Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 5/15 tsamba 26-29
  • Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuzonda Dziko
  • “Yehova Ali Nafe”
  • Wokhulupirikabe kwa Zaka Zambiri Pambuyo Pake
  • Iye Anatsatira Yehova ndi Mtima Wonse
  • Nthaŵi Zonse Tsatirani Yehova ndi Mtima Wonse
  • Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la Kanani
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Zimene Yoswa Anakumbukira
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Muzitumikira Yehova Ndi Mtima Wonse
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Musaiwale Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 5/15 tsamba 26-29

Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?

“OLUNGAMA alimba mtima ngati mkango.” (Miyambo 28:1) Amasonyeza chikhulupiriro, amadalira Mawu a Mulungu, ndipo amapita patsogolo muutumiki wa Yehova molimba mtima pokumana ndi upandu uliwonse.

Pamene Aisrayeli anali mu Sinai Mulungu atawalanditsa muundende wa ku Igupto m’zaka za zana la 16 B.C.E., makamaka amuna aŵiri anasonyeza kuti anali olimba mtima monga mikango. Iwo anasonyezanso kukhulupirika kwa Yehova poyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta. Mmodzi wa amuna ameneŵa anali Yoswa wa fuko la Efraimu, amene anali mtumiki wa Mose ndi amene pambuyo pake anasankhidwa kukhala womloŵa m’malo. (Eksodo 33:11; Numeri 13:8, 16; Deuteronomo 34:9; Yoswa 1:1, 2) Winayo anali Kalebi, mwana wa Yefune wa fuko la Yuda.​—Numeri 13:6; 32:12.

Kalebi anachita chifuniro cha Yehova mokhulupirika ndi mwachangu. Utumiki wake wokhulupirika wanthaŵi yaitali kwa Mulungu unamkhozetsa kunena kuti anali ‘atatsatira Yehova ndi mtima wonse.’ (Yoswa 14:8) “Ndinali wokhulupirika kotheratu kwa AMBUYE, Mulungu wanga,” limatero The New American Bible. Kalebi “anamvera mokhulupirika,” kapena “anachita mokhulupirika chifuno cha,” Yehova Mulungu. (Today’s English Version; The New English Bible) Mwanjira ina, Kalebi analengeza kuti: “Ine . . . ndinatsatira AMBUYE Mulungu wanga ndi mtima wonse.” (New International Version) Bwanji za inu? Kodi mukutsatira Yehova ndi mtima wonse?

Kuzonda Dziko

Dziyerekezereni muli pakati pa Aisrayeli Yehova atangowamasula kumene muukapolo kwa Aigupto. Onani mmene mneneri Mose akutsatirira mokhulupirika malangizo operekedwa ndi Mulungu. Inde, ndipo tawonani chidaliro cha Kalebi chakuti Yehova ali ndi anthu Ake.

Chimenechi ndicho chaka chachiŵiri kuchokera pamene Eksodo (Kutuluka) mu Igupto kunachitika, ndipo Aisrayeliwo amanga msasa pa Kadesi-Barinea m’chipululu cha Parana. Iwo aima pamalire a Dziko Lolonjezedwa. Mose ali pafupi kutumiza azondi 12 m’Kanani atalamulidwa ndi Mulungu. Iye akuti: “Kwerani uko kumwera, nimukwere kumapiri; mukawone dziko umo liliri; ndi anthu akukhala m’mwemo, ngati ali amphamvu kapena ofooka, ngati achepa kapena achuluka; ndi umo liliri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iliri midziyo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m’malinga; ndi umo iliri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe. Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m’dzikomo.”​—Numeri 13:17-20.

Amuna 12 amenewo akuyamba ulendo wawo wowopsawo. Ulendowo ukutenga masiku 40. Ku Hebroni iwowa akuwona anthu amisinkhu yaikulu kwambiri. M’chigwa cha Esikolo, akuwona zipatso za m’dzikomo ndipo akulingalira kutengera zina za zipatsozi komwe achokera. Tsango limodzi la mphesa ndilolemera kwambiri kwakuti liyenera kusenzedwa mopika ndi anthu aŵiri!​—Numeri 13:21-25.

Atabwerera kumsasa wa Aisrayeli, azondiwo akusimba kuti: “Tinakafika kudziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi. Komatu anthu okhala m’dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo njamalinga, yaikulu ndithu; ndipo tinawonakonso ana a Anaki. Aamaleke akhala m’dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala kumapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m’mphepete mwa Yordano.” (Numeri 13:26-29) Azondi khumiwo sali okonzekera kulandira malamulo a Mulungu ndi kuguba kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.

“Yehova Ali Nafe”

Komabe, pokhala ndi chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu, mzondi wopanda manthayo Kalebi akufulumiza ena kuti: “Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.” Komano azondi khumiwo akukana, akumanena kuti nzika za ku Kanani nzamphamvu kuposa Aisrayeli. Azondi amantha ndi opanda chikhulupiriro ameneŵa akudziwona monga ngati ziŵala podziyerekezera nawo.​—Numeri 13:30-33.

“Yehova ali nafe; musamawaopa,” akufulumiza motero Kalebi ndi Yoswa. Mawu awo akungoloŵa m’makutu ogontha. Pamene anthuwo akuyamba kunena zowaponya miyala, Mulungu akuloŵerera ndi kupereka chiweruzo kwa ong’ung’udzawo: ‘Simudzaloŵa inu m’dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m’mwemo, koma Kalebi mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo. Koma makanda anu, . . . ndidzawaloŵetsa, ndipo adzadziŵa dzikolo mudalikana. . . . Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m’chipululu zaka makumi anayi, . . . kufikira mitembo yanu yatha m’chipululu. Monga mwa kuŵerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anayi, tsiku limodzi kuŵerenga chaka chimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anayi.’​—Numeri 14:9, 30-34.

Wokhulupirikabe kwa Zaka Zambiri Pambuyo Pake

Chilango cha zaka 40 chikuchitika, ndipo imfa ikukantha mbadwo wonse wa anthu ong’ung’udza. Koma Kalebi ndi Yoswa akali okhulupirikabe kwa Mulungu. Pazigwa za Moabu, Mose ndi Mkulu wa Ansembe Eleazara aŵerenga amuna ankhondo a usinkhu wa zaka za 20 ndi kumka mtsogolo. Pa fuko lililonse la Israyeli, Mulungu akusankha munthu mmodzi kukhala ndi thayo logaŵira malo m’Dziko Lolonjezedwa. Kalebi, Yoswa, ndi Eleazara ali pakati pa osankhidwawo. (Numeri 34:17-29) Ngakhale kuti tsopano ngwazaka 79, Kalebi adakali wanyongabe, wokhulupirika, ndi wolimba mtima.

Pamene Mose ndi Aroni anaŵerenga anthu pa Sinai, atatsala pang’ono kukana kuloŵa m’dziko la Kanani chifukwa cha mantha, ankhondo a Israyeli anali okwanira 603,550. Zaka makumi anayi zitapita m’chipululu, panali gulu lankhondo locheperapo la okwanira 601,730. (Numeri 1:44-46; 26:51) Komabe, pokhala ndi Yoswa wowatsogolera ndi Kalebi wokhulupirikayo m’gulu lawo lankhondo, Aisrayeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa ndipo anakhala ndi zipambano zotsatizana. Monga momwe Yoswa ndi Kalebi nthaŵi zonse anayembekezerera, Yehova anali kupatsa anthu ake chipambano.

Powoloka mtsinje wa Yordano ndi amuna ankhondo a Israyeli, Yoswa ndi Kalebi okalambawo akulimbikira m’nkhondo zoulikazo. Komabe, zaka zisanu ndi chimodzi zankhondo zitapita, pali dera lalikulu la dzikolo loyenera kukhalidwa. Yehova adzapitikitsa nzika za dzikolo koma tsopano iye akulamula kuti dzikolo ligaŵidwe mwa choloŵa pakati pa mafuko a Israyeli.​—Yoswa 13:1-7.

Iye Anatsatira Yehova ndi Mtima Wonse

Monga ngwazi yomenyapo nkhondo zambiri, Kalebi akuimirira pamaso pa Yoswa nati: “Ndinali ine wa zaka makumi anayi muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi-Barinea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mawu, monga momwe anakhala mumtima mwanga. Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.” (Yoswa 14:6-8) Inde, Kalebi watsatira Yehova ndi mtima wonse, akumachita chifuniro cha Mulungu mokhulupirika.

“Ndipo,” Kalebi akuwonjezera, “Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala choloŵa chako, ndi cha ana ako kosalekeza, chifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse. Ndipo tsopano, tawonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi makumi anayi ndi zisanu kuyambira nthaŵi ija Yehova ananena kwa Mose mawu awa, poyenda Israyeli m’chipululu; ndipo tsopano tawonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lerolino. Koma lerolino ndiri wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kutuluka ndi kuloŵa. Ndipo tsopano, ndipatseni phiri iri limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi midzi yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.” Tsopano Kalebi akutenga Hebroni kukhala choloŵa.​—Yoswa 14:9-15.

Kalebi wokalambayo alandira gawo lovuta kwambiri​—chigawo chodzazidwa ndi anthu amatupi aakulu kwambiri. Komatu zimenezi nzosavuta kwambiri kwa womenya nkhondo wa zaka 85 ameneyu. M’kupita kwanthaŵi, zimphona zimene zikukhala m’Hebroni zikutha psiti. Otinieli, mwana wamwamuna wa mphwake wa Kalebi ndiponso woweruza mu Israyeli, akulanda Debiri. Pambuyo pake mizinda iŵiri yonseyo ikukhalidwa ndi Alevi, ndipo Hebroni ukukhala mzinda wothaŵirako wakupha munthu mwangozi.​—Yoswa 15:13-19; 21:3, 11-16; Oweruza 1:9-15, 20.

Nthaŵi Zonse Tsatirani Yehova ndi Mtima Wonse

Kalebi ndi Yoswa anali anthu opanda ungwiro. Komabe, anachita chifuniro cha Yehova mokhulupirika. Chikhulupiriro chawo sichinazilale pazaka 40 za mavuto m’chipululu amene anachitika chifukwa cha kulephera kumvera Mulungu kwa Israyeli. Mofananamo, atumiki a Yehova amakono samalola kanthu kalikonse kudodometsa utumiki wawo m’kutamanda Mulungu. Pozindikira kuti pali nkhondo pakati pa gulu la Mulungu ndi la Satana Mdyerekezi, iwo ngoima nji, akumafunafuna kukondweretsa Atate wawo wakumwamba mosalekeza m’zinthu zonse.

Mwachitsanzo, anthu ambiri a Yehova aika moyo wawo pachiswe mwa kuchitiridwa nkhanza ndipo ngakhale imfa kuti akapezeke pamgonero wa Ambuye, kapena Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. (1 Akorinto 11:23-26) Ponena za zimenezi mkazi wina Wachikristu wobindikiritsidwa mumsasa wachibalo wa Nazi mkati mwa Nkhondo Yadziko II anasimba kuti:

“Munthu aliyense anauzidwa kukakhala m’chipinda chochapira zovala pa 11 p.m. Nthaŵi yeniyeni ya 11 p.m. itangokwana, tinasonkhana, tinali okwanira 105. Tinaima mothithikana ndi mozinga nkhata, pakati pake [panali] choikapo mapazi choyalidwapo nsalu yoyera chokhala ndi zizindikiro. Tinagwiritsira ntchito kandulo, powopa kuti magetsi akatiululitsa. Tinadziwona monga ngati Akristu oyambirira osonkhana m’phanga. Linali phwando lolemekezeka. Tinasonyezanso chatsopano zoŵinda zathu ndi mtima wonse kwa Atate wathu za kugwiritsira ntchito nyonga yathu yonse kuchilikiza dzina Lake loyera, kuchilimika mokhulupirika kaamba ka Teokrase.”

Mosasamala kanthu ndi mayeso athu monga atumiki ozunzidwa a Yehova, tingadalire panyonga yoperekedwa ndi Mulungu kumtumikira molimba mtima ndi kudzetsa ulemu kudzina lake loyera. (Afilipi 4:13) Pamene tikuyesayesa kukondweretsa Yehova, kudzakhala kwabwino kwa ife kukumbukira Kalebi. Chitsanzo chake m’kutsatira Yehova ndi mtima wonse chinakopa mnyamata wina amene analoŵa ntchito yanthaŵi yonse yolalikira kalelo mu 1921. Iye analemba kuti:

“Ngakhale kuti kukhala mpainiya kwanga kunafuna kuti ndisiye ntchito yabwino kwambiri pakampani yosindikiza yamakono mu Coventry [England], sizinandidandaulitse. Kudzipatulira kwanga kunali kutathetsa nkhaniyo; moyo wanga unali wopatulidwira Mulungu. Ndinakumbukira za Kalebi, amene analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa limodzi ndi Yoswa ndi za amene kunanenedwa kuti, ‘Anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’ (Yos. 14:8) Zimenezo zinawonekera kwa ine kukhala mkhalidwe wa maganizo wokhumbika. Ndinadziŵa kuti kutumikira Mulungu ‘ndi mtima wonse’ kukachititsa moyo wanga wakudzipatulira kukhala wofunika kwambiri; kukandikhozetsa kukhala ndi mipata yokulirapo yobala zipatso zimene zimadziŵikitsa Mkristu.”

Kalebi anadalitsidwadi chifukwa cha kutsatira Yehova mokhulupirika ndi mtima wonse, nthaŵi zonse akumafuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Mofanana naye, enanso apeza chisangalalo chachikulu ndi madalitso aakulu muutumiki wa Mulungu. Nanunso zikukhalirenitu motero monga munthu amene amatsatira Yehova ndi mtima wonse mosalekeza.

[Chithunzi patsamba 26]

Kalebi ndi Yoswa anali okhulupirika kwa Yehova pansi pa chiyeso. Kodi ndinu wotero?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena