Tchalitchi cha ku Latin America Chikuthedwa Nzeru—Kodi Nchifukwa Ninji Mamiliyoni Akutulukamo?
KUYAMBIRA kumalire a kumpoto a Mexico kufikira kunsonga ya kummwera ya Chile, palibiretu mzinda kapena mudzi wa ku Latin America umene ulibe tchalitchi cha Roma Katolika pamsika wake waukulu. Komabe, “kusintha kwakukulu kukuchitika mu Latin America,” akunena motero Joseph E. Davis, mkulu wa programu ya gulu limene limachilikiza ntchito za Akatolika. Iye anavomerezanso kuti Latin America, chigawo cha dziko chimene kwa zaka zoposa mazana atatu chakhala muulamuliro wa Tchalitchi cha Roma Katolika, tsopano chili pampemphenu pa kusintha kwakukulu.
Kuchepa mphamvu kofulumira kwa ulamuliro wa Tchalitchi cha Katolika sikuli chinsinsi. Posachedwapa, chiŵerengero cha Akatolika okangalika chinayerekezeredwa kukhala chaching’ono cha 15 peresenti chabe ya chionkhetso cha chiŵerengero cha anthu a mu Latin America. Buku lakuti 1991 Britannica Book of the Year linasimba kuti: “Mabishopu a Roma Katolika ndi papa mwiniyo anasonyeza mantha akuti mumkhalidwe wa mbiri, Latin America Wachikatolika anali kusiya mochititsa mantha chikhulupiriro chake chakalecho.” Kodi nchifukwa ninji zimenezi zikuchitika? Kodi nchifukwa ninji ambiri akutuluka m’khola la Chikatolika? Kodi nchiyani chimene chachitikira awo amene amasochera?
Kufunafuna Yankho
Atsogoleri a Katolika amati mavuto awo achititsidwa ndi kufalikira kwa “timagulu tazipembedzo topatuka.” Wansembe wa ku Ulaya wogwira ntchito m’Bolivia anadandaula kuti: “Tchalitchi changokhala ngati mtengo umene ukufooledwa ndi timagulu tachipembedzo topatuka tonga namsongole.”
Mu Argentina, zipembedzo zatsopano 140 zimasimbidwa kukhala zitabuka chaka chilichonse, kumene kungathandizire kuwona chifukwa cha kutsika kwa ziŵalo za Tchalitchi cha Katolika kuchokera pa 90 peresenti kufikira pa 60 kapena 70 peresenti chiyambire pakati pa zaka za m’ma 1970. Mu Tijuana, Mexico, 10 peresenti ya nzika mamiliyoni aŵiri zimamka kuzipembedzo 372 zosakhala za Katolika kumeneko. Magazini a Time anasimba kuti: “Modabwitsa, m’matchalitchi pa Sande mumakhala pafupifupidi nzika zambiri za Brazil Zachiprotestanti kuposa Zachikatolika.” Nkosadabwitsa, kunena monga momwe nyuzipepala ina inanenera kuti, pamene “makadinala a ku Latin America anakumana ndi papa ku Vatican City kudzakambitsirana nkhani ziŵiri zofunika koposa za tchalitchi lerolino,” imodzi mwa nkhanizo inali ya “vuto la timagulu tazipembedzo topatuka.”
Pakusonkhana kwake ndi mabishopu a ku Mexico, papa ananena kuti kupambana kwa zipembedzo zambiri zatsopano “kukuchitika chifukwa cha mkhalidwe wamphwayi ndi wosimbwa wa ana a tchalitchi amene sakukwaniritsa ntchito yawo yaulaliki.” Kodi nchifukwa ninji “ana a tchalitchi” ali amphwayi pokhutiritsa zosoŵa zauzimu za nzika za Latin America pamene kuli kwakuti ambiri a ameneŵa amalemekeza Baibulo? Nkhani ina yolembedwa ndi mkonzi mu Última Hora, ya ku La Paz, Bolivia, imafotokoza kuti: “Tchalitchi chaloŵa m’zochitika za dziko kumlingo wakuti tsiku lililonse chimawonekera kukhala chikusiya malo ake enieni. Sikuyenera kutidabwitsa, monga momwe zikuchitikiradi, kupeza kuti, ansembe akukhala kwambiri akatswiri a zakakhalidwe ka anthu, azachuma, atola nkhani, kapena andale za dziko kuposa kukhala kwawo atsogoleri achipembedzo.”
Andale za Dziko Kwambiri Kuposa Kukhala Alaliki?
Kududukira kwa tchalitchi m’ndale m’ma 1970 ndi m’ma 1980 mosakayikira kwawonjezera kuipidwa kumene nzika zambiri za ku Latin America tsopano zili nako pa Chikatolika. Kupenda kumene kunafalitsidwa mu 1985 kunali ndi mawu otsatirapowa ponena za gulu la Maryknoll, Catholic Foreign Mission Society of America, ndi mamishoni ake ambirimbiriwo a ku Latin America: “Gulu la Maryknoll lachititsa uthenga wa kusintha kwachiwawa wa Marx ndi Lenin kukhala wolandiridwa ndi anthu onse makamaka chifukwa chakuti laloledwa kugwira ntchito monga dzanja la Tchalitchi cha Katolika. Uthenga wake wafikira osati kokha anthu wamba opita kutchalitchi, komanso opanga malamulo otchuka a mu America.”
Lingaliraninso yotchedwa kuti nkhondo yoipitsitsa mu imene, modabwitsa, nzika za Argentina zoyambira pa 10,000 kufikira 30,000 zinabedwa ndi kuphedwa popanda kuzenga mlandu kumapeto kwa ma 1970. Nkhani ina yolembedwa ndi mkonzi mu National Catholic Reporter, pamutu wakuti “Mwazi Uipitsa Tchalitchi cha mu Argentina,” inati: “Chokumana nacho cha Argentina chimafanana kwambiri ndi mchitidwe wa tchalitchi cha Katolika cha ku Jeremani wa Nazi, kachiŵirinso zimenezi zimadzutsa chikayikiro chakuti kaya mphamvu ndiyo imene ili yofunika kutchalitchi kuposa lamulo la Uthenga Wabwino la kuchitira umboni chowonadi.”
Kukhumbira kukhala ndi mphamvu kwa tchalitchi m’maboma adziko kumachisonyeza bwino lomwe kuti sichili bwenzi la Mulungu. Baibulo limati: “Kodi simudziŵa kuti kupanga dzikoli kukhala bwenzi lanu ndiko kumpanga Mulungu kukhala mdani wanu? Munthu aliyense amene amasankha dzikoli kukhala bwenzi lake amadzipangitsa kukhala mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4, Jerusalem Bible la Katolika) Pamenepa, mposadabwitsa kuti anthu ambiri samayembekezeranso Tchalitchi cha Katolika kuwatsogolera mwauzimu. Koma kodi nchiyani chimene chachitikira anthu amene atuluka m’khola la Katolika?
Nkhosa Zopanda Mbusa
Iwo ali ofanana kwambiri ndi anthu amene atsogoleri auzimu Achiyuda a m’zaka za zana loyamba analephera kuwasamalira. Baibulo limati Yesu “anamva nawo chisoni chifukwa chakuti anali osautsidwa ndi onyanyalidwa, monga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36, JB) Ambiri atuluka m’Tchalitchi cha Katolika kumka kuzotchedwa kuti zipembedzo zolalikira. Kodi zipembedzo zimenezi zasamalira bwino nkhosa zosocherazo? Kodi Aprotestanti ngoyedzamira kwambiri pakukhala monga momwe Yesu ananenera za otsatira owona kuti: “Sakhala a dziko lapansi, monga ine sindikhala wa dziko lapansi”?—Yohane 17:14.
Zipembedzo zambiri zimene sizili za Katolika zimayesayesa kukulitsa mawonekedwe a kukhala zomvera Baibulo mmalo mwa kukhala zotsatira miyambo ya zipembedzo. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimangokhala zachiphamaso chabe. Ziphunzitso zazikulu za magulu Achiprotestanti nzofanana ndi zija za Tchalitchi cha Katolika kwakuti openyerera ambiri anganene mosavuta mwambi wa ku Andes wakuti: “Es la misma cholita con otra pollera” (Ndimtsikana Wachimwenye yemwe uja m’siketi ina).
Mwachitsanzo, pafupifupi timagulu tonse ta Chiprotestanti timaphunzitsa kuti Mulungu ali Utatu, komatu chimenechi sichiphunzitso cha m’Baibulo. The Encyclopedia of Religion imavomereza kuti: “Lerolino otembenuza ndi akatswiri a maphunziro azaumulungu amagwirizana kuti Baibulo Lachihebri lilibe chiphunzitso cha Utatu . . . Nachonso Chipangano Chatsopano chilibe chiphunzitso chotsimikizirika cha Utatu.”a
Aprotestanti ngogwirizanitsidwa kwambiri ndi dzikoli ndi ndale zake monga momwedi aliri Akatolika. Encyclopedia of Latin America imati: “Chiprotestanti mu Latin America chadziloŵetsanso mu . . . ndale zosonkhezera anthu kuvotera mtsogoleri wa chipani. Kaŵirikaŵiri mapasitala akumaloko amakhala othandizira kuchirikiza anthu andale zadziko ndi kuvotera boma kuti lidzayanjane ndi matchalitchi awo.” Latin American Research Review imati: “Chiprotestanti chayanjana ndi ndale za dziko mu Guatemala chiyambire pamene chinafika m’dzikoli,” ikumawonjezera kuti “chakhala chipangizo choperekera malingaliro a ndale za dziko ndi makhalidwe achitaganya monga mpangidwe wa chipembedzo.”
Kutenga mbali kwa Chiprotestanti m’ndale za dziko kaŵirikaŵiri kwatsogolera Chiprotestanti kutenga mbali munkhondo. Malemu Harry Emerson Fosdick, wolingaliridwa kukhala mmodzi wa atsogoleri otchuka kwambiri Achiprotestanti m’mbiri ya ku Amereka, anavomereza kuti: “Mbiri yathu ya Maiko a Kumadzulo yakhala ya nkhondo zotsatizanatsatizana. Tatulutsa amuna ankhondo, taphunzitsa amuna ankhondo; talemekeza nkhondo; tapanga anthu ankhondo kukhala ngwazi zathu ndipo ngakhale m’matchalitchi athu taika mbendera zankhondo . . . Ndi mbali imodzi ya pakamwa pathu tatamanda Kalonga wa Mtendere ndipo ndi inayo talemekeza nkhondo.”
Kodi Muyenera Kuchitanji?
Litafotokoza chipembedzo chonyenga kukhala hule wophiphiritsira amene akuchita chigololo ndi maboma a dziko lapansi, buku la Baibulo la Chivumbulutso limanena kuti: “Tulukani, anthu anga, mwa iye, kotero kuti musagaŵane naye m’maupandu ake ndi kukhala nayo miliri imodzimodziyo.”—Chivumbulutso 18:4, JB.
Anthu ambiri amazindikira kuti m’tchalitchicho muli kuipa kwakukulu, komabe, iwo amazengereza kutulukamo chifukwa chakuti Tchalitchi cha Roma chili ndi mbiri yakale. Komabe, kumbukirani kuti, dongosolo la kulambira Lachiyuda linali lakale; komabe Mulungu anakana Ayuda kukhala anthu ake osankhidwa pamene anapatuka paziphunzitso zake zowona. Atumiki okhulupirika a Mulungu anatuluka m’Chiyuda pamene anazindikira kuti tsopano Mulungu anali kugwiritsira ntchito mpingo Wachikristu. Kodi mungazindikire motani mpingo wowona Wachikristu lerolino?
Pafupifupi nzika miliyoni imodzi za ku Latin America zakhala Mboni za Yehova m’zaka makumi aŵiri zapitazo. Kodi nchifukwa ninji zinasinthira kuchipembedzo china motero? Nyuzipepala ina ku Martínez de la Torre, Veracruz, Mexico, inapenda funso limeneli. Iyo inati: “Ophunzira Baibulo ameneŵa ngopangidwa ndi pafupifupi 100 peresenti ya omwe kale anali ochilikiza kusintha zinthu m’ndale a zipembedzo zosiyanasiyana, makamaka Akatolika, amene aona chipembedzo chikutengeka ndi ndale ndi kugwirizana kwake ndi michitidwe yosagwirizana ndi Baibulo monga ngati kuloŵerana chikhulupiriro, chisembwere, ndi chiwawa. Kugwirizana ndi malamulo a khalidwe a m’Malemba a mayendedwe kwakhala magwero okhutiritsa kwa iwo popanda kubwereranso kumafano ndi ziphunzitso za magwero osadziŵika. Zimenezi zawapatsa umodzi wa chikhulupiriro woyamikirika umene umawalekanitsa ndi ena kulikonse kumene amapezeka.”
Nyuzipepala ina ya ku Latin America imanena motere: “Mboni za Yehova ndianthu ogwira ntchito zolimba, owona mtima, ndi owopa Mulungu. Izo nzachikatikati ndi zokonda kusunga mwambo ndipo chipembedzo chawo nchozikidwa paziphunzitso za m’Baibulo.” Tikukupemphani kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kulikonse kumene mumakhala. Mudzaona kuti chiyembekezo chawo ndi moyo wawo wonse zimazikidwa m’Baibulo. Inde, mudzaphunzira mmene mungapembedzere Mulungu “mumzimu ndi m’chowonadi.”—Yohane 4:23, 24.
[Mawu a M’munsi]
a Onani kabuku kakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? kofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
[Tchati patsamba 21]
MBONI ZA YEHOVA M’MAIKO ENA A KU LATIN AMERICA
1971 1992
Dziko Ofalitsa Ofalitsa
Argentina 20,750 96,780
Bolivia 1,276 8,868
Brazil 72,269 335,039
Chile 8,231 44,067
Colombia 8,275 55,215
Costa Rica 3,271 14,018
Dominican Republic 4,106 15,418
Ecuador 3,323 22,763
El Salvador 2,181 20,374
Guadeloupe 1,705 6,830
Guatemala 2,604 13,479
Honduras 1,432 6,583
Mexico 54,384 354,023
Panama 2,013 7,732
Paraguay 901 4,115
Peru 5,384 43,429
Puerto Rico 8,511 25,315
Uruguay 3,370 8,683
Venezuela 8,170 60,444
CHIONKHETSO 212,156 1,143,175