Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kugaŵanikana?
CHOCHITITSA kugawanikana kwa chipembedzo, kapena malekano, chandandalitsidwa m’bukhu lanazonse lina lachipembedzo kukhala chambali zitatu: chiphunzitso, gulu, ndi ndale zadziko. Tiyeni tiwone ngati kusanthulaku kumagwirizana ndi mkhalidwe wa Tchalitchi cha Katolika.
Nthanthi Yaumulungu kapena Chowonadi cha Baibulo?
M’kusanthula kwake kwa chochititsa kugawanikana kwaposachedwapa m’Tchalitchi cha Katolika, wansembe René Laurentin analemba kuti: “Chochititsa chotsimikizirika nchomvekera kwa ine. Ndi nthanthi zosiyana.” Iye akunena za nthanthi yopita patsogolo. Iyi njosemphana ndi mwambo, ndiko kuti, gulu loyanja mwambo wakalekale loimiridwa ndi Akibishopu Lefebvre. Mkulu wa gulu la Dominican, Jean-Pierre Lintanf akuti: “Chikhulupiriro nchimodzi, nthanthi zaumulungu nzambiri.”
Nthanthi zosiyanasiyana, zomwe ziri ndi thayo la kugawanikana m’tchalitchi, zikanapewedwa tchalitchicho chikanamamatira ku Baibulo monga magwero a ziphunzitso zake. Ndithudi, Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican unalamulira kuti: “Mawu opatulika ndiwo chipangizo chamtengo wapatali m’dzanja lamphamvu la Mulungu cha kufikira umodzi umene Mpulumutsi amapereka kwa anthu onse.” Komabe, mwa kunyalanyaza phindu logwirizanitsa la Baibulo, Msonkhano umodzimodziwo wa Vatican unati: “Tchalitchi sichimaika zitsimikizo zake za zowonadi zovumbulidwa m’Malemba oyera okha. Chotero, zonse ziŵiri Malemba ndi Mwambo ziyenera kuvomerezedwa ndikulemekezedwa ndi kaimidwe kodzipereka ndi ulemu wofanana.” Ndipo kachiŵirinso: “Maphunziro aumulungu opatulika amadalira pa Mawu a Mulungu olembedwa, kuphatikizapo Mwambo wopatulika.”
Mawu awa a Yesu kwa Afarisi angagwiritsiridwe ntchito bwino kwambiri kwa akuluakulu a Tchalitchi cha Katolika: “Mwapangitsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake ndi miyambo yanu.” (Mateyu 15:6, The New Jerusalem Bible) Mkazi wowona mtima Wachikatolika analembera magazine Achikatolika mu Falansa kuti: “Ngati mtsogoleri wachipembedzo sakusonkhezeredwa konse kulalikira Mawu Abwino, kodi kungakudabwitseni kuti chiŵerengero cha okhulupirika nchochepera, kapena kuti akufunafuna kwinakwake? (Ponena za Mboni za Yehova ndi omamatira kumwambo, chikhulupiriro chawo chimawapanga kukhala osiyana.)”
Kugawanikana kwa Akuluakulu
Tsopano lingalirani chochititsa kugawanikana kwa gulu m’tchalitchi. Kulekana kobweretsedwa ndi Akibishopu Lefebvre anali ochita mwachindunji ndi ziphunzitso zoikidwiratu za Chikatolika za “Olowa Mmalo Atumwi” ndi utsogoleri wa papa. Lefebvre akunena kuti “mphamvu ya kuphunzitsa, kulamulira, ndi kupatulikitsa imene Kristu anapatsa Atumwi Ake . . . inapitirizidwa m’magulu a abishopu a Tchalitchicho.” Komabe, kwanenedwa kuti bishopu wa Roma, papa, “ngwamkulu pa abishopu onse, osati muudindo wokha kapena ulemu, koma m’mphamvu zaupasitala.”—New Catholic Encyclopedia.
Koma kodi ziphunzitso zoikidwiratuzi nzozikidwa pa Baibulo? Bukhu lanazonse Lachikatolika limodzimodzili likuvomereza kuti “munthu samapezamo m’Chipangano Chatsopano mawu aliwonse a Kristu osonyeza mmene udindo wa atumwi unati ukasamaliridwe.” Ndipo likuvomerezanso kuti “ulamuliro wa papa sunamvedwe mokwanira kapena kunenedwa mwa myaa m’Tchalitchi Chakumadzulo [Chachilatini]” kufikira zaka za zana lachisanu C.E.
Pakali pano dongosolo la ukulu la Tchalitchi cha Katolika likutokosedwa kuchokera kwa wachikulire kufikira ku wamng’ono. Ndicho chochititsa kugaŵanako, pamene abishopu, akatswiri a maphunziro a zaumulungu, ansembe, ndi anthu wamba afotokoza kusamvana kwawo poyera ndi papa pankhani za chikhulupiriro, makhalidwe, ndi kayendetsedwe ka tchalitchi. “Chilengezo cha pa Cologne” chinati: “Ngati papa asamalira zosakhala za mu ofesi yake, iye sangalimbikitse chimvero m’Chikatolika.”
Chogawanikana Mwandale Zadziko
Economist ya ku Briteni inanena motere: “Monga mmene ochilikiza Lefebvre akulingalira, tchalitchi chawo chakhala mnkhole wachinyengo chomwe chawapereka m’manja mwa Amarxist, okonda zamakono ndi Aprotesitanti. Monsignor Lefebvre akukhulupirira kuti Masinthidwe Achifrenchi anayambitsa zamakono ndi ufulu wochititsa chisoni m’dziko, ndikuti Vatican II njomwe inayambitsa Masinthidwe Achifrenchi . . . m’tchalitchi.” Akatolika omamatira kumwambo ambiri amagwirizana ndi lingaliroli. Komabe, Akatolika osamamatira kumwambo ngokonda kusintha mayanjano, ena amapita nazo patali ndi kuvomereza lamulo la kupanga masinthidwe ndi zida zankhondo. Chotero, ndale zadziko nchochititsa kugawanikana china pakati pa Akatolika.
Pomaliza nkhani yake yakuti “Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kugaŵanikana Kotereku Pakati pa Akristu?” wansembe Laurentin anati kuyera kwa Tchalitchi cha Katolika kukadalira pa kugwirizana kwake ndi mawu a Yesu akuti: “Kuli kukondana kwanu kwa wina ndi mnzake, kumene kudzazindikiritsa munthu aliyense kuti muli akuphunzira anga.”—Yohane 13:35, NJB.
Kugwiritsira ntchito maziko amenewo, Akatolika owona mtima ambiri padziko lonse afikira pakulingalira kuti kunena kwa Tchalitchi cha Katolika kwakuti ndicho tchalitchi chokha chowona nkopanda maziko. Ichi nchifukwa cha kuzindikira, monga mmeneso Yesu ananenera, kuti “palibe banja logawanikana lokha limene limakhalitsa,” ambiri athadi “kuchithawa” tchalitchicho.—Mateyu 12:25, NJB.
Akatolika ambirimbiri tsopano akufunafuna “banja” lopangidwa ndi Akristu owona, omwe ngogwirizana ndi chikondi chaubale weniweni ndi osagawanikana kaya ndi ziphunzitso zosakhala zam’malemba, kusagwirizana kwa akulu, kapena ndi malingaliro otsutsa andale zadziko. Anthu mamiliyoni ambiri apeza chimene ankafunafuna pamene anayamba kugwirizana ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 31]
Yesu anatsutsa Afarisi kaamba ka kukweza miyambo yawo pamwamba pa Mawu a Mulungu