Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 7/8 tsamba 28-29
  • “Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kuda Nkhaŵa Kwakukulu”?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kuda Nkhaŵa Kwakukulu”?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Akatolika Aufulu Ngakuda Nkhaŵa
  • Akatswiri a Maphunziro a Zaumulungu Osamvana
  • Akatolika Ambiri Ngozizwitsidwa
  • Kulekana Kwatsopano
    Galamukani!—1990
  • Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kugaŵanikana?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Umodzi Wachikristu Ngwothekera?
    Galamukani!—1991
  • Kupanikizidwa kwa Tchalitchi cha Katolika
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 7/8 tsamba 28-29

“Kodi Nchifukwa Ninji Pali Kuda Nkhaŵa Kwakukulu”?

PAPA JOHN PAUL II “anasoŵa chochita” ndi kulekana kwa gulu la Akibishopu Lefebvre la Chikatolika chamwambo. Iye anati, tchalitchi, pakumva izi “chinaipidwa kwenikweni.”

Wansembe Wachikatolika Joaquín Ortega, wachiŵiri kwa mlembi wa bungwe la abishopu a Roma Katolika mu Spanya, anamverera chisoni motere mkhalidwewo: “Tagwera ‘mumkupiti wa chiphunzitso cha Chikatolika.’ Anthu akusankha chowasangalatsa monga ngati ziphunzitso zathu zinali zachabechabe.”

Akibishopu Lefebvre adalingalirabe kuti Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican unawononga mwambo wa Tchalitchi cha Katolika, ndikuchititsa masinthidwe atchalitchiwo. Chotero, iye akulingalira kuti, msonkhanowo unakana chikhulupiriro chakuti Akatolika ngatchalitchi chowona.

Kuika zigomeko za Lefebvre ndi atsatiri ake mofupikira, International Herald Tribune inalemba kuti: “Omamatira ku mwambowo akutsutsa kuti mwinamwake tchalitchicho chinaphophonya msonkhanowo usanachitike, kapena kuti icho nchophophonya tsopano, komatu ziŵirizi sizingachitikire pamodzi. Ngati chinaphophonya msonkhanowo usanachitike, iwo akuti, pamenepo chiyenera kukhala chidalinso cholakwa m’ziphunzitso zina. ‘Ife tapangidwira kusonyeza kumamatira kwathu ku tchalitchi chanthaŵi zonse,’ anatero akibishopuyo.”

Komabe, Akatolika owona mtima ambiri akukaikira kaya chimene tchalitchi chinaphunzitsa ndi kulondola Vatican II isanakhale chinali chowona kapena chophophonya.

Akatolika Aufulu Ngakuda Nkhaŵa

Akatolika aufulu ambiri ngakuda nkhaŵa kuti chimene akuchilingalira kukhala masitepe opita patsogolo okhazikitsidwa pa Vatican II akudodometsedwa chifukwa cha machitachita a Lefebvre. Iwo awopsyedwa ndi ndemanga zaposachedwapa zochitidwa ndi mkulu wa Vatican, zonga ngati za Kadinala Ratzinger, mtetezi wa mwambo Wachikatolika. Iye ndiye wotsogolera wa oimira Vatican amene kwa zaka mazana anayi anatchedwa Mpingo wa Zilango Zankhanza Zoyera.

Kadinala Ratzinger, woyang’anira Mpingo Wopatulika kaamba ka Chiphunzitso cha Chikhulupiriro mu Roma, anati: “Malekano amadza kokha ngati anthu aleka kulondola ndikukonda zowonadi zakutizakuti ndi mapindu a chikhulupiriro Chachikristu.” Akatolika opita patsogolo akukaikira kuti mwinamwake kadinalayo ankakumbukira “zowonadi ndi mapindu” amene anazindikiritsa Tchalitchi cha Roma Katolika m’masiku akumbuyo Vatican II isanakhale.

Pofotokoza kukaikiraku, nkhani yokhala ndi mutu wakuti “Phindu la Kulekana,” yofalitsidwa m’nyuzipepala Yachifrenchi Le Monde, inati: “Ndani yemwe adziŵa ngati Vatican siinayambe—mosazindikira kapena mosavomereza—kulondola ‘mwambo mosaphatikiza Lefebvre’? . . . Kodi [Vatican] tsopano sikuyesera kukopanso atsogoleri achipembedzo okhoterera kumwambo ndi anthu wamba ndipo kuposa apa kukonzanso akuluakulu ndi makhalidwe Achikatolika kumene atokosedwa poyera, makamaka Kumadzulo kwa Yuropu ndi North America?”

Akatswiri a Maphunziro a Zaumulungu Osamvana

Mu January 1989, akatswiri amaphunziro a zaumulungu Achikatolika 163 a West Germany, Netherlands, Austria, ndi Switzerland anapereka chikalata chomwe tsopano chikutchedwa Chilengezo cha Cologne. M’milungu yotsatira, iwo anagwirizana ndi akatswiri amaphunziro a zaumulungu Achikatolika mazana angapo a m’maiko ena, kuphatikizapo Italiya. Kusamvana kwakukuluko kunachititsidwa ndi kuikidwa dala kwa mkulu woyanja mwambo wakalekale wa gululo kochitidwa ndi Vatican kukhala akibishopu wa Cologne, Jeremani, motsutsana ndi zokhumba akulu akumaloko. Koma kutipidwako kunachititsidwa ndi zina zosakhala kuikidwa kwa abishopu otsogolerawo. Iko kunaphatikizapo njira zotengedwa ndi Vatican zopereka chilango kuti afooketse akatswiri a maphunziro a zaumulungu omwe anasonyeza “malingaliro a maphunziro a zaumulungu amene Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican unagogomezera.” Akatswiri a maphunziro a zaumulungu anakaikiranso kuyenera kwa papa kwa kukakamiza malingaliro ake “m’chigawo cha kuphunzitsa ziphunzitso,” makamaka za kuchepetsa kubala.

Poyankha chilengezochi, Kadinala Ratzinger ananena mwagogogo kuti amene akana kaimidwe ka Vatican kokhudza kuchepetsa kubala ndi konena za chisudzulo akumasulira molakwika liwu lakuti “chikumbumtima” ndi “ufulu” ndipo akuswa kuphunzitsa kwamwambo kwa tchalitchi. Iye posachedwapa anakumbutsa akuluakulu a ku U.S. kuti asalole chiphunzitso chawo kusonkhezeredwa ndi “malingaliro olakwika” a akatswiri a maphunziro a zaumulungu.

Akatolika Ambiri Ngozizwitsidwa

Katswiri wa maphunziro a zaumulungu Wachifrenchi Wachikatolika pamene anafunsidwa ndi Le Monde analengeza kuti: “Kukakhala kulakwa kunena kuti . . . vuto iri likuyambukira akatswiri amaphunziro a zaumulungu okha. Iwo akulongosola kokha kuda nkhaŵa kwakukulu kwa Akatolika ambiri.”

Akatolika owona mtima ambiri akudabwa ngati akibishopu Lefebvre woukirayo, ngakhale kuti ngwochotsedwa mumpingo, sangakhale ‘adalephera kumenyanako komatu nkupambana nkhondoyo.’ Kwenikweni, kuyesayesa kukupangidwa kubwezeretsa m’khola atsatiri a Lefebvre. Misa ikunenedwanso m’chinenero cha Chilatini m’matchalitchi ambiri Achikatolika, ndipo abishopu oyanja mwambo wakalekale wa gululo akuikidwa m’mathayo. Mosangalatsa, Akatolika omamatira kumwambo akufunsa kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji Monsignor Lefebvre anachotsedwa mumpingo pamene ansembe Achikatolika mu Holland amene amadalitsa “kukwatirana” kwa ogonana ofanana ziŵalo ndi ansembe a ku South America omwe amachilikiza ufulu wa kusinthanso wa zaumulungu adakali mbali ya tchalitchi?’

Zonsezi zimapangitsa Akatolika ambiri kukhala osokonezeka. M’katolika Wachifrenchi analemba m’nyuzipepala Yachikatolika La Croix (Mtanda) kuti: “Akristu wamba, ngati ine, akuvutika chifukwa chakuti ophatikizidwawo [m’kusamvana kwa tchalitchi] sakukambitsirana zinthu ndikumvana. Anthu ena akuphonya machitachita achipembedzo, mwinatu Tchalitchi chomwe.”

Mosakaikira, anthu oterewa sangamvetsetse chifukwa chimene chomwe amachilingalira kukhala tchalitchi chowona chiri chogawanikana chotere. Ngakhale wansembe Wachikatolika René Laurentin anafunsa kuti: “Kodi nchifukwa ninji pali kugaŵanikana kotereku pakati pa Akristu?” Tiyeni tilingalire zifukwa zake mwachidule.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Omamatira kumwambowo akutsutsa kuti mwinamwake tchalitchicho chinaphophonya msonkhanowo usanachitike, kapena kuti icho nchophophonya tsopano, komatu ziŵirizi sizingachitikire pamodzi.”—International Herald Tribune.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena