Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/15 tsamba 3-4
  • Kodi Kwenikweni Uthenga Wabwino Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kwenikweni Uthenga Wabwino Nchiyani?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Uthenga Wabwino Nchiyani?
  • Chimene Chiri Uthenga Wabwino
  • Uthenga Womvekera Bwino
  • Kodi Umene Ena Amati Uthenga Wabwino wa Yudasi N’chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Uthenga Wabwino Ungakupindulitseni Motani?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Ngale Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Luka
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Nkhani Zokhudza Moyo wa Yesu Zinalembedwa Liti?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/15 tsamba 3-4

Kodi Kwenikweni Uthenga Wabwino Nchiyani?

MKATI mwa nyengo ya Krisimasi, anthu m’maiko ambiri amaumva, ndipo ngakhale kuulankhula iwo eni, Uthenga Wabwinowo. Liwulo nlozoloŵereka kwambiri, koma kodi liri ndi tanthauzo lowonjezereka kuposa mmene ambiri amalingalirira? Kodi Uthenga Wabwino ungatanthauze kanthu kena kapadera kabwino kwa inu ndi okondedwa anu?

“Uthenga Wabwino” umatanthauza “mbiri yabwino,” ndipo ndithudi, mbiri yabwino njosangalatsa osati kokha panthaŵi ya Krisimasi koma panthaŵi iriyonse. Komabe Uthenga Wabwinowo suli kokha mbiri yabwino iriyonse. Uwo uli mbiri yabwino yapadera yochokera ku magwero otsimikizirika okhudza nkhani yakutiyakuti. M’chenicheni, uwo uli uthenga umene Mulungu wausankha kuti ulengezedwe kwa anthu onse.

Eugênio Salles akibishopu wa ku Rio de Janeiro, Brazil, analankhula za mbiri yabwino imeneyo pamene anachichiza kuti: “Tiyenera kuchita mogwirizana ndi Uthenga Wabwino ndipo osati monga mwa ziganizo zathu.” Akibishopuyo analondola. Komabe, kuchita mogwirizana ndi Uthenga Wabwino, kumafunikira kuti tidziŵe chimene Uthenga Wabwinowo uli. Kodi tingaudziŵe motani? Ndipo kodi kuchita mogwirizana ndi Uthenga Wabwino kudzatithandiza motani?

Kodi Uthenga Wabwino Nchiyani?

Kaŵirikaŵiri mpangidwe wa Uthenga Wabwino umamvedwa molakwa. Mu 1918 bungwe la Federal Council of the Churches of Christ mu Amereka linatamanda Chigwirizano cha Mitundu chimene tsopano kulibeko kukhala chisonyezero cha ndale zadziko cha Ufumu wa Mulungu padziko lapansi ndipo linalengeza kuti “magwero ake anali Uthenga Wabwino.” Chigwirizanocho chinalephera momvetsa chisoni m’chonulirapo chake chakusungitsa mtendere. Mwachiwonekere, bungwelo linalakwa. Chigwirizano cha Mitundu chinalibe unansi uliwonse ndi Uthenga Wabwino.

M’zaka zaposachedwapa, ochilikiza nthanthi yaufulu atchula momasuka liwulo Uthenga Wabwino polankhula za ziganizo zawo zokhudza kusintha kwandale zadziko kapena kwamakhalidwe a anthu. Mwakutero anyalanyaza chimene chiridi Uthenga Wabwino. Magazini a ku Brazil Veja anati: “Tchalitchi cha Katolika chinayamba kuyanja ufumu woyanja makhalidwe a anthu, chikumanyalanyaza zosoŵa zauzimu za okhulupirika ake. Kaŵirikaŵiri awo amene anafunafuna liwu lakuti Mulungu mu ulaliki anapezamo kokha zigomeko zosyasyalika zotsutsana ndi kuchitira tsankho anthu.”

Kuwongolera mikhalidwe ya moyo kapena kusinthidwa kwa madongosolo andale zadziko kungakhale mbiri yabwino kwa ena. Komabe, imeneyo sindiyo mbiri yabwinoyo, Uthenga Wabwinowo. Akumavomereza kulephera kwa tchalitchi chake kulalikira umene ulidi Uthenga Wabwino, bishopu wina anati: “Tinanyalanyaza chiphunzitso chauzimu cha okhulupirika athu kuyambira m’ma 60 chifukwa chakudodometsedwa ndi kukondetsa zinthu zakuthupi kwachiphunzitso chathu.”

Lipoti lina mu magazini a nyuzi a United States a Time likupereka lingaliro lakuti nawonso Aprotestanti asochera pa Uthenga Wabwino. Magaziniwo akuti: “Sikokha kuti zipembedzo zamakolo zikulephera kumveketsa uthenga wawo; izo ziri zosatsimikizira kwambiri chimenedi chiri uthengawo.” Kodi uthenga wawo uyenera kukhala chiyani? Kodi Uthenga Wabwino nchiyani?

