Ngale Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Luka
MWANA wa Yehova, Yesu Kristu, ndiwodziŵika bwino lomwe kukhala wachifundo. Chotero ndimoyenerera chotani nanga, kuti mlembi wa Uthenga Wabwino Luka ayenera kugogomezera chisoni, chifundo, ndi kukomerana mtima! Kwa Ayuda ndi Akunja mofananamo, iye analemba cholembera chogwira mtima cha moyo wa Yesu pa dziko lapansi.
Mbali zina za Uthenga Wabwino umenewu zimasonyeza kuti ngwazi yophunziradi ndi imene inaulemba uwo. Mwachitsanzo, iwo uli ndi mawu oyamba olembedwa mwaluso ndi manenedwe akuya. Nsonga zoterozo zimagwirizana ndi chenicheni chakuti Luka anali sing’anga wophunzira bwino lomwe. (Akolose 4:14) Ngakhale kuti iye sanakhale wokhulupirira kufikira Yesu atamwalira, iye anapitapo ndi Paulo ku Yerusalemu pambuyo pa ulendo wachitatu waumishonale wa mtumwiyo. Chotero, pambuyo pa kumangidwa kwa Paulo kumeneko ndi kuponyedwa m’ndende ku Kaisareya, wofufuza mwaluso ameneyu anakhoza kusonkhanitsa nkhani mwa kufunsa mboni zowona ndi maso ndi kufufuza m’zolembera za poyera. (1:1-4; 3:1, 2) Uthenga wake Wabwino uyenera kukhala unalembedwera ku Kaisareya m’nthaŵi ya kubindikiritsidwa kwa mtumwiyo kwa zaka ziŵiri kumeneko, chifupifupi 56-58 C.E.
Zochitika Zina Zapadera
Zozizwitsa za Yesu zosachepera pa zisanu ndi chimodzi ziri zapadera mu Uthenga Wabwino wa Luka. Izi ndizo: kugwira nsomba kozizwitsa (5:1-6); kuukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye ku Nayini (7:11-15); kuchiritsa mkazi wopeteka (13:11-13); kuchiritsa mwamuna wambulu (14:1-4); kuchiritsa akhate khumi (17:12-14); ndi kubwezeretsa khutu la kapolo wa mkulu wansembe.—22:50, 51.
Chapaderanso m’cholembera cha Luka ndicho mafanizo ena a Yesu. Awa amaphatikizapo: amangawa aŵiri (7:41-47); Msamariya wachifundo (10:30-35); mtengo wamkuyu wosabala (13:6-9); chakudya chamadzulo chachikulu (14:16-24); mwana woloŵerera (15:11-32); munthu wachuma ndi Lazaro (16:19-31); ndi mkazi wamasiye ndi woweruza wosalungama.—18:1-8.
Zochitika Zokhudza Mtima
Sing’anga Luka anasonyeza kudera nkhaŵa kwake kwa akazi, ana, ndi okalamba. Ndiye yekha amene anatchula kusabala kwa Elisabeti, kukhala kwake ndi pakati, ndi kubadwa kwa Yohane. Ndi Uthenga Wabwino wake wokha umene unasimba za kuwonekera kwa mngelo Gabrieli kwa Mariya. Luka anasonkhezeredwa kunena kuti khanda la Elisabeti linadumpha m’mimba mwake pamene Mariya analankhula kwa iye. Ndiye yekha amene anasimba za mdulidwe wa Yesu ndi kuperekedwa kwake ku kachisi, kumene Iye anawonedwa ndi Simeoni wokalamba ndi Anna. Ndipo uli Uthenga Wabwino wa Luka umene umatipatsa chidziŵitso chonena za ubwana wa Yesu ndi Yohane Mbatizi.—1:1–2:52.
