Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/15 tsamba 29
  • Phindu la Malembo Apamanja Agumbwa a Nash

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phindu la Malembo Apamanja Agumbwa a Nash
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zolembedwa mu Mpukutu Wagumbwa wa Nash
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Umboni wa Kusungidwa kwa Umulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Baibulo Linapulumuka Modabwitsa
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Mpukutu Wotchedwa “Nyimbo ya Panyanja” Umatithandiza Kudziwa Zinthu Zakale
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/15 tsamba 29

Phindu la Malembo Apamanja Agumbwa a Nash

KODI mungapime bwanji mosaphonyetsa deti lakulembedwa kwa malemba apamanja akalekale a Baibulo Lachihebri? Limenelo linali vuto lomwe linayang’anizana ndi Dr. John C. Trever mu 1948 pamene kwanthaŵi yoyamba anawona Mpukutu wa Yesaya wa m’Nyanja Yakufa. Mpangidwe wa zilembo Zachihebri unamchititsa chidwi. Iye anadziŵa kuti zilembozo zinali njira yodziŵira nyengo ya kulembedwa kwake, koma kodi iye akaziyerekezera ndi chiyani? Molondola, iye anati: Kokha ndi malembo apamanja Agumbwa a Nash. Chifukwa ninji? Kodi malembo apamanja amenewa nchiyani, ndipo kodi anachokera kuti?

Malembo apamanja Agumbwa a Nash amaphatikizapo zigawo zinayi chabe za mizera 24 ya malemba Achihebri, ukulu wake ukumafikira 7.5 cm m’bwambi ndi 12.5 cm muutali. Anapatsidwa dzina la W. L. Nash, mlembi wa Society of Biblical Archaeology, amene anawapeza kwa wamalonda wina wa ku Igupto mu 1902. Anafalitsidwa ndi S. A. Cooke m’chaka chotsatira mu Proceedings yofalitsidwa ndi bungwelo ndipo anaperekedwa ku Laibulale ya Yunivesite ya Cambridge, ku Mangalande, kumene ali. Phindu lachidutswa cha gumbwa chimenechi liri m’nyengo yakulembedwa kwake. Asikolala anapima nyengoyo kukhala zaka za zana lachiŵiri kapena loyamba B.C.E., chotero chinali tsamba la malembo apamanja Achihebri oyambirira koposa onse amene anapezedwa.

Pamene Dr. Trever anayerekezera mawonekedwe a malembo apamanja Agumbwa a Nash ndi mpukutuwo pachipangizo chowonera zinthu zazing’ono, anayang’anitsitsa mpangidwe ndi mawonekedwe a zilembozo chirichonse pachokha. Mosakaikira konse, zinali zofanana kwambiri. Ngakhale zinatero, kunawonekera kukhala kosakhulupirika kwa iye kuti malembo apamanja opezedwa chatsopano aakuluwo, angakhale akale kwambiri mofanana ndi malembo Agumbwa a Nash. Komabe m’kupita kwanthaŵi, mapendedwe akewo anatsimikizira kukhala olondola. Mpukutu wa Yesaya wa m’Nyanja Yakufa unali wa m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E.!

Zolembedwa mu Mpukutu Wagumbwa wa Nash

Kupendedwa kwa malembo apamanja a Mpukutu Wagumbwa wa Nash kumavumbula kuti mizera yake 24 yonseyo njosakwanira, yopeleŵera ndi liwu limodzi kapena zilembo koyambira ndi kothera kwa mizerayo. Unali ndi mbali za Malamulo Khumi a mu Eksodo chaputala 20, limodzi ndi mavesi ena a Deuteronomo chaputala 5 ndi 6. Chotero amenewa sanali malembo apamanja a Baibulo ozoloŵereka koma malemba osanganikirana okhala ndi chifuno chapadera. Mwachiwonekere anali mbali ya malangizo osonkhanitsidwa okumbutsa Ayuda thayo lawo kwa Mulungu. Chigawo cha lemba choyambira pa Deuteronomo 6:4, chotchedwa Sema, chinabwerezedwa mwakaŵirikaŵiri. Vesilo limati: “Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi.”

Zilembo zinayi Zachihebri, YHWH, “Yehova,” m’vesi limeneli zikuwonekera kaŵiri pamzera womalizira wa gumbwayo, ndipo zikuwonekera mmalo ena asanu. Zimawonekeranso kamodzi, koma popanda chilembo choyamba.

Kwenikweni Sema inalinganizidwira kugogomezera “kuti Mulungu ali mmodzi.” Malinga ndi Talmud Yachiyuda (Berakoth 19a), liwu lomalizira, ʼE·chadhʹ (“Mmodzi”), “liyenera kugogomezeredwa makamaka pamene anali kutchulidwa masilabo a liwu lirironse.” (W. O. E. Oesterley ndi G. H. Box) Ponena za Mulungu, ʼE·chadhʹ wotalikitsidwa ameneyu analengezanso kukhala kwake wapadera.

Lerolino, mpukutu Wagumbwa wa Nash uli ndi amsinkhu ake ambiri, makamaka pakati pa miputu yopezeka m’mapanga m’mbali mwa magombe a Nyanja Yakufa pafupi ndi Qumran. Mapendedwe osamalitsa atsimikizira kuti ambiri a malembo apamanja amenewa amapezeka kukhala a m’zaka za zana loyamba ndi lachiŵiri B.C.E.a Ngakhale kuti sulinso mpukutu wa malembo apamanja woyambirira Wachihebri umene wadziŵika, malembo apamanja Agumbwa a Nash akali opindulitsabe kwambiri. Akali chikhalirebe malembo apamanja a Baibulo Achihebri okha a deti lakalekale lotero opezedwa ku Igupto.

[Mawu a M’munsi]

a Wonani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, tsamba 10-13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena