Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi ndithayo lotani limene Akristu ali nalo m’kuchepetsa kuipitsidwa kwa malo athu—mtunda, nyanja, ndi mpweya?
Monga Mboni za Yehova, tiri odera nkhaŵa kwambiri ndi mavuto ochuluka okhudza malo okhala zinyama ndi anthu amene tsopano akuyambukira malo athuwa dziko lapansi. Kuposa anthu ochulukitsa, ife timazindikira kuti dziko lapansi linalengedwera kukhala malo okhala angwiro, ndi abwino ku banja langwiro laumunthu. (Genesis 1:31; 2:15-17; Yesaya 45:18) Tirinso ndi chitsimikiziro cha Mulungu chakuti ‘adzawononga iwo akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Chotero kuli koyenera kupanga zoyesayesa zosankitsa ndi zanzeru kupewa kuwonjezera mosafunika kuipitsa chiunda chathuchi kosalekeza kochitidwa ndi munthu. Komabe, tawonani, liwu lakutilo “zosankitsa.” Kulinso koyenerera mogwirizana ndi Malemba kusamala kuti tisalole nkhani za kuipitsidwa kwa malo okhala ndi zizoloŵezi kuti zikhale nkhaŵa zathu zopambanitsa.
Ngakhale kukhala ndi moyo kozoloŵereka kwaumunthu kumatulutsa zinyansi. Mwachitsanzo, kaŵirikaŵiri kulimidwa, kukonzedwa, ndi kudyedwa kwa zakudya kumatulutsa zinyansi, ngakhale kuti zambiri zake zingakhale zokhoza kuwola. (Salmo 1:4; Luka 3:17) Mwachiwonekere, chakudya cha nsomba yosanjikikayo chimene Yesu woukitsidwa anakonzera ophunzira ake chinachititsa utsi, phulusa, ndi zinyalala za minga ya nsomba. (Yohane 21:9-13) Koma madongosolo a zinthu zamoyo ndi zopanda moyo kapena zungulirezungulire wa dziko lapansi ngolinganizidwira kuphatikizapo zimenezo.
Anthu a Mulungu sayenera kukhala osazindikira nkhani zokhudza malo okhala anthu ndi zinyama. Yehova anafuna kuti anthu ake akale achitepo kanthu kutaya zinyansi, michitidwe imene inali ndi cholinga cha kukhala ndi malo okhala audongo ndi aukhondo. (Deuteronomo 23:9-14) Ndipo popeza kuti tidziŵa lingaliro lake la awo amene akuwononga dziko lapansi, ife ndithudi sitiyenera kunyalanyaza zinthu zimene tingachite kusunga malo ali audongo. Tingathe kusonyeza zimenezi mwakutaya zinyansi kapena zinyalala mmalo oyenerera, makamaka zinyalala zaupandu. Ife mwachikumbumtima timachita mogwirizana ndi zoyesayesa za dongosolo lakuzunguliritsa zinthu, timakhala ndi chifukwa chowonjezereka chakutero ngati kutero kuli lamulo loperekedwa ndi Kaisara. (Aroma 13:1, 5) Ndipo anthu ena amapeza chikhutiro kuchokera kunjira zowonjezereka, monga ngati kusankha kugwiritsira ntchito zinthu zokhoza kuwola mmalo mwa zimene zingawonjezere miyulu ya zinyalala pamtunda ndi pansi pa nyanja.
Komabe, mlingo umene Mkristu adzachita zimenezi, iri nkhani yaumwini kusiyapo ngati afunikira kuti atero mwalamulo. Kuli kwachiwonekere kuchokera kuzoulutsira mawu kuti anthu opanda ungwiro amagwera mosavuta mumsampha wakuchita monkitsa. Uphungu wa Yesu ulidi woyenerera wakuti: ‘Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. . . . upenya bwanji kachitsotso m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwemwini suganizira?’ (Mateyu 7:1, 3) Kukumbukira mfundoyi kungatithandize kusaiŵala mbali zina zofunika:
Mneneri Yeremiya analemba kuti: ‘Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siiri mwa iyemwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’ (Yeremiya 10:23) Kunyalanyaza lamulo la makhalidwe abwino limeneli kwaika anthu pa kuwombana mwachindunji ndi ‘nthaŵi zowaŵitsa zovuta kuchita nazo,’ monga momwe zalembedwera pa 2 Timoteo 3:1-5. Ndipo zimene Mulungu anachititsa kuti zilembedwe pa Chivumbulutso 11:18 zimatsimikizira kuti zoyesayesa za anthu za kuchotsa padziko lapansi mavuto ake aakulu amalo okhala anthu ndi zinyama, kuphatikizapo kuipitsidwa kwawo, sizidzapambana kotheratu. Pangakhale kupita patsogolo pang’ono cha apa ndi apo, koma njira yokha yokhalitsa yothetsera imafunikiritsa kuloŵerera kwa Mulungu.
Chifukwa chake timasumika zoyesayesa zathu ndi chuma panjira ya Mulungu yothetsera, mmalo mwakuyesayesa kuthetsa zizindikiro zachiphamaso. Mwakutero timatsatira chitsanzo cha Yesu, amene anathera mbali yaikulu ya uminisitala wake ‘kuchitira umboni chowonadi.’ (Yohane 18:37) Mmalo mwakudyetsa dziko kapena kupereka mpumulo pa utenda wa anthu pamlingo waukulu—kuphatikizapo kuipitsidwa kwa malo—Yesu anasonya kunjira yachikwanekwane yothetsera mavuto okantha mtundu wa anthu.—Yohane 6:10-15; 18:36.
Pamene kukonda anthu anzathu kumatisonkhezera kupeŵa kuipitsa mosafunikira mtunda, mpweya, kapena madzi, timapitirizabe kuchitira umboni chowonadi. Zimenezi zimaphatikizapo kuphunzitsa anthu kugwiritsira ntchito chowonadi cha Baibulo ndipo chotero kupeŵa kuipitsa matupi awo ndi utsi, zakumwa zoledzeretsa zopambanitsa, kapena anamgoneka aupandu. Pamene mamiliyoni ambiri atsopano afikira kukhala ophunzira, iwo aphunzira zizoloŵezi zaudongo ndi kudera nkhaŵa ena. Chotero ntchito yolalikira yathandizira kwenikweni kuchepetsa vuto lodziŵika la kuipitsidwa kwa mpweya ndi malo lerolino. Koma chofunika kwambiri, ophunzira Achikristu amayesayesa kusanduliza umunthu wawo ndi zizoloŵezi tsopano kotero kuti adzayenere kuloŵa m’dziko lapansi laudongo, Laparadaiso limene Mulungu adzapereka mwamsanga kwa olambira ake owona.