Kuthandiza Anthu Kuyandikira kwa Yehova
“Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.”—YOHANE 14:6.
1. Kodi Yesu ataukitsidwa, anapatsa ophunzira ake lamulo liti, ndipo pamene Mboni za Yehova zamvera lamulolo, chachitika n’chiyani?
YESU KRISTU analamula otsatira ake ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.’ (Mateyu 28:19) Zaka khumi zapitazo, Mboni za Yehova zathandiza anthu oposa mamiliyoni atatu kubwera kwa Mulungu, kenaka n’kumawabatiza monga chizindikiro chawo chakuti adzipatulira kwa iye kuti azichita chifuniro chake. Timasangalala kwambiri kuwathandiza kuyandikira kwa Mulungu.—Yakobo 4:8.
2. Ngakhale kuti ambiri atsopano akubatizidwa, kodi n’chiyani chimene chachitika?
2 Komabe, m’mayiko ena mmene ophunzira atsopano ambiri abatizidwa, chiŵerengero cha olengeza Ufumu sichinawonjezeke molingana ndi kuchuluka kwa ophunzirawo. N’zoona kuti pali ena amene anamwalira, popeza kuti chaka chilichonse chiŵerengero cha anthu omwalira chimakhala ngati 1 peresenti. Komabe, m’zaka zoŵerengeka zapitazo, anthu ochuluka ndithu anagwa pazifukwa zina. N’chifukwa chiyani? M’nkhani inoyi ndi yotsatirayo, tiona mmene anthu amakokedwera kwa Yehova ndi kuonanso zifukwa izi ndi izi zimene ena amagwera.
Cholinga cha Kulalikira Kwathu
3. (a) Kodi ntchito imene ophunzira a Yesu aikiziridwa ikufanana bwanji ndi ya mngelo wotchulidwa pa Chivumbulutso 14:6? (b) Kodi ndi njira iti imene yaoneka kuti n’njabwino kwambiri yokopera chidwi cha anthu pa uthenga wa Ufumu, koma pali vuto lanji?
3 “Nthaŵi yachimaliziro” ino, ophunzira a Yesu ali ndi ntchito yofalitsa “chidziŵitso” chonena za “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Danieli 12:4; Mateyu 24:14) Akugwira ntchito imodzimodzi ndi mngelo uja “wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) M’dziko lino limene anthu ake n’ngotanganidwa ndi zinthu wamba, nthaŵi zonse njira yabwino kwambiri yokopera chidwi cha anthu pankhani ya Ufumu wa Mulungu ndi kuwathandiza kuyandikira kwa Yehova n’njakuwauza za chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Ngakhale kuti zimenezo n’zomveka, aja amene amasonkhana ndi anthu a Mulungu chifukwa chongofuna kudzaloŵa m’Paradaiso basi, sali olimbadi poyenda panjira yopita kumoyo.—Mateyu 7:13, 14.
4. Malinga ndi kunena kwa Yesu ndi kwa mngelo wouluka mumlengalenga, kodi cholinga cha ntchito yathu yolalikira n’chiyani?
4 Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Mngelo amene akuuluka mumlengalenga akulengeza “Uthenga Wabwino wosatha” ndipo akuuza iwo akukhala padziko kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo m’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.” (Chivumbulutso 14:7) Ndiye kuti cholinga chathu chachikulu polalikira uthenga wabwino n’chakuwathandiza anthu kuyandikira kwa Yehova kudzera mwa Kristu Yesu.
Mbali Yathu Pantchito ya Yehova
5. Kodi Paulo ndi Yesu ananena mawu ati osonyeza kuti tikugwira ntchito ya Yehova, osati yathu?
5 Mtumwi Paulo, polembera Akristu odzozedwa, ananena za “utumiki wa chiyanjanitso” ndiponso ananena kuti Mulungu akudziyanjanitsa yekha ndi anthu pamaziko a nsembe yadipo ya Yesu Kristu. Kunena kwake Paulo anati zili “monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife,” ndi kuti “tiumiriza inu m’malo mwa Kristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.” Mfundo yokondweretsa mtima zedi! Kaya ndife “atumiki [“akazembe,” NW] m’malo mwa Kristu” kapena nthumwi zokhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi, tisaiŵale kuti ntchitoyi si yathu, koma n’nja Yehova. (2 Akorinto 5:18-20) Mulungu ndiyedi amene amakoka anthu obwera kwa Kristu ndi kuwaphunzitsa. Yesu anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Chalembedwa mwa aneneri, ‘Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu.’ Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.”—Yohane 6:44, 45.
6. Kodi Yehova akugwedeza bwanji amitundu kwa nthaŵi yoyamba, ndipo panthaŵi imodzimodziyo, ndani akupeza chitetezo mu “nyumba” yake ya kulambira koona?
6 Masiku otsiriza ano, kodi Yehova amakoka bwanji anthu ndi kuwatsegulira “pa khomo la chikhulupiriro”? (Machitidwe 14:27; 2 Timoteo 3:1) Njira yaikulu n’njakuuza Mboni zake kulengeza mauthenga ake achipulumutso ndi achiweruzo chimene adzapereka pa dongosolo loipa la zinthuli. (Yesaya 43:12; 61:1, 2) Ulaliki umenewu wa padziko lonse ukugwedeza mitundu—chizindikiro chakuti posachedwapa padzakhala chiweruzo chosakaziratu. Koma nthaŵi imodzimodziyo, anthu “amtengo wapatali” m’maso mwa Mulungu akutuluka m’dongosolo lino ndipo akupeza chitetezo mu “nyumba” yake ya kulambira koona. Choncho Yehova akukwaniritsa mawu ake aulosi amene analembedwa ndi Hagai, kuti: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.”—Hagai 2:6, 7; Chivumbulutso 7:9, 15.
7. Kodi Yehova amatsegula bwanji mitima ya anthu ndi kuwakokera kwa iye ndi kwa Mwana wake?
7 Yehova akutsegula mitima ya anthu oopa Mulungu amenewa—“zinthu zabwino za amitundu”—kuti ‘amvere zimene zikunena’ Mboni zake. (Hagai 2:7, Jewish Publication Society; Machitidwe 16:14) Yehova, monga mmene anali kuchitira m’zaka za zana loyamba, amagwiritsa ntchito angelo kutsogoza Mboni zake kwa anthu oona mtima amene am’fuulira kuti awathandize. (Machitidwe 8:26-31) Anthu akamaphunzira za zinthu zodabwitsa zimene Mulungu wawakonzera kudzera mwa Mwana Wake, Yesu Kristu, chikondi cha Yehova chimawakokera kwa iye. (1 Yohane 4:9, 10) Inde, Mulungu amakokera anthu kwa iye ndi kwa Mwana wake mwa ‘kuwakomera mtima,’ kapena kuti “chikondi chokhulupirika.”—Yeremiya 31:3, NW, mawu amtsinde.
Kodi Yehova Amakoka Ndani?
8. Kodi Yehova amakoka anthu a mtundu wanji?
8 Yehova amakokera kwa iye ndi kwa Mwana wake onse om’funa Iye. (Machitidwe 17:27) Amenewa akuphatikizapo anthu amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa” m’Dziko Lachikristu, kapena tingoti padziko lonse. (Ezekieli 9:4) Anthuwo ‘amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.’ (Mateyu 5:3, NW) Indedi, iwo ndiwo “ofatsa . . . a m’dziko,” amene adzakhala kosatha m’paradaiso padziko lapansi.—Zefaniya 2:3.
9. Kodi Yehova amaona bwanji kuti anthu ‘akufuna moyo wosatha,’ ndipo amawakoka bwanji?
9 Yehova amadziŵa mtima wa munthu. Mfumu Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukam’funafuna Iye udzam’peza.” (1 Mbiri 28:9) Malinga ndi mmene mtima ndi mzimu, kapena kuti maganizo a munthuyo alili, Yehova atha kuona ngati munthuyo angalandire makonzedwe a Mulungu akukhululukira machimo ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dongosolo latsopano lolungama la Mulungu. (2 Petro 3:13) Mwa Mawu ake amene Mboni zake zimawalalikira ndi kuwaphunzitsa kwa ena, Yehova akukokera kwa iye ndi kwa Mwana wake “onse ofuna moyo wosatha,” ndipo amenewa ‘amakhala okhulupirira.’—Machitidwe 13:48, NW.
10. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova akamakoka ena n’kumasiya ena sizikutanthauza kuti iye anaikiratu tsogolo lawo iwo asanabadwe?
10 Kodi Yehova akamakoka anthu ena n’kumasiya ena, zikutanthauza kuti iye anaikiratu tsogolo lawo iwo asanabadwe? Ayi si choncho! Mulungu amakoka anthu, amatero malingana ndi zikhumbo zawo. Amawalola kudzisankhira okha. Yehova wapatsa anthu okhala padziko lapansi lero mwayi wofanana ndi umene Aisrayeli anapatsidwa zaka 3,000 zapitazo, pamene Mose anati: “Ndaika pamaso panu lerolino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa. . . . Ndichititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira Iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.”—Deuteronomo 30:15-20.
11. Kodi Aisrayeli akanasankha bwanji moyo?
11 Taonani kuti Aisrayeli anapatsidwa mwayi wosankha moyo ‘mwa kukonda Yehova, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira Iye.’ Pamene mawu amenewo ananenedwa, Aisrayeli anali asanalitenge Dziko Lolonjezedwa lija. Anali kudikira pa Zigwa za Moabu, kukonzekera kuwoloka Mtsinje wa Yordano kuti akaloŵe m’Kanani. Ngakhale kuti iwo sakanalephera kumaganiza za dziko ‘labwino ndi lalikulu loyenda mkaka ndi uchi’ limene anali atatsala pang’ono kulilandiralo, anafunikira kukonda Yehova ndi kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira kuti alandire zimene ankayembekezera. (Eksodo 3:8) Mose anamveketsapo bwino, chifukwa anati: ‘[Ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene, NW] ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, [pamenepo, NW] mudzakhala ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m’dziko limene muloŵako kulilandira.’—Deuteronomo 30:16.
12. Kodi chitsanzo cha Aisrayeli chikutiphunzitsa chiyani ponena za ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa?
12 Kodi zimene takambiranazi sizikutiphunzitsa kanthu kena kokhudza ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa m’nthaŵi yamapeto ino? Timaganiza za dziko la Paradaiso likudzalo ndipo timalankhula za ilo mu utumiki wathu. Koma ifeyo ngakhale ophunzira amene timapanga sitidzaona lonjezo limenelo litakwaniritsidwa ngati ifeyo pamodzi ndi iwowo timatumikira Mulungu pazifukwa zadyera. Ifeyo limodzi ndi anthu amene tikuphunzitsa tiyenera kuphunzira ‘kukonda Yehova, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira Iye,’ monga anachitira Aisrayeli. Tikamakumbukira zimenezi pochita utumiki wathu, ndiye kuti tikugwira ntchito limodzi ndi Mulungu kukokera anthu kwa iye.
Antchito Anzake a Mulungu
13, 14. (a) Malinga ndi kunena kwa 1 Akorinto 3:5-9, kodi timakhala bwanji antchito anzake a Mulungu? (b) Kodi anthu akamawonjezeka, ndani amene ayenera kutamandidwa, ndipo n’chifukwa chiyani?
13 Paulo anayerekeza kugwira kwathu ntchito limodzi ndi Mulungu ndi kulima munda. Analemba kuti: “Ndipo Apolo n’chiyani, ndi Paulo n’chiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anam’patsa. Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphoto yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu . . . ndi inu.”—1 Akorinto 3:5-9.
14 Poti ndife antchito anzake a Mulungu, tiyenera kubzala mokhulupirika “mawu a Ufumu” m’mitima ya anthu, ndiyeno chidwi chilichonse chimene anthuwo ali nacho tichithirire mwa kukonzekera bwino maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo. Ngati nthakayo, kutanthauza mtima, ili yabwino, Yehova adzachitapo mbali yake mwa kukulitsa mbewu ya choonadi cha Baibulo n’kukhala mtengo wobala zipatso. (Mateyu 13:19, 23) Adzam’kokera munthuyo kwa iye yekha ndi kwa Mwana wake. Potsirizira penipeni, olengeza Ufumu akamawonjezeka chimakhala chifukwa chakuti Yehova ndiye amakonza mitima ya anthuwo, kukulitsa mbewu ya choonadi ndi kuwakokera anthuwo kwa iye yekha ndi kwa Mwana wake.
Ntchito Yomanga Yokhalitsa
15. Kodi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo lotani posonyeza mmene tingathandizire ena kukulitsa chikhulupiriro?
15 Pamene tikukondwera poona anthu akuwonjezeka, timafunanso ndithu kuwaona akupitiriza kukonda Yehova, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira. Timakhumudwa tikamaona ena akuzirala nagwa. Kodi tingachitepo kanthu kuti zimenezi zisamachitike? Mwa fanizo lina, Paulo anasonyeza mmene tingathandizire ena kukulitsa chikhulupiriro. Analemba kuti: “Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, maudzu, dziputu, ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbuluka m’moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.”—1 Akorinto 3:11-13.
16. (a) Kodi mafanizo aŵiri amene Paulo ananena akusiyana bwanji cholinga chake? (b) Kodi ntchito yathu yomanga ingakhale bwanji yosakhutiritsa ndipo yosachedwa kugwira moto?
16 M’fanizo la Paulo la munda, kukula kwa mbewu kumadalira khama la kubzala, kuithirira nthaŵi zonse, komanso dalitso la Mulungu. Fanizo lina la mtumwiyo likusonyeza udindo umene mtumiki wachikristu amakhala nawo chifukwa cha mmene ntchito yake yomanga imadzakhalira. Kodi wamanga pamaziko olimba ndi zomangira zolimba? Paulo anachenjeza kuti: “Yense ayang’anire umo amangira pamenepo.” (1 Akorinto 3:10) Pamene tangodzutsa chidwi cha munthu wina mwa kumuuza za chiyembekezo cha moyo wosatha m’Paradaiso, kodi timangom’phunzitsa mfundo zazikulu za chidziŵitso cha Malemba ndiyeno n’kumangogogomeza zimene munthuyo ayenera kuchita kuti apeze moyo wosatha? Kodi pophunzitsa, timangolimbikira kunena kuti: ‘Ngati mukufuna kukhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso, muyenera kumaphunzira, kupita ku misonkhano, ndi kugwira nawo ntchito yolalikira’? Ngati timatero, ndiye kuti sitikumanga chikhulupiriro cha munthuyo pamaziko olimba, ndipo chimene tikumanga sichingalephere kugwira msanga moto wa ziyeso ndipo sichingakhalitse. Kuyesa kukokera anthu kwa Yehova mwa kungowauza za chiyembekezo cha moyo m’Paradaiso chifukwa chom’tumikira kwa zaka zingapo kuli ngati kumanga ndi “mtengo, maudzu, dziputu.”
Kukulitsa Chikondi pa Mulungu Komanso pa Kristu
17, 18. (a) Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti chikhulupiriro cha munthu chikhale cholimba? (b) Kodi tingam’thandize bwanji munthu kuti Kristu akhale mumtima mwake?
17 Kuti chikhulupiriro chikhale cholimba, maziko ake ayenera kukhala unansi wa munthu mwini ndi Yehova Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu. Monga anthu opanda ungwiro, tingakhale ndi unansi wamtendere umenewo ndi Mulungu kudzera mwa Mwana wake basi. (Aroma 5:10) Kumbukirani kuti Yesu anati: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” Kuti tithandize ena kukulitsa chikhulupiriro, “palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.” Kodi mawu amenewo akutanthauzanji?—Yohane 14:6; 1 Akorinto 3:11.
18 Kumanga pamaziko a Kristu kumatanthauza kuphunzitsa mwa njira yakuti wophunzira Baibulo afikire pakukonda kwambiri Yesu atadziŵa bwino za ntchito Yake monga Momboli, Mutu wa mpingo, Mkulu wa Ansembe wachikondi, ndiponso Mfumu yolamulira. (Danieli 7:13, 14; Mateyu 20:28; Akolose 1:18-20; Ahebri 4:14-16) Kumatanthauza kuwathandiza kuona Yesu kukhala weniweni ndithu moti azikhala m’mitima yawo. Mapemphero athu powapempherera ayenera kukhala ngati la Paulo popempherera Akristu a ku Efeso. Analemba kuti: ‘Ndipinda maondo anga kwa Atate, . . . kuti Kristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m’mitima yanu; kuti muzike mizu ndi kutsendereka m’chikondi.’—Aefeso 3:14-17.
19. Kodi tikamakulitsa chikondi cha Kristu m’mitima ya ophunzira Baibulo, chimachitika n’chiyani, koma kodi tiyenera kuwaphunzitsa chiyani?
19 Tikamamanga mwanjira yoti ophunzira athu n’kukhala ndi chikondi pa Kristu m’mitima yawo, ndiye kuti adzayambanso kukonda Yehova Mulungu. Chikondi, kukoma mtima, ndi chifundo zimene Yesu anali nazo zinkasonyeza mosasintha mikhalidwe ya Yehova. (Mateyu 11:28-30; Marko 6:30-34; Yohane 15:13, 14; Akolose 1:15; Ahebri 1:3) Choncho, pamene anthu adziŵa Yesu ndi kum’konda, amadziŵanso Yehova ndi kum’konda.a (1 Yohane 4:14, 16, 19) Tifunikira kuwaphunzitsa ophunzira Baibulo kuti Yehova ndiye anakonza zonse zimene Kristu wachitira anthu, ndi kuti tiyenera kum’yamikira Iyeyo, kum’tamanda, ndi kum’lambira monga “Mulungu wa chipulumutso chathu.”—Salmo 68:19, 20; Yesaya 12:2-5; Yohane 3:16; 5:19.
20. (a) Kodi tingawathandize bwanji anthu kuyandikira kwa Mulungu ndi kwa Mwana wake? (b) Kodi tidzakambirana zotani m’nkhani yotsatira?
20 Poti ndife antchito anzake a Mulungu, tiyeni tithandize anthu kuyandikira kwa iye ndiponso kwa Mwana wake, kuwathandiza kukulitsa chikondi ndi chikhulupiriro m’mitima yawo. Mwa njira imeneyo, Yehova adzakhala weniweni kwa iwo. (Yohane 7:28) Kudzera mwa Kristu, iwo adzakhala paubwenzi weniweni ndi Mulungu, ndipo adzam’konda ndi kum’mamatira. Sadzaleka kum’tumikira mwachikondi, pokhulupirira kuti malonjezo odabwitsa a Yehova adzakwaniritsa panthaŵi yake. (Maliro 3:24-26; Ahebri 11:6) Komabe, pamene tikuthandiza ena kukulitsa chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chikondi chawo, ifenso tiyenera kumanga chikhulupiriro chathu kuti chikhale ngati chombo cholimba chokhoza kudutsa namondwe panyanja. Zimenezo tidzakambirana m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Buku lothandiza kwambiri kum’dziŵa bwino Yesu, komanso kudziŵa Yehova, Atate wake kudzera mwa iyeyo ndilo la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kubwereramo
◻ Kodi nthaŵi zambiri timadzutsa motani chidwi cha anthu pa uthenga wa Ufumu, koma kodi pali ngozi yotani?
◻ Kodi ndi anthu otani amene Yehova amakokera kwa iye mwini ndi kwa Mwana wake?
◻ Kodi kuloŵa kwa Aisrayeli m’Dziko Lolonjezedwa kunadalira chiyani, ndipo tikuphunzirapo chiyani pamenepa?
◻ Kodi ifeyo timachita mbali yotani pothandiza anthu kuyandikira kwa Yehova ndi Mwana wake?
[Chithunzi patsamba 10]
Ngakhale kuti timapatsa anthu chiyembekezo cha moyo wosatha m’Paradaiso, cholinga chathu chachikulu ndicho kuwakokera kwa Yehova
[Zithunzi patsamba 13]
Maulendo athu obwereza angakhale ogwira mtima ngati tikonzekera bwino