Misonkhano Yachigawo ya “Kuphunzitsa Kwaumulungu”
ONSE okhala ndi chikhumbo chakuphunzitsidwa ndi Yehova akuyang’anira mtsogolo mwachidwi kumisonkhano Yachigawo ya “Kuphunzitsa Kwaumulungu.” Programu yamasiku anayi idzagogomezera mbali zofunika zakuphunzitsa Kwamalemba kumene kumatetezera Akristu nthaŵi zino zamavuto aumwini omakulakula ndi chipwirikiti chadziko. Programuyo idzawathandiza kuima nji motsutsana ndi ‘chirichonse chotsutsana ndi chiphunzitso cha moyo’ ndi kukhala aphunzitsi abwinopo a Mawu a Mulungu.—1 Timoteo 1:10.
Ndizitsanzo zabwino kwambiri chotani nanga zakuzitsanzira! Mphunzitsi Wamkulu koposa siwina koma Yehova Mulungu mwiniyo! Chotero, Elihu molondola anauza Yobu kuti Yehova anali “wakutilangiza ife koposa nyama zapadziko, wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m’mlengalenga.” Iye anafunsanso ponena za Yehova kuti: “Mphunzitsi wakunga iye ndani?” (Yobu 35:11; 36:22) Mulungu akutchulidwa pa Yesaya 30:20 kukhala “Mphunzitsi Wamkulu.”
Wachiŵiri yekha kwa Yehova monga mphunzitsi ndiye Yesu Kristu. Iye anadziŵika monga “Mphunzitsi” ndipo monga ‘Mlangizi,’ akumatchulidwa monga wotero pafupifupi nthaŵi 50 m’Mauthenga Abwino. Mosasamala kanthu zakuchiritsa kwake kothutsa maganizo ndi zozwizitsa zina, Yesu sanadziŵike monga Sing’anga koma monga Mphunzitsi, Mlangizi.—Mateyu 8:19; Luka 5:5; Yohane 13:13.
Moyenerera bwino, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake ndi atumwi kukhala aphunzitsi monga momwe iye analiri. Tingathe kuwona zimeneza pa Mateyu 10:5 mpaka 11:1 ndi Luka 10:1-11. Mwamsanga asanakwere kumwamba, Yesu anapereka kwa ophunzira ake ntchito yodziŵika yakuphunzitsa yolembedwa pa Mateyu 28:19, 20. Bukhu la Machitidwe, kudzanso makalata ouziridwa amene amalitsatira m’Malemba Achigiriki Achikristu, amasimba mmene otsatira oyambirira a Yesu anachitira ntchito yophunzitsa imeneyi mwachangu, mwaluso, ndi mokhulupirika.
Ntchito yophunzitsa imeneyi njofulumira kwambiri lerolino koposa ndi kale lonse. Tikukhala ndi moyo m’masiku otsiriza adongosolo lino la zinthu, ndipo chifukwa cha zimenezi, miyoyo ikuphatikizidwa. Kuti anthu asagaŵane m’machimo a Babulo Wamkulu ndi kusalandira mbali ya miliri yake, iwo ayenera kuphunzitsidwa ndi kuthandizidwa kutuluka m’Babulo ndi kutenga kaimidwe kawo kumbali ya Yehova ndi Ufumu wake.—Chivumbulutso 18:4.
Kuthandiza Mboni za Yehova zonse, m’zoyesayesa zawo zakuchita ntchito yawo yophunzitsa, Yehova kupyolera mwa gulu lake wagaŵira Misonkhano Yachigawo ya “Kuphunzitsa Kwaumulungu.” Misonkhano ya masiku anayi imeneyi idzayambira ku Chigawo Chadziko Chakumpoto kuchiyambiyambi kwa nyengo ya chisanu. Mtumiki wodzipatulira aliyense wa Yehova atsimikiziretu kudzafika pa umodzi wa misonkhano imeneyi, ndi kukhala mvetseri wotchera khutu kuyambira pa nyimbo ndi pemphero lotsegulira pa Lachinayi masana mpaka pemphero lomaliza pa Sande masana.