Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 3/1 tsamba 20-23
  • Mulungu Amakulitsa—Kodi Inu Mumachita Mbali Yanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Amakulitsa—Kodi Inu Mumachita Mbali Yanu?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Amakulitsa
  • ‘Sali Kanthu Kapena Wowokayo’
  • Antchito Anzake a Mulungu
  • Chitani Mbali Yanu
  • ‘Musapumitse Dzanja Lanu’
  • Apolo—Mlaliki wa Choonadi Chachikristu Wolankhula Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kuthandiza Anthu Kuyandikira kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1999
  • ‘Mulungu Ndi Amene Amakulitsa’!
    Nsanja ya Olonda—2008
Nsanja ya Olonda—1993
w93 3/1 tsamba 20-23

Mulungu Amakulitsa​—Kodi Inu Mumachita Mbali Yanu?

TAYEREKEZERANI malowo. Muli m’dimba lokongola, lozunguliridwa ndi mitengo yaitali, zitsamba zobiriŵira, ndi maluŵa ambirimbiri amawonekedwe okongola. Kapinga wobiriŵira bwino lomwe wotambalala cha m’mphepete mwa mtsinje wosamaliridwa bwino umene ukuyenda tawatawa madzi oyera mbee. Palibe chimene chikudodometsa malo okongolawo. Mutachita chidwi, mukufunsa amene anapanga malo okongola amenewa. Poyankha wolima dimbayo modekha akunena kuti Mulungu amakulitsa zinthu zonse.

Mwachibadwa, inu munadziŵa zimenezo. Ndipo mukukumbukira mawu a wolima dimbayo pamene mufika panyumba ndipo mukuwona malo akumbuyo kwa nyumba yanu osasamalidwa, kumene kulibe chomera chochititsa kaso, zinyalala zangoti mbwee, ndipo madzi amvula adzaza maenje mochititsa nyansi. Inu mukukhumba kwambiri kukhala ndi dimba lofanana ndi limene munakachezakolo. Chotero, mutakhulupirira zolimba mawu a wolima dimbayo, mukugwada ndi kupempherera mwaphamphu kwa Mulungu kuti ameretse maluŵa okongola panyumba panu. Kodi chidzachitika nchiyani? Ndithudi, palibe chirichonse.

Bwanji ponena za kukula kwauzimu? Mungakhale ndi chikhumbo chachikulu chakuwona zinthu zikukula mwauzimu, monga ngati ophunzira atsopano kulabadira ku chowonadi cha Mawu a Mulungu kapena kupita patsogolo kwa inu mwini. Ndipo mungapemphere mwaphamphu kwa Yehova kuti akulitse motero, muli ndi chikhutiro champhamvu chakuti iye ali ndi mphamvu yakutero. Koma kodi chikhumbo chanu champhamvu, pemphero lanu laphamphu, ndi chidaliro chanu m’mphamvu ya Mulungu mwa izo zokha zingachititse kukulako?

Mulungu Amakulitsa

Mwina mwake inu mukulingalira kuti mbali yanu m’kuchititsa kukula kwauzimu njosanunkha kanthu, ngakhale yopanda tanthauzo. Kodi mtumwi Paulo sanapereke lingaliro limeneli pa 1 Akorinto 3:5-7? Iye analemba kuti: ‘Apolo chiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa. Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wowokayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.’

Molondola Paulo akuvomereza kuti pamene zinthu zikula, thamo lonse lipita kwa Mulungu. Wolima dimba angatipule nthaka, kubzala mbewu, ndipo angasamalire bwino lomwe zomerazo, koma potsirizira pake chiri chifukwa cha mphamvu yolenga yodabwitsa ya Mulungu kuti zinthuzo zimakula. (Genesis 1:11, 12, 29) Pamenepa, kodi nchiyani chimene Paulo akutanthauza pamene anena kuti “chotero sali kanthu kapena wowokayo, kapena wothirirayo”? (“Sali olima dimba limodzi ndi kufesa kwawo ndi kuthirira zimene ziri kanthu,” The New English Bible.) Kodi iye akululuza mbali ya mminisitala aliyense m’kupangidwa kwa ophunzira atsopano, akumapereka lingaliro lakuti potsirizira pake siziri kanthu konse mmene tikuchitira uminisitala wathu?

‘Sali Kanthu Kapena Wowokayo’

Kumbukirani kuti m’mbali imeneyi yakalata yake, Paulo sakulankhula zauminisitala Wachikristu koma kupusa kwakutsatira anthu mmalo mwa kutsatira Yesu Kristu. Ena m’Korinto anali kupereka thamo lopambanitsa kwa atumiki odziŵika a Yehova, monga ngati Paulo ndi Apolo. Ena anali kupangitsa mipatuko ndi kukweza anthu amene analingalira kukhala apamwamba kuposa abale awo Achikristu.​—1 Akorinto 4:6-8; 2 Akorinto 11:4, 5, 13.

Kulemekeza anthu, mwanjirayi sikuli koyenerera. Ndiko kuganiza kwakuthupi, ndipo kumatulutsa nsanje ndi ndewu. (1 Akorinto 3:3, 4) Paulo akusonyeza zotulukapo za kuganiza kotero. Iye akuti: ‘Pali makani pakati pa inu. Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena: Ine ndine wa Paulo, koma ine wa Apolo, koma ine wa Kefa, Koma ine wa Kristu.’​—1 Akorinto 1:11, 12.

Chifukwa chake, pamene analemba kuti, “wowokayo ndi wothirirayo sali kanthu” (Phillips), mtumwiyo akutsutsa kuganiza kwakuthupi kotero, akumagogomezera kufunika kwa kuyang’ana kwa Yesu Kristu monga Mtsogoleri ndi kuvomereza kuti ulemerero wonse wa chiwonongeko mu mpingo umamka kwa Mulungu. Atumwi ndi akulu ena anali chabe atumiki ampingo. Palibe aliyense ayenera kukwezedwa kapena iwo eni kufunafuna kutchuka kapena mbiri. (1 Akorinto 3:18-23) Chotero wofesa ndi wothirira sali kanthu, akutero Paulo, “pomuyerekezera ndi uyo amene amapereka moyo kwa mbewuyo.”​—1 Akorinto 3:7, Phillips.

Antchito Anzake a Mulungu

Chifukwa chake, ponena izi, mtumwi Paulo sanali kululuza kufunika kwa mbali yathu m’kufesa ndi m’kuthirira. Iye sanatanthauze kuti tiyambe kuganiza kuti, “Mulungu adzakulitsa zinthu m’nthaŵi yake,” ndiyeno ife nkungokhala manja lende ndi kumuyembekezera kutero. Iye anadziŵa kuti zimene tichita ndi mmene timazichitira ziri kanthu ponena za mmene zinthu zikulira.

Ndicho chifukwa chake Paulo analimbikitsa Akristu mosalekeza kugwira ntchito zolimba muuminisitala wawo ndi kuwongolera maluso awo monga aphunzitsi. Talingalirani uphungu umene akupereka kwa mwamuna wachichepereyo Timoteo. ‘Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.’ (1 Timoteo 4:16) “Ndi kulamulira mwamphamvu . . . . , lalikira mawu, uchite mofulumira . . . . limodzi ndi kupirira konse ndi luso lakuphunzitsa. . . . . tsiriza kotheratu uminisitala wako.” (2 Timoteo 4:1, 2, 5, NW) Sipakakhala tanthauzo lirilonse kuti Timoteo agwire ntchito zolimba kuwongolera maluso ake ngati kufesa kwake ndi kuthirira zinali zosapindulitsa pakupangitsa kukula kwa zinthu.

Mofanana ndi Paulo ndi Apolo, inunso mungathe kukhala ndi mwaŵi wosayerekezeka wakutumikira monga mmodzi wa antchito anzake a Mulungu. (1 Akorinto 3:9; 2 Akorinto 4:1; 1 Timoteo 1:12) Motero, ntchito yanu njofunika. Wolima dimba samayembekezera kuti mozizwizitsa Mulungu atulutse dimba lokongola popanda kuyesayesa kopangidwa ndi wolima dimbayo. Kodi ziyenera kukhala zosiyana ndi kukula kwauzimu? Kutalitali. Mofanana ndi mlimi amene moleza mtima “adikira chipatso chofunikatu cha dziko,” tiyenera ife choyamba kuchita mwaphamphu kufesa ndi kuthirira, tikumayembekezera pamene Mulungu akulitsa.​—Yakobo 1:22; 2:26; 5:7.

Chitani Mbali Yanu

Popeza kuti, monga momwe mtumwi Paulo akunenera, “yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwakuchititsa kwake iye yekha,” timachita bwino kudzifunsa mmene tikuchitira ntchitoyo.​—1 Akorinto 3:8.

Katswiri wamadimba Geoffrey Smith akuti: “Palibe ziyeneretso zapadera zimene zimafunika kuti mukhale wolima dimba kusiyapo kukhala ndi chikondwerero m’zomera.” (Shrubs & Small Trees) Mofananamo, palibe ziyeneretso zachibadwa zapadera zimene ziri zofunika kwa ife kuti tikhale antchito anzake a Mulungu, kusiyapo kukondwerera kokha mowona mtima anthuwo ndi kufunitsitsa kugwiritsidwa ntchito ndi Mulungu.​—2 Akorinto 2:16, 17; 3:4-6; Afilipi 2:13.

Pendani wina wa uphungu wabwino woperekedwa ndi olima madimba aluso. Monga momwe katswiri wina akunenera, ngati wolima dimba watsopano ali wofunitsitsa kumvetsera kwa okhala ndi chidziŵitso chokulirapo kuposa iye, “wophunzirayo angathe mofulumira kukhala katswiri.” Ndipo, katswiri mmodzimodziyo akuti, “nthaŵi zonse katswiriyo amapeza kanthu kena katsopano kakukaphunzira.” (The Encyclopedia of Gardening) Kodi inu mumavomereza mofunitsitsa chithandizo ndi chiphunzitso zimene Yehova wapereka kotero kuti mungathe kufesa ndi kuthirira mogwira mtima? Ngati mumatero, kaya ndinu watsopano pantchito kapena muli ndi chidziŵitso nayo, mungathe kukulitsa maluso owonjezereka monga wantchito mnzake wa Mulungu ndipo mwakutero kukhala “woyeneretsedwa mokwanira kuphunzitsa ena.”​—2 Timoteo 2:2.

Ngati iye ali wofunitsitsa kumvetsera ndi kuphunzira, akutero Geoffrey Smith, “watsopanoyo adzapeŵa mbuna zoipitsitsa.” Ngati timvetsera ku chitsogozo chimene Yehova amapereka kupyolera mwa Mawu ake ndi gulu lake, tidzachita zinthu mwanjira yake. Mwachitsanzo, pamenepo tidzapeŵa mbuna zonga kukangana mopusa ndi awo amene amangofuna kukangana kapena kumenyanira mawu.​—Miyambo 17:14; Akolose 4:6; 2 Timoteo 2:23-26.

Uphungu wina wabwino wokhudza kukhala wolima dimba wabwino ndiwo kuganiza kaye zinthu mosamalitsa musanafulumire kukatipula nthaka. “Khasu lisanayambe kukumba nthaka,” ikutero The Encyclopedia of Gardening, “therani nthaŵi muli chete kupenda [ziyembekezo zanu].” Kodi mumagwera mu msampha wakukangaza koloŵa muuminisitala Wachikristu popanda choyamba kupereka chisamaliro ndi lingaliro lapemphero lonena za zimene mufuna kukwaniritsa ndi mmene mungazichitire bwino koposa? Dziŵani zolinga zanu bwino lomwe musanayambe. Mwachitsanzo, ganizani za mtundu wa anthu amene mungakumane nawo ndi zothetsa nzeru zimene mungayang’anizane nazo, ndipo konzekerani kusamalira zimenezi. Izi zidzakukhozetsani ‘kupindula anthu ochuluka [pamene] mukhala zinthu zonse kwa anthu amitundu yonse.’​—1 Akorinto 9:19-23.

‘Musapumitse Dzanja Lanu’

Ngati tiyamikira mwaŵi wakutumikira monga antchito anzake a Mulungu, sitidzachepetsa mbali yathu m’kugwirira ntchito pamodzi. ‘Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zilola bwino ngakhale izizi, kaya izozo, kaya zonse ziŵiri zidzakhala bwino.’ (Mlaliki 11:6) Zotulukapo zomalizira ziri kwa Yehova, koma tidzatuta kokha ngati tayamba kufesa mwachangu.​—Mlaliki 11:4.

Palibe dimba limene linapangidwa kukhala lokongola mwakutipula wamba kwachiphamaso ndi kungomwazamwaza mbewu. Mofananamo, zowonjezereka zikufunika muuminisitala Wachikristu kuposa kukhala ndi phande kwachiphamaso m’kugaŵira mabukhu a Baibulo. Monga antchito anzake a Mulungu, tifunikira kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi kulengeza mwachangu ndi mosamala, tikumafunafuna anthu okhoterera ku chilungamo. (Machitidwe 13:48) Kumbukirani lamulo lamakhalidwe abwino m’mawu a mtumwi Paulo pa 2 Akorinto 9:6 lakuti: “Iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.”

Mofanana ndi olima madimba abwino onse, timayesa kufesa m’nthaka yabwino. Komabe, pamene kanthu kafesedwa ngakhale m’nthaka yabwino koposa, amenewo sindiwo mapeto azinthu. Geoffrey Smith akuti: “Izi sizitanthauza kuti mutafesa palibenso chirichonse chofunika kwa munthu wofesayo kusiyapo kugula mpando wa ndakhuta ndalema ndi sumbulelo yaikulu.” Ayi, kuti zinthu zikule, kuyesayesa nkofunika m’kuthirira ndi kutetezera mbewu.​—Yerekezerani ndi Miyambo 6:10, 11.

M’chenicheni, uminisitala Wachikristu, ungatanthauze nyengo zazitali zantchito yakalavulagaga pamene kukuwonekera kukhala kulibe chimene chikuchitika. Koma mwadzidzidzi, ndipo nthaŵi zina mosayembekeza, zotulukapo zodabwitsa zingafike. Geoffrey Smith akuti: “Kulima dimba kumaphatikizapo nyengo zazitali zantchito yofananayo yotopetsa yotsatiridwa ndi nyengo za ulemerero wambiri kotero kuti kukumba konse, kulimirira, ndi nkhaŵa zazikulu zimaiwalidwa.” Inunso mungathe kukhala ndi nthaŵi zachikhutiro chachikulu pamene mtima wolabadira uvomereza uthenga wachowonadi​—malinga ngati muli wofunitsitsa kuswa mphanje, kufesa, kulimirira, ndi kuthirira.​—Yerekezerani ndi Miyambo 20:4.

Paulo ndi Apolo anadziŵa kuti ntchito yawo yakulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira sinawabweretsere kutchuka kwapadera mu mpingo Wachikristu. Iwo anazindikira kuti ali Mulungu amene amakulitsa. Komabe, iwo anafesa ndipo anathirira​—mwachangu. Titsatiretu chitsanzo chawo ndi kudzichititsa ife eni kugwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu monga “aminisitala kupyolera mwa amene [ena anafikira kukhala] okhulupirira.”​—1 Akorinto 3:5, 6, NW.

[Chithunzi patsamba 23]

Mulungu akulitsa zinthu zonse​—koma wolima dimba amachitanso mbali yake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena