12 KALEBE
Anakhalabe Wokhulupirika kwa Mulungu Wake
PA NTHAWI imene Mose anathawa ku Iguputo, banja lina la Chiisiraeli linakhala ndi mwana dzina lake Kalebe. Ngakhale kuti mwanayu anabadwira ku ukapolo, m’kupita kwa nthawi, anamasulidwa. Pamene Mose ankabwerera ku Iguputo kuti akapulumutse Aisiraeli, n’kuti Kalebe ali ndi zaka pafupifupi 40. Kalebe ayenera kuti anagoma komanso kusangalala kwambiri ataona Yehova akuonetsa mphamvu zake kudzera m’Miliri 10. Anaonanso mmene Yehova analekanitsira madzi pa Nyanja Yofiira ndi kupulumutsa anthu ake.
Kalebe sanaiwale zochitika zolimbitsa chikhulupiriro zimenezi. Patadutsa miyezi yochepa, ali paphiri la Sinai, Aisiraeli ambiri anasiya kutumikira Yehova koma Kalebe anakhalabe wokhulupirika. Pambuyo pake, Mose anapatsa Kalebe ntchito yapadera yoti akazonde Dziko Lolonjezedwa limodzi ndi Yoswa komanso atsogoleri ena 10 a ku Isiraeli.
Molimba mtima, amuna 12 amenewa anapita ku Kanani ndipo anakhala masiku 40 akufufuza zokhudza dzikolo, anthu ake komanso zipatso zake. Pobwerera, ananyamula phava lalikulu la mphesa. Phavali linali lalikulu kwambiri moti anachita kunyamulizana anthu awiri. Koma n’kutheka kuti Kalebe anakhumudwa ndi lipoti lomwe amuna 10 enawo anapereka. Baibulo limati: “Iwo anapitiriza kuuza Aisiraeliwo lipoti loipa.” Anati sangathe kugonjetsa anthu a ku Kanani chifukwa anali amphamvu komanso anali ndi matupi akuluakulu ndipo ananenanso kuti anthuwo anali mbadwa za Anefili. Koma kunali kukokomeza chabe, chifukwa Anefili anali atawonongedwa kalekale pa Chigumula. Lipotili linafooketsa anthu mpaka ena anaganiza zosankha mtsogoleri wina kuti abwererenso ku Iguputo.
Kalebe ndi Yoswa anakhalabe okhulupirika. Iwo anayesetsa kulimbikitsa Aisiraeli anzawo omwe anali ndi chikhulupiriro chochepa kuti: “Yehova ali nafe. Musawaope.” Koma zimenezi zinapangitsa kuti Aisiraeliwo akwiye kwambiri. Moti anayamba kunena kuti apha Kalebe ndi Yoswa powagenda ndi miyala.
Yehova anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi. Aisiraeli anasiya kumukhulupirira ngakhale kuti panali pasanapite nthawi yaitali kuchokera pomwe anawachitira zinthu zambiri powapulumutsa ku Iguputo. Koma Mulungu anaona kulimba mtima komanso chikhulupiriro cha Kalebe ndi Yoswa. Yehova ananena kuti: “Mtumiki wanga Kalebe anali wosiyana ndi ena, ndipo wakhala akunditsatira ndi mtima wonse.” Yehova anasankha kuti m’badwo wonsewo womwe unalibe chikhulupiriro uthere m’chipululu.a Koma Kalebe ndi Yoswa ndi omwe Yehova anawalola kuti akhalebe ndi moyo mpaka kukalowa m’Dziko Lolonjezedwa.
Kalebe anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale pomwe Aisiraeli ena sanatero ndipo ankafuna kumupha
Pa zaka zonse 40 zomwe Aisiraeli ankayenda m’chipululu, Kalebe anapitiriza kusonyeza chikhulupiriro ndi kulimba mtima. Iye anathandiza Mose mokhulupirika komanso pambuyo poti Mose wamwalira, iye anathandizanso Yoswa potsogolera anthu a Mulungu kuwoloka mtsinje wa Yorodano mpaka kukalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale atakalamba, Kalebe anasonyeza kulimba mtima pomenyana ndi adani a Mulungu ku Kanani.
Patatha zaka 6 anthu a Mulungu atawoloka mtsinje wa Yorodano, iwo anali atalanda mbali yaikulu ya Dziko Lolonjezedwa. Tsopano nthawi inakwana kuti Kalebe asankhe dera loti akakhale ndi banja lake. Iye anasankha ku Heburoni, dera lomwe amuna 10 opanda chikhulupiriro aja anati kunali asilikali amatupi akuluakulu ndipo sangathe kuwagonjetsa. Ngakhale kuti Kalebe anali ndi zaka 85, iye ankakhulupirira kwambiri Yehova moti ananena kuti: “Yehova adzakhala nane, ndipo ndikawathamangitsa ndithu ngati mmene Yehova analonjezera.” Izi ndi zomwe zinachitikadi, Kalebe analanda mzindawo n’kumakhala kumeneko. Baibulo limati: “Kenako mʼdzikolo munakhala mopanda nkhondo.”
Zaka zambiri m’mbuyomo, Mose anauza Kalebe kuti: “Watsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.” Sitikukayikira kuti Kalebe anapitiriza kuchita zimenezi mpaka pa nthawi yomwe anamwalira. Ndipo adzateronso akadzaukitsidwa.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Kalebe anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi mphesa za m’Dziko Lolonjezedwa zinalidi zazikulu ngati mmene lemba la Numeri 13:23 limanenera? (w06 6/15 16 ¶1-2)
2. Kodi m’Dziko Lolonjezedwa munalidi “mkaka ndi uchi” wambiri ngati mmene Kalebe ndi Yoswa ananenera? (Num. 14:8; w11 3/1 15) A)
Institute of Archaeology/Hebrew University © Tel Rehov Excavations
Chithunzi A: Ming’oma ya njuchi yadongo ya ku Isiraeli ya zaka za m’ma 900 mpaka kumayambiriro kwa 800 B.C.E.
3. Kodi pomwe Mose ankatumiza amuna 12 kuti akafufuze zokhudza Dziko Lolonjezedwa, kunali kutatsala mtunda wautali bwanji kuti akafike m’dzikolo? (w04 10/15 17 ¶11-12) B
Chithunzi B
4. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Kalebe chifukwa cha kukhulupirika ndi kulimba mtima kwake? (w06 10/1 18 ¶11)
Zomwe Tikuphunzirapo
Ngakhale kuti Kalebe anali wokhulupirika, anayendayendabe m’chipululu limodzi ndi Aisiraeli ena onse. Komabe modzichepetsa anapitirizabe kudalira Yehova. Kodi tingatsanzire Kalebe pa zochitika ngati ziti?
Kodi chitsanzo cha Kalebe chingatithandize bwanji tikamakakamizidwa ‘kutsatira gulu la anthu’? (Eks. 23:2) C
Chithunzi C
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Kalebe m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Kalebe akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi chikhulupiriro cha Kalebe chikugwirizana bwanji ndi kulimba mtima kumene iye anasonyeza?
“Kulimba Mtima Chifukwa cha Chikhulupiriro ndi Kuopa Mulungu” (w06 10/1 16-19 ¶1-12)
Kodi mwina ndi chiyani chimene chinachititsa kuti Kalebe yemwe anali ndi zaka 85 anene kuti: “Ine ndinatsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse”? (Yos. 14:8)
“Kodi Mumatsatira Yehova Ndi Mtima Wonse?” (w93 5/15 26-29-wcgr)
a Zomwe Yehova anasankhazi, sizinaphatikizepo Alevi kapena Aisiraeli ena onse omwe pa nthawiyi anali asanakwanitse zaka 20.—Num. 14:29.