Kodi Ntchito Yanu Idzapulumuka Moto?
“Yense ayang’anire umo amangira [pamazikowo].”—1 AKORINTO 3:10.
1. Kodi Akristu okhulupirika amayembekezera zotani kwa aja ofuna kukhala ophunzira?
BANJA lachikristu likuyang’ana mwana wawo amene wangobadwa kumene. Wofalitsa Ufumu akuona kuti nkhope ya wophunzira Baibulo ikuonetsa kuti akufunitsitsa ndipo ali ndi chidwi. Mkulu wachikristu akuphunzitsa ali papulatifomu ndipo akuona mwa omvetsera munthu wokondwerera watsopano akufunafuna malemba mwakhama m’Baibulo lake. Atumiki okhulupirika a Yehova amenewa ali ndi mitima yodzaza chiyembekezo. Sangachitire mwina kusiyapo kufunsa kuti, ‘Kodi munthu ameneyu adzafika pakumkonda Yehova, kumtumikira—ndi kukhalabe wokhulupirika?’ Inde, zimenezo sizichitika zokha. Zimafuna kulimbikira.
2. Kodi mtumwi Paulo anawakumbutsa motani Akristu achihebri za kufunika kwa ntchito yophunzitsa, ndipo zimenezi zingatisonkhezere kudzipenda ife eni motani?
2 Pokhala mphunzitsi waluso iye mwini, mtumwi Paulo anagogomezera kufunika kwa ntchito yophunzitsa ndi kupanga ophunzira pamene analemba kuti: “Mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi.” (Ahebri 5:12) Akristu amene iye analembera sanali kupita patsogolo kwenikweni, tikalingalira za utali wa nthaŵi imene anakhala okhulupirira. Iwo anali osakonzekera kuphunzitsa ena komanso anafunikira kukumbutsidwa za mbali zoyambirira za choonadi. Lerolino, tonsefe tingachite bwino nthaŵi ndi nthaŵi kupenda maluso athu monga aphunzitsi ndi kuona mmene tingawawongolere. Miyoyo ili pangozi. Kodi tingachitenji?
3. (a) Kodi Paulo anaifanizira ndi chiyani ntchito yopanga ophunzira achikristu? (b) Monga omanga achikristu, kodi tili ndi mwayi wotani waukulu?
3 M’fanizo lotanthauza zambiri, Paulo anafanizira ntchito yopanga ophunzira ndi ntchito yomanga nyumba. Anayamba mwa kunena kuti: “Ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.” (1 Akorinto 3:9) Chotero timachita nawo ntchito yomanga yokhudza anthu; timathandiza kuwamanga kukhala ophunzira a Kristu. Timatero monga antchito anzake a Iye amene ‘anamanga zonse.’ (Ahebri 3:4) Ati mwayi wake kukula! Tiyeni tione mmene uphungu wouziridwa wa Paulo kwa Akorinto ungatithandizire kukhala aluso kwambiri pantchito yathu. Makamaka tisumika maganizo pa “luso la kuphunzitsa.”—2 Timoteo 4:2, NW.
Kuika Maziko Oyenera
4. (a) Kodi Paulo anali ndi udindo wotani pantchito yomanga yachikristu? (b) Nchifukwa chiyani tinganene kuti Yesu ndi omvetsera ake ankadziŵa za kufunika kwa maziko abwino?
4 Kuti nyumba ikhale yolimba ndi yokhalitsa, imafunikira maziko abwino. Nchifukwa chake Paulo analemba kuti: “Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwinimamangidwe waluso, ndinaika maziko.” (1 Akorinto 3:10) Pogwiritsa ntchito fanizo lofanana, Yesu Kristu anasimba za nyumba imene inapulumuka mphepo yamkuntho chifukwa woimanga anasankha maziko olimba. (Luka 6:47-49) Yesu ankadziŵa bwino za kufunika kwa maziko. Analipo pamene Yehova anakhazika dziko lapansi pa maziko ake.a (Miyambo 8:29-31) Anthu amene anali kumvera Yesu akulankhula ankadziŵanso kufunika kwa maziko abwino. Nyumba zokha zomwe zikanapulumuka zigumula ndi zivomezi zomwe nthaŵi zina zinkachitika ku Palestina ndi zija zomwe anazimanga pa maziko olimba. Nanga kodi Paulo anali kunena za maziko ati?
5. Kodi maziko a mpingo wachikristu ndani, ndipo zimenezi zinaloseredwa motani?
5 Paulo analemba kuti: “Palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.” (1 Akorinto 3:11) Uku sikuyamba kutchula Yesu kuti ali ngati maziko. Ndipotu Yesaya 28:16 analosera kuti: ‘Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m’Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wamtengo wake [wa maziko, NW] okhazikika ndithu.’ Yehova kwa nthaŵi yaitali anali atafuna kuti Mwana wake akhale maziko a mpingo wachikristu.—Salmo 118:22; Aefeso 2:19-22; 1 Petro 2:4-6.
6. Kodi Paulo anawaika motani maziko oyenera mwa Akristu a ku Korinto?
6 Kodi maziko a Mkristu aliyense payekha nchiyani? Malinga ndi kunena kwa Paulo, palibe maziko ena a Mkristu woona kusiyapo aja oikidwa m’Mawu a Mulungu—Yesu Kristu. Ndithudi Paulo anaika maziko amenewo. Ku Korinto, kumene anthu ankalemekeza kwambiri filosofi, iye sanafune kukondweretsa anthu ndi nzeru yadziko. M’malo mwake, Paulo analalikira “Kristu wopachikidwa,” zimene amitundu anangoti “chinthu chopusa” zedi. (1 Akorinto 1:23) Paulo anaphunzitsa kuti Yesu ngwofunika kwambiri pazolinga za Yehova.—2 Akorinto 1:20; Akolose 2:2, 3.
7. Kodi tingatengepo phunziro lotani pakudzitcha kwa Paulo kuti “mwinimamangidwe waluso”?
7 Paulo anatchula kuti anaphunzitsa “ngati mwinimamangidwe waluso.” Mawu amenewa sanali kudzikuza ayi. Anali kungovomereza za mphatso yapadera imene Yehova anampatsa—yokonza kapena kuyang’anira ntchito. (1 Akorinto 12:28) Inde, ife lero tilibe mphatso zozizwitsa zimene Akristu a m’zaka za zana loyamba anapatsidwa. Ndipo mwina sitingaganize kuti ndife aphunzitsi amene ali ndi mphatso. Komatu tili otero m’lingaliro lina lofunika. Talingalirani: Yehova amatipatsa mzimu wake woyera kuti utithandize. (Yerekezerani ndi Luka 12:11, 12.) Ndipo tili ndi chikondi cha Yehova ndi chidziŵitso cha ziphunzitso zoyambirira za Mawu ake. Zimenezi ndi mphatso zabwino kwambiri zogwiritsa ntchito pophunzitsa ena. Titsimikizetu mtima kuzigwiritsa ntchito kuika maziko abwino.
8. Kodi timamuika motani Kristu monga maziko mwa ofuna kukhala ophunzira?
8 Pamene tiika Kristu kukhala maziko, sitimuonetsa monga khanda limene silingadziteteze m’chodyeramo ng’ombe, kapenanso kukhala wolingana ndi Yehova monga mbali ya Utatu. Sititero ayi chifukwa zikhulupiriro zosakhala zamalemba zimenezo zili maziko a Akristu onyenga. Koma timaphunzitsa kuti iye anali munthu wamkulu koposa onse amene anakhalako, kuti anapereka moyo wake wangwiro m’malo mwathu, ndi kutinso lero ali Mfumu yoikidwa ya Yehova yolamulira kumwamba. (Aroma 5:8; Chivumbulutso 11:15) Timayesetsanso kusonkhezera ophunzira athu kutsatira mapazi a Yesu ndi kutsanzira mikhalidwe yake. (1 Petro 2:21) Timafuna kuti iwo asonkhezeredwe kwambiri ndi kukangalika kwa Yesu mu utumiki, chisoni chake kwa ofatsa ndi oponderezedwa, chifundo chake kwa ochimwa osweka mtima ndi tchimo lawo, kulimba mtima kwake kosagwedera poyang’anizana ndi mayesero. Inde, Yesu ndi maziko amtengo wake. Koma chotsatira nchiyani?
Kumanga ndi Zomangira Zoyenera
9. Ngakhale kuti Paulo makamaka anali woika maziko, kodi anali ndi nkhaŵa yotani kwa aja amene analandira choonadi chimene anawaphunzitsa?
9 Paulo analemba kuti: “Koma ngati wina amanga pamazikowo, golidi, siliva, miyala yamtengo wake, mtengo, maudzu, dziputu, ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbuluka m’moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.” (1 Akorinto 3:12, 13) Kodi Paulo anatanthauzanji? Talingalirani zochitika zakumbuyo. Paulo makamaka anali woika maziko. Pamaulendo ake aumishonale, anayendayenda kumzinda ndi mzinda, kulalikira kwa anthu ambiri omwe sanamvepo za Kristu. (Aroma 15:20) Pamene anthu analandira choonadi chimene anawaphunzitsa, mipingo inapangidwa. Paulo ankasamala kwambiri za okhulupirira amenewo. (2 Akorinto 11:28, 29) Komabe, ntchito yake inafuna kuti apitirizebe maulendo ake. Chotero atatha miyezi 18 akuika maziko ku Korinto, anachoka nakalalikira kumizinda ina. Komabe, anafunitsitsa kwambiri kudziŵa mmene ena anapitirizira ndi ntchito imene iye anachita kumeneko.—Machitidwe 18:8-11; 1 Akorinto 3:6.
10, 11. (a) Kodi Paulo anaisiyanitsa motani mitundu ya zomangira? (b) Kodi m’Korinto wakale mungakhale munali nyumba zenizeni zamitundu yotani? (c) Kodi ndi nyumba zotani zomwe zingapulumuke moto, ndipo zimenezo zikupereka chitsanzo chotani kwa Akristu opanga ophunzira?
10 Zikukhala ngati ena amene anali kumanga pamaziko amene Paulo anaika ku Korinto sanali kumanga bwino. Pofuna kuvumbula vutolo, Paulo akusiyanitsa mitundu iŵiri ya zomangira: golidi, siliva, ndi miyala yamtengo wake kumbali ina; mitengo, maudzu, ndi dziputu kumbali inanso. Nyumba ingamangidwe ndi zomangira zabwino, zokhalitsa ndi zosagwira moto; kapenanso ingamangidwe msangamsanga ndi zomangira zosalimba, zakanthaŵi, ndi zogwira moto. Mosakayikira mzinda waukulu ngati Korinto unali ndi nyumba zambiri zomangidwa ndi zomangira zamitundu iŵiriyo. Munali akachisi aakulu opangidwa ndi miyala yaikulu yamtengo wapatali, mwinamwake yokhala ndi golidi ndi siliva kutsogolo kwake kapena m’mbali zina ndi zina.b Mwinamwake nyumba zokhalitsa zimenezi zinali zazitali ndipo mmunsi mwake munali nyumba, zithando, ndi pogulitsira, zomangidwa ndi matabwa osakonzeka ndiponso zofolera ndi udzu.
11 Kodi chingachitikire nyumba zimenezi patabuka moto nchiyani? Yankho lake linali lachidziŵikire m’tsiku la Paulo mofanananso ndi m’tsiku lathu. Kwenikweni, mzinda wa Korinto unagonjetsedwa ndi kutenthedwa ndi Kazembe wa Roma Mummius kalelo mu 146 B.C.E. Nyumba zambiri zamitengo, udzu, kapena dziputu ziyenera kuti zinawonongedweratu. Bwanji nanga za nyumba zolimba zamiyala, zokometseredwa ndi siliva ndi golidi? Mosakayikira, zimenezi zinapulumuka. Ophunzira a Paulo ku Korinto ayenera kuti anadutsa nyumba ngati zimenezo tsiku ndi tsiku—nyumba zaulemerero zamiyala zimene zinapulumuka masoka akale amene anasakaziratu nyumba zina zapafupi zosakhalitsa kwenikweni. Komatu Paulo anaigogomezera bwino zedi mfundo imeneyi! Pophunzitsa, tizidziyesa omanga. Tikufuna kumanga ndi zomangira zabwino koposa ndipo zokhalitsa kwambiri. Tikatero zitheka kuti ntchito yathu idzakhalitsa. Kodi zomangira zokhalitsa zimenezo nchiyani, ndipo nchifukwa chiyani zifunika kuzigwiritsa ntchito?
Kodi Ntchito Yanu Idzapulumuka Moto?
12. Kodi ndi motani mmene Akristu ena a ku Korinto ankachitira ntchito yoipa pomanga?
12 Mwachionekere, Paulo anaona kuti Akristu ena ku Korinto sanali kumanga bwino. Chinalakwika nchiyani? Malinga ndi nkhaniyo, mumpingo munali magaŵano, kukopeka ndi maumunthu ngakhale kuti zimenezo zinasokoneza umodzi wa mpingo. Ena ankati, “Ine ndine wa Paulo,” pamene ena ankaumirira kuti, “Ndine wa Apolo.” Ena mwachionekere ankadziyesa anzeru kwambiri. Choncho nzosadabwitsa kuti panatsatira malingaliro athupi, ukhanda wauzimu, ndi “nkhwidzi ndi ndewu” zochuluka. (1 Akorinto 1:12; 3:1-4, 18) Mzimu umenewu sunalephere kuonekera m’chiphunzitso chimene chinaperekedwa mumpingo ndi mu utumiki. Zotsatira zake zinali zakuti ntchito yawo yopanga ophunzira inali yoipa, yofanana ndi kumanga nyumba ndi zomangira zosalimba. Sikanapulumuka “moto.” Kodi Paulo anali kulankhula za moto wotani?
13. Kodi moto wa m’fanizo la Paulo ukuimira chiyani, ndipo Akristu onse ayenera kusamala za chiyani?
13 Ulipo moto umene tonsefe timakumana nawo pamoyo wathu—ziyeso za chikhulupiriro chathu. (Yohane 15:20; Yakobo 1:2, 3) Akristu a ku Korinto anafunikira kudziŵa, monga momwedi ifenso tifunikira kudziŵa kuti aliyense amene tikuphunzitsa choonadi adzayesedwa. Ngati sitiphunzitsa bwino, zotsatira zake zingakhale zachisoni. Paulo anachenjeza kuti: “Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho. Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzawonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.”c—1 Akorinto 3:14, 15.
14. (a) Kodi ndi motani mmene zinthu za Akristu opanga ophunzira ‘zingawonongekere,’ koma kodi angapulumuke motani monga mwa moto? (b) Kodi tingapewe motani kutayikidwa?
14 Mawu amenewo akufuna kuwaganizapo kwambiri! Zingakhale zopweteka kulimbikira kuthandiza munthu wina kukhala wophunzira, ndiyeno kumuona akugonja pachiyeso kapena chizunzo ndipo m’kupita kwa nthaŵi kusiya njira ya choonadi. Paulo akuvomereza zomwezo pamene akuti zikatere zathu zonse zimawonongeka. Zimenezo zingakhale zopweteka kwambiri moti chipulumutso chathu chikufotokozedwa kukhala “monga momwe mwa moto”—monga munthu amene zake zonse zatenthedwa ndi moto ndipo iye nkupulumutsidwa ali pafupi kutenthedwa. Nangano kodi ifeyo tingaipewe motani ngozi ya kutayikidwa zathu zonse? Timange ndi zomangira zokhalitsa! Ngati tiphunzitsa ophunzira athu mwanjira yoti tikuwafika pamtima, kuwasonkhezera kuyamikira mikhalidwe yachikristu yamtengo wapatali monga nzeru, kuzindikira, kuopa Yehova, ndi chikhulupiriro chenicheni, ndiye kuti tikumanga ndi zomangira zokhalitsa zosagwira moto. (Salmo 19:9, 10; Miyambo 3:13-15; 1 Petro 1:6, 7) Amene amapeza mikhalidwe imeneyi amapitiriza kuchita chifuniro cha Mulungu; chiyembekezo chawo chokhala ndi moyo kosatha nchotsimikizirika. (1 Yohane 2:17) Komano kodi tingaligwiritse ntchito motani fanizo la Paulo kuti litithandize? Talingalirani zitsanzo zina.
15. Kodi tingachite motani kuti titsimikize kupewa kuchita ntchito yoipa pomanga ophunzira Baibulo athu?
15 Pophunzitsa ophunzira Baibulo, tisakweze anthu m’malo mwa Yehova Mulungu. Cholinga chathu sichakuti tiwaphunzitse kutiona ngati ndife gwero la nzeru zonse. Tikufuna kuti iwo aziyang’ana kwa Yehova, Mawu ake, ndi gulu lake kaamba ka chitsogozo. Pofuna kukwaniritsa zomwezo, sitiwauza malingaliro athuathu poyankha mafunso awo. M’malo mwake, timawaphunzitsa kupeza mayankho, kugwiritsa ntchito Baibulo ndi zofalitsa zomwe “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka. (Mateyu 24:45-47) Pazifukwa zofananazo, timasamala kusawachitira nsanje ophunzira Baibulo athu. M’malo moipidwa pamene ena aonetsa chidwi mwa iwo, tiyenera kulimbikitsa ophunzira athu ‘kufutukula’ chikondi chawo, kufika pakudziŵa ambiri mumpingo ndi kuwaŵerengera.—2 Akorinto 6:12, 13, NW.
16. Kodi akulu angamange motani ndi zomangira zosagwira moto?
16 Akulunso achikristu amathandiza kwambiri pakumanga ophunzira. Pophunzitsa mpingo, amayesetsa kumanga ndi zomangira zosagwira moto. Iwo angasiyane maluso awo a kuphunzitsa, chidziŵitso, ndi maumunthu, koma sadyerera kusiyana kumeneku kuti akope ena kukhala otsatira awo. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:29, 30.) Sitikudziŵa kwenikweni chifukwa chake ena ku Korinto ankanena kuti, “Ine ndine wa Paulo,” kapena kuti, “Ndine wa Apolo.” Koma ndife otsimikiza kuti palibe aliyense wa akulu okhulupirika amenewa amene analimbikitsa magaŵano. Paulo sanali kukondwera ndi malingaliro amenewo; anawatsutsa zolimba. (1 Akorinto 3:5-7) Mofananamo lero, akulu amakumbukira kuti akuweta ‘gulu la Mulungu.’ (1 Petro 5:2) Si la munthu wina aliyense. Chotero akulu amatsutsa zolimba mzimu umene munthu mmodzi angakhale nawo wofuna kulamulira gulu la nkhosa kapena bungwe la akulu. Malinga ngati chikhumbo chimene chimasonkhezera akulu kutumikira mpingo chimaphatikizapo kudzichepetsa, kufuna kufika anthu pamtima, ndi kuthandiza nkhosa kutumikira Yehova ndi moyo wonse, amamanga ndi zomangira zosagwira moto.
17. Kodi makolo achikristu amayesetsa motani kumanga ndi zomangira zosagwira moto?
17 Makolonso achikristu imawakhudza kwambiri nkhani imeneyi. Iwo amalakalaka kwambiri kuona ana awo atakhala ndi moyo wosatha! Ndiye chifukwa chake amalimbikira ‘kuphunzitsa’ ana awo mapulinsipulo a Mawu a Mulungu kuwaloŵetsa m’mitima yawo. (Deuteronomo 6:6, 7) Amafuna kuti ana awo adziŵe choonadi, osati monga mpambo wa malamulo kapena monga ndakatulo ya zikhulupiriro, koma monga njira ya moyo wachikwanekwane, wofupa, ndi wachimwemwe. (1 Timoteo 1:11, NW) Kuti amange ana awo kukhala ophunzira okhulupirika a Kristu, makolo achikondi amayesetsa kugwiritsa ntchito zomangira zosagwira moto. Amachita moleza mtima ndi ana awo, kuwathandiza kuchotsa mikhalidwe imene Yehova amada ndi kukulitsa mikhalidwe imene iye amakonda.—Agalatiya 5:22, 23.
Kodi Ndi Mlandu Wayani?
18. Pamene wophunzira wasiya chiphunzitso cholama, nchifukwa chiyani makamaka sungakhale mlandu wa amene akuyesetsa kumphunzitsa?
18 Nkhani imeneyi ikudzutsa funso lofunika. Ngati wina amene tikuyesetsa kumthandiza wasiya choonadi, kodi zitanthauza kuti tinalephera ifeyo monga aphunzitsi—kuti tinamanga ndi zomangira zosalimba? Osati kwenikweni. Mawu a Paulo akutikumbutsa kuti kuchita nawo ntchito yomanga ophunzira ndi udindo waukulu zedi. Tiyenera kuchita zonse zotheka kuti timange bwino. Koma Mawu a Mulungu sakutiuza kusenza udindo wonsewo ndiyeno kudzimva wamlandu pamene aja amene tikuyesetsa kuwathandiza afulatira choonadi. Pali zinthu zina zimene zikuphatikizidwa kuwonjezera pa ntchito yathu monga omanga. Mwachitsanzo, onani zimene Paulo akunena ngakhale za mphunzitsi amene sanachite ntchito yabwino pomanga: “Zidzawonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa.” (1 Akorinto 3:15) Ngati munthu ameneyu angapeze chipulumutso m’kupita kwa nthaŵi—pamene umunthu wachikristu umene anayesetsa kumanga mwa wophunzira wake ukuonetsedwa kukhala ‘utatenthedwa’ ndi chiyeso chonga moto—kodi tingati chiyani? Tinganene kuti Yehova makamaka akuona wophunzirayo kuti ndiye adzayankha mlandu pazimene wasankha, kaya kukhala wokhulupirika kapena ayi.
19. Kodi tidzapenda chiyani m’nkhani yotsatira?
19 Kudziyankhira mlandu pawekha ndi nkhani yofunika kwambiri. Imakhudza aliyense wa ife. Makamaka, kodi Baibulo limaphunzitsa zotani pankhaniyo? M’nkhani yathu yotsatira tidzapenda zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a “Maziko a dziko” angatanthauze mphamvu zachilengedwe zimene zimaligwira—ndi zakumwamba zonse—kuti likhazikike zolimba. Ndiponso, dziko lapansi linamangidwa mwanjira yakuti “silidzagwedezeka” konse, kapena kuwonongeka.—Salmo 104:5.
b “Miyala yamtengo wake” imene Paulo anatchula kwenikweni sinali ngale, monga diamondi ndi rubi. Mwina inali miyala yomangira yamtengo wapatali monga marble, alabasitero, kapena granite.
c Paulo anali kukayikira chipulumutso cha “ntchito” ya womangidwayo, osati cha womangayo ayi. The New English Bible imati pavesili: “Ngati nyumba ya munthu iima, adzafupidwa; ngati itenthedwa, adzatayikidwa; komano adzapulumutsa moyo wake, monga momwe munthu angaupulumutsire ku moto.”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi “maziko” mwa Mkristu woona nchiyani, ndipo amaikidwa motani?
◻ Kodi tingaphunzireponji pa zomangira zosiyanasiyana?
◻ Kodi “moto” umaimira chiyani, ndipo ungapangitse motani zinthu za ena ‘kuwonongeka’?
◻ Kodi aphunzitsi a Baibulo, akulu ndi makolo angamange motani ndi zomangira zosagwira moto?
[Chithunzi patsamba 9]
M’mizinda yakale yambiri, nyumba zamiyala zosagwira moto zinali pamodzi ndi nyumba zosalimba