Kumanga Maumunthu Achikristu mwa Ana Athu
AMAYI a Wanda, omwe anasiidwa ndi amuna awo, anagwira ntchito zolimba kumanga mikhalidwe Yachikristu mwa mwana wawo wamkazi. Pamene Wanda anali ndi zaka 12, kuphunzitsa kumeneku kunaikidwa pachiyeso. Panthaŵiyo, Wanda, limodzinso ndi ang’ono ake mchimwene ndi mchemwali, anakakamizika kusiya amayi awo kukakhala ndi abambo ake kwakanthaŵi. Abambo ake anali osakhulupirira, chotero kodi Wanda akachita motani pamene amayi ake sanali kumyang’anira?
Chokumana nacho chomwe chimagwera makolo onse Achikristu ndinthaŵi pamene ana awo ayenera kudzipangira zosankha, kuyesa chikhulupiriro chawo. Ana angalekanitsidwe ndi makolo awo Achikristu, monga momwe zinaliri ndi Wanda. Iwo angayang’anizane ndi chitsenderezo cha mabwenzi awo kuti achite choipa kusukulu. Kapena angayang’anizane ndi ziyeso zamphamvu. Makolo Achikristu amayembekezera ndi kupemphera kuti pamene zimenezo zichitika, ana awo adzakhala ndi maumunthu Achikristu olimba mokhoza kupirira chiyesocho.
Kodi makolo angamange motani maumunthu Achikristu olimba mwa ana awo? Tisanapeze zimene zinachitikira Wanda, tiyeni tiwone mmene Baibulo limatithandizira kuyankha funsolo. Maziko a yankholo akupezeka m’mawu aŵa a mtumwi Paulo olembedwera Akristu ku Korinto: ‘Palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, maudzu, dziputu, ntchito ya yense idzawonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbuluka m’moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.’—1 Akorinto 3:11-13.
Mazikowo
Kodi Paulo analemberanji mawu ameneŵa? Iye anali atayamba programu yomanga maumunthu Achikristu ku Korinto, koma programuyo inagwera m’mavuto. Ndithudi, programu yomanga ya Paulo sinaloŵetsemo ana akeake akuthupi. Inaloŵetsamo aja amene anakhala Akristu kupyolera m’kulalikira kwake. Koma iye anaŵawona monga ana auzimu, ndipo zimene ananena nzofunikanso kwa makolo.—1 Akorinto 4:15.
Paulo adabwera ku Korinto nthaŵi ina kumbuyoko ndipo adakhazikitsa mpingo Wachikristu kumeneko. Amene anachitapo kanthu pa kulalikira kwake anapanga masinthidwe aakulu m’maumunthu awo. Ena kalelo anali anthu achisembwere, mbala, olambira mafano, ndi oledzera. (1 Akorinto 6:9-11) Koma anali okhoza kusinthira ku kulingalira Kwachikristu chifukwa Paulo anali atakhazikitsa maziko abwino, kunena kwake titero. Kodi maziko amenewo anali chiyani? “Palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.”—1 Akorinto 3:11.
Kodi ndimotani mmene Paulo anakhazikitsira maziko ameneŵa pamene ankaphunzitsa okhulupirira atsopanowo m’Korinto? Iye akutiuza kuti: ‘Ine, abale, mmene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu. Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziŵe kanthu mwa inu, koma Yesu Kristu, ndi iye wopachikidwa.’ (1 Akorinto 2:1, 2; Machitidwe 18:5) Iye sanalunjikitse chidwi kwa iyemwini kapena kukometsera chowonadi kuchipanga chokopa mwaukatswiri wamaphunziro wachiphamaso. Mmalomwake, iye anakokera chidwi pa Yesu Kristu ndimmene ameneyu anagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu.
Ndithudi, Yesu ndimaziko olimba aakulu a kumanga Chikristu. Iye anapereka nsembe yadipo. Tsopano ali Mfumu yakumwamba ndipo monga wotero adzawononga adani a Mulungu posachedwapa pa Armagedo. Ndiyeno adzapereka chilungamo cha Mulungu mkati mwa kulamulira kwa zaka chikwi, ndipo monga Mkulu Wansembe wa Mulungu, mwapang’onopang’ono adzafitsa fuko la anthu ku ungwiro. Kodi ndimaziko ena ati amene munthu angafune?
Chotero, pomanga maumunthu Achikristu mwa ana athu, timachita bwino kutsanzira Paulo ndi kutsimikizira kuti iwo amazindikira mfundo zofunika zimenezi. Kuchokera ku ukhanda wawo, tiyenera kuŵaphunzitsa ana athu kukonda Yesu kaamba ka zimene watichitira ndi zimene akutichitirabe.—1 Petro 1:8.
Kumangako
Komabe, pamene kuli kwakuti Paulo anakhazikitsa maziko abwino ameneŵa, ntchito yomangayo inabwerera m’mbuyo pamene iye anachoka. (1 Akorinto 3:10) Vutolo silinali losiyana ndi zimene makolo ambiri amakumana nazo lerolino. Iwo amalera ana awo m’chikhulupiriro Chachikristu ndipo amatsimikizira kuti anawo amvetsetsa chowonadi. Koma pamene akula, anawo amapatuka kapena kuchikana chikhulupirirocho. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Kaŵirikaŵiri nchifukwa cha milimo yogwiritsiridwa ntchito.
Paulo ananena kuti maumunthu angamangidwe ndi milimo ya mtengo wapatali yonga: golidi, siliva, ndi miyala ya mtengo wake. Kapena kuti angamangidwe ndi milimo yosalimba yonga: mtengo, maudzu, ndi dziputu. (1 Akorinto 3:12) Tsopano, ngati womanga agwiritsira ntchito golidi, siliva, ndi miyala ya mtengo wake, iye ayenera kumanga mtundu wa nyumba yapamwamba koposa, ya mtengo wapatali koposa. Koma womanga wogwiritsira ntchito mtengo, maudzu, ndi dziputu akungomanga chinthu chosakhalitsa, chapakanthaŵi, ndi chosalimba.
Kukuwoneka kuti milimo yosalimba yauzimu inkagwiritsiridwa ntchito ku Korinto. Amene anatsatira kukhazikitsa maziko kwa mtumwi Paulo anali kumanga mosalimba, kumanga nyumba zosalimba, ndi zosakhoza kukhalitsa. Akorinto anayamba kuyang’ana kwa anthu, ndipo panali magaŵano, nkhwidzi, ndi ndewu pakati pawo. (1 Akorinto 1:10-12; 3:1-4) Kodi zimenezi zinakachinjirizidwa motani? Mwakugwiritsira kwawo ntchito milimo yabwino, yokhalitsa.
Imeneyi imaimira mikhalidwe ya mtengo wapatali yomwe iri mbali ya umunthu Wachikristu. Mikhalidwe yotani? Mtumwi Petro anatchula umodzi kuti: ‘Mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golidi.’ (1 Petro 1:6, 7) Mfumu Solomo anatchulanso ina iŵiri: kukhala ndi nzeru ndi luntha, ‘kuposa malonda a siliva.’ (Miyambo 3:13-15) Ndipo Mfumu Davide anatikumbutsa kuti kuwopa Yehova ndi kuzindikira malamulo ake “zifunika koposa golidi.”—Salmo 19:9, 10.
Milimo iyi ndi ina ya mtengo wapatali ingamangidwe kukhala maumunthu Achikristu kuŵathandiza ana athu kupulumuka ziyeso. Komabe, kodi tingakhale otsimikiza motani kuti tikumanga ndi milimo yotero? Mwakupereka chisamaliro pa mitima, ponse paŵiri ya ana athu ndi yathu yomwe.
Ntchito Yomanga Yachipambano
Mbali imene mtima wa makolo umachita m’ntchito yomangayi ikuwonedwa m’lamulo loperekedwa ndi Yehova kwa makolo ku mtundu wakale wa Israyeli lakuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu.” Ndiyeno anapitiriza kuti: ‘Ndipo mudziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Chotero, tisanayambe kumanga ena, tiyenera kudzimanga tokha. Ana athu ayenera kuwona kuti maumunthu athu ngopangidwa ndi milimo yoyenerera mwa zimene timanena ndi kuchita.—Akolose 3:9, 10.
Ndiyeno, chiphunzitso chathu chiyenera kufikira mitima yawo. Yesu, womanga wachipambano koposa wa maumunthu Achikristu, anafikira mitima mwakugwiritsira ntchito mafanizo ndi mafunso. (Mateyu 17:24-27; Marko 13:34) Makolo amapeza kuti maluso amodzimodziŵa ngogwira mtima kwambiri. Iwo amagwiritsira ntchito mafanizo kupangitsa chowonadi Chachikristu kukopa mitima ya ana awo achichepere, ndipo amagwiritsira ntchito mafunso olingaliridwa bwino kuti azindikire zimene ana awo okulirapo akuganiziradi, mmene akulingalirira m’mitima yawo.—Miyambo 20:5.
Pamene Mose ankayesa kumanga chikhumbo mwa Aisrayeli chokhala okhulupirika, iye anati: ‘Sungani malamulo a Yehova ndi malemba ake . . . kuti kukukomereni inu.’ (Deuteronomo 10:13) Mofananamo, makolo amachita bwino osati kungofotokoza momvekera bwino kwa ana awo chimene miyezo ya Mulungu ili komanso kusonyeza mokhutiritsa chifukwa chimene zinthu zonga ngati kuwona mtima, chiyero chamakhalidwe, ndi mayanjano abwino ziliri kaamba ka ubwino wawo.
Pomalizira pake, Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Pamene ana mwaumwini afika pa kumdziŵa Yehova pa msinkhu waung’ono, kuphunzira kulankhula naye za mavuto awo, ndi kusangalala ndi kuyankhidwa kwa mapemphero awo, iwo amakulitsa mbali yofunika koposa ya umunthu Wachikristu: unansi waumwini ndi Mlengi wawo.
Motowo
Paulo anapeza kuti pamene ntchito yomanga ku Korinto sinachitidwe bwino, mikhalidwe yakudziko, yonga ngati mipatuko ndi magaŵano, inayambika. Izi zinali zowopsa chifukwa chakuti, monga momwe anafotokozera, ‘moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.’—1 Akorinto 3:13.
Kodi motowo nchiyani? Ungakhale chiyeso chirichonse chimene Satana amadzetsa pa Akristu. Ungakhale chitsenderezo cha mabwenzi, chiyeso chathupi, kukondetsa zinthu zakuthupi, chizunzo, ngakhale zisonkhezero zokwichisa za kukaikira. Ziyeso zotero nzotsimikizira kudza. ‘Ntchito ya yense idzawonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbuluka m’moto.’ Makolo anzeru amamanga maumunthu a ana awo akuyembekezera kuti anawo adzayesedwa. Koma iwo ngachidaliro kuti ndi chithandizo cha Yehova, ana awo angapulumuke kuyesedwako. Ngati makolo ali ndi kaimidwe kamaganizo kameneka, adzadalitsidwa kwakukulu.
Mphothoyo
Paulo anati: ‘Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho.’ (1 Akorinto 3:14) Mtumwi Paulo analandira mphotho. Kwa Akristu m’mzinda wa Tesalonika, kumenenso anachita ntchito yomanga, iye analemba kuti: ‘Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Sindinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m’kufika kwake? Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.’—1 Atesalonika 2:19, 20.
Amayi a Wanda analandira mphotho imeneyi. Pamene Wanda wazaka 12 anawona kuti walekanitsidwa ndi amayi ake, analira kwambiri poyamba mpaka kugona. Ndiyeno anakumbukira uphungu wa amayi ake wokambitsirana mavuto ake ndi Yehova m’pemphero. Iye anapemphera ndipo pomwepo anakhala ndi lingaliro lakuyang’ana m’bukhu la manambala a telefoni kuti awone ngati panali Mboni za Yehova zirizonse pafupi. Iye anazifunsa izo nauzidwa kuti banja lina linkakhala pafupi kutsidya la msewu kuchokera panyumba ya abambo ake. “Ndinakondwera kwabasi!” akutero Wanda.
Ndichilimbikitso cha banjalo, Wanda anakonzekeretsa ang’ono akewo mchimwene ndi mchemwali kuyambanso zochita Zachikristu. “Ndinali ndithayo la kudzikonzekeretsa enife kaamba ka misonkhano,” iye akufotokoza motero. “Ndinkachapa zovala zathu, kupesa tsitsi lathu, ndi kutsimikizira kuti tinali aukhondo ndi owoneka bwino.” Inali ntchito yolimba kwa msungwana wachichepereyo, koma anaichita. Nthaŵi ina abambo ake anayesa kuŵaletsa kupita kumisonkhano, koma anawo anachonderera, ndipo anaŵalola kupita.
Pambuyo pake, anawo anagwirizananso ndi amayi awo. Pamene Wanda anali ndi zaka 15 zakubadwa, anakhala Mkristu wobatizidwa, m’kupita kwanthaŵi anasonyeza chikhumbo chake cha kukhala mishonale. Inde, ntchito ya amayi a Wanda inapambana chiyeso. Iwo anasangalala ndi mphotho yowona mwana wawo wamkazi akuima nji payekha kaamba ka chowonadi. Makolo onse Achikristu apezetu chipambano chofananacho pamene akugwira ntchito yomanga maumunthu Achikristu mwa ana awo.
[Bokosi patsamba 27]
Monga momwe nkhaniyi ikusonyezera, pamene kuli kwakuti makolo amayesayesa zolimba kumanga maumunthu Achikristu mwa ana awo, ana nawonso ali ndi thayo. Mofanana ndi Akristu onse, iwo ayenera kugwira ntchito yodzimanga okha. (Aefeso 4:22-24) Ngakhale kuti makolo ali ndi mwaŵi wabwino wothandizira, kwakukulukulu munthu yense payekha ayenera kupanga chosankha cha kutumikira Yehova.