Kulekana Kwatsopano
Ndi Mlembi wa Galamukani! mu Falansa
JUNE 30, 1988, idzakhala deti lokumbukirika m’zolembera za Tchalitchi cha Roma Katolika. Patsiku limenelo, akibishopu Wachifrenchi Marcel Lefebvre ananyoza Vatican. Iye anachita mwambo wopatulikitsa abishopu anayi pa seminale yake yamwambo Wachikatolika mu Switzerland. Kachitidweka kanachititsa kumchotsa Lefebvre ndi abishopu anayi atsopanowo mumpingo. Uku kunapanga kulekana koyamba m’Tchalitchi cha Katolika chiyambire 1870. M’chaka chimenecho otchedwa Akatolika Akalekale anapatuka ku tchalitchi choyambirira pankhani ya kusalakwa kwa papa.
Zochititsa Kupatukana
Kupatukana pakati pa Vatican ndi gulu loyanja mwambo wakalekale Wachikatolika la Akibishopu Lefebvre kunakhala kukuchitika mwakachetechete kwanthaŵi yaitali. Zochititsa kulekanako zinayambika kalekale pa Msonkhano Wachiŵiri wa Vatican, wochitidwa kuchokera mu 1962 mpaka 1965. Papa John XXIII, amene anaitanitsa msonkhanowo, anakhazikitsa zolinga ziŵiri za msonkhanowo. Chimodzi chinatchedwa aggiornamento (kuzipanga zatsopano), ndipo chinacho chinali kugwirizanitsanso matchalitchi onse otchedwa Achikristu.
Ngakhale kuti Akibishopu Lefebvre, monga mkulu Wachikatolika, anapezeka pa Vatican II, iye sanavomerezane ndi chirichonse cha zolinga zimenezi. Monga woumirira mwambo wakalekale, ncholinga chake kuti Tchalitchi cha Katolika sichimafunikira kukonzedwanso mwatsopano. Mwakumamatira ndi mtima wonse ku malingaliro amwambo Wachikatolika omwe amati “kunja kwa Tchalitchi kulibe chipulumuko,” Lefebvre ngokhutiritsidwa kuti njira yokha imene “Akristu” angagwirizanitsidwenso mothekera njakuti osakhala Akatolika onse amamatire ku chikhulupiriro cha Roma Katolika.
Motsutsana ndi Ufulu wa Chipembedzo
Chaka chimodzi pambuyo pakuchotsedwa kwake mumpingo, polankhulira Akatolika oyanja mwambo wakalekale wa gululo omwe amachilikiza gulu lake, Akibishopu Lefebvre analengeza kuti: “Monga gulu tiri otsutsana ndi lingaliro la ufulu wachipembedzo ndi zotulukapo zake, makamaka kusanganizana zipembedzo, komwe pandekha ndikukulingalira kukhala kosavomerezeka.”
Iye sanali kuyamba zatsopano. Ankatsatira mokhulupirika mwambo Wachikatolika. Pa August 15, 1832, Papa Gregory XVI anafalitsa chikalata chotchedwa Mirari vos, mmene iye anatsutsa ufulu wa chikumbumtima kukhala “lingaliro lolakwika, kapena mwinamwake kupenga.” Zaka makumi atatu mphambu ziŵiri pambuyo pake, Papa Pius IX anafalitsa Ndandanda yake ya Zophophonya, mmene iye anatsutsa lingaliro lakuti “munthu aliyense ngwaufulu kulandira ndi kuvomereza chipembedzo chimene, mwakulingalira kwake, amachikhulupirira kukhala chowona.”
Mwakukana kusanganizana zipembedzo, Akibishopu Lefebvre ankangosonyeza kumamatira kwake ku chimene chiphunzitso choikidwiratu cha Katolika chimachitcha “kukhalapo kwa Tchalitchi chimodzi,” ndiko kuti, pali kokha “[tchalitchi] cha Katolika Chimodzi, Choyera, ndi cha Atumwi.”
Kukwiyitsidwa ndi Misa “Yachiprotestanti”
Masinthidwe a malamulo amwambo Achikatolika obweretsedwa ndi Vatican II ndiko vuto lenileni kwa Akibishopu Lefebvre ndi atsatiri ake. Mkulu woukirayu amalingalira masinthidwewa kukhala anasandutsa Misa “kukhala Yachiprotesitanti.” Siiri nkhani yongogwiritsira ntchito zinenero zamakono m’malo mwa Chilatini; Lefebvre akulingalira kuti zambiri zasinthidwa ncholinga cha kukondweretsa Aprotestanti ndikuti ngakhale m’Chilatini malamulo ovomerezedwa ndi Papa Paul VI “ngampatuko.”
Kuti atsimikizire kuti Misa yamwambo Wachilatini ikupitirizidwa, Akibishopu Lefebvre anakhazikitsa seminale pa Ecône, Switzerland, mu 1970. Iyo inayang’aniridwa ndi Gulu la Ansembe a Pius X Woyera, imene Lefebvre anakhazikitsa chaka chimodzimodzicho. Pamene gulu lake linakula, iye anakhazikitsa maseminale ena a gulu loyanja mwambo wakalekale Wachikatolika m’Yuropu ndi maiko a Amereka. Anyamata awo mazana ambiri amalandira malangizo akuya aunsembe oyanja mwambo wakalekalewo.
Mkulu woukirayo waika ansembe amwambo oposadi 200, ngakhale kuti analetsedwa kuchita tero ndi Papa Paul VI mu 1976. Awa amakondwerera Misa Yachilatini m’nyumba zoyang’aniridwa ndi avirigo ndipo amasonkhanira m’matchalitchi Achikatolika opanda lamulo.a Vatican imavomereza kuti Lefebvre ali pafupifupi ndi atsatiri achangu amwambo zikwi zana limodzi padziko lonse, koma akuluakulu ena atchalitchi amati nambalayo ili pafupi ndi theka la miliyoni. Lefebvre iyemwini amati Akatolika mamiliyoni ambiri amavomerezana ndi malingaliro ake.
Kufunikira Mlowa Mmalo
M’tchalitchi cha Katolika, bishopu angaike ansembe. Komabe, papa yekha ndiye angavomereze kuikidwa kwa bishopu. Pofuna bishopu woika ansembe atsopano, Lefebvre wokalambayo anazindikira kuti Gulu la Ansembe ake linali pangozi yakutha iye atafa. Mwachiwonekere poyembekezera kuti ichi chingachitike, Vatican inalowa m’kukambitsirana kwakutali ndi iye, potsirizira pake inapereka chigamulo. Zinafunikira nzakuti iye avomereze kuikidwa kochitidwa ndi bishopu wovomerezedwa ndi Vatican kapena kuti ngati anapitiriza kuika bishopu iyemwini, iye akachotsedwa mumpingo.
Pa June 30, 1988, pachochitika chamwambo chosonkhanidwa ndi atsatiri ake zikwi zambiri, mkulu woukirayo anapatulikitsa mwamwambo abishopu anayi. Nyuzipepala ya ku Paris yotchedwa International Herald Tribune inasimba kuti: “Kachitidwe kopatulikitsa abishopu anayi kochitidwa ndi Akibishopu Lefebvre nkonyoza malamulo a Vatican omwe anatheketsa papa kukweza abishopu 24 ku Gulu la Akadinala. Vatican inachotsapo seŵero lapadera ncholinga cha kusamalira kachitidwe ‘komvetsa chisoni’ ka Akibishopu Lefebvre. ‘Nditsiku la maliro,’ anatero Kadinala [Wachifrenchi] Decourtray.”
Kulekana uku m’Tchalitchi cha Katolika sikunachititse chisoni m’Vatican mokha koma kwasiyanso Akatolika owona mtima mamiliyoni ambiri ali othedwa nzeru ndi kusokonezeka padziko lonse.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “The Rebel Archbishop,” yofalitsidwa m’kope la Awake! la December 22, 1987.