Pamene Luka analemba za mkazi wamasiye wovutitsidwa ndi chisoni wa ku Nayini yemwe anaferedwa mwana wake yekha wamwamuna, ananena kuti Yesu “anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye” ndipo kenaka nabwezeretsa mwamuna wachichepereyo. (7:11-15) Chosimbidwa mu Uthenga Wabwino wa Luka wokha, ndi chotenthetsanso maganizo, ndicho chochitika chophatikizapo Zakeyu, wosonkhetsa misonkho wamkulu. Pokhala wamfupi, iye anakwera mumtengo kuti awone Yesu. Zinali zodabwitsa chotani nanga pamene Yesu adati akakhala ku nyumba ya Zakeyu! Luka akusonyeza kuti kuchezetsako kunali dalitso lalikulu kwa wochereza wachimwemweyo.—19:1-10.
Wolembedwa ndi Sing’anga
Uthenga Wabwino umenewu uli ndi matchulidwe kapena mawu ambiri okhala ndi matanthauzo kapena zodziŵika za mankhwala. Mawu ameneŵa sanagwiritsiridwa ntchito konse mlingaliro la zamankhwala ndi alembi ena a Malemba Achikristu Achigriki. Koma tingayembekezere chinenero cha zamankhwala m’zolembedwa za sing’anga.
Mwachitsanzo, ndi Luka yekha yemwe ananena kuti mpongozi wake wa Petro anali ndi “nthenda yolimba yamalungo.” (4:38) Iye analembanso kuti: “Tawona, munthu wodzala ndi khate.” (5:12) Kwa alembi ena a Uthenga Wabwino, chinali chokwanira kungotchula khate. Koma sizinali tero ndi sing’anga Luka, yemwe anasonyeza kuti nthenda ya mwamunayo inafika poipa.
Chidziŵitso m’Miyambo
Luka ananena kuti pambuyo pa kubadwa kwa Yesu, Mariya “anamkulunga iye m’nsalu.” (2:7) Mwamwambo, khanda lobadwa chatsopano linasambitsidwa ndi kupakidwa mchere, mwinamwake kuti awumitse khungu ndi kulilimbitsa. Kenaka khandalo linakulungidwa m’nsalu, mongadi mtembo. Nsaluzo zinakhalitsa thupilo lowongoka ndi lofunda, ndipo kuzikulunga izo pansi pa chibwano ndi kumutu kuyenera kukhala kunaphunzitsa mwanayo kupumira m’mphuno. Ripoti la zaka za zana la 19 pa miyambo yofananayo yokulunga thupi linagwira mawu wochezera wina ku Betelehemu kukhala akumati: “Ndinatenga kamwanako m’manja mwanga. Thupi lake linali lolimba ndi losakhotakhota, lomangidwa mothina ndi chiguduli choyera ndi chobiriŵira. Manja ndi miyendo yake inakulungidwiradi mkati, ndipo mutu wake unamangidwa m’kansalu kofiira, ndi kofeŵa, kamene kanapita kunsi kwa chibwano chake ndi kudutsa mphumi yake mwa mpindilo zaduku.”
Uthenga Wabwino wa Luka umatipatsanso chidziŵitso m’miyambo ya maliro ya zaka za zana loyamba. Yesu anali pafupi ndi chipata cha Nayini pamene anawona “anthu anali kunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye,” ndipo “anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi naye.” (7:11, 12) Kuika maliro mwachisawawa kunachitikira kunja kwa mzinda, ndipo mabwenzi a wakufayo anaperekeza mtembowo kumanda. Chonyamulirapo bokosi lamaliro mothekera chinapangidwa mumkhalidwe wosakhalitsa chokhala ndi mitengo yotulukira m’ngodya zake imene inatheketsa amuna anayi kuinyamula pa mapeŵa awo pamene gulu loperekeza mtembo linkapita kumanda.
M’fanizo lina lolembedwa ndi Luka, Yesu analankhula za mwamuna wina womenyedwa ndi achifwamba. M’samariya wachifundo “anamanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo.” (10:34) Iyi inali njira yamwambo yosamalira kuvulala. Mafuta a azitona ankafeŵetsa ndi kuwumitsa zirondazo. (Yesaya 1:6) Koma bwanji ponena za vinyo? The Journal of the American Medical Association inanena kuti: “Vinyo anali mankhwala aakulu mu Grisi. . . . Hippocrates wa ku Cos (460-370 BC) . . . anagwiritsira ntchito vinyo mokulira, akumuyamikira kukhala chodzoleka pazironda, chofooketsako malungo, chophangukitsa, ndi chokodzetsa.” Fanizo la Yesu linakhudza mphamvu ya vinyo ya kupha tizirombo m’thupi ndi kuchinjiriza matenda, limodzinso ndi kuthekera kwa mafuta a azitona m’kuthandiza kuchiritsa zironda. Ndithudi, nsonga ya fanizolo ndiyakuti mnansi wabwino amachita mwachifundo. Ndimo mmene tiyenera kuchitira ndi ena.—10:36, 37.
Maphunziro a Kudzichepetsa
Luka yekha anafotokoza fanizo limene Yesu anapereka powona alendo akusankha malo apamwamba pa chakudya. Mkati mwa mapwando, alendo anakhala pa makama oikidwa kumbali zitatu za gome. Otumikira anaifikira iyo kuchokera ku mbali yachinayi. Mwamwambo, kama iriyonse inatenga anthu atatu, aliyense akuyang’ana ku gome pamene ankayedzamira pa chigongono cha kumanzere namandya chakudya ndi dzanja lamanja. Malo atatuwo anasonyeza kuti munthu anali ndi malo apamwamba, apakati, kapena apansi pa kamayo. Wokhala ndi malo apansi pa kama wachitatu anali ndi malo otsika kuposa onse pa chakudyacho. Yesu anati: ‘Pamene muitanidwa ku phwando, sankhani malo otsika ndipo wocherezayo adzakuuzani, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno. Pamenepo inu mudzakhala ndi ulemu pamaso a alendo anzanu.’ (14:7-10) Inde, lolani kuti modzichepetsa tiike ena patsogolo pathu. M’chenicheni, pogwiritsira ntchito fanizolo, Yesu ananena kuti: “Munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.”—14:11.
Logogomezeranso kudzichepetsa, ndi lapadera mu Uthenga Wabwino wa Luka, linali fanizo la Yesu lonena za wosonkhetsa msonkho ndi Mfarisi womapemphera m’kachisi. Pakati pa zinthu zina, Mfarisiyo ananena kuti: “Ndisala chakudya kaŵiri sabata limodzi.” (18:9-14) Lamulo linafuna kusala kudya kumodzi kokha pa chaka. (Levitiko 16:29) Koma Afarisi anasala kudya mopambanitsa. Yemwe ali m’fanizolo anasala kudya pa tsiku lachiŵiri la mlungu chifukwa chakuti limenelo linalingaliridwa kukhala nthaŵi pamene Mose anakwera kunka ku Phiri la Sinai, kumene analandira magome aŵiri a Mboni. Iye ananenedwa kukhala anatsika ku phirilo pa tsiku lachisanu la mlungu. (Eksodo 31:18; 32:15-20) Mfarisiyo anasonyeza kusala kudya kwake kwa pakati pa mlungu kukhala umboni wa kukhulupirika kwake. Koma fanizoli liyenera kutisonkhezera kukhala odzichepetsa, osati odzilungamitsa.
Ngale zimenezi kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Luka zimatsimikizira kuti uli wapadera ndi wa chilangizo. Zochitika zofotokozedwa mu nkhaniyo zimatithandiza kukumbukiranso zochitika zosangalatsa mu moyo wa Yesu wa pa dziko lapansi. Timapindulanso ndi chidziŵitso chakumbuyo cha miyambo ina. Koma ife makamaka tidzadalitsidwa ngati tigwiritsira ntchito maphunziro oterowo onga onena za chifundo ndi kudzichepetsa ophunzitsidwa bwino motero mu Uthenga Wabwino umenewu wa Luka, sing’anga wokondeka.