Chimene Chiri Uthenga Wabwino

Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary imafotokoza “Uthenga Wabwino” kukhala “uthenga wonena za Kristu, ufumu wa Mulungu, ndi chipulumutso.” Liwulo “uthenga wabwino” lafotokozedwanso kukhala “kumasuliridwa kwa uthenga Wachikristu (uthenga wamakhalidwe a anthu)”; “uthenga kapena ziphunzitso za mphunzitsi wachipembedzo.” Kodi mafotokozedwe onsewa ngolondola? Ayi, siali ngati tikulankhula za Uthenga Wabwinowo. Uthenga Wabwino weniweni ngwochokera m’Baibulo; chifukwa chake, oyamba okha amafotokozedwe atatu amenewa ngolondola. Aŵiri omalizira amangosonyeza kokha njira imene liwu lakuti “uthenga wabwino” lafikira pakugwiritsiridwa ntchito lerolino.

Mogwirizana ndi lingaliro limeneli, Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words imanena kuti m’Malemba Achikristu Achigiriki (“Chipangano Chatsopano”), Uthenga Wabwino “umatanthauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi wa chipulumutso kupyolera mwa Kristu, wolandiridwa mwa chikhulupiriro, pamaziko a imfa Yake yopereka dipo.” Kuli kofunika kuzindikira zimenezi chifukwa chakuti ganizo lolondola la mbiri yabwino yowona nlogwirizanitsidwa kwambiri ndi ubwino wathu wamakono ndi chimwemwe chathu chamtsogolo.

Uthenga Womvekera Bwino

Monga momwe bukhu lamaumboni lotchulidwalo likusonyezera, Uthenga Wabwino ngwogwirizana kwambiri ndi Yesu Kristu​—kotero kuti zolembedwa zinayi za Baibulo za moyo wake padziko lapansi zimatchedwa Mauthenga Abwino anayi. Kuyambira pachiyambi penipeni pa moyo wake waumunthu, mbiri yonena za Yesu inali mbiri yabwino. Polengeza za kubadwa kwake, mngeloyo anati: “Tawonani! Ndikulengeza kwa inu mbiri yabwino [kapena, uthenga wabwino] wachisangalalo chachikulu chimene anthu onse adzakhala nacho, chifukwa chakuti wakubadwirani inu lero Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.”​—Luka 2:10, 11, NW.

Yesu wobadwa chatsopanoyo akakula kukhala Kristuyo, Mesiya wolonjezedwayo. Iye akavumbula chifuno cha Mulungu cha chipulumutso, kupereka moyo wake wangwiro waumunthu mmalo mwa anthu, akaukitsidwa, ndiyeno kukhala Mfumu yosankhidwa ya Ufumu wa Mulungu. Ndithudi iri mbiri yabwino! Ndicho chifukwa chake uthenga wonena za iye umatchedwa Uthenga Wabwino.

Mkati mwa uminisitala wake wachidule padziko lapansi, Yesu anali wachangu kwambiri m’kulalikira mbiri yabwino. Timaŵerenga mu Uthenga Wabwino wa Mateyu kuti: “Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa ufumuwo.” (Mateyu 9:35) Kulalikira kwake sikunali chabe kopangitsa anthu kupeza bwinopo. Marko akusimba Yesu kukhala akunena kuti: “Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.” (Marko 1:15) Inde, awo amene analabadira ndi kumvera uthenga wabwino anapeza kuti unasintha miyoyo yawo.

Pambuyo pa imfa ya Yesu, otsatira ake anapitirizabe kulalikira Uthenga Wabwino. Sikokha kuti iwo analankhula za Ufumuwo koma anawonjezera mbiri yachimwemwe yakuti Yesu anaukitsidwira ku dzanja lamanja la Mulungu kumwamba ndipo anali atalipirira anthu mtengo wa moyo wake wangwiro waumunthu. Monga wosankhidwa ndi Mulungu kulamulira padziko lapansi monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, iye akakhala Woimira wa Mulungu m’kuwononga adani a Mulungu ndi m’kubwezeretsa dziko lapansi kukhala paradaiso.​—Machitidwe 2:32-36; 2 Atesalonika 1:6-10; Ahebri 9:24-28; Chivumbulutso 22:1-5.

Lerolino, mbiri yabwino ikuphatikizapo chinthu chowonjezereka. Mogwirizana ndi umboni wonse waulosi wokwaniritsidwa, Yesu tsopano anaikidwa pampando wachifumu, ndipo ife tikukhala ndi moyo m’masiku otsiriza adongosolo lino lazinthu. (2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 12:7-12) Nthaŵi imene Ufumuwo udzachitapo kanthu motsutsana ndi adani a Mulungu ikuyandikira mofulumira. Kodi ndi mbiri yabwino kwambiri iti imene ingakhaleko koposa imeneyi?

Tidzawona m’nkhani yotsatira mmene Uthenga Wabwino uliri wamphamvu. Unathandiza mkazi wina kuwonjoka amene anali atakodwa mumsampha wakuchita matsenga. Unathandiza mwamuna wina woikidwa m’ndende chifukwa chaumbala kupeza chimwemwe. Ndipo udzakupindulitsaninso kwambiri​—ngati mumvetsera ndi kulabadira mbiri yabwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena