsalira odzozedwa. Malinga ndi chiyembekezo Chamalemba, “khamu lalikulu” tsopano limaposa chiŵerengero cha otsalira a “kagulu ka nkhosa” kuposa pa 480 kwa 1. (Luka 12:32; Chivumbulutso 7:4-9) Posamalira zabwino za Ufumu zomawonjezereka, otsalirawo amafunikiradi ndipo amayamikira chigwirizano ndi chichirikizo zoperekedwa ndi khamu lalikulu.

Monga momwe kope lino la Nsanja ya Olonda lafotokozera, pali gulu limene likutumikira ndi Israyeli wauzimu lerolino limene limafanana ndi Anetini ndi ana a akapolo a Solomo omwe anabwerera kuchokera kuukapolo wa ku Babulo pamodzi ndi Ayuda otsalira; osakhala Aisrayeli amenewo anaposadi chiŵerengero cha Alevi omwe anabwerera. (Ezara 2:40-58; 8:15-20) ‘Opatsidwa’ ochokera mwa khamu lalikulu la lerolino ali amuna Achikristu ofikapo omwe akhala ndi chidziŵitso chachikulu kaamba ka kusamalira mathayo auyang’aniro panthambi, m’ntchito yoyendayenda, ndi m’mipingo 66,000 yokhazikitsidwa tsopano padziko lonse lapansi.

Posachedwapa, Sukulu za Utumiki Waufumu zinachitidwa padziko lonse zikumapereka malangizo kwa oyang’anira ndi atumiki otumikira owathandizira. Mu United States mokha, oyang’anira okwanira 59,420 anapezekapo. Chotero “akulu” ameneŵa anakonzekeretsedwa kuchita mathayo awo bwino koposa.​—1 Petro 5:1-3; yerekezerani ndi Aefeso 4:8, 11.

Ku malikulu a Mboni za Yehova ku Brooklyn, ‘opatsidwa’ ena atumikira kwa zaka zambirimbiri. Iwowo amaphatikizapo oyang’anira okhwima a khamu lalikulu omwe apeza chuma cha maluso ndi chidziŵitso. Chifukwa chake, Bungwe Lolamulira lasankha angapo mwa oyang’anira oterowo kuti akhale othandiza m’misonkhano ya makomiti a Bungwe Lolamulira. Ameneŵa sali kwenikweni amuna omwe akhala muutumiki kwanthaŵi yaitali koposa. Mmalomwake, iwo ngofikapo, amuna achidziŵitso okhala ndi ziyeneretso zakupereka chithandizo m’magawo akutiakuti. Kugaŵiridwa kwawo kuti agwire ntchito pamodzi ndi komiti inayake sikumawakwezera pamalo apadera. Iwo ali monga momwe Yesu ananenera kwa ophunzira ake, “nonse muli abale.” (Mateyu 23:8) Komabe, amuna ameneŵa adzaikiziridwa zambiri, ndipo motero ‘zambiri zidzafunidwa’ kwa iwo.​—Luka 12:48.

Tikusangalala m’ligubo lomka patsogolo la gulu la Yehova la lerolino. Kwa zaka khumi zapitazo, pakhala pafupifupi chiwonjezeko cha 100 peresenti pa chiŵerengero cha ochita utumiki wakumunda, mogwirizana ndi ulosi wonena za Davide Wamkulu, Yesu Kristu wakuti: “Kuwonjezereka kwa boma lake ndi mtendere kudzakhala kopanda mapeto.” (Yesaya 9:7, King James Version) Mofanana ndi mmene Anetini anagwirira ntchito pamodzi ndi ansembe m’kukonzanso malinga a Yerusalemu, leronso ulosi wonena za gulu la Yehova ukukwaniritsidwa: “Alendo adzamanga malinga ako.” (Yesaya 60:10; Nehemiya 3:22, 26) Anetini amakono akuyamikiridwa ndi changu chomwe akuchisonyeza m’kumanga kulambira kowona, akuthandiza “ansembe a Yehova” m’ntchito iriyonse kapena utumiki umene angagaŵiridwe m’gulu la Yehova la padziko lonse.​—Yesaya 61:5, 6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena