Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 26 tsamba 66-tsamba 67 ndime 1
  • Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la Kanani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la Kanani
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Azondi 12
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Zimene Yoswa Anakumbukira
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 26 tsamba 66-tsamba 67 ndime 1
Amuna a ku Isiraeli akuona dziko la Kanani

MUTU 26

Anthu 12 Anapita Kukafufuza Dziko la Kanani

Aisiraeli atachoka paphiri la Sinai anadutsa m’chipululu cha Parana n’kukafika pamalo otchedwa Kadesi. Ali pamalowa, Yehova anauza Mose kuti: ‘Sankha amuna 12 kuchokera mu fuko lililonse kuti apite kukaona dziko la Kanani limene ndikufuna kulipereka kwa Aisiraeli.’ Ndiyeno Mose anasankha amuna 12 n’kuwauza kuti: ‘Pitani ku Kanani mukaone ngati dzikolo ndi labwino kulimamo mbewu. Mukaonenso ngati anthu ake ali amphamvu kapena ofooka komanso ngati amakhala m’matenti kapena m’mizinda.’ Zitatero, anthuwo anauyamba ulendo wopita ku Kanani ndipo pa gululi panali Yoswa ndi Kalebe.

Aisiraeli akudandaula ndipo afooka

Patatha masiku 40, anthuwa anabwerera ndipo anatenga zipatso za nkhuyu, makangaza ndi mphesa. Iwo anati: ‘Dziko lake ndi labwino kwambiri koma anthu ake ndi amphamvu ndipo amakhala m’mizinda ya mipanda italiitali.’ Ndiyeno Kalebe anati: ‘Komabe tingathe kuwagonjetsa anthuwo. Tiyeni tipite pompano.’ Kodi ukudziwa chifukwa chake Kalebe ananena zimenezi? Chifukwa chakuti iye ndi Yoswa ankakhulupirira kwambiri Yehova. Koma anthu ena 10 aja anati: ‘Ayi tisapite. Anthu ake ndi akuluakulu komanso amphamvu moti ife timangooneka ngati tiziwala.’

Aisiraeli atamva zimenezi anakhumudwa kwambiri. Anayamba kudandaula kuti: ‘Tiyeni tisankhe mtsogoleri wina ndipo tibwerere ku Iguputo. Kodi pali chifukwa choti tipitire m’dziko limeneli n’kukaphedwa?’ Koma Yoswa ndi Kalebe anati: ‘Musapandukire Yehova ndipo musachite mantha. Yehova atiteteza.’ Komabe Aisiraeliwo sanamvere, moti mpaka ankafuna kupha Yoswa ndi Kalebe.

Kodi Yehova anatani? Iye anauza Mose kuti: ‘Aisiraeli ndawachitira zinthu zambirimbiri koma sakundimverabe. Chifukwa cha zimenezi, akhala m’chipululumu kwa zaka 40 ndipo onse afera momwemu. Anthu amene akalowe m’dziko limene ndalonjezali ndi ana awo okha limodzi ndi Yoswa komanso Kalebe.’

“N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”​—Mateyu 8:26

Mafunso: Kodi chinachitika n’chiyani anthu 12 okafufuza dziko la Kanani aja atabwerako? Kodi Yoswa ndi Kalebe anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova?

Numeri 13:1-33; 14:1-38; Deuteronomo 1:22-33; Salimo 78:22; Aheberi 3:17-19

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena