Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi anthu amene salandira Chikristu chowona tsopano lino ndi kufa chisautso chachikulu chisanayambe adzaukitsidwa?
Nkwabwino kwa tonsefe kuti tikanize chikhoterero cha kuchita monga ngati oŵeruza, tikumazindikira kuti potsirizira pake, chiweruzo cha Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu ndicho chimene chili kanthu. (Yohane 5:22; Machitidwe 10:42; 2 Timoteo 4:1) Koma Malemba amatipatsa mawu ena othandiza poyankha funsoli.
Kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu padziko lonse ndiko mbali yofunika kwambiri ya ‘chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu.’ (NW) Chizindikiro chimenechi chakhala chikuwonedwa chiyambire kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lino. Ntchito yolalikira ikuchititsa kulekanitsidwa kwa anthu a mitundu yonse mokwaniritsa fanizo la Yesu la “nkhosa” ndi “mbuzi.” Pamene ntchito yolalikira ndi kulekanitsa imeneyi idzakwaniritsidwa, ‘chisautso chachikulu’ chidzathetsa dongosolo loipa lilipoli.—Mateyu 24:3, 21, 22; 25:31-46.
Yehova, limodzi ndi Mwana wake, adzaweruza kaya ngati munthu aliyense amene akana uthenga wa Ufumu nafa chisautso chachikulu chisanabuke ali m’gulu la mbuzi. Yesu ananena kuti mbuzi ‘zidzachoka kumka kuchilango cha nthaŵi zonse.’ Chifukwa chake, tinganene kuti awo amene ali otsimikizidwa ndi Mulungu kukhala mbuzi sadzaukitsidwa. Iwo ali ndi chiweruzo chofanana ndi chija cha awo amene “adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha” panthaŵi ya chisautso chachikulu.—2 Atesalonika 1:9.
Koma bwanji za ambiri amene sakuwoneka kukhala ndi mwaŵi wokwanira wakumvetsera uthenga wa Ufumu kotero kuti apange chosankha chakulandira chowonadi kapena kuchikana asanafe ‘m’masiku ano otsiriza’?—2 Timoteo 3:1.
Ambiri amene amafa pamene ntchito yolalikira idakali mkati chisautso chachikulu chisanachitike mwachiwonekere adzaukitsidwa. Zimenezi zikusonyezedwa ndi zimene timaŵerenga pa Chivumbulutso 6:7, 8 ponena za okwera pakavalo ophiphiritsira. Anthu ambiri afa ndi nkhondo, kupereŵera kwa chakudya, ndi miliri yakupha. Popeza kuti “Hade” ndiye amene amatuta mikhole imeneyi ya “Imfa,” iwowa adzaukitsidwa mu Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu, pamene Hade adzatulutsa akufa ake onse amene ali nawo. (Chivumbulutso 20:13) Ambiri amene adzaukitsidwira kumoyo angakhale anamvapo kalelo za uthenga wa Ufumu asanafe.
Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kuti Yesu sanapatse anthu mphamvu yakuweruza onga nkhosa ndi onga mbuzi! Anthu opanda ungwiro sangadziŵe bwino lomwe za ukulu wa mwaŵi umene munthu anali nawo kuti amve ndi kulandira mbiri yabwino. Kodi tingadziŵe kuti mkhalidwe wa mtima wake unali wotani kapena kaya ngati iye anakondadi chilungamo? Kodi tingadziŵe mmene banja lake, chipembedzo chake, kapena zisonkhezero zina zinayambukirira kulabadira kwake? Mwachiwonekere ayi. Komabe, tingatsimikizire kuti Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu angathe kudziŵa zimenezo ndi kuweruza mwangwiro, moyenera, ndi molungama.—Deuteronomo 32:4; Yesaya 11:1-5.
Motero, sitiyenera kumakamba ponena za amene angaukitsidwe kapena amene sadzatero pakati pa awo amene afa posachedwa. Sitikuloledwa kuchita chimenechi. (Yerekezerani ndi Luka 12:13, 14.) Kuli kwanzeru kwambiri kuti tiyembekezere pazigamulo za Oweruza olungama, Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Tikatero tidzakhaladi ndi mtendere wowonjezereka wa maganizo monga atumiki a Yehova. Zidzatithandizanso kusamalira bwino ntchito imene tagaŵiridwa kuchita—‘kupita ndi kukapanga anthu amitundu yonse kukhala ophunzira, kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamula.’—Mateyu 28:19, 20.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Nkhosa za Leicester, Meyers