Kuzengereza Kunali Kwakupha!
MABANJA atatu, achikulire asanu ndi aŵiri ndi ana asanu ndi mmodzi, anathaŵa mothedwa nzeru kupulumutsa miyoyo yawo. Mwachiwonekere anali ataunjikana pamodzi pobisala m’nyumba ya munthu wina, akumayembekezera kupulumuka miyala yomagwa ngati matalala. Koma pamene phokoso la miyala yolakatika linaleka, panafika chowopsa chatsopano—mtambo wakuda bii waphulusa lopuitsa. Tsopano panalibe kuchitira mwina kusiyapo kuthaŵa.
Patsogolo panali mwamuna, mwinamwake wantchito, amene anathamanga ndi thumba la chakudya ataliika papheŵa. Anatsatiridwa ndi anyamata aŵiri, mmodzi wa zaka zakubadwa pafupifupi zinayi, winayo zisanu, akuthamanga atagwirana manja. Enawo anatsatira—akuchita piringupiringu mwamantha, akulimbana, kudzandiradzandira, kuthedwa nzeru akufunafuna pothaŵira. Iwo anayesayesa kupuma, koma m’malo mwa mpweya, anali kupuma phulusa lachinyontho. Mmodzi motsatizana ndi mnzake, 13 onsewo anagwa ali kwala ndipo potsirizira pake anakwiriridwa ndi phulusa lovumbalo. Mitembo yawo yomvetsa chisoniyo ikakhala yokwiriridwa kufikira akatswiri ofukula m’mabwinja anaifukula pafupifupi zaka 2,000 pambuyo pake ndi kufotokoza zochitika zomvetsa chisoni zamphindi zawo zomalizira.
Mikhole 13 imeneyi inali kokha oŵerengeka mwa anthu oyerekezeredwa kukhala 16,000 amene anawonongekera mu m’zinda wakale wa Pompeii, Italiya, pa August 24, wa 79 C.E. Ambiri anapulumuka mwakuchoka mu mzindawo pamene Phiri la Vesuvius linatulutsa kuphulika kwake koyambako. Komabe, awo amene anazengereza—kwakukulukulu anthu achuma amene sanafune kusiya nyumba zawo ndi chuma—anakwiriridwa mamita 6 pansi pa mathanthwe ndi phulusa.
Chimene chinachitika mu Pompeii pafupifupi zaka 2,000 zapitazo chingakhale mbiri yakale. Koma m’njira zambiri chikufanana ndi mkhalidwe woyang’anizana ndi fuko lonse la anthu lerolino. Chizindikiro cha padziko lonse, cholaula kwambiri kuposa kuchita mabingu kwa Phiri la Vesuvius, chikupereka chenjezo lakuti dongosolo ladziko lamakonoli likuyang’anizana ndi chiwonongeko chimene chiri pafupi kwambiri. Kuti tipulumuke, tiyenera kuchitapo kanthu mofulumira. Kuzengereza kuli kwakupha. Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza chimene chizindikirocho chiri ndi mmene tingalabadirire mwanzeru.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chithunzithunzi pachikuto ncha National Park Service
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Soprintendenza Archeologica di Pompei